BAIBULO LA DZIKO LATSOPANO LA MALEMBA OPATULIKA (LOKONZEDWANSO MU3 2023)

Kodi MʼBaibulo Muli Nkhani Zotani?

Chichewa
Kodi MʼBaibulo Muli Nkhani Zotani?
https://cms-imgp.jw-cdn.org/img/p/1001061100/univ/wpub/1001061100_univ_sqr_xl.jpg
nwt p. 5

Kodi MʼBaibulo Muli Nkhani Zotani?

MʼBaibulo muli uthenga wa Mulungu, kapena kuti mawu ake, omwe ndi ofunika kwa ife masiku ano. Baibulo limafotokoza zimene tingachite kuti zinthu zizitiyendera bwino ndiponso kuti tizisangalatsa Mulungu. Limayankhanso mafunso awa:

KODI MUNGAPEZE BWANJI MALEMBA MʼBAIBULO?

MʼBaibulo muli mabuku 66 ndipo lili ndi zigawo ziwiri. Chigawo choyamba (ena amati Chipangano Chakale) chinalembedwa mʼChiheberi ndi Chiaramu. Chigawo chachiwiri ndi cha Malemba a Chigiriki (ena amati Chipangano Chatsopano). Buku lililonse linagawidwa mʼmachaputala ndi mavesi. Mukapeza lemba, mudzaona kuti limayamba ndi dzina la buku kenako chaputala nʼkumaliza ndi vesi kapena mavesi. Mwachitsanzo, Genesis 1:1 likutanthauza kuti buku la Genesis chaputala 1 vesi 1.