Salimo 125:1-5
Nyimbo Yokwerera Kumzinda.
125 Anthu amene amakhulupirira Yehova+Ali ngati phiri la Ziyoni, limene silingagwedezekeKoma lidzakhalapo mpaka kalekale.+
2 Mofanana ndi mapiri amene azungulira Yerusalemu,+Yehova wazungulira anthu ake,+Kuyambira panopa mpaka kalekale.
3 Ndodo yachifumu ya oipa sidzapitiriza kukhala padziko limene laperekedwa kwa anthu olungama,+Kuti olungamawo* asayambe kuchita zinthu zoipa.+
4 Inu Yehova, anthu abwino muwachitire zabwino,+Muchitire zabwino anthu owongoka mtima.+
5 Koma anthu amene apatuka panjira yabwino nʼkuyamba kuyenda mʼnjira zokhotakhota,Yehova adzawachotsa limodzi ndi anthu ochita zoipa.+
Mu Isiraeli mukhale mtendere.
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “manja a olungamawo.”