Salimo 29:1-11
Nyimbo ya Davide.
29 Mʼpatseni Yehova zimene akuyenera kulandira, inu ana a amphamvu,Mʼpatseni Yehova zimene akuyenera kulandira chifukwa cha ulemerero ndi mphamvu zake.+
2 Mʼpatseni Yehova ulemerero woyenera dzina lake.
Weramirani* Yehova mutavala zovala zopatulika zokongola.*
3 Mawu a Yehova akumveka pamwamba pa madzi,Mawu a Mulungu waulemerero akugunda ngati bingu.+
Yehova ali pamwamba pa madzi ambiri.+
4 Mawu a Yehova ndi amphamvu,+Mawu a Yehova ndi aulemerero.
5 Mawu a Yehova akuthyola mitengo ya mkungudza,Inde, Yehova akuthyolathyola mitengo ya mkungudza ya ku Lebanoni.+
6 Iye akuchititsa Lebanoni* kuti adumphedumphe ngati mwana wa ngʼombe,Komanso Sirioni+ kuti adumphedumphe ngati mwana wa ngʼombe yakutchire.
7 Yehova akamalankhula, mphenzi zimangʼanima.+
8 Mawu a Yehova akuchititsa kuti chipululu chiphiriphithe,+Yehova akuchititsa kuti chipululu cha Kadesi+ chiphiriphithe.
9 Mawu a Yehova akuchititsa kuti mbawala zazikazi ziphiriphithe kenako nʼkuberekaNdipo akuchititsa kuti munkhalango mukhale mopanda chilichonse.+
Ndipo onse mʼkachisi wake akunena kuti: “Ulemerero!”
10 Yehova wakhala pampando wake wachifumu pamwamba pa madzi osefukira,*+Yehova ndi Mfumu ndipo adzalamulira mpaka kalekale.+
11 Yehova adzapatsa anthu ake mphamvu.+
Yehova adzadalitsa anthu ake powapatsa mtendere.+
Mawu a M'munsi
^ Kapena kuti, “Lambirani.”
^ Mabaibulo ena amati, “chifukwa cha kukongola kwa chiyero chake.”
^ Zikuoneka kuti akunena za phiri la Lebanoni.
^ Kapena kuti, “pa nyanja yaikulu yakumwamba.”