Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Matanthauzo a Mawu Ena a MʼBaibulo

A B C D E F G H I K L M N O P R S T U W Y Z

A

 • A·selʹgei·a.​—

  Onani KHALIDWE LOPANDA MANYAZI.

 • Abi.

  Umenewu unali mwezi wa 5 pakalendala yopatulika ya Ayuda komanso mwezi wa 11 pakalendala ya anthu onse, Aisiraeli atabwera kuchokera ku ukapolo wa ku Babulo. Unkayambira pakati pa July mpaka pakati pa August. Dzinali silitchulidwa mʼBaibulo, koma amangoti “mwezi wa 5.” (Nu 33:38; Eza 7:9)—Onani Zakumapeto B15.

 • Abibu.

  Dzina lenileni la mwezi woyamba pakalendala yopatulika ya Ayuda komanso mwezi wa 7 pakalendala ya anthu onse. Dzinali limatanthauza “Maso Obiriwira (a Mbewu).” Mweziwu unkayambira pakati pa March mpaka pakati pa April. Ayuda atabwera kuchokera ku Babulo unayamba kutchedwa Nisani. (De 16:1)—Onani Zakumapeto B15.

 • Achipani cha Herode.​—

  Onani HERODE; ANTHU AMENE ANKATSATIRA HERODE.

 • Adara.

  Umenewu unali mwezi wa 12 pakalendala yopatulika ya Ayuda komanso mwezi wa 6 pakalendala ya anthu onse, Aisiraeli atabwera kuchokera ku ukapolo wa ku Babulo. Unkayambira pakati pa February mpaka pakati pa March. (Est 3:7)—Onani Zakumapeto B15.

 • Aepikureya.

  Anthu amene ankatsatira katswiri wina wa nzeru za anthu, dzina lake Epicurus (341-270 B.C.E.). Aepikureya ankalimbikitsa mfundo yakuti chofunika kwambiri pa moyo wa munthu nʼkusangalala.—Mac 17:18.

 • Afarisi.

  Kagulu kachipembedzo ka Chiyuda komwe kanalipo mu nthawi ya Yesu ndi atumwi. Sanali ansembe, koma ankatsatira kwambiri Chilamulo ngakhalenso timfundo take tingʼonotingʼono. Ankalemekezanso kwambiri miyambo ya makolo. (Mt 23:23) Afarisi ankatsutsa kwambiri miyambo ndi chikhalidwe cha Agiriki. Popeza anali akatswiri a Chilamulo ndi miyambo ya makolo, anali ndi mphamvu zambiri ndipo ankakonda kuuza anthu zochita. (Mt 23:2-6) Ena anali oweruza mʼKhoti Lalikulu la Ayuda. Nthawi zambiri ankatsutsa Yesu pa nkhani yosunga Sabata, miyambo ya makolo komanso kucheza ndi anthu ochimwa ndiponso okhometsa misonkho. Koma ena ngati Saulo wa ku Tarisi, anakhala Akhristu.—Mt 9:11; 12:14; Mko 7:5; Lu 6:2; Mac 26:5.

 • Akaya.

  MʼMalemba a Chigiriki a Chikhristu mawuwa amanena za chigawo chakumʼmwera kwa Girisi chomwe chinkalamuliridwa ndi Aroma ndipo likulu lake linali ku Korinto. (Mac 18:12)—Onani Zakumapeto B13.

 • Akerubi.

  Angelo audindo wapamwamba omwenso amagwira ntchito zapadera. Ndi osiyana ndi aserafi.—Ge 3:24; Eks 25:20; Yes 37:16; Ahe 9:5.

 • Akuluakulu a zamalamulo.

  Mʼboma la Ababulo, akuluakulu a zamalamulo anali anthu ogwira ntchito mʼboma amene ankadziwa bwino malamulo komanso ankaweruza milandu ina. Mʼzigawo zolamulidwa ndi Aroma, anthu amenewa ankakhala akuluakulu a boma. Ntchito zina zimene ankagwira zinali kukhazikitsa bata, kuyangʼanira za ndalama, kuweruza ophwanya malamulo komanso kulamula kuti anthu alangidwe.—Da 3:2; Mac 16:20.

 • Alamoti.

  Mawu onena za nyimbo otanthauza “Atsikana” ndipo mwina ankanena za mawu asapulano a atsikana. Nʼkuthekanso kuti ankasonyeza kuti nyimboyo iyenera kuimbidwa ndi mawu okwera.—1Mb 15:20; Sl 46:Kam.

 • Alefa ndi Omega.

  Mayina a chilembo choyamba ndi chomaliza mu afabeti ya Chigiriki. Mayina amenewa anagwiritsidwa ntchito limodzi maulendo atatu mʼbuku la Chivumbulutso ngati dzina laudindo la Mulungu. Mʼmavesiwa, mawuwa amatanthauza “woyamba ndi womaliza” komanso “chiyambi ndi mapeto.”—Chv 1:8; 21:6; 22:13.

 • Ame.

  “Zikhale momwemo,” kapena “ndithu.” Mawuwa akuchokera ku mawu a Chiheberi akuti, ’a·manʹ, omwe amatatanthauza “kukhulupirika, kudalirika.” “Ame” ankanenedwa povomereza lumbiro, pemphero kapena mfundo inayake. Mʼbuku la Chivumbulutso mawuwa amagwiritsidwa ntchito ngati dzina laudindo la Yesu.—De 27:26; 1Mb 16:36; Chv 3:14.

 • Amedi; Mediya.

  Mbadwa za mwana wa Yafeti dzina lake Madai. Zinkakhala kudera lamapiri la ku Iran ndipo dziko lawo linayamba kutchedwa Mediya. Amedi anagwirizana ndi Ababulo kuti agonjetse Asuri. Pa nthawiyo, Amedi ankalamuliranso chigawo cha Perisiya. Koma kenako Koresi anagalukira Amedi. Ufumu wa Mediya unagwirizana ndi ufumu wa Perisiya nʼkupanga ufumu wa Amedi ndi Aperisiya womwe unagonjetsa ufumu wa Babulo mu 539 B.C.E. Amedi ena analipo ku Yerusalemu pa Pentekosite mu 33 C.E. (Da 5:28, 31; Mac 2:9)—Onani Zakumapeto B9.

 • Ana a Aroni.

  Mbadwa za Aroni yemwe anali mdzukulu wa Levi. Aroni ndi amene anali woyamba kusankhidwa kuti akhale mkulu wa ansembe potsatira Chilamulo cha Mose. Ana a Aroni ankatumikira monga ansembe pachihema komanso pakachisi.—1Mb 23:28.

 • Anefili.

  Ana achiwawa amene angelo anabereka atakwatira ana aakazi a anthu Chigumula chisanachitike.—Ge 6:4.

 • Anetini.

  Anthu otumikira pakachisi omwe sanali Aisiraeli. Mawu ake a Chiheberi amatanthauza “Operekedwa,” kutanthauza kuti anaperekedwa kuti azitumikira pakachisi. Nʼkutheka kuti Anetini ambiri anali mbadwa za Agibiyoni amene Yoswa anawapatsa ntchito yoti “azitunga madzi ndi kutola nkhuni za Aisiraeli onse ndiponso zapaguwa lansembe la Yehova.”—Yos 9:23, 27; 1Mb 9:2; Eza 8:17.

 • Angelo.

  Pa Chiheberi ndi mal·ʼakhʹ, pa Chigiriki agʹge·los. Mawu onsewa amatanthauza “opereka uthenga,” koma akamanena za mizimu yopereka uthenga amagwiritsa ntchito mawu akuti “angelo.” (Ge 16:7; 32:3; Yak 2:25; Chv 22:8) Angelo ndi mizimu yamphamvu yomwe inalengedwa ndi Mulungu kale kwambiri anthu asanalengedwe. MʼBaibulo amatchulidwanso kuti “oyera masauzande masauzande,” “ana a Mulungu” komanso “nyenyezi zamʼmawa.” (De 33:2; Yob 1:6; 38:7) Anawalenga mmodzimmodzi ndipo sanawalenge kuti azibereka ana. Alipo oposa 100 miliyoni. (Da 7:10) Baibulo limasonyeza kuti angelo ali ndi makhalidwe osiyanasiyana ndipo aliyense ali ndi dzina. Iwo ndi odzichepetsa, salola kuti azilambiridwa ndipo nthawi zambiri sanena mayina awo. (Ge 32:29; Lu 1:26; Chv 22:8, 9) Ali ndi maudindo osiyanasiyana ndipo amapatsidwa ntchito zosiyanasiyana monga kutumikira kumpando wa Yehova, kupereka mauthenga, kuthandiza atumiki a Yehova apadziko lapansi, kupereka ziweruzo za Mulungu komanso kuthandiza pa ntchito yolalikira uthenga wabwino. (2Mf 19:35; Sl 34:7; Lu 1:30, 31; Chv 5:11; 14:6) Mʼtsogolomu adzathandiza Yesu kumenya nkhondo ya Aramagedo.—Chv 19:14, 15.

 • Anthu amene ankatsatira Herode.

  Amadziwikanso kuti “a chipani cha Herode.” Anali a chipani amene ankagwirizana ndi zolinga zandale za Aherode onse amene ankalamulira pansi pa ufumu wa Aroma. Nʼkutheka kuti Asaduki ena anali mʼchipani chimenechi. Anthu a chipani cha Herodewa anagwirizana ndi Afarisi potsutsa Yesu.—Mko 3:6.

 • Anthu otsatira nzeru za Sitoiki.

  Anthu amene ankaphunzira nzeru za Sitoiki ndipo ankakhulupirira kuti munthu amakhala wosangalala ngati amagwiritsa ntchito luso lake la kuganiza kuti amvetse malamulo amʼchilengedwe nʼkumawatsatira. Ankaonanso kuti munthu wanzeru sasonyeza kwenikweni kuti akumva ululu kapena wasangalala.—Mac 17:18.

 • Aramagedo.

  Pa Chiheberi Har Meghid·dohnʹ, kutanthauza “Phiri la Megido.” Mawuwa amagwiritsidwa ntchito ponena za “nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse” pamene “mafumu a dziko lonse lapansi kumene kuli anthu” adzasonkhane kuti amenyane ndi Yehova. (Chv 16:14, 16; 19:11-21)—Onani CHISAUTSO CHACHIKULU.

 • Aramu; Anthu a Chiaramu.

  Mbadwa za mwana wa Semu dzina lake Aramu zimene zinkakhala kumadera akumapiri a Lebanoni mpaka ku Mesopotamiya komanso kuchokera kumapiri a Tarasi chakumpoto kufika ku Damasiko nʼkumalowera chakumʼmwera. Dera limeneli, lomwe mʼChiheberi linkatchedwa Aramu, linayamba kudziwika kuti Siriya ndipo anthu ake ankatchedwa Asiriya.—Ge 25:20; De 26:5; Ho 12:12.

 • Areopagi.

  Phiri lalitali ku Atene, kumpoto chakumadzulo kwa Akuropolisi. Linalinso dzina la khoti limene anthu ankakumanako. Anthu ena a nzeru za Sitoiki ndi Epikureya anatenga Paulo nʼkupita naye kumeneko kuti akafotokoze zimene ankakhulupirira.—Mac 17:19.

 • Asaduki.

  Gulu lachipembedzo lotchuka la Chiyuda ndipo anthu ake ankakhala olemera, olamulira komanso ansembe. Asaduki ankayangʼanira zochitika zapakachisi. Iwo ankatsutsa miyambo komanso zikhulupiriro za Afarisi. Sankakhulupirira zoti akufa adzauka komanso zoti kuli angelo. Asaduki ankatsutsanso Yesu.—Mt 16:1; Mac 23:8.

 • Asamariya.

  Poyamba dzinali linali la Aisiraeli a mu ufumu wakumpoto wa mafuko 10 koma pambuyo pogonjetsedwa ndi Asuri mu 740 B.C.E., dzinali linayamba kuphatikizanso anthu a mitundu ina amene Asuri anawabweretsa kuderali. Pa nthawi ya Yesu, dzinali silinkanenanso za mtundu wa anthu kapena zokhudza ndale koma linkanena za anthu achipembedzo cha mbali ya kumene kunali Sekemu ndi Samariya. Anthu achipembedzo chimenechi ankakhulupirira zinthu zosiyana ndi zimene Ayuda ankakhulupirira.—Yoh 8:48.

 • Aserafi.

  Angelo amene amaima mozungulira mpando wachifumu wa Yehova kumwamba. Mawu a Chiheberi akuti sera·phimʹ amatanthauza “oyaka moto.”—Yes 6:2, 6.

 • Asia.

  MʼMalemba a Chigiriki a Chikhristu, dzinali limanena za chigawo cha Aroma chimene masiku ano ndi mbali yakumadzulo kwa dziko la Turkey komanso madera a zilumba za Samos ndi Patmos. Likulu lake linali ku Efeso. (Mac 20:16; Chv 1:4)—Onani Zakumapeto B13.

 • Asilikali Oteteza Mfumu.

  Gulu la asilikali a Chiroma amene ankateteza mfumu ya Aroma. Asilikali amenewa anali ndi mphamvu zambiri pothandiza kuti mfumu izilamulira kapena ichotsedwe pampando.—Afi 1:13.

 • Asitoreti.

  Mulungu wamkazi wa Akanani wa nkhondo komanso wobereketsa. Anali mkazi wa Baala.—1Sa 7:3.

 • Aterafi.

  Milungu ya banja kapena mafano ndipo anthu ankaigwiritsa ntchito kuti adziwe zinthu zina. (Eze 21:21) Ena ankakhala aakulu komanso ooneka ngati munthu pomwe ena ankakhala angʼonoangʼono. (Ge 31:34; 1Sa 19:13, 16) Zimene ofukula zinthu zakale anapeza ku Mesopotamia zimasonyeza kuti kukhala ndi aterafi kunkakhudza nkhani yolandira cholowa cha banja. (Mwina nʼchifukwa chake Rakele anatenga aterafi a bambo ake.) Zimenezi sizinkachitika ku Isiraeli. Komabe pa nthawi ya oweruza ndi mafumu anthu ena ankagwiritsa ntchito mafano a aterafi. Ndipo aterafi anali mʼgulu la zinthu zimene mfumu yokhulupirika Yosiya inaziwononga.—Owe 17:5; 2Mf 23:24; Ho 3:4.

 • Azazeli.

  Nʼkutheka kuti mawu ake a Chiheberi amatanthauza “Mbuzi Imene Imasowa.” Pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo, mbuzi ya Azazeli inkapititsidwa kuchipululu ndipo zinkaimira kuti mbuziyo yatenga machimo amene mtunduwo unachita chaka chapita ndipo yapita nawo.—Le 16:8, 10.

B

 • Baala.

  Mulungu wa Akanani amene ankaonedwa kuti ndi wobweretsa mvula, wobereketsa komanso mwini wa mlengalenga. Dzina lakuti “Baala” linkagwiritsidwanso ntchito ponena za milungu ina ingʼonoingʼono. Mawu ake a Chiheberi amatanthauza “Mwiniwake; Mbuye.”—1Mf 18:21; Aro 11:4.

 • Bango.

  Dzina la zomera zosiyanasiyana zimene zimamera mʼmadera omwe kumakhala madzi. Bango limene limatchulidwa mʼBaibulo ndi lotchedwa Arundo donax. (Yob 8:11; Yes 42:3; Mt 27:29; Chv 11:1)—Onani BANGO LOYEZERA.

 • Bango loyezera.

  Bangoli linali lalitali mikono 6. Tikatengera muyezo wa mkono umene ambiri ankagwiritsa ntchito, bangoli linali la mamita 2.67, koma tikatengera mkono wina wotalikirapo linali la mamita 3.11. (Eze 40:3, 5; Chv 11:1)—Onani Zakumapeto B14.

 • Belezebule.

  Dzinali limanena za Satana yemwe ndi kalonga kapena wolamulira wa ziwanda. Nʼkutheka kuti linasinthidwa kuchokera ku dzina lakuti Baala-zebabu, yemwe ndi Baala amene ankalambiridwa ndi Afilisiti ku Ekironi.—2Ki 1:3; Mt 12:24.

 • Botolo la Alabasitala.

  Dzina la timabotolo ta mafuta onunkhira timene tinkapangidwa kuchokera ku miyala yomwe inkapezeka kufupi ndi ku Alabastron, mʼdziko la Egypt. Nthawi zambiri mabotolowa ankakhala ndi khosi loningʼa lomwe ankalimata kuti mafuta a mtengo wapataliwa asamatayike. Kenako mwalawu unayamba kudziwikanso ndi dzina lomweli.—Mko 14:3.

 • Buli.

  Mwezi wa 8 pakalendala yopatulika ya Ayuda komanso mwezi wachiwiri pakalendala ya anthu onse. Dzinali linachokera ku mawu omwe amatanthauza “zokolola.” Mweziwu unkayambira pakati pa October mpaka pakati pa November. (Eks 29:18)—Onani Zakumapeto B15.

 • Bwalo.

  Malo a mkati mwa mpanda ndipo ankazungulira chihema chonse. Kenako anali malo a mkati mwa mpanda ozungulira nyumba yaikulu pakachisi. Guwa la nsembe zopsereza linali mʼbwalo la chihema komanso mʼbwalo lamkati la kachisi. (Onani Zakumapeto B5, Zakumapeto B8, Zakumapeto B11.) Baibulo limanenanso za mabwalo a nyumba za anthu ndi nyumba zachifumu.—Eks 8:13; 27:9; 1Mf 7:12; Est 4:11; Mt 26:3.

 • Bwanamkubwa.

  Munthu amene ankayangʼanira chigawo cholamulidwa ndi Aroma. Anali ndi mphamvu zoweruza milandu komanso kumenya nkhondo. Ngakhale kuti panali anthu ena amene ankaona ngati zomwe wasankha ndi zabwino kapena ayi, iye anali ndi mphamvu zambiri mʼchigawo chimene ankayangʼaniracho.—Mac 13:7; 18:12.

C

 • Chaka cha Ufulu.

  Chaka cha 50 chilichonse kuchokera pamene Aisiraeli analowa mʼDziko Lolonjezedwa. Chaka chimenechi Aisiraeliwo sankayenera kulima minda yawo komanso akapolo a Chiheberi ankayenera kumasulidwa. Malo amene anagulitsidwa ochokera kwa makolo ankayenera kubwezedwa. Tingati chaka chonse cha ufulu chinali chaka chachikondwerero. Anthu ankasangalala kuti alandiranso ufulu umene anali nawo pamene Mulungu anakhazikitsa mtunduwu.—Le 25:10.

 • Chakhumi.

  Limodzi mwa magawo 10 kapena kuti 10 peresenti ya zinthu, imene inkaperekedwa ngati mphatso makamaka pa zinthu zokhudza kulambira. (Mki 3:10; De 26:12; Mt 23:23) MʼChilamulo cha Mose, chakhumi cha zokolola kapena ziweto chinkaperekedwa kwa Alevi chaka chilichonse kuti azigwiritsa ntchito pa moyo wawo. Nawonso Alevi ankatenga chakhumi pa zimene alandirazo nʼkupereka kwa ansembe amʼbanja la Aroni kuti azigwiritsa ntchito pa moyo wawo. Pankakhalanso zakhumi zina zimene anthu ankapereka. Akhristu sanalamulidwe kuti azipereka chakhumi.

 • Chakudya Chamadzulo cha Ambuye.

  Chakudya chenicheni, chomwe ndi mikate yopanda zofufumitsa ndiponso vinyo, zomwe zimaimira thupi ndi magazi a Yesu. Mwambo wokumbukira imfa ya Yesu. Mwambowu umatchedwanso “Chikumbutso” chifukwa choti Malemba amalamula Akhristu kuti aziuchita chaka chilichonse.—1Ak 11:20, 23-26.

 • Chiaramu.

  Chilankhulo chofanana ndi Chiheberi ndipo afabeti yakenso ndi yofanana ndi ya Chiheberi. Poyamba chinkalankhulidwa ndi anthu a ku Aramu, koma kenako chinkagwiritsidwa ntchito ndi anthu a mu Ufumu wa Asuri ndi wa Babulo pa nkhani zamalonda. Chinalinso chilankhulo cha boma mu Ufumu wa Perisiya. (Eza 4:7) Mbali zina za buku la Ezara, Yeremiya ndi Danieli zinalembedwa mʼChiaramu.—Eza 4:8–6:18; 7:12-26; Yer 10:11, Da 2:4b–​7:28.

 • Chidindo.

  Chipangizo chodindira (padongo ndi zinthu zina) chomwe chinkasonyeza kuti chinthucho ndi chenicheni. Chinkasonyezanso umwini ndiponso mgwirizano. Zidindo zakale zinkakhala zolimba (za mwala, minyanga kapena mtengo) ndipo zojambula zake kapena zilembo zake ankazilemba chobwerera mʼmbuyo. Mawu akuti chidindo amagwiritsidwanso ntchito mophiphiritsa posonyeza kuti chinthu ndi chenicheni kapena chili ndi mwiniwake. Mawu amene anamasuliridwa kuti chidindo amanenanso za chinthu chimene chabisidwa kapena ndi chachinsinsi.—Eks 28:11; Ne 9:38; Chv 5:1; 9:4.

 • Chigiriki.

  Chilankhulo cha anthu a ku Girisi ndipo anthu akumeneko kapena amene makolo awo anachokera kumeneko amatchedwa Agiriki. MʼMalemba a Chigiriki a Chikhristu mawu akuti Agiriki amanenanso za anthu onse omwe si Ayuda kapena amene ankatengera chilankhulo ndi chikhalidwe cha Agiriki.—Yow 3:6; Yoh 12:20.

 • Chigololo.

  Mwamuna kapena mkazi wapabanja akagonana ndi munthu wina amene si mwamuna kapena mkazi wake mwa kufuna kwake.—Eks 20:14; Mt 5:27; 19:9.

 • Chiguduli.

  Nsalu yokhuthala yopangira masaka osungira mbewu. Chiguduli chinkapangidwa kuchokera ku ubweya wakuda wa mbuzi ndipo chinali chovala chimene anthu ankavala polira, mogwirizana ndi chikhalidwe chawo.—Ge 37:34; Lu 10:13.

 • Chigwa.

  Mawu amene amasuliridwa kuti chigwa angatanthauze chigwa chenicheni kapena mʼmbali mwa mtsinje momwe nthawi zambiri munkakhala mouma pa nyengo yotentha. Mawuwa angatanthauzenso mtsinje weniweniwo. Mitsinje ina inkalandira madzi kuchokera ku akasupe ndipo inkakhala ndi madzi kwa chaka chonse. Mʼmavesi ena mawuwa anamasuliridwa kuti “khwawa.”—Ge 26:19; Nu 34:5; De 8:7; 1Mf 18:5; Yob 6:15.

 • Chihema.

  Chitenti chimene Aisiraeli ankagwiritsa ntchito polambira pamene ankachoka ku Iguputo ndipo ankatha kuchinyamula. Munkakhala likasa la pangano la Yehova ndipo linali umboni wakuti Mulungu ali nawo. Aisiraeli ankapereka nsembe komanso kulambira kuchihemako. Nthawi zina chimatchulidwa kuti “chihema chokumanako.” Anachipanga ndi matabwa nʼkuchikuta ndi nsalu komanso kuchikongoletsa ndi akerubi. Chinali ndi zipinda ziwiri, choyamba chinkatchedwa Malo Oyera ndipo chachiwiri chinkatchedwa Malo Oyera Koposa. (Yos 18:1; Eks 25:9)—Onani Zakumapeto B5.

 • Chihema chokumanako.

  Mawuwa amanena za chihema cha Mose komanso chihema chopatulika chimene chinamangidwa mʼchipululu.—Eks 33:7; 39:32.

 • Chikhatho.

  Muyezo umenewu ankayeza kuchokera kumapeto kwa chala chachikulu kukafika kumapeto kwa chala chachingʼono, dzanja likakhala lotambasula. Popeza mkono unkakhala masentimita 44.5, ndiye kuti chikhatho chinkakhala masentimita 22.2. (Eks 28:16; 1Sa 17:4)—Onani Zakumapeto B14.

 • Chikole.

  Munthu akabwereka ndalama ankapereka chinthu chake ngati chikole potsimikizira kuti adzabweza ndalamayo. MʼChilamulo cha Mose munali malamulo ena okhudza chikole amene ankateteza anthu ovutika.—Eks 22:26; Eze 18:7.

 • Chikondi chokhulupirika.

  Nthawi zambiri mawuwa amamasuliridwa kuchokera ku mawu a Chiheberi akuti cheʹsedh, omwe amatanthauza chikondi chimene chimasonyezedwa chifukwa cha kudzipereka, kukhulupirika komanso kugwirizana kwambiri. Kawirikawiri mawuwa amagwiritsidwa ntchito ponena za chikondi chimene Mulungu amasonyeza anthu, koma amanenanso za chikondi cha pakati pa anthu.—Eks 34:6; Ru 3:10.

 • Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa.

  Chimodzi mwa zikondwerero zitatu zimene Aisiraeli ankachita chaka chilichonse. Chinkayamba pa Nisani 15, pambuyo pa tsiku la Pasika ndipo chinkachitika kwa masiku 7. Anthu ankadya mikate yopanda zofufumitsa yokha pokumbukira ulendo wawo wochoka ku Iguputo.—Eks 23:15; Mko 14:1.

 • Chikondwerero cha Misasa.

  Chinkatchedwanso kuti Chikondwerero cha Mahema kapena Chikondwerero cha Zokolola. Chinkachitika mʼmwezi wa Etanimu kuyambira pa 15 mpaka pa 21. Aisiraeli ankachita chikondwererochi akamaliza kukolola zinthu zawo mʼmunda ndipo inali nthawi yachisangalalo komanso yothokoza Yehova chifukwa chowapatsa zokolola. Pa nthawi ya chikondwererochi anthu ankakhala mʼmisasa kuti azikumbukira ulendo wawo wochoka ku Iguputo. Chinali chimodzi mwa zikondwerero zimene amuna ankafunika kukachita nawo ku Yerusalemu.—Le 23:34; Eza 3:4.

 • Chikondwerero cha Zokolola; Chikondwerero cha Masabata.​—

  Onani PENTEKOSITE.

 • Chikondwerero Chopereka Kachisi kwa Mulungu.

  Chaka chilichonse pa tsikuli ankakumbukira kuyeretsa kachisi pambuyo poti anadetsedwa ndi Antiochus Epiphanes. Chinkayamba pa 25 mʼmwezi wa Kisilevi ndipo chinkachitika kwa masiku 8.—Yoh 10:22.

 • Chilamulo.

  Mawuwa akalembedwa ndi “C” wamkulu amanena za Chilamulo cha Mose kapena mabuku 5 oyambirira a mʼBaibulo. Koma akalembedwa ndi “c” wamngʼono amanena za malamulo osiyanasiyana a mʼChilamulo cha Mose kapena mfundo ya mulamulo linalake.—Nu 15:16; De 4:8; Mt 7:12; Aga 3:24.

 • Chilamulo cha Mose.

  Malamulo amene Yehova anapereka kwa Aisiraeli kudzera mwa Mose mʼchipululu cha Sinai mu 1513 B.C.E. Mabuku 5 oyambirira a mʼBaibulo amatchulidwanso kuti Chilamulo.—Yos 23:6; Lu 24:44.

 • Chimulu cha Dothi.

  MʼChiheberi, “Millo” ndipo mawuwa amachokera ku mawu otanthauza “kudzaza.” Baibulo la Septuagint linawamasulira kuti “malo okhala ndi mpanda wolimba kwambiri.” Nʼkutheka kuti anali malo kapena chinthu chochita kumangidwa mu Mzinda wa Davide, koma sichikudziwika kuti chinali chotani.—2Sa 5:9; 1Mf 11:27.

 • Chinsinsi chopatulika.

  Mbali ya cholinga chimene Mulungu ali nacho ndipo Mulunguyo ndi amene anachiyambitsa. Chinali chobisika mpaka nthawi yochiulula itafika ndipo ankachiulula kwa anthu okhawo amene iye wafuna kuwaululira.—Mko 4:11; Akl 1:26.

 • Chipilala.

  Chinthu chokhala ngati nsanamira. Zipilala zina zinkamangidwa pokumbukira zinthu zinazake zimene zinachitika. Kachisi komanso nyumba zina zimene Solomo anamanga zinali ndi zipilala. Anthu osalambira Mulungu ankamanga zipilala nʼkumazigwiritsa ntchito polambira milungu yawo yabodza ndipo Aisiraeli ena ankachitanso zimenezi. (Owe 16:29; 1Mf 7:21; 14:23)—Onani MUTU WA CHIPILALA.

 • Chipilala chopatulika.

  Chinthu chooneka ngati nsanamira chomwe nthawi zambiri ankachipanga ndi miyala. Zikuoneka kuti ankachipanga ngati maliseche a mwamuna ndipo chinkaimira Baala kapena milungu ina yabodza.—Eks 23:24.

 • Chisautso chachikulu.

  Mawu a Chigiriki amene anamasuliridwa kuti “chisautso,” amanena za kuvutika kapena kusowa mtendere chifukwa chopanikizika ndi mavuto enaake. Yesu ananena kuti ku Yerusalemu kudzakhala “chisautso chachikulu” chimene sichinachitikepo. Koma ananenanso makamaka za “chisautso chachikulu” chimene chidzachitike padzikoli iyeyo atatsala pangʼono ‘kubwera ndi ulemerero waukulu.’ (Mt 24:21, 29-31) Paulo ananena kuti chisautsochi chidzakhala chiweruzo cholungama chimene Mulungu adzapereke kwa anthu “osadziwa Mulungu komanso kwa anthu amene samvera uthenga wabwino” wonena za Yesu Khristu. Chaputala 19 cha Chivumbulutso chimasonyeza kuti Yesu ndi amene adzatsogolere magulu ankhondo akumwamba pomenyana ndi “chilombo, mafumu a dziko lapansi ndi asilikali awo.” (2At 1:6-8; Chv 19:11-21) Baibulo limasonyeza kuti a “khamu lalikulu” adzapulumuka chisautso chimenechi. (Chv 7:9, 14)—Onani ARAMAGEDO.

 • Chisonga chotosera.

  Ndodo yosongoka kumapeto imene alimi ankagwiritsa ntchito potsogolera nyama. Mawuwa amagwiritsidwanso ntchito ponena za mawu a munthu wanzeru amene amalimbikitsa munthu kutsatira malangizo othandiza. Mawu akuti “kuponya miyendo nʼkumamenya zisonga zotosera” akuchokera pa zimene ngʼombe yamakani inkachita posafuna kutsogoleredwa. Inkaponya miyendo kuti imenye ndodoyi, koma zotsatira zake zinali zoti inkadzivulaza.—Mac 26:14; Owe 3:31.

 • Chitsamba chowawa.

  Zitsamba zowawa kwambiri koma zonunkhira bwino. MʼBaibulo mawuwa amagwiritsidwanso ntchito mophiphiritsa pofotokoza mavuto owawa kwambiri amene munthu amakumana nawo chifukwa chochita chiwerewere komanso chifukwa cha ukapolo, kupanda chilungamo ndi mpatuko. Pa Chivumbulutso 8:11, mawu akuti “chitsamba chowawa” amanena za chakumwa china chowawa kwambiri komanso chapoizoni (chotchedwa absinthe).—De 29:18; Miy 5:4; Yer 9:15; Amo 5:7.

 • Chivundikiro chophimbira machimo.

  Chinthu chophimbira likasa la pangano chimene mkulu wa ansembe ankachiwaza magazi pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo. Mawu ake a Chiheberi amanena za “kuphimba (machimo)” kapena “kufufuta (machimo).” Chivundikirochi chinkapangidwa ndi golide ndipo chinali ndi kerubi mmodzi mbali ina wina mbali ina. Nthawi zina chimangotchedwa “chivundikiro.” (Eks 25:17-22; 1Mb 28:11; Ahe 9:5)—Onani Zakumapeto B5.

 • Chiwerewere.

  Mawu ake a Chigiriki ndi akuti por·neiʹa, ndipo amagwiritsidwa ntchito mʼMalemba ponena za zinthu zokhudza kugonana zimene Mulungu amaletsa. Mawuwa amanena za chigololo, uhule, kugonana kwa anthu omwe sali pabanja, kugonana kwa amuna kapena akazi okhaokha komanso kugonana ndi nyama. Amagwiritsidwanso ntchito mophiphiritsa mʼbuku la Chivumbulutso ponena za hule lachipembedzo lotchedwa “Babulo Wamkulu” chifukwa choti amagwirizana ndi olamulira amʼdzikoli pofuna kupeza mphamvu komanso chuma. (Chv 14:8; 17:2; 18:3; Mt 5:32; Mac 15:29; Aga 5:19)—Onani HULE.

 • Chizindikiro.

  Chinthu chomwe nthawi zambiri chinkaonekera ndipo chinkakhala umboni wa zinazake, kaya za nthawi yomweyo kapena zamʼtsogolo.—Ge 9:12, 13; 2Mf 20:9; Mt 24:3; Chv 1:1.

 • Chizindikiro chopatulika cha kudzipereka.

  Chitsulo chonyezimira chagolide woyenga bwino chomwe ankalembapo mochita kugoba mawu a mʼChiheberi akuti “Yehova ndi Woyera.” Chizindikirochi chinkaikidwa patsogolo pa nduwira ya mkulu wa ansembe. (Eks 39:30)—Onani Zakumapeto B5.

 • Chodetsedwa.

  Mawuwa anganene za kuda kwenikweni kapena kusakhala ndi makhalidwe abwino. Komabe mʼBaibulo, nthawi zambiri mawuwa amanena za chinthu chosavomerezeka komanso chomwe si choyera mogwirizana ndi Chilamulo cha Mose. (Le 5:2; 13:45; Mt 10:1; Mac 10:14; Aef 5:5)—Onani KUYERA.

 • Chokolo.

  Mwambo umene patapita nthawi unadzaikidwa mʼChilamulo cha Mose. Ngati mwamuna wamwalira opanda mwana, mchimwene wake ankakwatira mkazi wotsalayo kuti amuberekere ana nʼcholinga choti dzina la mʼbale wakeyo lisathe. Unkatchedwanso ukwati wapachilamu.—Ge 38:8; De 25:5.

 • Chopondera mphesa.

  Nthawi zambiri ankakhala maenje awiri opangidwa pamwala walaimu. Dzenje lina linkakhala pamwamba, lina mmunsi ndipo pankakhala kangalande kolumikiza maenjewo. Anthu akamaponda mphesa mʼdzenje lalikululo, madzi ake ankapita mʼdzenje lalingʼono. Mawuwa amagwiritsidwanso ntchito mophiphiritsa ponena za chiweruzo cha Mulungu.—Yes 5:2; Chv 19:15.

 • Chovala pachifuwa.

  Chovala chokhala ndi miyala yamtengo wapatali chimene mkulu wa ansembe wa Aisiraeli ankavala pachifuwa popita ku Malo Oyera. Chinkatchedwa “chovala pachifuwa chachiweruzo” chifukwa chakuti chinkakhala ndi Urimu ndi Tumimu zomwe zinkagwiritsidwa ntchito pofuna kudziwa chiweruzo cha Yehova. (Eks 28:15-30)—Onani Zakumapeto B5.

 • Choyera.

  MʼBaibulo, mawuwa samangonena za ukhondo. Amanenanso za kupewa chilichonse chodetsa pa nkhani ya makhalidwe ndiponso moyo wauzimu. MʼChilamulo cha Mose, mawuwa ankanenanso za kudziyeretsa potsatira mwambo.—Le 10:10; Sl 51:7; Mt 8:2; 1Ak 6:11.

 • Chuku.

  Matenda a mbewu oyambitsidwa ndi mafangasi. Ena amati chuku chotchulidwa mʼBaibulo chinkachititsa mbewu kukhala ngati zili ndi dzimbiri lakuda (Puccinia graminis).—1Mf 8:37.

D

 • Dagoni.

  Mulungu wa Afilisiti. Sizikudziwika kuti dzinali linachokera pa mawu ati, koma akatswiri ena amanena kuti limagwirizana ndi mawu a Chiheberi akuti dagh (nsomba).—Owe 16:23; 1Sa 5:4.

 • Dalakima.

  MʼMalemba a Chigiriki a Chikhristu imeneyi inali ndalama yasiliva yomwe inkalemera magalamu 3.4. Malemba a Chiheberi amatchulanso za dalakima yagolide ya mʼnthawi ya Aperisiya yomwe ndi yofanana ndi dariki. (Ne 7:70; Mt 17:24)—Onani Zakumapeto B14.

 • Dama.​—

  Onani CHIWEREWERE.

 • Dariki.

  Ndalama yagolide ya ku Perisiya yomwe inkalemera magalamu 8.4. (1Mb 29:7)—Onani Zakumapeto B14.

 • Dekapoli.

  Dzina la mizinda ya Agiriki yomwe inalipo 10 (kuchokera ku mawu a Chigiriki akuti deʹka, kutanthauza “10,” ndi poʹlis, “mzinda”). Linalinso dzina la dera lakumʼmawa kwa nyanja ya Galileya ndi mtsinje wa Yorodano kumene kunali ina mwa mizindayi. Anthu a chikhalidwe cha Agiriki ankakhala mʼmizinda imeneyi komanso kuchitiramo malonda. Yesu anadutsapo mʼdera limeneli koma palibe umboni wakuti analowa mʼmizindayi. (Mt 4:25; Mko 5:20)—Onani Zakumapeto A7 ndi B10.

 • Dinari.

  Ndalama yasiliva ya Aroma yomwe inkalemera magalamu 3.85 ndipo inali ndi chithunzi cha Kaisara mbali imodzi. Anali malipiro a ganyu ya tsiku limodzi komanso ndalama ya msonkho umene Aroma ankafuna kuti Ayuda azipereka. (Mt 22:17; Lu 20:24)—Onani Zakumapeto B14.

 • Dipo.

  Ndalama kapena zinthu zina zoperekedwa pofuna kumasula munthu ku ukapolo, chilango, kuvutika, uchimo kapena udindo. (Yes 43:3) Dipo linkafunika pa zochitika zosiyanasiyana. Mwachitsanzo, ku Isiraeli ana aamuna oyamba kubadwa a anthu kapena a ziweto anali a Yehova choncho pankafunika kuwaperekera dipo kuti amasuke ndipo asakhalenso oyenera kumangogwira ntchito ya Yehova basi. (Nu 3:45, 46; 18:15, 16) Ngati munthu sanasamalire bwino ngʼombe yake ndipo yapha munthu, mwiniwake wa ngʼombeyo ankafunika kupereka dipo kuti asaphedwe. (Eks 21:29, 30) Koma panalibe dipo lowombolera munthu wopha mnzake mwadala. (Nu 35:31) Baibulo limanena za dipo lofunika kwambiri limene Khristu anapereka pololera kufa nʼcholinga choti amasule anthu omvera ku uchimo ndi imfa.—Sl 49:7, 8; Mt 20:28; Aef 1:7.

 • Dzombe.

  Ziwala zimene zimayenda mʼchigulu. Chilamulo cha Mose sichinkaletsa kudya dzombe. Dzombe linkakhala mliri ngati lilipo lambirimbiri komanso likuwononga zinthu zambiri.—Eks 10:14; Mt 3:4.

E

 • Edomu.

  Dzina lina la Esau, mwana wa Isaki. Mbadwa za Esau (Edomu) zinkakhala kudera lamapiri la Seiri lomwe linali pakati pa Nyanja Yakufa ndi gombe la Akaba. Kenako derali linayamba kudziwika kuti Edomu. (Ge 25:30; 36:8)—Onani Zakumapeto B3 ndi Zakumapeto B4.

 • Efa.

  Muyezo wa zinthu monga ufa ndi tirigu komanso choyezera chenichenicho. Muyezowu unali wofanana ndi wa mtsuko woyezera ndipo unali pafupifupi malita 22. (Eks 16:36; Eze 45:10)—Onani Zakumapeto B14.

 • Efodi.

  Chovala changati epuloni chimene ansembe ankavala. Efodi wa mkulu wa ansembe anali wapadera ndipo anali ndi chapachifuwa chokhala ndi miyala 12 yamtengo wapatali. (Eks 28:4, 6)—Onani Zakumapeto B5.

 • Efuraimu.

  Dzina la mwana wachiwiri wa Yosefe. Kenako linadzakhala dzina la fuko lina la Isiraeli. Ufumu wa Isiraeli utagawika, fuko la Efuraimu linali lotchuka kwambiri moti linkaimira ufumu wonse wa mafuko 10.—Ge 41:52; Yer 7:15.

 • Eluli.

  Umenewu unali mwezi wa 6 pakalendala yopatulika ya Ayuda komanso mwezi wa 12 pakalendala ya anthu onse, Aisiraeli atabwera kuchokera ku ukapolo wa ku Babulo. Unkayambira pakati pa August mpaka pakati pa September. (Ne 6:15)—Onani Zakumapeto B15.

 • Etanimu.

  Umenewu unali mwezi wa 7 pakalendala yopatulika ya Ayuda komanso mwezi woyamba pakalendala ya anthu onse. Unkayambira pakati pa September mpaka pakati pa October. Ayuda atabwera kuchokera ku Babulo, mweziwu unayamba kutchedwa Tishiri. (1Mf 8:2)—Onani Zakumapeto B15.

F

 • Fano; Kulambira mafano.

  Fano ndi chifaniziro cha chinthu chenicheni kapena chongoyerekezera chimene anthu amagwiritsa ntchito polambira. Kulambira mafano kumatanthauza kupereka ulemu, kukonda komanso kulambira chifaniziro.—Sl 115:4; Mac 17:16; 1Ak 10:14.

 • Farao.

  Dzina laudindo la mafumu a ku Iguputo. Baibulo limatchula mayina a Afarao 5 (Sisaki, So, Tirihaka, Neko ndi Hofira) koma Afarao ena sanatchulidwe mayina. Ena omwe sanatchulidwe mayinawo ndi amene nkhani zawo zimakhudza Abulahamu, Mose ndi Yosefe.—Eks 15:4; Aro 9:17.

 • Fatomu.

  Muyezo woyezera kuya kwa madzi ndipo ndi wofanana ndi mamita 1.8. (Mac 27:28)—Onani Zakumapeto B14.

 • Filisitiya; Afilisiti.

  Dera lakumʼmwera kwa Isiraeli linayamba kutchedwa Filisitiya ndipo anthu a ku Kerete amene ankakhala kumeneko ankatchedwa Afilisiti. Davide anawagonjetsa koma anapitirizabe kudzilamulira ndiponso kukhala adani a Aisiraeli. (Eks 13:17; 1Sa 17:4; Amo 9:7)—Onani Zakumapeto B4.

 • Firate.

  Mtsinje wautali komanso wofunika kwambiri wakumʼmwera kwa Asia ndipo unali umodzi mwa mitsinje ikuluikulu ya ku Mesopotamia. Mtsinjewu umatchulidwa koyamba pa Genesis 2:14 kuti unali umodzi mwa mitsinje 4 ya mu Edeni. Nthawi zambiri umangotchulidwa kuti “Mtsinje.” (Ge 31:21) Mtsinjewu unali malire akumpoto kwa dziko limene Aisiraeli anapatsidwa. (Ge 15:18; Chv 16:12)—Onani Zakumapeto B2.

G

 • Galeta.

  Ngolo ya matayala awiri yokokedwa ndi mahosi ndipo nthawi zambiri inkagwiritsidwa ntchito kunkhondo.—Eks 14:23; Owe 4:13; Mac 8:28.

 • Gehena.

  Mawu ake a Chigiriki amanena za Chigwa cha Hinomu chomwe chinali kumʼmwera komanso kumʼmwera chakumadzulo kwa Yerusalemu wakale. (Yer 7:31) Ulosi wina unanena kuti amenewa ndi malo amene mitembo ingatayidweko. (Yer 7:32; 19:6) Palibe umboni wakuti ankaponyako nyama kapena anthu amoyo nʼcholinga choti apse kapena azizunzika. Choncho malowa sakuimira malo enaake osaoneka kumene mizimu ya anthu imazunzidwa pamoto mpaka kalekale. Mʼmalomwake, Yesu ndi ophunzira ake anagwiritsa ntchito mawu akuti Gehena ponena mophiphiritsira za “imfa yachiwiri” yomwe imaimira kuphedwa, osadzakhalakonso mpaka kalekale.—Chv 20:14; Mt 5:22; 10:28.

 • Gera.

  Muyezo wa kulemera kwa zinthu ndipo unali wofanana ndi magalamu 0.57. Magera 20 ankakwana sekeli imodzi. (Le 27:25)—Onani Zakumapeto B14.

 • Giliyadi.

  Kwenikweni dzinali limanena za dera lachonde lomwe linali kumʼmawa kwa Yorodano ndipo linkafika kumpoto ndi kumʼmwera kwa chigwa cha Yaboki. Koma nthawi zina dzinali linkagwiritsidwa ntchito ponena za chigawo chonse cha Isiraeli chakumʼmawa kwa Yorodano kumene kunkakhala fuko la Rubeni, la Gadi komanso hafu ya fuko la Manase. (Nu 32:1; Yos 12:2; 2Mf 10:33)—Onani Zakumapeto B4.

 • Gititi.

  Mawuwa ndi okhudza nyimbo koma tanthauzo lake silikudziwika. Zikuoneka kuti akuchokera ku mawu a Chiheberi akuti gath. Ena amakhulupirira kuti mawuwa amanena za nyimbo yokhudza kupanga vinyo chifukwa chakuti mawu oti gath amatanthauza mopondera mphesa.—Sl 81:Kam.

 • Goli.

  Mtengo umene anthu ankanyamula paphewa nʼkukoleka katundu mbali zonse. Pena unkakhala mtengo umene ankaika pakhosi pa nyama (nthawi zambiri inkakhala ngʼombe) kuti zizikoka ngolo kapena zinthu zina. Popeza akapolo ankagwiritsa ntchito magoli ponyamula katundu wolemera, mawu akuti goli amagwiritsidwanso ntchito mophiphiritsa ponena za ukapolo, kugonjera munthu wina, kuponderezedwa komanso kuvutika. Mawu akuti kuchotsa kapena kuthyola goli ankatanthauza kumasula munthu kuti asakhalenso kapolo, asaponderezedwenso kapena asadyeredwenso masuku pamutu.—Le 26:13; Mt 11:29, 30.

 • Gulaye.

  Chingwe choponyera miyala chomwe chinkapangidwa ndi mlulu, zikopa kapena minyewa ndi ubweya wa nyama. Pakati pake pankakhala potambalala ndipo ndi pomwe ankaikapo choponyera chomwe nthawi zambiri unkakhala mwala. Mbali imodzi ya gulaye ankaimangirira pamkono ndipo mbali inayo ankaigwira, nʼkuisiya poponya. Pagulu la asilikali akale pankakhalanso oponya gulaye.—Owe 20:16; 1Sa 17:50.

 • Gulu lampatuko.

  Gulu la anthu limene limatsatira mfundo zinazake kapena mtsogoleri winawake ndipo limakhala ndi zikhulupiriro zake. Mawuwa amagwiritsidwa ntchito ponena za magulu awiri a Chiyuda, Afarisi ndi Asaduki. Anthu omwe sanali Akhristu ankanena kuti Akhristu ndi “gulu lampatuko” kapena “gulu lampatuko la anthu a ku Nazareti” mwina poona kuti linachoka mʼchipembedzo cha Chiyuda. Patapita nthawi magulu ampatuko anayambika mumpingo wa Chikhristu. Mwachitsanzo buku la Chivumbulutso limanena za “mpatuko wa Nikolao.”—Mac 5:17; 15:5; 24:5; 28:22; Chv 2:6; 2Pe 2:1.

 • Gumbwa.

  Zomera zofanana ndi bango zomwe ankagwiritsa ntchito popanga zinthu monga mabasiketi, nsengwa ndi maboti. Zinkagwiritsidwanso ntchito popanga zinthu zolembapo zokhala ngati mapepala zomwe ankapangira mipukutu.—Eks 2:3.

 • Guwa.

  Malo okwera opangidwa ndi dothi, miyala, chimwala kapena mitengo yokutidwa ndi chitsulo amene ankawagwiritsa ntchito polambira. Pamalowa ankaperekerapo nsembe zonunkhira komanso nsembe zina. Mʼchipinda choyamba cha chihema komanso cha kachisi munali “guwa lansembe lagolide” lalingʼono loperekerapo nsembe zonunkhira. Linapangidwa ndi matabwa okutidwa ndi golide. “Guwa lansembe lakopa” lalikulu loperekerapo nsembe zina linali pabwalo. (Eks 27:1; 39:38, 39; Ge 8:20; 1Mf 6:20; 2Mb 4:1; Lu 1:11)—Onani Zakumapeto B5 ndi B8.

H

 • Hades.

  Mawu a Chigiriki amene amafanana tanthauzo ndi mawu a Chiheberi akuti “Sheol.” Amamasuliridwa kuti “Manda” (“M” wamkulu), pofuna kusonyeza kuti amenewa ndi manda a anthu onse.—Onani MANDA.

 • Heme.

  Mulungu wa Agiriki, mwana wa Zeu. Anthu a ku Lusitara analakwitsa nʼkumatchula Paulo kuti Heme poganiza kuti iye ndi mulungu wawoyo. Iwo ankakhulupirira kuti mulungu ameneyu ankapereka uthenga wochokera kwa milungu komanso ankathandiza anthu kuti azilankhula mwaluso.—Mac 14:12.

 • Herode.

  Dzina la mafumu a kubanja limene linasankhidwa ndi Aroma kuti lizilamulira Ayuda. Herode Wamkulu anatchuka chifukwa chomanganso kachisi wa ku Yerusalemu komanso chifukwa cholamula kuti ana aphedwe pofuna kupha Yesu. (Mt 2:16; Lu 1:5) Herode Arikelawo ndi Herode Antipa anali ana a Herode Wamkulu ndipo anapatsidwa zigawo zina za ufumu wa bambo awo kuti azilamulira. (Mt 2:22) Antipa anali bwanamkubwa amene ankatchulidwanso kuti “mfumu” ndipo ndi amene ankalamulira pa zaka zitatu ndi hafu zimene Yesu anachita utumiki wake padzikoli, mpaka nthawi ya zochitika za mʼMachitidwe chaputala 12. (Mko 6:14-17; Lu 3:1, 19, 20; 13:31, 32; 23:6-15; Mac 4:27; 13:1) Kenako Herode Agiripa Woyamba, mdzukulu wa Herode Wamkulu, anaphedwa ndi mngelo wa Mulungu atangolamulira kwa nthawi yochepa. (Mac 12:1-6, 18-23) Zitatero mwana wake, Herode Agiripa Wachiwiri, anayamba kulamulira ndipo analamulira mpaka nthawi imene Ayuda anagalukira Aroma.—Mac 23:35; 25:13, 22-27; 26:1, 2, 19-32.

 • Higayoni.

  Mawu ogwiritsa ntchito potsogolera nyimbo. Mogwirizana ndi mmene awagwiritsira ntchito pa Salimo 9:16, mwina mawuwa amasonyeza nthawi yoimba mochokera pansi pamtima, yoimba ndi zeze kapena yosiya kaye kuimba kuti munthu aganizire mozama.

 • Hini.

  Muyezo wa zinthu zamadzimadzi komanso choyezera chenichenicho. Muyezowu unali wofanana ndi malita 3.67. (Eks 29:40)—Onani Zakumapeto B14.

 • Hisope.

  Chomera cha nthambi komanso masamba ofewa chomwe ankagwiritsa ntchito powaza magazi kapena madzi pamwambo woyeretsa. Nʼkutheka kuti chinali cha marjoram (Origanum maru; Origanum syriacum). Koma chimene chatchulidwa pa Yohane 19:29, chiyenera kuti chinali marjoram amene anamumangirira kunthambi ya mtengo kapena mtundu winawake wa mapira wotchedwa durra (Sorghum vulgare). Tikutero chifukwa chakuti mapira a mtundu umenewu ankakhala ndi phesi lalitali ndipo zinali zotheka kutengera vinyo wosasa nʼkuika pakamwa pa Yesu.—Eks 12:22; Sl 51:7.

 • Homeri.

  Choyezera zinthu ngati ufa ndi tirigu ndipo chinkafanana ndi muyezo wa kori. Chinali cha malita 220 potengera muyezo wa mtsuko. (Le 27:16)—Onani Zakumapeto B14.

 • Horebe; Phiri la Horebe.

  Dera lamapiri lozungulira phiri la Sinai. Dzina lina la phiri la Sinai. (Eks 3:1; De 5:2)—Onani Zakumapeto B3.

 • Hule.

  Munthu amene amagonana ndi anthu ena omwe sanakwatirane nawo, makamaka pofuna kupeza ndalama. (Mawu a Chigiriki amene anamasuliridwa kuti “hule” ndi porʹne, ndipo amachokera kumawu otanthauza “kugulitsa.”) Nthawi zambiri mawuwa amanena za akazi ngakhale kuti Baibulo limanenanso za mahule aamuna. Chilamulo cha Mose chinkaletsa uhule ndipo sichinkalola kutenga malipiro auhule nʼkukapereka kumalo opatulika a Yehova. Izi zinali zosiyana ndi anthu a mitundu ina, amene ankagwiritsa ntchito mahule apakachisi kuti apeze ndalama zamsonkho. (De 23:17, 18; 1Mf 14:24) Baibulo limagwiritsanso ntchito mawuwa ponena za anthu, mitundu kapena mabungwe amene amalambira mafano uku akunena kuti akulambiranso Mulungu. Mwachitsanzo, buku la Chivumbulutso limanena kuti zipembedzo zonse zimene zimatchedwa “Babulo Wamkulu,” ndi hule chifukwa choti zimagwirizana ndi olamulira a dzikoli kuti zipeze chuma komanso mphamvu.—Chv 17:1-5; 18:3; 1Mb 5:25.

I

 • Iluriko.

  Chigawo chimene chinkalamulidwa ndi Aroma kumpoto chakumadzulo kwa Girisi. Paulo anafikako pa utumiki wake, koma Baibulo silinena ngati analalikirako kapena anangofikako basi. (Aro 15:19)—Onani Zakumapeto B13.

 • Isiraeli.

  Dzina limene Mulungu anapatsa Yakobo. Kenako dzinali linkaimira mbadwa zonse za Yakobo. Mbadwa za ana 12 a Yakobo zinkatchedwanso ana a Isiraeli, nyumba ya Isiraeli, amuna a Isiraeli kapena Aisiraeli. Dzina lakuti Isiraeli linkagwiritsidwanso ntchito ponena za ufumu wakumpoto wa mafuko 10 umene unagalukira ufumu wakumʼmwera. Patapita nthawi, dzinali linayambanso kuimira Akhristu odzozedwa omwe amatchedwa “Isiraeli wa Mulungu.”—Aga 6:16; Ge 32:28; 2Sa 7:23; Aro 9:6.

 • Itiyopiya.

  Dziko lakale lakumʼmwera kwa Iguputo. Dera la dzikoli linkafika kumʼmwera kwenikweni kwa dziko la Egypt komanso hafu ya kumpoto kwa dziko la Sudan. Dzinali nthawi zina limagwiritsidwa ntchito pomasulira dzina la Chiheberi lakuti “Kusi.”—Est 1:1.

K

 • Kabu.

  Chinthu choyezera zinthu ngati ufa ndipo chinali cha malita 1.22 potengera muyezo wa mtsuko umodzi. (2Mf 6:25)—Onani Zakumapeto B14.

 • Kachisi.

  Nyumba ya ku Yerusalemu imene inalowa mʼmalo mwa chihema ndipo Aisiraeli ankakumana kumeneko kuti alambire Mulungu. Kachisi woyamba anamangidwa ndi Solomo ndipo anawonongedwa ndi Ababulo. Wachiwiri anamangidwa ndi Zerubabele pambuyo poti Aisiraeli abwera ku ukapolo wa ku Babulo ndipo kenako anamangidwanso ndi Herode Wamkulu. MʼMalemba, kachisiyu nthawi zambiri amatchedwa “Nyumba ya Yehova.” (Eza 1:3; 6:14, 15; 1Mb 29:1; 2Mb 2:4; Mt 24:1)—Onani Zakumapeto B8 ndi Zakumapeto B11.

 • Kaisara.

  Dzina lakubanja lina la Chiroma lomwe linadzakhala dzina laudindo la olamulira a ku Roma. Ena mwa olamulira otchulidwa mʼBaibulo amene ankadziwika ndi dzinali ndi Augusto, Tiberiyo ndi Kalaudiyo. Nayenso Nero anali Kaisara ngakhale kuti satchulidwa mʼBaibulo. Mawu akuti Kaisara amagwiritsidwanso ntchito mʼMalemba a Chigiriki a Chikhristu pofotokoza za ulamuliro wa boma kapena wa dziko.—Mko 12:17; Mac 25:12.

 • Kalonga.

  Mawuwa amatanthauza mwana wa mfumu, munthu waudindo, mtsogoleri wa mafuko a Aisiraeli komanso mkulu wa boma. (Ge 12:15; 1 Mb 27:22; Est 3:12; Yer 38:17) Yehova amatchedwanso “Kalonga wa gululo” ndiponso “Kalonga wa akalonga.” (Da 8:11, 25) Mikayeli mkulu wa angelo amatchedwa “kalonga wamkulu.” (Da 12:1) Ziwanda zimene zinkatsogolera maulamuliro amphamvu kwambiri padziko lonse, a Perisiya ndi Girisi, zimatchedwanso akalonga.—Da 10:13, 20.

 • Kamutu ka mʼMasalimo.

  Timawu takumayambiriro kwa salimo tomwe timafotokoza amene analemba salimolo, mmene zinthu zinalili, kaimbidwe kake kapena cholinga cha salimolo.—Onani timitu ta Salimo 3, 4, 5, 6, 7, 30, 38, 60, 92, 102.

 • Kanani.

  Chidzukulu cha Nowa ndiponso mwana wa 4 wa Hamu. Mafuko 11 amene anabadwa kuchokera kwa Kanani anakakhala mʼdziko limene lili kumʼmawa kwa nyanja ya Mediterranean pakati pa Iguputo ndi Siriya. Dziko limeneli linkadziwika kuti “dziko la Kanani.” (Le 18:3; Ge 9:18; Mac 13:19)—Onani Zakumapeto B4.

 • Kasidi; Akasidi.

  Poyamba mawuwa ankanena za dera lapakati pa mtsinje wa Tigirisi ndi Firate komanso anthu amene ankakhala mʼderali. Patapita nthawi, mayinawa ankagwiritsidwa ntchito ponena za ku Babeloniya komanso anthu onse okhala kumeneko. Mawu akuti “Akasidi” amanenanso za anthu ophunzira amene ankadziwa sayansi, mbiri yakale, zilankhulo komanso zinthu zakuthambo, koma ankakhulupiriranso nyenyezi ndiponso zamatsenga.—Eza 5:12; Da 4:7; Mac 7:4.

 • Kasiya.

  Zinthu zopangidwa kuchokera ku makungwa a mtengo wa kasiya (Cinnamomum cassia). Mtengo umenewu uli mʼgulu limodzi ndi mtengo wa sinamoni. Kasiya ankamugwiritsa ntchito popanga mafuta onunkhira komanso anali chimodzi mwa zinthu zimene ankapangira mafuta opatulika odzozera.—Eks 30:24; Sl 45:8; Eze 27:19.

 • Katani.

  Nsalu yabwino kwambiri yokongoletsedwa ndi zifaniziro za akerubi ndipo inkasiyanitsa Malo Oyera ndi Malo Oyera Koposa muchihema komanso mʼkachisi. (Eks 26:31; 2Mb 3:14; Mt 27:51; Ahe 9:3)—Onani Zakumapeto B5.

 • Kemosi.

  Mulungu wamkulu wa Amowabu.—1Mf 11:33.

 • Khalidwe lopanda manyazi.

  Kuchokera ku mawu a Chigiriki akuti a·selʹgei·a, ndipo amanena za khalidwe lililonse lophwanya kwambiri malamulo a Mulungu. Munthu wake amasonyeza kuti alibiretu manyazi, ndi wachipongwe, wopanda ulemu komanso amaderera mwinanso kunyansidwa ndi olamulira, malamulo ndiponso mfundo zoyenera kutsatira. Mawuwa sanena za kulakwitsa zinthu zingʼonozingʼono.—Aga 5:19; 2Pe 2:7.

 • Khate; Wakhate.

  Matenda oopsa apakhungu. MʼMalemba mawu akuti khate sankangonena za matenda akhate amene anthu amawadziwa masiku ano chifukwa sankangogwira anthu okha, koma ankagwiranso zovala ndi nyumba. Munthu wodwala khate amadziwika kuti wakhate.—Le 14:54, 55; Lu 5:12.

 • Khonde Lazipilala la Solomo.

  Mʼnthawi ya Yesu, amenewa anali malo okhala ndi denga amene anthu ankatha kudutsamo ndipo anali chakumʼmawa kwa bwalo lakunja. Anthu ambiri ankakhulupirira kuti imeneyi inali mbali yotsala ya kachisi wa Solomo. Yesu anayenda pamalo amenewa ‘mʼnyengo yoziziraʼ komanso Akhristu oyambirira ankakumana pamalowa kuti alambire Mulungu. (Yoh 10:22, 23; Mac 5:12)—Onani Zakumapeto B11.

 • Khoti Lalikulu la Ayuda.

  Khoti la Ayuda lalikulu lomwe linali ku Yerusalemu. Pa nthawi ya Yesu, oweruza amʼkhotili ankakhala mkulu wa ansembe, anthu ena amene anakhalapo akulu a ansembe, anthu akubanja la mkulu wa ansembe, akulu, mitu ya mafuko, mitu ya mabanja komanso alembi ndipo onse pamodzi ankakwana 71.—Mko 15:1; Mac 5:34; 23:1, 6.

 • Khristu.

  Dzina laudindo la Yesu lochokera ku mawu a Chigiriki akuti Khri·stosʹ. Mawuwa amafanana ndi mawu a Chiheberi amene anamasuliridwa kuti “Mesiya” kapena “Wodzozedwa.”—Mt 1:16; Yoh 1:41.

 • Kisilevi.

  Umenewu unali mwezi wa 9 pakalendala yopatulika ya Ayuda komanso mwezi wachitatu pakalendala ya anthu onse, Aisiraeli atabwera kuchokera ku ukapolo wa ku Babulo. Unkayambira pakati pa November mpaka pakati pa December. (Ne 1:1; Zek 7:1)—Onani Zakumapeto B15.

 • Korali.

  Chinthu cholimba ngati mwala chomwe chinkapangika kuchokera ku mafupa a tinyama tingʼonotingʼono tamʼmadzi. Korali ankapezeka mʼnyanja zikuluzikulu ndipo ankakhala wofiira, woyera komanso wakuda. Ankapezeka kwambiri mʼNyanja Yofiira. Pa nthawi imene Baibulo linkalembedwa, korali wofiira anali wamtengo wapatali ndipo ankapangira mikanda ndi zinthu zina zodzikongoletsera.—Miy 8:11.

 • Kori.

  Choyezera zinthu ngati ufa komanso zamadzimadzi. Chinali cha malita 220, potengera mtsuko woyezera. (1Mf 5:11)—Onani Zakumapeto B14.

 • Kudzipereka kwa Mulungu.

  Kuopa Yehova Mulungu, kumulambira komanso kumutumikira mosonyeza kuti ndife okhulupirika ku ulamuliro wake wa chilengedwe chonse.—1Ti 4:8; 2Ti 3:12.

 • Kudzoza.

  Mawu ake a Chiheberi amatanthauza “kupaka zinthu zamadzimadzi.” Anthu ankathira munthu kapena zinthu mafuta posonyeza kuti zasankhidwa kuti zigwire ntchito yapadera. MʼMalemba a Chigiriki a Chikhristu, mawuwa amagwiritsidwanso ntchito ponena za kupereka mzimu woyera kwa anthu amene ali ndi chiyembekezo chopita kumwamba.—Eks 28:41; 1Sa 16:13; 2Ak 1:21.

 • Kuika manja.

  Anthu ankaika manja pa munthu kapena kumugwira pamutu pomupatsa ntchito yapadera, kumudalitsa, kumuchiritsa kapena kumuthandiza kuti alandire mphatso ya mzimu woyera. Nthawi zina anthu ankaika manja pamutu pa nyama asanaipereke nsembe.—Eks 29:15; Nu 27:18; Mac 19:6; 1Ti 5:22.

 • Kukhalapo.

  Mʼmavesi ena a mʼMalemba a Chigiriki a Chikhristu, mawuwa amanena za kukhalapo kwa Yesu Khristu kuchokera pa nthawi imene anakhala Mfumu Mesiya mpaka mapeto a dziko loipali. Kukhalapo kwa Khristu si kwa nthawi yochepa koma ndi kwa nthawi yotalikirapo.—Mt 24:3.

 • Kukhulupirira mizimu.

  Chikhulupiriro chakuti munthu akafa, chinachake chimakhalabe ndi moyo ndipo amatha kulankhulana ndi anthu ena kudzera mwa wolankhula ndi mizimu. Mawu a Chigiriki amene anawamasulira kuti “kuchita zamizimu” ndi akuti phar·ma·kiʹa, ndipo amatanthauza “kupereka mankhwala.” Ankagwiritsa ntchito mawuwa chifukwa chakuti kalelo anthu ankagwiritsa ntchito mankhwala akafuna kupeza mphamvu ya ziwanda kuti azichita zamizimu.—Aga 5:20; Chv 21:8.

 • Kukoma mtima kosatha.

  Mawu ake a Chigiriki kwenikweni amanena za chinthu chovomerezeka ndiponso chosangalatsa. Nthawi zambiri mawuwa amagwiritsidwa ntchito ponena za mphatso yoperekedwa chifukwa cha kukoma mtima komanso mtima wopatsa. Akamanena za kukoma mtima kwa Mulungu, mawuwa amanena za mphatso yaulere yoperekedwa mowolowa manja ndi Mulungu, popanda kuyembekezera kuti wolandirayo abweze kenakake. Choncho ndi umboni wa kuwolowa manja, chikondi komanso kukoma mtima kumene Mulungu amasonyeza anthu. Mawu ake a Chigiriki nthawi zina amamasuliridwanso kuti “chifundo” ndiponso “mphatso yoperekedwa chifukwa cha kukoma mtima.” Woperekayo sayembekezera kubwezeredwa ndipo sayangʼana ngati munthuyo ndi woyenera kupatsidwa mphatsoyo. Koma amangopereka chifukwa choti ndi wowolowa manja.—2Ak 6:1; Aef 1:7.

 • Kukunkha.

  Kutola mbewu zimene anthu okolola azisiya mwadala kapena mosadziwa. Chilamulo cha Mose chinkanena kuti anthu akamakolola asamachotse mbewu zonse zamʼmbali mwa munda wawo kapena kumaliziratu maolivi ndi mphesa mʼmitengo. Mulungu anapereka ufulu kwa anthu osauka, ovutika, alendo, ana amasiye komanso akazi amasiye kuti azitola zimene zatsala pokolola.—Ru 2:7.

 • Kukwapula.

  MʼMalemba a Chigiriki a Chikhristu mawuwa amanena za kumenya munthu ndi ndodo kapena ndi mkwapulo wazingwe wokhala ndi timfundo kapena tinthu tobaya.—Yoh 19:1.

 • Kulakwa; Zolakwa.

  Kuphwanya lamulo. Zinthu zophwanya lamulo zimene munthu wachita. MʼBaibulo mawuwa amafanana ndi akuti “kuchimwa” kapena “uchimo.”—Sl 51:3; Aro 5:14.

 • Kulapa.

  Baibulo limagwiritsa ntchito mawuwa ponena za kusintha maganizo komanso kuipidwa ndi moyo umene unkakhala nawo poyamba, zolakwika zimene unachita kapena zinthu zimene unalephera kuchita. Kulapa kwenikweni kumathandiza kuti munthu asiye kuchita zinthu zolakwika.—Mt 3:8; Mac 3:19; 2Pe 3:9.

 • Kulira.

  Kusonyeza chisoni moonekera chifukwa choti munthu waferedwa kapena wakumana ndi mavuto enaake. Kale anthu ankalira kwa nthawi yaitali. Kuwonjezera pamenepo, ankalira mokweza, kuvala zovala zapadera, kudzithira phulusa mʼmutu, kungʼamba zovala komanso kudzimenya pachifuwa. Nthawi zina pamaliro, anthu ankaitana olira aganyu.—Ge 23:2; Est 4:3; Chv 21:4.

 • Kuphimba.​—

  Onani KUPHIMBA MACHIMO.

 • Kuphimba machimo.

  MʼMalemba a Chiheberi, mawuwa amanena za kupereka nsembe zothandiza kuti anthu agwirizane ndi Mulungu komanso azimulambira. MʼChilamulo cha Mose, nsembe zinkaperekedwa pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo kuti anthu agwirizanenso ndi Mulungu, ngakhale kuti anthuwo anachimwa kapenanso mtundu wonsewo unachimwa. Nsembe zimenezi zinkaimira nsembe ya Yesu imene inaphimbiratu machimo a anthu kamodzi kokha nʼkuwapatsa mwayi wogwirizananso ndi Yehova.—Le 5:10; 23:28; Akl 1:20; Ahe 9:12.

 • Kupita ku ukapolo.

  Kuchotsa anthu mʼdziko lawo nʼkupita nawo kwina ndipo nthawi zambiri amapita pomvera lamulo la anthu amene agonjetsa dzikolo. Mawu ake a Chiheberi amatanthauza “kunyamuka.” Aisiraeli anapita ku ukapolo wodziwika bwino maulendo awiri. Anthu a mu ufumu wakumpoto wa mafuko 10 anatengedwa ndi Asuri kupita ku ukapolo ndipo kenako anthu a mu ufumu wa mafuko awiri wakumʼmwera anatengedwa ndi Ababulo kupita ku ukapolo. Aisiraeli amene analipobe ku ukapolo wa Asuri ndi Ababulo anabwerera kwawo atamasulidwa ndi Koresi, mfumu ya Perisiya.—2Mf 17:6; 24:16; Eza 6:21.

 • Kupuntha; Malo opunthira mbewu.

  Kuchotsa mbewu kumapesi komanso mankhusu ake. Malo amene ankagwirira ntchitoyi. Ngati ndi mbewu zochepa, athu ankagwira ntchitoyi pamanja ndipo ankagwiritsa ntchito ndodo. Koma ngati ndi zambiri ankagwiritsa ntchito zipangizo zopunthira ndipo zina mwa zipangizozi zinkayendetsedwa ndi nyama. Malo opunthira ankakhala ozungulira komanso okwera kuti pazidutsa mphepo ndiye mbewuzo ankazimwaza pamwambapo nʼkumadutsitsapo chopunthira.—Le 26:5; Yes 41:15; Mt 3:12.

 • Kusala kudya.

  Kukhala osadya chakudya chilichonse kwa nthawi inayake. Aisiraeli ankasala kudya pa tsiku la Mwambo Wophimba Machimo, pa nthawi ya mavuto komanso akamafuna kuti Mulungu awatsogolere. Ayuda anakhazikitsa nthawi 4 zoti azisala kudya pachaka pokumbukira nthawi yovuta pa moyo wawo. Akhristu sanalamulidwe kuti azisala kudya.—Eza 8:21; Yes 58:6; Lu 18:12.

 • Kuukitsidwa.

  Munthu wakufa akadzutsidwa. Mawu ake a Chigiriki ndi akuti a·naʹsta·sis ndipo amatanthauza “kudzuka” kapena “kuimirira.” Baibulo limatchula anthu 9 amene anaukitsidwa ndipo wina ndi Yesu amene anaukitsidwa ndi Yehova Mulungu. Ngakhale kuti anthu enawo anaukitsidwa ndi Eliya, Elisa, Yesu, Petulo ndi Paulo, zoona zake ndi zoti ankaukitsidwa ndi mphamvu ya Mulungu. Mfundo yakuti “Mulungu adzaukitsa olungama ndi osalungama omwe” padzikoli imagwirizana ndi cholinga cha Mulungu. (Mac 24:15) Baibulo limanenanso za kuuka “koyamba” kopita kumwamba kwa abale ake a Yesu odzozedwa ndi mzimu.—Afi 3:11; Chv 20:5, 6; Yoh 5:28, 29; 11:25.

 • Kuyera.

  Yehova ndi woyera. Mawu akuti kuyera amatanthauza kukhala ndi makhalidwe osadetsedwa ndiponso kupatulika. (Eks 28:36; 1Sa 2:2; Miy 9:10; Yes 6:3) Mawu a Chiheberi amene anawamasulira kuti kuyera ngati akunena za anthu (Eks 19:6; 2Mf 4:9), nyama (Nu 18:17), zinthu (Eks 28:38; 30:25; Le 27:14), malo (Eks 3:5; Yes 27:13), nthawi (Eks 16:23; Le 25:12) kapena zochitika zina (Eks 36:4), amatanthauza kuti chinthucho ndi chapadera, chopatulika, choyeretsedwa kuti chikhale cha Mulungu kapena choikidwa padera kuti chigwiritsidwe ntchito potumikira Yehova. MʼMalemba a Chigiriki a Chikhristu mawu akuti “kuyera” amatanthauzanso kuikidwa padera kuti chikhale cha Mulungu. Mawuwa amagwiritsidwanso ntchito ponena za kukhala ndi makhalidwe osadetsedwa.—Mko 6:20; 2Ak 7:1; 1Pe 1:15, 16.

L

 • Lepitoni.

  Kale pamene Malemba a Chigiriki a Chikhristu ankalembedwa, lepitoni kanali kandalama kakopa kakangʼono kwambiri ka Ayuda. (Mko 12:42; Lu 21:2; mawu amʼmunsi.)—Onani Zakumapeto B14.

 • Levi; Mlevi.

  Mwana wachitatu wa Yakobo ndipo mayi ake anali Leya. Komanso ndi dzina la fuko la Levi. Ana ake atatu anadzakhala atsogoleri a magulu atatu akuluakulu a Alevi. Nthawi zina mawu akuti “Alevi” amanena za fuko lonse, koma nthawi zambiri amapatulapo banja la Aroni lomwe munkachokera ansembe. Fuko la Levi silinalandire malo mʼDziko Lolonjezedwa, koma linapatsidwa mizinda 48 ya mʼmalo amene anaperekedwa kwa mafuko ena.—De 10:8; 1Mb 6:1; Ahe 7:11.

 • Leviyatani.

  Nyama yamʼmadzi. Pa Yobu 3:8 ndi 41:1, zikuoneka kuti mawuwa akunena za ngʼona kapena nyama ina yamʼmadzi yaikulu komanso yamphamvu. Pamene pa Salimo 104:26, ayenera kuti akunena za nyama ina yamʼmadzi yaikulu yotchedwa whale. Mʼmalemba ena dzinali limagwiritsidwa ntchito mophiphiritsa ndipo munthu sangadziwe kuti akunena nyama iti.—Sl 74:14; Yes 27:1.

 • Likasa la Pangano.

  Bokosi lopangidwa ndi matabwa a mtengo wa mthethe ndipo analikuta ndi golide. Linkasungidwa mʼMalo Oyera Koposa a chihema ndipo kenako mʼMalo Oyera Koposa a kachisi wa Solomo. Linali ndi chivundikiro chagolide cholimba chokhala ndi akerubi awiri oyangʼanizana. Mkati mwake munali miyala iwiri ya Malamulo Khumi ndi zinthu zina. (De 31:26; 1Mf 6:19; Ahe 9:4)—Onani Zakumapeto B5 ndi B8.

 • Lipenga.

  Chipangizo chochita kuuzira chopangidwa ndi chitsulo chimene ankachigwiritsa ntchito poimba komanso pofuna kupereka chizindikiro. Mogwirizana ndi Numeri 10:2, Yehova anapereka malangizo okhuza mmene angapangire malipenga awiri asiliva oti aziwagwiritsa ntchito poitanitsa msonkhano, pouza anthu mumsasa kuti asamuke komanso polengeza nkhondo. Malipenga amenewa ayenera kuti ankakhala owongoka mosiyana ndi “malipenga a nyanga ya nkhosa” omwe ankakhala opindika. Panalinso malipenga ena omwe ankagwiritsidwa ntchito poimba pakachisi, koma Baibulo silifotokoza kuti ankawapanga bwanji. Nthawi zambiri kulira kwa lipenga mophiphiritsa kumayendera limodzi ndi kulengeza ziweruzo za Yehova kapena zinthu zina zapadera zochokera kwa Mulungu.—2Mb 29:26; Eza 3:10; 1Ak 15:52; Chv 8:7–11:15.

 • Logi.

  MʼBaibulo, umenewu ndi muyezo waungʼono kwambiri woyezera zinthu zamadzimadzi. Zolemba zina za Ayuda (Jewish Talmud) zimafotokoza kuti malogi 12 ankakwana hini imodzi. Mogwirizana ndi zimenezi tingati logi inkakhala malita 0.31. (Le 14:10)—Onani Zakumapeto B14.

 • Lonjezo.

  Munthu ankalonjeza kwa Mulungu kuti achita zinazake, apereka zinazake, azichita utumiki winawake kapena sazichita zinthu zina ngakhale kuti si zoletsedwa. Linkafanana ndi lumbiro.—Nu 6:2; Mla 5:4; Mt 5:33.

 • Lubani.

  Utomoni wouma wa mitengo kapena zitsamba zina za mʼgulu la Boswellia. Lubani akawotchedwa amanunkhira bwino kwambiri. Anali mʼgulu la zinthu zopangira zonunkhira zopatulika zapachihema komanso zamʼkachisi. Ankamupereka limodzi ndi nsembe ya ufa komanso ankamuika pakati pa mapisi onse a mikate yoonetsa kwa Mulungu mʼMalo Oyera.—Eks 30:34-36; Le 2:1; 24:7; Mt 2:11.

 • Lumbiro.

  Mawu amene munthu amanena potsimikizira kuti zinazake ndi zoona kapena lonjezo lotsimikizira kuti munthu adzachita kapena sadzachita zinazake. Nthawi zambiri linkakhala lonjezo limene munthu ankapanga kwa winawake wamkulu, makamaka kwa Mulungu. Yehova anatsimikizira pangano lake kwa Abulahamu polumbira.—Ge 14:22; Ahe 6:16, 17.

M

 • Maere.

  Timiyala kapena timapisi ta mitengo timene ankatigwiritsa ntchito posankha zochita. Ankatiika pakansalu kapena mʼchiwiya chinachake nʼkukhutchumula. Kamene kagwa nʼkamene kankasankhidwa. Nthawi zambiri ankapemphera kaye asanachite zimenezi. Mawu a chilankhulo choyambirira, amene anamasuliridwa kuti “maere” angatanthauzenso “gawo” kapena “cholowa.”—Yos 14:2; Sl 16:5; Miy 16:33; Mt 27:35.

 • Mahalati.

  Mawuwa ayenera kuti ndi okhuza nyimbo ndipo amapezeka pakamutu ka pa Salimo 53 ndi 88. Zikuoneka kuti mawuwa amagwirizana ndi mawu a Chiheberi amene amatanthauza “kufooka” kapena “kudwala.” Choncho nyimbo zake zimakhala zachisoni kapena zodandaula ndipo izi zikugwirizana ndi mawu amʼmasalimo awiri amenewa.

 • Mailo.

  Kutalika kwa malo ndipo mawu a chilankhulo choyambirira amene anawamasulira kuti “mailo” amapezeka kamodzi mʼMalemba a Chigiriki a Chikhristu pa Mateyu 5:41, ndipo nʼkutheka kuti amanena za mailo ya Aroma imene inkakhala mamita 1,479.5. Malemba ena amene ali ndi mawu otanthauza “mailo” ndi Luka 24:13, Yohane 6:19 ndi Yohane 11:18 ndipo zikuoneka kuti mʼchilankhulo choyambirira analemba kutalika kwake mʼmasitadiya ndiye anasinthidwa kukhala mamailo.—Onani Zakumapeto B14.

 • Makangaza.

  Chipatso chooneka ngati apozi chokhala ndi tinthu ngati chimanga tomwe timakhala ndi madzi mkati mwake. Tinthu timeneti timakhala ndi njere zapinki kapena zofiira. Zinthu zokongoletsera zooneka ngati makangaza ankaziika pachovala cha mkulu wa ansembe komanso anaziika pamutu wa chipilala cha Yakini ndi Boazi zimene zinali kutsogolo kwa kachisi.—Eks 28:34; Nu 13:23; 1Mf 7:18.

 • Makedoniya.

  Chigawo cha kumpoto kwa Girisi ndipo chinali chotchuka mu ulamuliro wa Alekizanda Wamkulu. Chigawochi chinali choima pachokha mpaka nthawi imene chinagonjetsedwa ndi Aroma. Pa nthawi imene Paulo anapita ku Europe, chigawo cha Makedoniya chinkalamulidwa ndi Aroma. Paulo anafika ku Makedoniya maulendo atatu. (Mac 16:9)—Onani Zakumapeto B13.

 • Malemba.

  Malemba opatulika a Mawu a Mulungu. Mawuwa amapezeka mʼMalemba a Chigiriki a Chikhristu okha.—Lu 24:27; 2Ti 3:16.

 • Malikamu.

  Nʼkutheka kuti ndi dzina lina la Moleki, yemwe ndi mulungu wamkulu wa Aamoni. (Zef 1:5)—Onani MOLEKI.

 • Malo okwera.

  Malo amene nthawi zambiri ankakhala pamwamba pa phiri kapena ankachita kupangidwa. Ngakhale kuti nthawi zina malowa ankakhala olambirirapo Mulungu, nthawi zambiri ankalambirirapo milungu yabodza.—Nu 33:52; 1Mf 3:2; Yer 19:5.

 • Malo opatulika.

  Malo apadera amene anthu amalambirirako, malo oyera. Koma nthawi zambiri mawuwa amanena za chihema kapena kachisi wa ku Yerusalemu. Mawuwa amanenanso za malo amene Mulungu amakhala kumwamba.—Eks 25:8, 9; 2Mf 10:25; 1Mb 28:10; Chv 11:19.

 • Malo Oyera.

  Chigawo choyamba komanso chachikulu cha chihema kapena kachisi ndipo nʼchosiyana ndi chigawo chamkati kwambiri chotchedwa Malo Oyera Koposa. Mʼchihema, mʼMalo Oyera munkakhala choikapo nyale chagolide, guwa lansembe zofukiza lagolide, tebulo la mikate yachionetsero ndiponso ziwiya zagolide. MʼMalo Oyera amʼkachisi munkapezeka guwa lagolide, zoikapo nyale 10 zagolide ndiponso matebulo 10 a mikate yachionetsero. (Eks 26:33; Ahe 9:2)—Onani Zakumapeto B5 ndi B8.

 • Malo Oyera Koposa.

  Chipinda chamkati kwambiri mwa chihema komanso kachisi kumene ankasungako likasa la pangano. Ankatchedwanso kuti “Malo Opatulika Koposa.” Mogwirizana ndi Chilamulo cha Mose, mkulu wa ansembe yekha ndi amene ankaloledwa kulowa mʼMalo Oyera Koposa ndipo ankayenera kulowamo pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo basi.—Eks 26:33; Le 16:2, 17; 1Mf 6:16; Ahe 9:3.

 • Mana.

  Chakudya chimene Aisiraeli ankadya mʼchipululu kwa zaka 40. Yehova ndi amene ankawapatsa. Tsiku lililonse mʼmawa kupatulapo la Sabata, mana ankapezeka pansi atakutidwa ndi mame. Aisiraeli ataona mana koyamba ankafunsa kuti, “Ichi nʼchiyani?” kapena mʼChiheberi “man huʼ?” (Eks 16:13-15, 35) Mʼmalemba ena amamasuliridwa kuti “tirigu wochokera kumwamba” (Sl 78:24), “chakudya chochokera kumwamba” (Sl 105:40) komanso “chakudya cha amphamvu” (Sl 78:25). Yesu anagwiritsanso ntchito mawu oti mana mophiphiritsa.—Yoh 6:49, 50.

 • Manda.

  Akalembedwa ndi “m” wamngʼono amanena za manda amodzi, koma akalembedwa ndi “M” wamkulu amanena za manda a anthu onse omwe pa Chiheberi ndi “Sheol” ndipo pa Chigiriki ndi “Hades.” Baibulo limafotokoza kuti Manda ndi malo ophiphiritsa kumene munthu sangachite chilichonse ndipo sadziwa kalikonse.—Lu 4:18, 43; Mac 5:42; Chv 14:6.

 • Manda achikumbutso.

  Malo amene amaikamo thupi la munthu amene wamwalira. Mawuwa anamasuliridwa kuchokera ku mawu a Chigiriki akuti mne·meiʹon. Mawu a Chigirikiwa amachokera ku mawu otanthauza “kukumbutsa” posonyeza kuti munthu womwalirayo akukumbukiridwa.—Yoh 5:28, 29.

 • Mankhusu.

  Makoko amene amachotsa popuntha mbewu ngati mpunga kapena tirigu. Mankhusu amagwiritsidwanso ntchito mophiphiritsa ngati chizindikiro cha zinthu zopanda pake komanso zosafunika.—Sl 1:4; Mt 3:12.

 • Mapeto a nthawi ino.

  Nthawi yotifikitsa pamapeto a dziko lolamulidwa ndi Satanali. Nthawi imeneyi ikuyendera limodzi ndi nthawi ya kukhalapo kwa Khristu. Motsogoleredwa ndi Yesu, angelo ‘adzachotsa oipa pakati pa olungamaʼ nʼkuwawononga. (Mt 13:40-42, 49) Ophunzira a Yesu ankafunitsitsa kudziwa kuti nthawi ya “mapeto” imeneyi idzakhalapo liti. (Mt 24:3) Asanabwerere kumwamba, Yesu analonjeza otsatira ake kuti adzakhala nawo mpaka nthawi imeneyi.—Mt 28:20.

 • Mapiri a ku Lebanoni.

  Limodzi mwa magulu awiri a mapiri a ku Lebanoni. Mapiriwa ali kumadzulo ndipo kumʼmawa kuli mapiri ena. Pakati pake pali chigwa chachitali komanso chachonde. Mapiriwa ali mʼmbali mwenimweni mwa nyanja ya Mediterranean ndipo ndi aatali kuyambira mamita 1,800 mpaka kukafika mamita 2,100. Kalelo mʼmapiri a ku Lebanoni munali mitengo ikuluikulu ya mkungudza yomwe anthu a mitundu yozungulira ankaiona kuti ndi yamtengo wapatali (De 1:7; Sl 29:6; 92:12)—Onani Zakumapeto B7.

 • Masikili.

  Mawu a Chiheberi omwe tanthauzo lake silidziwika bwinobwino ndipo amapezeka pakamutu ka pa Salimo 13. Nʼkutheka kuti amatanthauza “ndakatulo ya kuganiza mozama.” Ena amaganiza kuti mwina mawuwa tanthauzo lake ndi lofanana ndi la mawu ena ofanana nawo omwe amamasuliridwa kuti ‘kutumikira mwanzeru.’—2Mb 30:22; Sl 32:Kam.

 • Masiku otsiriza.

  Mawu amenewa amagwiritsidwa ntchito mʼmaulosi a mʼBaibulo pofotokoza nthawi imene zochitika zapadzikoli zidzafike pachimake. (Eze 38:16; Da 10:14; Mac 2:17) Mogwirizana ndi zimene ulosi umanena, nthawi imeneyi ikhoza kukhala zaka zochepa kapena zambiri. Nthawi zambiri Baibulo limagwiritsa ntchito mawuwa ponena za masiku otsiriza a dziko loipali omwe akuyendera limodzi ndi nthawi ya kukhalapo kwa Yesu kosaonekera.—2Ti 3:1; Yak 5:3; 2Pe 3:3.

 • Matangadza.

  Chinthu chimene ankaikamo munthu pofuna kumulanga. Mʼmatangadza ena, munthu ankamulowetsa mapazi okha pomwe ena ankamulowetsa mapazi, manja ndi khosi moti thupi linkapindika.—Yer 20:2; Mac 16:24.

 • Matumba achikopa.

  Matumba opangidwa ndi zikopa za nyama monga nkhosa kapena mbuzi omwe ankasungiramo vinyo. Vinyo watsopano ankaikidwa mʼmatumba atsopano chifukwa chakuti vinyoyo akayamba kuwira ankatulutsa mpweya wa carbon dioxide womwe unkachititsa kuti matumba afufume. Koma matumbawo akakhala kuti ndi akale ankangophulika.—Yos 9:4; Mt 9:17.

 • Mbadwa.

  Gulu la anthu kapena munthu amene anabadwa kuchokera kwa kholo linalake. Mawuwa angatanthauzenso munthu kapena anthu omwe anabadwa komanso kukulira mʼdera kapena dziko linalake.—Ge 12:7; Eks 12:19.

 • Mdulidwe.

  Kudula khungu la kunsonga kwa chiwalo cha mwamuna. Abulahamu ndi mbadwa zake analamulidwa kuti azichita zimenezi, koma si lamulo kwa Akhristu. Nthawi zina mawuwa amagwiritsidwa ntchito mophiphiritsa.—Ge 17:10; 1Ak 7:19; Afi 3:3.

 • Mdyerekezi.

  Dzina lofotokozera Satana mʼMalemba a Chigiriki a Chikhristu ndipo limatanthauza “Woneneza.” Satana anapatsidwa dzina loti Mdyerekezi chifukwa chakuti ndi woneneza komanso wotsutsa wamkulu wa Yehova, mawu ake komanso dzina lake loyera.—Mt 4:1; Yoh 8:44; Chv 12:9.

 • Mdzakazi.

  Mkazi wachiwiri wa munthu ndipo nthawi zambiri ankakhala mtsikana yemwe anali kapolo.—Eks 21:8; 2Sa 5:13; 1Mf 11:3.

 • Merodaki.

  Mulungu wamkulu wa mzinda wa Babulo. Hamurabi, yemwe anali mfumu ya Babulo komanso wopanga malamulo, anasankha mzinda wa Babulo kuti ukhale likulu la dziko la Babeloniya. Zitatero, Merodaki (kapena kuti Madaki) anayamba kutchuka kwambiri moti analowa mʼmalo mwa milungu ina yonse yoyamba ndipo anakhala mulungu wamkulu wa ku Babulo. Patapita nthawi, dzina lakuti Merodaki (kapena Madaki) linasinthidwa nʼkukhala “Belu” (“Mwiniwake”), ndipo Merodaki ankadziwikanso kuti Beli.—Yer 50:2.

 • Mesiya.

  Mawuwa anachokera ku mawu a Chiheberi otanthauza “kudzozedwa” kapena “wodzozedwa.” Mawu a Chigiriki ofanana nawo ndi akuti “Khristu.”—Da 9:25; Yoh 1:41.

 • Mfulu; Munthu womasulidwa.

  Mu ulamuliro wa Aroma, anthu ena ankabadwa ndi ufulu wonse monga nzika pomwe ena ankakhala ndi ufulu akamasulidwa ku ukapolo. Omasulidwawonso analipo magulu awiri. Ena akamasulidwa ankakhala nzika koma sankagwira nawo ntchito mʼboma pomwe ena akamasulidwa sankapatsidwa ufulu wonse umene nzika zinkakhala nawo.—1Ak 7:22.

 • Mfumukazi Yakumwamba.

  Dzina la mulungu wamkazi amene Aisiraeli ampatuko ankalambira masiku a Yeremiya. Ena amanena kuti mawuwa amanena za mulungu wamkazi wa Ababulo dzina lake Ishtar (Astarte). Poyamba, anthu a ku Babulo anali ndi mulungu wina wofanana ndi ameneyu dzina lake Inana ndipo dzinali linkatanthauza “Mfumukazi Yakumwamba.” Anthu ankaona kuti mulunguyu amakhudzana ndi zinthu zakumwamba komanso ndi wobereketsa. Astarte amatchedwanso “Mayi Wakumwamba” mʼzolemba zina za ku Iguputo.—Yer 44:19.

 • Mheberi.

  Abulamu (Abulahamu) ndi amene anali woyamba kutchulidwa ndi dzina limeneli ndipo linkamusiyanitsa ndi anthu a Chiamori amene anayandikana nawo. Kenako mbadwa za Abulahamu, kudzera mwa mdzukulu wake Yakobo, zinkatchedwa Aheberi ndipo chilankhulo chawo chinkatchedwa Chiheberi. Pamene Yesu anali padzikoli, Chiheberi chinali ndi mawu ambiri a Chiaramu ndipo ndi chilankhulo chimene iye ndi ophunzira ake ankalankhula.—Ge 14:13; Eks 5:3; Mac 26:14.

 • Mikate yoonetsa kwa Mulungu.​—

  Onani MIKATE YACHIONETSERO.

 • Mikitamu.

  Mawu a Chiheberi opezeka pa timitu ta mʼmasalimo 6 (Sl 16, 56-60). Tanthauzo la mawuwa silidziwika bwinobwino, koma amafanana ndi mawu akuti “zolemba.”

 • Milikomu.

  Mulungu amene Aamoni ankalambira. Nʼkutheka kuti nʼchimodzimodzi ndi mulungu wotchedwa Moleki. (1Mf 11:5, 7) Chakumapeto kwa moyo wake, Solomo anamangira mulungu wabodzayu malo okwezeka.—Onani MOLEKI.

 • Mina.

  Ndalama komanso muyezo wa kulemera. Mʼbuku la Ezekieli imatchedwa mane. Malinga ndi zimene ofukula zinthu zakale anapeza, ndalama zokwana mina imodzi zinali zofanana ndi masekeli 50 ndipo sekeli inkalemera magalamu 11.4. Mina yotchulidwa mʼMalemba a Chiheberi ndalama zake zinkalemera magalamu 570. Nʼkutheka kuti panalinso mina ina yachifumu ngati mmene zinalili ndi muyezo wa mkono. MʼMalemba a Chigiriki a Chikhristu, mina inali yofanana ndi madalakima 100 ndipo inkalemera magalamu 340. Ma mina 60 ankakwana talente imodzi. (Eza 2:69; Lu 19:13)—Onani Zakumapeto B14.

 • Mipukutu yazikopa.

  Zikopa za nkhosa, mbuzi ndi ana a ngʼombe zomwe ankazikonza kuti azilembapo. Zinali zolimba kusiyana ndi gumbwa ndipo ankazigwiritsa ntchito polemba Baibulo. Mipukutu yazikopa imene Paulo anapempha Timoteyo kuti amupititsire iyenera kuti panalembedwa mbali ina ya Malemba a Chiheberi. Mipukutu ina ya ku Nyanja Yakufa inali yachikopa.—2Ti 4:13.

 • Miyambi; Miyambo.

  Mawu anzeru kapena nthano imene imaphunzitsa anthu kapenanso kunena mfundo yoona mʼmawu ochepa. Miyambi ya mʼBaibulo itha kukhala mawu okuluwika kapena ndagi. Mfundo za choonadi zimafotokozedwa mʼmiyambi mʼnjira yomveka bwino kapena moyerekezera ndi zinthu zina. Koma miyambi ina inadzakhala yonyoza anthu ena.—Mla 12:9; 2Pe 2:22.

 • Mizinda yothawirako.

  Mizinda ya Alevi imene munthu amene wapha mnzake mwangozi ankathawirako pothawa wobwezera magazi. Mizinda 6 yothawirako inali mʼmalo osiyanasiyana mʼDziko Lolonjezedwa ndipo inasankhidwa ndi Mose, kenako Yoswa, potsatira zimene Yehova ananena. Munthu akafika mumzindawu, ankafotokoza nkhani yake kwa akulu pageti la mzindawo ndipo ankamulandira bwino. Poopa kuti anthu opha anzawo mwadala angapezerepo mwayi, munthuyo ankakazengedwa mlandu kumzinda umene anaphera mnzakeyo kuti zidziwike ngati alidi wosalakwa. Akapezeka kuti ndi wosalakwadi, ankabwerera kumzinda wothawirako ndipo ankayenera kukhala mumzindawo osatuluka mpaka imfa yake kapena imfa ya mkulu wansembe.—Nu 35:6, 11-15, 22-29; Yos 20:2-8.

 • Mkate wachionetsero.

  Mitanda 12 ya mkate imene inkaikidwa mʼMalo Oyera apachihema kapena mʼkachisi. Inkaikidwa patebulo, mbali ina 6 mbali ina 6. Inkatchedwanso kuti “mikate yosanjikiza,” komanso “mikate yoonetsa kwa Mulungu.” Pa tsiku la Sabata, mikateyi ankaichotsapo nʼkuikapo yatsopano. Ansembe okha ndi amene ankayenera kudya mikate yomwe yachotsedwayo. (2Mb 2:4; Mt 12:4; Eks 25:30; Le 24:5-9; Ahe 9:2)—Onani Zakumapeto B5.

 • Mkhalapakati.

  Munthu amene amagwirizanitsa mbali ziwiri kapena magulu awiri. Malemba amasonyeza kuti Mose anali mkhalapakati wa pangano la Chilamulo, pomwe Yesu ndi mkhalapakati wa pangano latsopano.—Aga 3:19; 1Ti 2:5.

 • Mkhristu.

  Dzina limene Mulungu anapereka kwa otsatira a Khristu.—Mac 11:26; 26:28.

 • Mkono.

  Muyezo wodziwira kutalika kwa chinthu ndipo ankayeza kuchokera pa chigongono kufika pamapeto pa chala chapakati. Kwa Aisiraeli, muyezo wa mkono unali pafupifupi masentimita 44.5, koma analinso ndi muyezo wina wotalikirapo umene unali pafupifupi masentimita 51.8. (Ge 6:15; Lu 12:25)—Onani Zakumapeto B14.

 • Mkulu wa Angelo.

  MʼBaibulo, dzina lakuti “mkulu wa angelo” limagwiritsidwa ntchito mʼnjira yosonyeza kuti alipo mmodzi yekha. Baibulo limatchula dzina la mkulu wa angelo kuti ndi Mikayeli.—Da 12:1; Yuda 9; Chv 12:7.

 • Mkulu wa ansembe.

  MʼChilamulo cha Mose, ameneyu anali wansembe wa udindo waukulu amene ankaimira anthu pamaso pa Mulungu komanso ankayangʼanira ansembe ena. Ankadziwikanso kuti “wansembe wamkulu.” (2Mb 26:20; Eza 7:5) Iye yekha ndi amene ankaloledwa kulowa mʼMalo Oyera Koposa amʼchihema ndipo kenako amʼkachisi koma ankachita zimenezi pa Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo basi. Mawu akuti “mkulu wa ansembe” amanenanso za Yesu Khristu.—Le 16:2, 17; 21:10; Mt 26:3; Ahe 4:14.

 • Mkulu wa boma.

  Munthu waudindo wotsikirapo poyerekeza ndi masatarapi mu ufumu wa Babulo. Akuluakulu a boma otchulidwa mʼBaibulo ankayangʼanira anthu anzeru mʼnyumba yachifumu ku Babulo. Akuluakulu a boma amatchulidwanso mu ulamuliro wa Mfumu Dariyo wa ku Mediya.—Da 2:48; 6:7.

 • Mkulu; Wachikulire.

  Bambo wamkulu. Koma mʼMalemba mawuwa amanena za munthu amene ali ndi udindo kudera kapena mʼdziko. Mʼbuku la Chivumbulutso mawuwa amanenanso za zolengedwa zakumwamba. Mawu a Chigiriki akuti pre·sbyʹte·ros amamasuliridwa kuti “mkulu” akamanena za anthu amene ali ndi udindo wotsogolera mumpingo wa Chikhristu.—Eks 4:29; Miy 31:23; 1Ti 5:17; Chv 4:4.

 • Mlembi.

  Munthu wokopera Malemba a Chiheberi. Pa nthawi ya Yesu, mawuwa ankanena za anthu amene anali ophunzira Chilamulo omwenso ankatsutsa Yesu.—Eza 7:6 mawu amʼmunsi; Mko 12:38, 39; 14:1.

 • Mliri.

  Matenda alionse amene ankafalikira mofulumira komanso kupha anthu ambiri. Nthawi zambiri miliri inkachitika chifukwa choti Mulungu wapereka chiweruzo chake.—Nu 14:12; Eze 38:22, 23; Amo 4:10.

 • Mlonda.

  Munthu amene amalondera anthu kapena katundu ndipo nthawi zambiri amachita zimenezi usiku. Alonda akale ankaliza lipenga akaona zoopsa. Iwo ankakonda kukhala pamwamba pa mipanda ya mzinda kapena pansanja kuti aziona anthu amene akubwera asanafike pafupi. Asilikali ankakhalanso ndi alonda awo. Aneneri analinso ngati alonda a mtundu wa Isiraeli chifukwa ankachenjeza anthu za tsoka limene likubwera.—2Mf 9:20; Eze 3:17.

 • Mnazareti.

  Dzina limene Yesu ankadziwika nalo chifukwa chakuti ankachokera mʼtauni ya Nazareti. Dzinali ndi logwirizana ndi mawu a Chiheberi otanthauza “mphukira” amene anagwiritsidwa ntchito pa Yesaya 11:1. Kenako otsatira a Yesu ankatchedwanso anthu a ku Nazareti.—Mt 2:23; Mac 24:5.

 • Mnaziri.

  Mawuwa akuchokera ku mawu a Chiheberi amene amatanthauza “Wosankhidwa,” “Wodzipereka,” “Wopatulidwa.” Anaziri analipo magulu awiri. Ena ankadzipereka okha kuti akhale anaziri pomwe ena ankasankhidwa ndi Mulungu. Mwamuna kapena mkazi ankatha kupanga lumbiro lapadera kwa Yehova kuti akhala Mnaziri pa nthawi inayake. Anthu amene ankadzipereka kuti akhale Anaziri ankaletsedwa zinthu zitatu. Sankafunika kumwa mowa kapena kudya zinthu zochokera ku mphesa, sankafunika kumeta tsitsi komanso sankafunika kukhudza mtembo. Anthu amene Mulungu wawasankha kuti akhale Anaziri ankakhala choncho kwa moyo wawo wonse ndipo Yehova ankafotokoza zimene ayenera kuchita.—Nu 6:2-7; Owe 13:5.

 • Mneneri.

  Munthu amene Mulungu ankamugwiritsa ntchito pouza anthu zimene akufuna. Aneneri ankalankhula mʼmalo mwa Mulungu. Ankafotokoza zimene zidzachitike mʼtsogolo, kuphunzitsa anthu mfundo za Yehova komanso kuwauza malamulo ndi ziweruzo zake.—Amo 3:7; 2Pe 1:21.

 • Moleki.

  Mulungu wa Aamoni ndipo zikuoneka kuti amatchedwanso Malikamu, Milikomu ndi Moloki. Mwina limeneli ndi dzina lake laudindo osati dzina lake lenileni. Chilamulo cha Mose chinkanena kuti aliyense wopereka nsembe ana ake kwa Moleki aziphedwa.—Le 20:2; Yer 32:35; Mac 7:43.

 • Moloki.​—

  Onani MOLEKI.

 • Mpando woweruzira milandu.

  Malo okwera amene anali ndi masitepe ndipo anthu audindo ankakhala pamenepo kuti alankhule ndi anthu kapena apereke chiweruzo. Mawu akuti “mpando woweruzira wa Mulungu” kapena “mpando woweruzira milandu wa Khristu” ndi ophiphiritsa ndipo amaimira zimene Yehova wakonza kuti adzaweruze anthu onse.—Aro 14:10; 2Ak 5:10; Yoh 19:13.

 • Mpatuko.

  Mawu ake a Chigiriki (a·po·sta·siʹa) amachokera ku mawu otanthauza “kuchoka.” Mawuwa amatanthauza “kusiya kapena kugalukira.” MʼMalemba a Chigiriki a Chikhristu mawuwa amagwiritsidwa ntchito ponena za anthu amene asiya kulambira koona.—Miy 11:9; Mac 21:21; 2At 2:3.

 • Mphatso zachifundo.

  Mphatso zimene zinkaperekedwa pothandiza anthu ovutika. Mphatso zoterezi sizitchulidwa mwachindunji mʼMalemba a Chiheberi, komabe mʼChilamulo munali malangizo osonyeza kuti Aisiraeli anali ndi udindo wothandiza anthu ovutika.—Mt 6:2.

 • Mphero.

  Mwala wozungulira umene ankauika pamwamba pa mwala unzake ndipo ankaugwiritsa ntchito popera ufa. Panali chikhomo chimene ankachiika pakati pa mwala wapansi chomwe chinkathandiza kuti mphero izizungulira. Kalelo, anthu ambiri ankakhala ndi mphero ndipo azimayi ndi amene ankazigwiritsa ntchito. Popeza banja linkadalira mphero kuti lipeze chakudya, Chilamulo cha Mose chinkaletsa kutenga mphero ngati chikole cha ngongole. Mphero zikuluzikulu zinkayendetsedwa ndi nyama.—De 24:6; Mko 9:42.

 • Mphete yodindira.

  Chidindo chimene munthu ankavala pachala kapena chimene chinkakhala pachingwe ndipo munthu ankavala chingwecho mʼkhosi. Chinkasonyeza kuti munthuyo ali ndi mphamvu kapena udindo winawake. (Ge 41:42)—Onani CHIDINDO.

 • Mpingo.

  Gulu la anthu limene linkasonkhana kuti lichite zinazake. MʼMalemba a Chiheberi mawuwa nthawi zambiri amanena za mtundu wa Aisiraeli. MʼMalemba a Chigiriki a Chikhristu mawuwa amanena za mipingo yosiyanasiyana ya Akhristu, koma nthawi zambiri amanena za Akhristu onse monga mpingo.—1Mf 8:22; Mac 9:31; Aro 16:5.

 • Mpukutu.

  Cholembapo chachitali chopangidwa kuchokera ku chikopa kapena gumbwa ndipo ankalemba mbali imodzi yokha. Nthawi zambiri ankaukulunga pakandodo. Malemba ankakoperedwa pamipukutu ndipo pamene Baibulo linkalembedwa, mabuku a nthawi imeneyo anali amenewa.—Yer 36:4, 18, 23; Lu 4:17-20; 2Ti 4:13.

 • Msonkhano.

  Gulu la anthu limene lasonkhana mochita kupangana. MʼMalemba a Chiheberi, mawuwa ankanena za Aisiraeli amene ankasonkhana kuti alambire Mulungu kapena achite zinthu zina zofunika kwa mtundu wonsewo.—De 16:8; 1Mf 8:5.

 • Msonkho.

  Zinthu zimene dziko kapena mfumu inkapereka ngati chizindikiro cha kugonjera ndipo ankachita zimenezi kuti akhalebe pamtendere kapena azitetezedwa. (2Mf 3:4; 18:14-16; 2Mb 17:11) Mawuwa amagwiritsidwanso ntchito ponena za msonkho umene munthu ankapereka kwa munthu mnzake.—Ne 5:4; Aro 13:7.

 • Mtengo.

  Mtengo woongoka umene ankapachikapo munthu amene ali ndi mlandu. Anthu a mitundu ina ankaphera munthu pamtengo kapena kupachika mtembo wake kuti achenjeze anthu ena kapena amuchititse manyazi. Asuri ankachita nkhanza kwambiri pankhondo chifukwa akagwira adani awo ankawapachika powaboola ndi mtengo pamimba womwe unkafika mʼchifuwa. Koma Ayuda, mogwirizana ndi malamulo awo, munthu amene wapalamula mlandu waukulu monga kunyoza Mulungu kapena kulambira mafano ankaphedwa kaye ndi miyala kapena mʼnjira ina, kenako nʼkupachika mtembo wake pamtengo kuti ena atengerepo phunziro. (De 21:22, 23; 2Sa 21:6, 9) Nthawi zina, Aroma ankangomangirira munthu pamtengo moti ankakhala masiku angapo kenako nʼkufa chifukwa cha ululu, ludzu, njala kapena kutentha kwa dzuwa. Koma nthawi zina ankamukhomera manja ndi mapazi pamtengo ngati mmene anachitira ndi Yesu. (Lu 24:20; Yoh 19:14-16; 20:25; Mac 2:23, 36)—Onani MTENGO WOZUNZIKIRAPO.

 • Mtengo wa moyo.

  Mtengo wamʼmunda wa Edeni. Baibulo silisonyeza kuti zipatso za mtengowu zinali ndi mphamvu yopatsa moyo. Koma unali chizindikiro chakuti Yehova angapereke moyo wosatha kwa anthu amene wawalola kudya zipatso za mtengowo.—Ge 2:9; 3:22.

 • Mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa.

  Mtengo umene unali mʼmunda wa Edeni womwe Mulungu anaugwiritsa ntchito ngati chizindikiro chakuti iye ali ndi ufulu wopatsa anthu mfundo zowathandiza kudziwa “chabwino” ndi “choipa.”—Ge 2:9, 17.

 • Mtengo woombera nsalu.

  Mtengo umene ankaugwiritsa ntchito poluka ulusi kuti apange nsalu.—Eks 39:27.

 • Mtengo wozunzikirapo.

  Mawu ake a Chigiriki ndi akuti stau·rosʹ, kutanthauza mtengo woima mowongoka ngati umene anapachikapo Yesu pomupha. Palibe umboni wakuti inkakhala mitengo iwiri yopingasa, ngati mitanda imene anthu osalambira Mulungu ankagwiritsa ntchito ngati chizindikiro chachipembedzo kwa nthawi yaitali Khristu asanabwere. Mawu akuti “mtengo wozunzikirapo” amasonyeza tanthauzo la mawu ake a Chigiriki chifukwa mawu akuti stau·rosʹ amagwiritsidwanso ntchito ponena za kuzunzika, kuvutika kapena manyazi ndipo zonsezi ndi zimene otsatira a Yesu amakumana nazo. (Mt 16:24; Ahe 12:2)—Onani MTENGO.

 • Mtsuko woyezera.

  Mogwirizana ndi zimene ofufuza zinthu zakale anapeza pazidutswa za choyezera chokhala ndi dzina limeneli, mtsukowu unkakhala wa pafupifupi malita 22. Zoyezera zina amazifotokoza potengera kukula kwa mtsuko umenewu. (1Mf 7:38; Eze 45:14)—Onani Zakumapeto B14.

 • Mtumiki Wamkulu.

  Mawu ake a Chigiriki amatanthauza “Mtsogoleri Wamkulu.” Mawuwa amanena za udindo wofunika kwambiri wa Yesu Khristu womasula anthu kumavuto obwera chifukwa cha uchimo nʼkuwatsogolera ku moyo wosatha.—Mac 3:15; 5:31; Ahe 2:10; 12:2.

 • Mtumiki wothandiza.

  Mawu ake a Chigiriki ndi akuti di·aʹko·nos, ndipo amamasuliridwa kuti “mtumiki.” “Mtumiki wothandiza” ndi munthu amene amatumikira mothandiza akulu mumpingo. Kuti munthu akhale mtumiki amafunika kukwaniritsa mfundo zina za mʼBaibulo.—1Ti 3:8-10, 12.

 • Mtumwi.

  Mawuwa amatanthauza “wotumidwa” ndipo amagwiritsidwa ntchito ponena za Yesu ndi anthu omwe anatumidwa kukatumikira anthu ena. Nthawi zambiri amagwiritsidwa ntchito ponena za gulu la ophunzira 12 amene Yesu anawasankha kuti azimuimira.—Mko 3:14; Mac 14:14.

 • Mule.

  Utomoni wonunkhira wochokera ku zitsamba zosiyanasiyana komanso mitengo ingʼonoingʼono ya mʼgulu la Commiphora. Mule anali mʼgulu la zinthu zopangira mafuta opatulika odzozera. Ankamugwiritsa ntchito ponunkhiritsa zinthu monga zovala kapena mabedi komanso ankamuphatikiza ndi mafuta odzola. Mule ankagwiritsidwanso ntchito pokonza thupi la munthu wakufa kuti akaliike mʼmanda.—Eks 30:23; Miy 7:17; Yoh 19:39.

 • Mulungu woona.

  Mawu ake a Chiheberi ankawagwiritsa ntchito ponena za “Mulungu.” Mʼmavesi ambiri mawuwa amasonyeza kuti Yehova ndi Mulungu woona ndipo ndi wosiyana ndi milungu yabodza. Mawu akuti “Mulungu woona” amathandiza kumveketsa bwino tanthauzo la mawu a Chiheberiwo mʼmavesi amenewa.—Ge 5:22, 24; 46:3; De 4:39.

 • Mutilabeni.

  Mawu amene amapezeka pakamutu ka pa Salimo 9. Anthu ena amati mawuwa amatanthauza “zokhudza imfa ya mwana wamwamuna.” Ndipo ena amati linali dzina kapena mawu oyamba amene ankawagwiritsa ntchito poimba salimoli.

 • Mutu wa chipilala.

  Mbali yapamwamba ya chipilala. Zipilala ziwiri zotchedwa Yakini ndi Boazi, zomwe zinali kutsogolo kwa kachisi wa Solomo, zinali ndi mitu ikuluikulu. (1Mf 7:16)—Onani Zakumapeto B8.

 • Mwala wapakona.

  Mwala umene unkaikidwa pakona polumikiza makoma awiri ndipo unkathandiza kuti makomawo alimbe. Mwala wapakona wofunika kwambiri unkakhala pamaziko. Anthu akafuna kumanga nyumba zikuluzikulu kapena mpanda wa mzinda ankasankha mwala wolimba kwambiri. Mawuwa amagwiritsidwanso ntchito mophiphiritsira ponena za kukhazikitsidwa kwa dziko. Yesu amanenedwa kuti ndi “mwala wapakona wa maziko” a mpingo wa Chikhristu womwe umayerekezeredwa ndi nyumba yauzimu.—Aef 2:20; Yob 38:6.

 • Mwamuna wofulidwa.

  Amuna oterewa anali atumiki a mʼnyumba yachifumu kapena oyangʼanira mfumukazi ndi akazi aangʼono a mfumu. Panalinso anthu ena amene ankapatsidwa udindo mʼnyumba yachifumu omwe sankakhala ofulidwa. Mawu oti kufulidwa amagwiritsidwanso ntchito mophiphiritsira ponena za anthu amene “sakwatira chifukwa cha Ufumu wakumwamba.” Iwo amadziletsa nʼcholinga choti azichita zambiri potumikira Mulungu.—Mt 19:12; Est 2:15; Mac 8:27.

 • Mwana wa Davide.

  Nthawi zambiri mawuwa amanena za Yesu pofuna kutsindika mfundo yakuti iye ndi mbadwa ya Davide ndipo ndi woyenera kukhala mfumu mogwirizana ndi pangano la Ufumu.—Mt 12:23; 21:9.

 • Mwana wa munthu.

  Mawu amene amapezeka maulendo 80 mʼMauthenga Abwino. Mawuwa amanena za Yesu Khristu ndipo amasonyeza kuti atabadwa, anakhala munthu weniweni, osati mngelo yemwe anangovala thupi la munthu. Mawuwa amasonyezanso kuti Yesu ndi amene anakwaniritsa ulosi wa pa Danieli 7:13, 14. MʼMalemba a Chiheberi, mawuwa anagwiritsidwa ntchito ponena za Ezekieli ndi Danieli powasiyanitsa ndi Mulungu amene anawapatsa uthenga woti auze anthu.—Eze 3:17; Da 8:17; Mt 19:28; 20:28.

 • Mwana woyamba kubadwa.

  Nthawi zambiri mawuwa ankanena za mwana wamwamuna wamkulu wa bambo (osati wa mayi). Kale, mwana wamwamuna woyamba kubadwa ankalemekezedwa kwambiri mʼbanja ndipo ndi amene ankatsogolera banjalo bambo ake akamwalira. Mawuwa amanenanso za mwana woyamba kubadwa wa nyama ndipo nthawi zina ankangotchedwa kuti “woyamba.”—Eks 11:5; 13:12; Ge 25:33; Akl 1:15.

 • Myuda.

  Dzina limene linkagwiritsidwa ntchito ponena za munthu wa fuko la Yuda pambuyo poti ufumu wa mafuko 10 a Isiraeli wagonjetsedwa. (2Mf 16:6) Aisiraeli atabwera ku ukapolo ku Babulo, dzina lakuti Ayuda linkagwiritsidwa ntchito ponena za Aisiraeli a mafuko osiyanasiyana amene anabwerera ku Isiraeli. (Eza 4:12) Patapita nthawi, dzinali linkagwiritsidwa ntchito padziko lonse posiyanitsa Aisiraeli ndi anthu a mitundu ina. (Est 3:6) Paulo anagwiritsanso ntchito dzinali mophiphiritsa pofuna kusonyeza kuti mtundu wa munthu si nkhani yaikulu mumpingo wa Chikhristu.—Aro 2:28, 29; Aga 3:28.

 • Mzati wopatulika.

  Mawu ake a Chiheberi ndi akuti ’ashe·rahʹ ndipo amatanthauza (1) mzati wopatulika woimira mulungu wamkazi wobereketsa wa a Kanani dzina lake Asherah, kapena (2) chifaniziro cha Asherah weniweniyo. Mizati yake inkakhala yowongoka ndipo mbali ina inkapangidwa kuchokera ku mitengo yomwe mwina inkakhala yosasema.—De 16:21; Owe 6:26; 1Mf 15:13.

 • Mzimu.

  Mawu a Chiheberi akuti ruʹach ndiponso a Chigiriki akuti pneuʹma, amene amamasuliridwa kuti mzimu amatanthauza zambiri. Matanthauzo onsewo amanena za chinthu chosaoneka koma mphamvu yake imaoneka. Mawu a Chiheberi komanso a Chigirikiwa amanena za (1) mphepo, (2) mphamvu ya moyo ya mʼzolengedwa zapadziko lapansi, (3) mphamvu yochokera mumtima wophiphiritsa wa munthu imene imamuchititsa kuti azichita kapena kulankhula mʼnjira inayake, (4) mawu ouziridwa ochokera kwa winawake wosaoneka, (5) mizimu ndiponso (6) mphamvu yogwira ntchito ya Mulungu kapena kuti mzimu woyera.—Eks 35:21; Sl 104:29; Mt 12:43; Lu 11:13.

 • Mzimu woyera.

  Mphamvu imene Mulungu amagwiritsa ntchito pofuna kukwaniritsa cholinga chake. Ndi woyera chifukwa chakuti umachokera kwa Yehova yemwe ndi woyera komanso wolungama kuposa aliyense ndiponso chifukwa choti Mulungu amaugwiritsa ntchito pofuna kuchita zinthu zoyera.—Lu 1:35; Mac 1:8.

 • Mzinda wa Davide.

  Dzina limene linaperekedwa ku mzinda wa Yebusi pambuyo poti Davide waugonjetsa nʼkumangapo nyumba yake yachifumu. Umatchedwanso kuti Ziyoni. Unali kumʼmwera chakumʼmawa komanso inali mbali yoyamba kumangidwa mumzinda wa Yerusalemu.—2Sa 5:7; 1Mb 11:4, 5.

N

 • Nado.

  Mafuta onunkhira komanso odula kwambiri. Ankakhala ofiirira ndipo ankachokera ku zomera zotchedwa Nardostachys jatamansi. Popeza anali odula, nthawi zina ankawasakaniza ndi mafuta ena otsikirapo ndipo nado wina sankakhala weniweni. Mpake kuti Maliko ndi Yohane ananena kuti mafuta amene Yesu anathiridwa anali “nado weniweni.”—Mko 14:3; Yoh 12:3.

 • Ndodo yachifumu.

  Ndodo imene wolamulira ankanyamula posonyeza kuti ndi mfumu komanso ali ndi mphamvu.—Ge 49:10; Ahe 1:8.

 • Nduwira.

  Nsalu imene ankavala kumutu ngati mpango. Mkulu wa ansembe ankavala nduwira ya nsalu yabwino kwambiri ndipo kutsogolo kwa nduwirayo kunkakhala kachitsulo konyezimira kagolide komwe ankakamangirira kuchingwe chabuluu. Mfumu inkavala nduwira mkati mwa chipewa chake chachifumu. Yobu anagwiritsa ntchito mawuwa mophiphiritsa pamene anayerekezera chilungamo chake ndi nduwira.—Eks 28:36, 37; Yob 29:14; Eze 21:26.

 • Nehiloti.

  Tanthauzo la mawuwa silikudziwika koma amapezeka pakamutu ka pa Salimo 5. Ena amaganiza kuti mawuwa amanena za choimbira chochita kuuzira chifukwa choti mawu ake a Chiheberi amafanana ndi oti cha·lilʹ (chitoliro). Komabe mwina mawuwa amangonena za kaimbidwe.

 • Ngʼanjo.

  Chinthu chosungunuliramo zitsulo kapena kuwotchera mbiya ndi zinthu zina zadothi. Kale anthu ankapanga ngʼanjo pogwiritsa ntchito njerwa kapena miyala. Ngʼanjo yowotchera mbiya, zinthu zina zadothi kapena laimu inkatchedwanso uvuni.—Ge 15:17; Da 3:17; Chv 9:2.

 • Nisani.

  Dzina latsopano limene anapatsa mwezi wa Abibu pambuyo poti Aisiraeli abwera ku ukapolo wa ku Babulo. Unali mwezi woyamba pakalendala yopatulika ya Ayuda komanso mwezi wa 7 pakalendala ya anthu onse. Unkayamba pakati pa mwezi wa March mpaka pakati pa April. (Ne 2:1)—Onani Zakumapeto B15.

 • Njira.

  MʼMalemba, mawuwa amagwiritsidwa ntchito mophiphiritsa ponena za njira yochitira zinthu kapena khalidwe linalake lomwe ndi lovomerezeka kapena losavomerezeka kwa Yehova. Anthu amene ankatsatira Yesu Khristu ankanenedwa kuti amatsatira “Njirayo” kutanthauza kuti ankakhulupirira Yesu komanso kumutsanzira ndipo zimenezi zinkaonekera pa moyo wawo.—Mac 19:9.

 • Nsembe.

  Zinthu zimene munthu amapereka kwa Mulungu pofuna kumuthokoza, kuvomereza kuti walakwitsa komanso pofuna kuti akhalenso naye pa ubwenzi. Kuyambira nthawi ya Abele, anthu ankapereka nsembe zosiyanasiyana mwa kufuna kwawo ndipo nsembe zina zinkakhala za nyama. Chilamulo cha Mose chitaperekedwa, kupereka nsembe linali lamulo. Yesu atapereka moyo wake ngati nsembe yangwiro, nsembe za nyama sizinalinso zofunika. Komabe Akhristu amapereka nsembe zauzimu kwa Mulungu.—Ge 4:4; Ahe 13:15, 16; 1Yo 4:10.

 • Nsembe yachakumwa.

  Nsembe ya vinyo imene ankaithira paguwa ndipo ankaipereka limodzi ndi nsembe zina zambiri. Paulo anagwiritsa ntchito mawuwa mophiphiritsa posonyeza kuti ankafunitsitsa kuthandiza Akhristu anzake.—Nu 15:5, 7; Afi 2:17.

 • Nsembe yakupalamula.

  Nsembe imene munthu ankapereka chifukwa cha machimo ake. Inkasiyana pangʼono ndi nsembe zina zamachimo chifukwa chakuti inkaperekedwa posonyeza kuti munthu akuvomereza zoti walakwira Mulungu kapena waphwanya ufulu wa munthu wina. Nsembeyi inkamasulanso munthu kuti asalangidwe chifukwa cha zimene analakwitsazo.—Le 7:37; 19:22; Yes 53:10.

 • Nsembe yalonjezo.

  Nsembe imene munthu ankapereka mwa kufuna kwake pambuyo poti walonjeza zinthu zinazake.—Le 23:38; 1Sa 1:21.

 • Nsembe yamachimo.

  Nsembe imene munthu ankapereka chifukwa choti wachita tchimo mosadziwa poti si wangwiro. Panali nyama zosiyanasiyana zimene ankapereka mogwirizana ndi udindo wa munthuyo komanso mmene zinthu zilili pa moyo wake. Ankatha kupereka nyama yaikulu monga ngʼombe kapena nyama yaingʼono monga njiwa.—Le 4:27, 29; Heb 10:8.

 • Nsembe yopsereza.

  Nyama imene inkatenthedwa paguwa la nsembe ngati nsembe yathunthu yopereka kwa mulungu. Palibe mbali iliyonse ya nyamayo (ngʼombe yamphongo, nkhosa yamphongo, mbuzi yamphongo, njiwa kapena nkhunda) imene inkatengedwa ndi wopereka nsembeyo.—Eks 29:18; Le 6:9.

 • Nsembe yoyendetsa uku ndi uku.

  Nsembe imene akamaipereka, munthu ankaitenga mʼmanja mwake ndipo wansembe ankaika manja ake pansi pa manja a munthuyo nʼkumayendetsa nsembeyo uku ndi uku. Nthawi zina wansembe ndi amene ankatenga nsembeyo nʼkumaiyendetsa uku ndi uku. Zimene ankachitazi zinkaimira kupereka nsembeyo kwa Yehova.—Le 7:30.

 • Nsembe zamgwirizano.

  Nsembe zimene ankazipereka kwa Yehova kuti akhale naye pamtendere. Amene ankadya nsembeyi ndi munthu woperekayo ndi banja lake, wansembe amene akupereka nsembeyo komanso ansembe ena amene akugwira ntchito pa tsikulo. Ankawotcha mafuta a nsembeyo ndipo akatero zinkakhala ngati Yehova wailandira. Magazi, omwe amaimira moyo, ankaperekedwanso kwa Yehova. Zinali ngati ansembe, banja limene lapereka nsembeyo komanso Yehova akudyera limodzi ndipo zimenezi zinkasonyeza kuti onse ali pamtendere.—Le 7:29, 32; De 27:7.

 • Nsembe zoyamikira.

  Nsembe zimene munthu ankapereka pofuna kutamanda Mulungu chifukwa cha chikondi chake chokhulupirika komanso kuwolowa manja kwake. Pa tsikulo anthu ankadya nyama, mikate ya zofufumitsa ndiponso mikate yopanda zofufumitsa. Nyamayi ankafunika kuidya tsiku lomwelo.—2Mb 29:31.

 • Nthanda.

  Mawuwa angatanthauzenso “nyenyezi yamʼmawa.” Imeneyi ndi nyenyezi yomalizira kutuluka imene imaonekera chakumʼmawa dzuwa lisanatuluke ndipo imasonyeza kuti kukucha.—Chv 22:16; 2Pe 1:19.

 • Nthawi.

  Mawu ake a Chigiriki ndi akuti ai·onʹ ndipo amatanthauza mmene zinthu zilili kapena zochitika zimene zikuchititsa nthawi inayake kukhala yosiyana ndi ina. Mawuwa sakunena za nthawi wamba. Baibulo likamanena kuti “nthawi ino” limatanthauza mmene zinthu zilili mʼdzikoli komanso mmene moyo wa anthu mʼdzikoli ulili. (2Ti 4:10) Mulungu atapereka Chilamulo kwa Aisiraeli, anayambitsa nthawi imene ena amaitchula kuti nthawi ya Aisiraeli kapena nthawi ya Ayuda. Koma pamene Yesu anapereka nsembe ya dipo, Mulungu anamugwiritsa ntchito poyambitsa nthawi ina yokhudza mpingo wa Akhristu odzozedwa. Uku kunali kuyamba kwa nthawi ya zinthu zenizeni zimene zinkaimiridwa ndi zinthu za mʼpangano la Chilamulo. Mawuwa amatha kugwiritsidwanso ntchito ponena za nthawi zosiyanasiyana, mmene zinthu zakhala zikuchitikira, mmene zilili panopa komanso mmene zidzakhalire mʼtsogolo.—Mt 24:3; Mko 4:19; Aro 12:2; 1Ak 10:11.

 • Nyanga.

  Mawuwa amanena za nyanga za nyama zomwe zinkagwiritsidwa ntchito ngati chomwera komanso chosungira zinthu ngati mafuta, inki ndi zodzikongoletsera. Zinkagwiritsidwanso ntchito ngati zipangizo zoimbira kapena zoperekera uthenga. (1Sa 16:1, 13; 1Mf 1:39; Eze 9:2) Mawu akuti “nyanga” nthawi zambiri amagwiritsidwanso ntchito mophiphiritsa ponena za mphamvu, kugonjetsa kapena kupambana.—De 33:17; Mik 4:13; Zek 1:19.

 • Nyanga za guwa lansembe.

  Zinthu zooneka ngati nyanga zimene zinkakhala mʼmakona 4 a maguwa ena. (Le 8:15; 1Mf 2:28)—Onani Zakumapeto B5 ndi B8.

 • Nyanja ya moto.

  Malo ophiphiritsira kumene ‘kumayaka moto ndi sulufule.’ Amatchulidwanso kuti “imfa yachiwiri.” Anthu ochimwa amene salapa, Mdyerekezi, imfa komanso Manda zidzaponyedwanso mʼnyanjayi. Popeza kuti Mdyerekezi yemwe ndi mzimu, komanso imfa ndi Manda zomwe sizipsa, zidzaponyedwa kumeneku, ndiye kuti nyanjayi ndi yophiphiritsa. Siikuimira kuzunza anthu mpaka kalekale koma kuziwonongeratu moti sizidzakhalakonso.—Chv 19:20; 20:14, 15; 21:8.

 • Nyenyezi yamʼmawa.​—

  Onani NTHANDA.

 • Nyimbo yoimba polira.

  Nyimbo yosonyeza kuti munthu ali ndi chisoni kwambiri chifukwa cha imfa ya mnzake kapena ya munthu amene amamukonda. Nyimbo ya maliro.—2Sa 1:17; Sl 7:Kam.

 • Nyimbo Yokwerera Kumzinda.

  Mawu apakamutu ka pa Salimo 120 mpaka 134. Pali maganizo osiyanasiyana okhudza tanthauzo la mawuwa. Koma anthu ambiri amakhulupirira kuti Aisiraeli ankaimba mosangalala masalimo 15 amenewa akamapita kukachita zikondwerero zitatu zapachaka kumzinda wa Yerusalemu womwe unali pamalo okwera mʼmapiri a ku Yuda.

O

 • Omeri.

  Muyezo wa zinthu ngati ufa ndi tirigu ndipo unali wofanana ndi malita 2.2. Ma omeri 10 ankakwana efa imodzi. (Eks 16:16, 18)—Onani Zakumapeto B14.

 • Onekisi.

  Miyalayi sinali yamtengo wapatali kwenikweni. Inali ya mtundu wa agate kapena chalcedony, koma yolimba. Inkakhala ndi mizere yoyera, yakuda, yabulawuni, yofiira, yotuwa komanso yagirini. Miyalayi inkagwiritsidwa ntchito popanga chovala chapadera cha mkulu wa ansembe.—Eks 28:9, 12; 1Mb 29:2; Yob 28:16.

 • Oweruza.

  Anthu amene Yehova ankawasankha kuti apulumutse anthu ake isanafike nthawi ya mafumu a Isiraeli.—Owe 2:16.

P

 • Pakati pa madzulo awiri.

  Nthawi imeneyi iyenera kuti inkayambira pamene dzuwa lalowa kukafika pamene mdima weniweni wagwa, mogwirizana ndi zimene akatswiri ena, Ayuda a Chikaraite ndiponso Asamariya amanena. Koma Afarisi ndi Arabi anali ndi maganizo osiyana ndi amenewa. Iwo ankati madzulo oyamba ndi pamene dzuwa layamba kupendeka ndipo madzulo achiwiri ndi kulowa kwa dzuwa kwenikweniko.—Eks 12:6.

 • Pangano.

  Mgwirizano wa pakati pa Mulungu ndi anthu kapena pakati pa anthu okhaokha. Amagwirizana kuti adzachita kapena sadzachita zinazake. Nthawi zina, amene ali mbali imodzi ya panganolo ndi amene ankayenera kuchita zimene zikufunikazo ndipo limeneli kwenikweni linkakhala lonjezo. Nthawi zina mbali zonse ziwiri zinkafunika kuchita zinazake. Kupatula pa mapangano a pakati pa Mulungu ndi anthu, Baibulo limanenanso za mapangano a pakati pa anthu, mafuko, mitundu kapena magulu a anthu. Mapangano ena, amene zotsatira zake ndi za nthawi yaitali, ndi a pakati pa Mulungu ndi Abulahamu, Davide komanso mtundu wa Isiraeli (pangano la Chilamulo) ndiponso Isiraeli wa Mulungu (pangano latsopano).—Ge 9:11; 15:18; 21:27; Eks 24:7; 2Mb 21:7.

 • Paradaiso.

  Paki yokongola kapena munda wamaluwa wokongola. Malo oyamba oterewa anali Edeni ndipo Yehova ndi amene anakonza malo amenewo kuti anthu awiri oyambirira azikhalamo. Yesu anasonyeza kuti dzikoli lidzakhala Paradaiso pamene ankalankhula ndi mmodzi mwa zigawenga zimene zinapachikidwa naye pafupi. Pa 2 Akorinto 12:4, mawuwa amanena za Paradaiso wamʼtsogolo ndipo pa Chivumbulutso 2:7, amanena za Paradaiso wakumwamba.—Nym 4:13; Lu 23:43.

 • Pasika.

  Chikondwerero chapachaka chimene chinkachitika pa 14 mʼmwezi wa Abibu (kenako unkatchedwa Nisani) pokumbukira kuti Aisiraeli anamasulidwa ku Iguputo. Pamwambowu ankapha mwana wa nkhosa (kapena wa mbuzi) nʼkumuwotcha ndipo ankamudya pamodzi ndi masamba owawa komanso mikate yopanda zofufumitsa.—Eks 12:27; Yoh 6:4; 1Ak 5:7.

 • Pentekosite.

  Chikondwerero chachiwiri pa zikondwerero zitatu zimene amuna a Chiyuda ankafunika kuchita ku Yerusalemu. Mawu akuti Pentekosite omwenso amatanthauza “(tsiku) la 50,” amagwiritsidwa ntchito mʼMalemba a Chigiriki ponena za Chikondwerero cha Zokolola kapena Chikondwerero cha Masabata chotchulidwa mʼMalemba a Chiheberi. Chinkachitika pa tsiku la 50 kuchokera pa Nisani 16.—Eks 23:16; 34:22; Mac 2:1.

 • Perisiya; Aperisiya.

  Dera komanso anthu amene nthawi zambiri amatchulidwa limodzi ndi Amedi. Poyamba, Aperisiya ankakhala kumʼmwera chakumadzulo kwa mapiri a ku Iran. Pa nthawi imene Koresi Wamkulu ankalamulira, Aperisiya ndi amene anali amphamvu kwambiri kuposa Amedi ngakhale kuti ankalamulira limodzi. (Malinga ndi zimene olemba mbiri ena amanena, bambo ake a Koresi anali a ku Perisiya ndipo mayi ake anali a ku Mediya.) Koresi anagonjetsa Ufumu wa Babulo mu 539 B.C.E. ndipo analola Ayuda amene anali ku ukapolo kuti abwerere kwawo. Ufumu wa Aperisiya unkayambira kumtsinje wa Indus kumʼmawa mpaka ku nyanja ya Aegean kumadzulo. Ayuda ankalamuliridwa ndi Aperisiya mpaka pamene Alekizanda Wamkulu anagonjetsa Aperisiyawo mu 331 B.C.E. Danieli anaona masomphenya okhudza Ufumu wa Perisiya ndipo ufumuwu umatchulidwa mʼbuku la Ezara, Nehemiya ndi Esitere. (Eza 1:1; Da 5:28; 8:20)—Onani Zakumapeto B9.

 • Phompho.

  Mawu ake a Chigiriki ndi akuti aʹbys·sos, ndipo amatanthauza “kuzama kwambiri” kapena “kuzama kosayerekezeka, kopanda malire.” Amagwiritsidwa ntchito mʼMalemba a Chigiriki a Chikhristu ponena za malo kapena moyo wangati wakundende. Mawuwa amanenanso za manda komanso zinthu zina.—Lu 8:31; Aro 10:7; Chv 20:3

 • Pimu.

  Muyezo komanso mtengo umene Afilisiti ankalipiritsa munthu akamunolela chinthu. Anthu ofukula zinthu zakale anapeza miyezo yamiyala ku Isiraeli yomwe inali ndi mawu a Chiheberi otanthauza “pimu” ndipo pa avereji, mwala uliwonse unali wolemera magalamu 7.8. Zimenezi zikusonyeza kuti pimu inali yopitirira hafu ya sekeli.—1Sa 13:20, 21.

 • Porneia.​—

  Onani CHIWEREWERE.

 • Puri.

  Chikondwerero chapachaka chimene chinkachitika pa 14 ndi pa 15 mwezi wa Adara. Ayuda ankachita izi pokumbukira kuti anapulumutsidwa pa nthawi ya Mfumukazi Esitere. Mawu akuti pu·rimʹ, omwe si a Chiheberi, amatanthauza “maere.” Chikondwerero cha Puri kapena Chikondwerero cha Maere chinapatsidwa dzinali potengera zimene Hamani anachita. Iye anachita maere kuti apeze tsiku limene angaphe Ayuda onse.—Est 3:7; 9:26.

R

 • Rahabi.

  Dzina limene limagwiritsidwa ntchito mophiphiritsa mʼbuku la Yobu, Masalimo ndi Yesaya (Rahabi wake si mayi wotchulidwa mʼbuku la Yoswa). Mʼbuku la Yobu, nkhani yake imatithandiza kudziwa kuti akunena za chilombo chamʼmadzi ndipo mʼmavesi ena chilombochi chimagwiritsidwa ntchito mophiphiritsa ponena za Iguputo.—Yob 9:13; Sl 87:4; Yes 30:7; 51:9, 10.

S

 • Sabata.

  Mawu ake a Chiheberi amatanthauza “kupuma” kapena “kusiya.” Linali tsiku la 7 pa mlungu wa Ayuda (linkayamba Lachisanu dzuwa likalowa nʼkukatha Loweruka dzuwa likalowanso). Chaka cha 7, chaka cha 50 ndiponso masiku ena a zikondwerero ankakhalanso a sabata. Pa Sabata, anthu sankayenera kugwira ntchito kupatula imene ansembe ankagwira kumalo opatulika. Mʼchaka cha Sabata, anthu sankayenera kulima minda yawo komanso sankayenera kukakamiza Aheberi anzawo kuti abweze ngongole. MʼChilamulo cha Mose, malamulo okhudza Sabata anali abwinobwino koma kenako atsogoleri achipembedzo anawonjezerapo mfundo zina moti pofika nthawi ya Yesu kusunga Sabata kunali kovuta kwambiri.—Eks 20:8; Le 25:4; Lu 13:14-16; Akl 2:16.

 • Salimo.

  Nyimbo yotamanda Mulungu. Masalimo ambiri anakonzedwa ngati nyimbo zoti anthu olambira Mulungu aziimba ndipo nthawi zina ankaimba pagulu polambira Yehova Mulungu kukachisi wa ku Yerusalemu.—Lu 20:42; Mac 13:33; Yak 5:13.

 • Samariya.

  Mzinda womwe kwa zaka 200 unali likulu la ufumu wakumpoto wa mafuko 10 a Isiraeli ndipo dzinali linkaimiranso dera lonselo. Mzindawu unamangidwa paphiri lotchedwa Samariya. Pa nthawi ya Yesu, dzina loti Samariya linkaimira dera lomwe kumpoto kwake kunali Galileya ndipo kumʼmwera kwake kunali Yudeya. Yesu ankapewa kulalikira kuderali, koma nthawi zina ankadutsako ndipo ankalankhulana ndi anthu akumeneko. Petulo anagwiritsa ntchito makiyi a Ufumu achiwiri pamene anthu a ku Samariya analandira mzimu woyera. (1Mf 16:24; Yoh 4:7; Mac 8:14)—Onani Zakumapeto B10.

 • Satalapi.

  Bwanamkubwa wa mu ufumu wa Babulo ndi Perisiya. Ankasankhidwa ndi mfumu kuti azilamulira zigawo.—Eza 8:36; Da 6:1.

 • Satana.

  Mawu ake a Chiheberi amatanthauza “wotsutsa.” Nthawi zambiri mawuwa amagwiritsidwa ntchito ponena za Satana Mdyerekezi yemwe ndi mdani wamkulu wa Mulungu.—Yob 1:6; Mt 4:10; Chv 12:9.

 • Sebati.

  Dzina la mwezi wa 11 pakalendala yopatulika ya Ayuda komanso mwezi wa 5 pakalendala ya anthu onse, Aisiraeli atabwera kuchokera ku ukapolo wa ku Babulo. Unkayamba pakati pa mwezi wa January mpaka pakati pa February. (Zek 1:7)—Onani Zakumapeto B15.

 • Sekeli.

  Ndalama komanso muyezo wa kulemera kwa zinthu. Sekeli inali yofanana ndi magalamu 11.4. Mawu akuti “sekeli yakumalo oyera” ayenera kuti ankagwiritsidwa ntchito ponena za muyezo wokwanira ndendende kapena wofanana ndi muyezo umene unkasungidwa kuchihema. Nʼkutheka kuti panali sekeli yachifumu (yosiyana ndi masekeli ena) kapena muyezo umene unkasungidwa kunyumba yachifumu.—Eks 30:13.

 • Selah.

  Mawu okhudza nyimbo kapena ndakatulo opezeka mʼbuku la Masalimo ndi Habakuku. Nʼkutheka kuti amatanthauza kuima kaye poimba nʼcholinga choti anthu aganizire kwambiri zimene akuimbazo kapena kuti atsindike mawu enaake amene aimbidwa. Baibulo la Chigiriki la Septuagint linamasulira mawuwa kuti di·aʹpsal·ma, kutanthauza “kuima kaye poimba.”—Sl 3:4; Hab 3:3.

 • Seminiti.

  Mawu amene amagwiritsidwa ntchito pa nyimbo ndipo amatanthauza “cha 8.” Mawuwa amanena za kuimba motsitsa. Akamanena za zida zoimbira, mawuwa amanena za zida za besi. Munyimbo amanena za zipangizo zoimbidwa motsitsa komanso mawu otsitsa mofanana ndi zipangizozo.—1Mb 15:21; Sl 6:Kam; 12:Kam.

 • Seya.

  Muyezo wa zinthu ngati ufa ndi tirigu. Tikatengera muyezo wa mtsuko ndiye kuti muyezo wa seya unali wofanana ndi malita 7.33. (2Mf 7:1)—Onani Zakumapeto B14.

 • Sheol.

  Amenewa ndi mawu a Chiheberi ofanana ndi a Chigiriki akuti “Hades.” Amamasuliridwa kuti “Manda” (wa “M” wamkulu) pofuna kusonyeza kuti ndi manda a anthu onse ndipo ndi osiyana ndi manda amodzi.—Ge 37:35; Sl 16:10; Mac 2:31 (mawu amʼmunsi).

 • Sipeloti.

  Tirigu wotsikirapo (Triticum spelta), ndipo ankavuta kumusiyanitsa ndi mankhusu ake popuntha.—Eks 9:32.

 • Siriya; Asiriya.​—

  Onani ARAMU; ANTHU A CHIARAMU.

 • Sivani.

  Dzina la mwezi wachitatu pakalendala yopatulika ya Ayuda komanso mwezi wa 9 pakalendala ya anthu onse, Aisiraeli atabwera kuchokera ku ukapolo ku Babulo. Unkayamba pakati pa mwezi wa May mpaka pakati pa June. (Est 8:9)—Onani Zakumapeto B15.

 • Sunagoge.

  Mawuwa amatanthauza “kubweretsa pamodzi” kapena “msonkhano.” Koma mʼmalemba ambiri mawuwa amanena za nyumba kapena malo amene Ayuda ankasonkhana kuti awerenge Malemba, alandire malangizo, alalikire komanso apemphere. Pa nthawi ya Yesu, tauni iliyonse yaikulu bwino ku Isiraeli inkakhala ndi sunagoge ndipo mizinda ikuluikulu inkakhala ndi masunagoge oposa mmodzi.—Lu 4:16; Mac 13:14, 15.

 • Suriti.

  Magombe awiri akuluakulu osazama akumpoto kwa Africa mʼdziko la Libya. Anthu oyenda panyanja ankaopako chifukwa choti mchenga unkasunthasuntha chifukwa cha mphepo. (Mac 27:17)—Onani Zakumapeto B13.

T

 • Talente.

  Muyezo waukulu kwambiri wa kulemera kwa zinthu komanso ndalama yaikulu kwambiri ya Aheberi. Ndalama zokwana talente imodzi zinkakhala zolemera makilogalamu 34.2. Talente ya Chigiriki inali yocheperapo ndipo inkalemera makilogalamu 20.4. (1Mb 22:14; Mt 18:24)—Onani Zakumapeto B14.

 • Tamuzi.

  (1) Dzina la mulungu amene azimayi ampatuko a Chiheberi ankamulirira ku Yerusalemu. Anthu ena amati dzinali linali la Mfumu Tamuzi ndipo atamwalira anthu anayamba kumuona ngati mulungu. Mʼzolemba zina za ku Babulo, Tamuzi amatchedwa Dumuzi ndipo ankaonedwa kuti ndi wachikondi wa mulungu wamkazi wobereketsa dzina lake Inana (mulungu wa Ababulo wotchedwa Ishtar). (Eze 8:14) (2) Dzina la mwezi wa 4 pakalendala yopatulika ya Ayuda komanso mwezi wa 10 pakalendala ya anthu onse, Aisiraeli atabwera kuchokera ku ukapolo wa ku Babulo. Unkayamba pakati pa mwezi wa June mpaka pakati pa July.—Onani Zakumapeto B15.

 • Tatalasi.

  MʼMalemba a Chigiriki a Chikhristu mawuwa amanena za moyo wokhala ngati wakundende ndipo angelo a mʼmasiku a Nowa anapatsidwa chilango chokhala moyo umenewo. Pa 2 Petulo 2:4, mawu amene anawagwiritsa ntchito akuti tar·ta·roʹo (“kuponya kutatalasi”) satanthauza kuti angelo amene anachimwa anaponyedwa ku tatalasi wotchulidwa munthano zambiri zachikunja (yomwe ndi ndende yapansi pa nthaka komanso malo amdima kumene milungu ingʼonoingʼono imakhala). Koma amatanthauza kuti Mulungu anawachotsa kumwamba, kuwalanda maudindo awo ndiponso anawachititsa kuti azikhala moyo ngati ali mumdima wandiweyani moti sangadziwe zolinga zilizonse za Mulungu. Mdimawu umasonyezanso kuti tsogolo lawo si lowala chifukwa Malemba amanena kuti angelo amenewa adzawonongedwa pamodzi ndi mtsogoleri wawo Satana Mdyerekezi ndipo sadzakhalaponso. Choncho mawu akuti Tatalasi amanena za moyo wotsika kwambiri umene angelo ogalukirawa akukhala. Mawuwa ndi osiyana ndi “phompho” lotchulidwa pa Chivumbulutso 20:1-3.

 • Tebeti.

  Dzina la mwezi wa 10 pakalendala yopatulika ya Ayuda komanso mwezi wa 4 pakalendala ya anthu onse, Aisiraeli atabwera kuchokera ku ukapolo wa ku Babulo. Unkayamba pakati pa mwezi wa December mpaka pakati pa January. Nthawi zambiri umangotchulidwa kuti “mwezi wa 10.” (Est 2:16)—Onani Zakumapeto B15.

 • Temberero.

  Kuopseza kapena kunena kuti zoipa zinazake zichitikira munthu kapena chinthu. Koma sizitanthauza zimene munthu amanena potukwana kapena akapsa mtima kwambiri. Temberero ndi kulengeza kapena kuneneratu zoipa zimene zichitikire munthu ndipo ngati yemwe watembererayo ndi Mulungu kapena munthu waudindo, mawu ake amakhala ngati ulosi ndipo zimachitikadi.—Ge 12:3; Nu 22:12; Aga 3:10.

 • Tishiri.​—

  Onani ETANIMU komanso Zakumapeto B15.

 • Tsiku la Chiweruzo.

  Tsiku kapena nthawi inayake pamene magulu a anthu, mitundu komanso anthu onse adzaweruzidwe ndi Mulungu. Pa nthawiyi, anthu amene adzaweruzidwe kuti sakuyenera kukhala ndi moyo, adzaphedwa. Padzakhalanso anthu ena amene adzapatsidwe mwayi woti akhale ndi moyo mpaka kalekale. Yesu ndi atumwi ake ananenapo za “Tsiku la Chiweruzo” pamene anthu amoyo komanso amene anamwalira adzaweruzidwe.—Mt 12:36.

 • Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo.

  Tsiku lofunika kwambiri kwa Aisiraeli ndipo linkatchedwanso kuti Yom Kippur (kuchokera ku mawu a Chiheberi akuti yohm hak·kip·pu·rimʹ, “tsiku lophimba”). Tsikuli linali pa 10 mwezi wa Etanimu. Pa tsiku lokhali pachaka, mkulu wa ansembe ankalowa mʼMalo Oyera Koposa a chihema ndipo kenako a kachisi. Akalowa ankapereka magazi a nyama kuti ikhale nsembe ya machimo ake, machimo a Alevi ena komanso a anthu ena onse. Tsikuli linkakhala la msonkhano wopatulika, losala kudya komanso la sabata lomwe anthu sankagwira ntchito zawo za tsiku ndi tsiku.—Le 23:27, 28.

 • Tsiku limene mwezi watsopano waoneka.

  Tsiku loyamba la mwezi uliwonse pakalendala ya Ayuda. Linkakhalanso tsiku la msonkhano, la chikondwerero komanso lopereka nsembe zapadera. Patapita nthawi, tsikuli linali tsiku la chikondwerero cha dziko lonse ndipo anthu sankagwira ntchito.—Nu 10:10; 2Mb 8:13; Akl 2:16.

 • Tsiku Lokonzekera.

  Tsiku loti mawa lake ndi Sabata ndipo pa tsikuli Ayuda ankachita zinthu zokonzekera Sabata. Tsikuli linkatha Lachisanu dzuwa likalowa ndipo pa nthawi imeneyo mʼpamenenso Sabata linkayambira. Tsiku la Ayuda linkayamba madzulo nʼkudzathanso madzulo.—Mko 15:42; Lu 23:54.

U

 • Ubatizo; Batiza.

  Mawuwa amatanthauza “kumiza” kapena kuviika mʼmadzi. Yesu ananena kuti otsatira ake ayenera kubatizidwa. Malemba amanenanso za ubatizo wa Yohane, kubatizidwa ndi mzimu woyera, kubatizidwa ndi moto komanso ubatizo wina.—Mt 3:11, 16; 28:19; Yoh 3:23; 1Pe 3:21.

 • Ufumu wa Mulungu.

  Mawuwa amanena za ulamuliro wa Mulungu wa chilengedwe chonse womwe umaimiridwa ndi boma la Mwana wake Khristu Yesu.—Mt 12:28; Lu 4:43; 1Ak 15:50.

 • Ulonda.

  Nthawi yolondera usiku. Nthawiyi inkagawidwa kuyambira pamene dzuwa lalowa mpaka pamene latuluka (kuyambira mʼma 6 koloko madzulo kufika 6 koloko mʼmawa). Poyamba Aheberi ankagawa usiku mʼmagawo atatu kapena kuti ‘maulonda.’ (Eks 14:24; Owe 7:19) Ulonda uliwonse unkakhala wapafupifupi maola 4. Pa nthawi ya Yesu, usiku unkagawidwa mʼmaulonda 4 ndipo ulonda uliwonse unkakhala wa maola pafupifupi atatu.—Mt 14:25; Mko 13:35; Lu 12:38.

 • Ulosi.

  Uthenga wouziridwa, woulula kapena kulengeza zimene Mulungu akufuna kuchita. Ulosi unkatha kukhala wofotokoza makhalidwe abwino, wolamula anthu kuti achite zinazake, wokhudza chiweruzo cha Mulungu kapena wonena kuti zinazake zidzachitika.—Eze 37:9, 10; Da 9:24; Mt 13:14; 2Pe 1:20, 21.

 • Ulusi wa mulifupi mwa nsalu.

  Umenewu ndi ulusi umene powomba nsalu unkayenda mulifupi mokhamokha. Panalinso ulusi wina umene unkayenda mulitali.—Le 13:59.

 • Ulusi wamulitali mwa nsalu.

  Umenewu ndi ulusi umene powomba nsalu unkayenda mulitali mokhamokha. Panalinso ulusi wina umene unkayenda mulifupi.—Owe 16:13.

 • Umboni.

  Mawu akuti “Umboni” nthawi zambiri amanena za Malamulo 10 olembedwa pamiyala iwiri amene Mose anapatsidwa.—Eks 31:18.

 • Urimu ndi Tumimu.

  Zinthu zimene mkulu wa ansembe ankazigwiritsa ntchito mofanana ndi maere pofuna kudziwa yankho lochokera kwa Yehova pa nkhani zokhudza mtundu wonse. Mkulu wa ansembe ankaika Urimu ndi Tumimu mkati mwa chovala chake chapachifuwa akamalowa mʼchihema. Zikuoneka kuti Aisiraeli anasiya kugwiritsa ntchito zinthuzi Ababulo atawononga Yerusalemu.—Eks 28:30; Ne 7:65.

 • Uthenga wabwino.

  MʼMalemba a Chigiriki a Chikhristu mawuwa amanena za uthenga wabwino wonena za Ufumu wa Mulungu komanso kupulumutsidwa chifukwa chokhulupirira Yesu Khristu.—Lu 4:18, 43; Mac 5:42; Chv 14:6.

 • Utumiki wopatulika.

  Utumiki kapena ntchito yomwe ndi yopatulika. Munthu akamachita utumikiwu kapena kugwira ntchitoyi amakhala kuti akulambira Mulungu.—Aro 12:1; Chv 7:15.

W

 • Wamasomphenya.

  Munthu amene ankathandizidwa ndi Mulungu kudziwa zimene Mulunguyo akufuna. Munthu amene maso ake atsegulidwa kuti azitha kuona zinthu zimene anthu ena onse sangazione. Mawu ake a Chiheberi amatanthauza “kuona,” kaya kuona kwenikweni kapena kophiphiritsa. Anthu ankapita kwa wamasomphenya kuti akafunsire nzeru pa vuto lomwe akumana nalo.—1Sa 9:9.

 • Wansembe wamkulu.

  Dzina lina la “mkulu wa ansembe” mʼMalemba a Chiheberi. MʼMalemba a Chigiriki, mawu akuti “ansembe aakulu” amanena za amuna olemekezeka pakati pa ansembe ndipo mwina ena a iwo anakhalapo akulu ansembe kapena anali atsogoleri a magulu 24 a ansembe.—2Mb 26:20; Eza 7:5; Mt 2:4; Mko 8:31.

 • Wansembe.

  Munthu amene ankaimira Mulungu kwa anthu amene ankawatumikira ndipo ankalangiza anthuwo zokhudza Mulungu komanso malamulo ake. Ansembe ankaimiranso anthu kwa Mulungu popereka nsembe komanso kupemphera mochonderera mʼmalo mwa anthuwo. Chilamulo cha Mose chisanaperekedwe, mutu wabanja ndi umene unkakhala wansembe wabanjalo. MʼChilamulo cha Mose amuna a mʼbanja la Aroni, omwe anali a fuko la Levi, ndi amene ankakhala ansembe. Amuna ena onse a fuko la Levi ankawathandiza. Pangano latsopano litakhazikitsidwa, Isiraeli wauzimu ndi amene anakhala mtundu wa ansembe ndipo Yesu ndi Mkulu wa Ansembe.—Eks 28:41; Ahe 9:24; Chv 5:10.

 • Woipayo.

  Mawu amene amanena za Satana Mdyerekezi amene amatsutsa Mulungu komanso mfundo zake zolungama.—Mt 6:13; 1Yo 5:19.

 • Wokana Khristu.

  Mawu ake a Chigiriki amatanthauza zinthu ziwiri. Amatanthauza wotsutsana ndi Khristu kapena wonamizira kuti ndi Khristu. Anthu, mabungwe komanso magulu amene amanamizira kuti akuimira Khristu kapenanso munthu amene amati ndi Mesiya, anganenedwe kuti ndi okana Khristu. Chimodzimodzinso anthu amene amatsutsa Khristu ndiponso otsatira ake.—1Yo 2:22.

 • Wokhulupirira nyenyezi.

  Munthu amene amaona kayendedwe ka dzuwa, mwezi ndi nyenyezi kuti adziwe zamʼtsogolo.—Da 2:27; Mt 2:1.

 • Wolankhula ndi mizimu.

  Munthu amene amati amalankhula ndi anthu amene anamwalira.—Le 20:27; De 18:10-12; 2Mf 21:6.

 • Wolosera zamʼtsogolo.

  Munthu amene amanena kuti amatha kuneneratu zamʼtsogolo. Ansembe amatsenga, olankhula ndi mizimu, okhulupirira nyenyezi ndi ena ali mʼgulu la anthu amene Baibulo limati ndi olosera zamʼtsogolo.—Le 19:31; De 18:11; Mac 16:16.

 • Wolowa Chiyuda.

  MʼMalemba, mawu amenewa amanena za munthu amene analowa Chiyuda ndipo ngati ndi wamwamuna ankadulidwa.—Mt 23:15; Mac 13:43.

 • Wopanda zofufumitsa.

  Kutanthauza mkate umene wapangidwa popanda kuikamo zofufumitsa.—De 16:3; Mko 14:12; 1Ak 5:8.

 • Wotsogolera nyimbo.

  Mawuwa amagwiritsidwa ntchito mʼbuku la Masalimo ndipo mʼChiheberi amatanthauza munthu amene ankakonza nyimbo, kutsogolera poimba, kuphunzitsa Alevi kuimba komanso kuwatsogolera akamaimba. Mawuwa amamasuliridwanso kuti “mkulu wa oimba.”—Sl 4:Kam; 5:Kam.

 • Woumba mbiya.

  Munthu amene ankaumba zinthu zadothi monga miphika, mbale ndi zina. Mawu ake a Chiheberi amatanthauza “wopanga.” Mphamvu zimene woumba zinthu zadothi amakhala nazo, amaziyerekezera ndi mphamvu zimene Yehova ali nazo pa anthu komanso mayiko.—Yes 64:8; Aro 9:21.

 • Woyangʼanira.

  Mwamuna amene udindo wake waukulu ndi kuyangʼanira kapena kuweta mpingo. Mawu ake a Chigiriki akuti e·piʹsko·pos amanena za kuyangʼanira pofuna kuteteza. Ndipo mawu akuti “woyangʼanira” komanso “mkulu” (pre·sbyʹte·ros) amanena za udindo wofanana, womwe munthu amakhala nawo mumpingo wa Chikhristu. Mawu akuti “mkulu” amasonyeza kuti munthu amene wapatsidwa udindowu amachita zinthu mwauchikulire ndipo mawu akuti “woyangʼanira” amatsindika za ntchito imene amagwira.—Mac 20:28; 1Ti 3:2-7; 1Pe 5:2.

Y

 • Yakobo.

  Mwana wa Isaki ndi Rabeka. Kenako Mulungu anamupatsa dzina lakuti Isiraeli ndipo anali kholo la mtundu wa Isiraeli (womwe unkatchedwanso Aisiraeli, kenako Ayuda). Iye anali bambo wa ana aamuna 12, omwe pamodzi ndi mbadwa zawo, anapanga mafuko 12 a Isiraeli. Dzina lakuti Yakobo linapitiriza kugwiritsidwa ntchito ponena za mtundu wa Isiraeli kapena kuti Aisiraeli.—Ge 32:28; Mt 22:32.

 • Yedutuni.

  Mawuwa tanthauzo lake silikudziwika bwinobwino, koma amapezeka pakamutu ka pa Salimo 39, 62 ndi 77. Zikuoneka kuti mawu a timitu timeneti anali malangizo a kaimbidwe ka masalimowo kapena kaimbidwe ka zida zake. Panalinso Mlevi wina woimba dzina lake Yedutuni choncho kaimbidwe aka kayenera kuti kakukhudzana ndi iyeyo kapena ana ake.

 • Yehova.

  Kamasuliridwe kofala mʼChichewa ka zilembo 4 zoimira dzina la Mulungu ndipo dzina limeneli likupezeka maulendo oposa 7,000 mʼBaibuloli.—Onani Zakumapeto A4 ndi A5.

 • Yuda.

  Mwana wa 4 wa Yakobo ndipo mayi ake anali Leya. Atatsala pangʼono kumwalira, Yakobo analosera kuti mfumu yamphamvu komanso imene idzalamulire kwa nthawi yaitali idzachokera mʼbanja la Yuda. Yesu anabadwa kuchokera mʼbanja la Yuda. Dzina lakuti Yuda linalinso la fuko ndipo kenako ufumu. Mu ufumu wa Yuda, womwe unkatchedwa ufumu wakumʼmwera, munali fuko la Yuda ndi la Benjamini ndipo nʼkumene kunali ansembe ndi Alevi. Ufumuwu unali kumʼmwera kwa dziko la Isiraeli ndipo nʼkumene kunali mzinda wa Yerusalemu komanso kachisi.—Ge 29:35; 49:10; 1Mf 4:20; Ahe 7:14.

Z

 • Zanyanga.

  Kugwiritsa ntchito mphamvu zochokera kwa ziwanda.—2Mb 33:6.

 • Zeu.

  Mulungu wamkulu pa milungu yambiri imene Agiriki ankalambira. Ku Lusitara, anthu ankalakwitsa nʼkumanena kuti Baranaba ndi Zeu. Zolemba zina zomwe zinapezeka pafupi ndi ku Lusitara zinali ndi mawu akuti “ansembe a Zeu” komanso “Zeu, mulungu wa dzuwa.” Ngalawa imene Paulo anakwera pochoka pachilumba cha Melita inali ndi chizindikiro cha “Ana a Zeu” omwe anali amapasa ndipo mayina awo anali Kasita ndi Polakisi.—Mac 14:12; 28:11.

 • Zida zankhondo.

  Zinthu zimene asilikali ankavala podziteteza. Zida zake zinali chipewa, chapachifuwa, lamba, chishango ndiponso zodzitetezera miyendo.—1Sa 31:9; Aef 6:13-17.

 • Zinthu zotenga kunkhondo.

  Katundu wa anthu, ziweto kapena zinthu zina zamtengo wapatali zimene anthu ankalanda anthu amene awagonjetsa pankhondo.—Yos 7:21; 22:8; Ahe 7:4.

 • Zipatso zoyambirira.

  Mbewu kapena zipatso zoyambirira kukolola komanso chinthu chilichonse choyambirira. Yehova ankafuna kuti Aisiraeli azimupatsa zinthu zoyambirira, kaya ndi mwana woyamba kubadwa wa munthu, wa nyama kapenanso mbewu ndi zipatso zoyambirira. Mtundu wa Aisiraeli unkapereka zinthu zoyambirira pa Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa ndiponso pa Pentekosite. Mawu akuti “zipatso zoyambirira” amagwiritsidwanso ntchito mophiphiritsa ponena za Yesu ndi otsatira ake odzozedwa.—1Ak 15:23; Nu 15:21; Miy 3:9; Chv 14:4.

 • Zivi.

  Dzina loyamba la mwezi wachiwiri pakalendala yopatulika ya Ayuda komanso mwezi wa 8 pakalendala ya anthu onse. Unkayamba pakati pa mwezi wa April mpaka pakati pa May. Mʼbuku lina la Ayuda lotchedwa Talmud komanso mʼmabuku ena, amene analembedwa pambuyo poti Aisiraeli abwera kuchokera ku ukapolo, mweziwu umadziwika ndi dzina lakuti Iyara. (1Mf 6:37)—Onani Zakumapeto B15.

 • Ziwanda.

  Mizimu yoipa yomwe ndi yamphamvu kuposa anthu komanso yosaoneka. Zimatchulidwa kuti “ana a Mulungu woona” pa Genesis 6:2 komanso “angelo” pa Yuda 6. Angelowa sanalengedwe oipa, koma anadzipangitsa kukhala adani a Mulungu posonyeza kusamumvera mʼmasiku a Nowa komanso pogwirizana ndi Satana amene anagalukira Yehova.—De 32:17; Lu 8:30; Mac 16:16; Yak 2:19.

 • Ziyoni; Phiri la Ziyoni.

  Dzina la mzinda wa Yebusi umene unali ndi mpanda wolimba ndipo unali kumpoto chakumadzulo kwa Yerusalemu. Davide atagonjetsa mzinda wa Ayebusiwu anamanga nyumba yake yachifumu pamalowa ndipo mzindawu unayamba kutchedwa “mzinda wa Davide.” (2Sa 5:7, 9) Yehova ankaona kuti phiri la Ziyoni ndi loyera makamaka pamene Davide anabweretsa Likasa kumeneku. Kenako mawu akuti Ziyoni ankanena za malo amene kunali kachisi paphiri la Moriya ndipo nthawi zina ankanenanso za mzinda wonse wa Yerusalemu. Mawuwa amagwiritsidwa ntchito mophiphiritsa mʼMalemba a Chigiriki a Chikhristu.—Sl 2:6; 1Pe 2:6; Chv 14:1.

 • Zodabwitsa; Zozizwitsa.

  Zinthu zimene zimachitika ndi mphamvu zapadera moti anthu samvetsa kuti zachitika bwanji. Mawu ena amene Baibulo limagwiritsa ntchito pofotokoza zinthu zimenezi ndi “zizindikiro” komanso “ntchito zamphamvu.”—Eks 4:21; Mac 4:22; Ahe 2:4.

 • Zofufumitsa.

  Zinthu zimene ankaika mʼzinthu zamadzimadzi kapena pokanda ufa kuti afufumitse. Nthawi zambiri ankagwiritsa ntchito ufa wokandakanda umene unafufuma kale. Kawirikawiri mawuwa amagwiritsidwa ntchito mʼBaibulo mophiphiritsa ponena za uchimo kapena kuwonongeka. Amagwiritsidwanso ntchito posonyeza kukula kapena kuwonjezeka kosaonekera.—Eks 12:20; Mt 13:33; Aga 5:9.

 • Zofukiza.

  Zinthu zonunkhira zopangidwa kuchokera kumitengo inayake zomwe zinkapsa pangʼonopangʼono nʼkumatulutsa kafungo kabwino. Zonunkhira zina zapadera zinkapangidwa posakaniza zinthu 4 ndipo zinkagwiritsidwa ntchito pachihema ndi pakachisi. Zinkawotchedwa mʼmawa ndi usiku paguwa la nsembe zofukiza la mʼMalo oyera. Pa tsiku la Mwambo Wophimba Machimo, zinkawotchedwa mʼMalo Oyera Koposa. Mawu oti zofukiza ankagwiritsidwanso ntchito mophiphiritsa ponena za mapemphero ovomerezeka a atumiki a Mulungu okhulupirika. Akhristu sanalamulidwe kuti azipereka nsembe zofukiza.—Eks 30:34, 35; Le 16:13; Chv 5:8.

 • Zofukizira nsembe.

  Ziwiya zagolide, zasiliva kapena zakopa zimene ankagwiritsa ntchito pachihema ndiponso mʼkachisi. Ankazigwiritsa ntchito powotcha nsembe, pochotsa makala paguwa lansembe komanso pochotsa phulusa pachoikapo nyale chagolide. Zinkadziwikanso kuti zoperekera nsembe.—Eks 37:23; 2Mb 26:19; Ahe 9:4.

 • Zolungama.

  Malemba akamati zinthu zolungama amatanthauza zinthu zoyenera mogwirizana ndi mfundo za Mulungu pa nkhani ya zoyenera ndi zolakwika.—Ge 15:6; De 6:25; Miy 11:4; Zef 2:3; Mt 6:33.

 • Zombo za ku Tarisi.

  Poyamba, mawuwa ankagwiritsidwa ntchito ponena za zombo zimene zinkapita ku Tarisi (panopa ndi Spain). Patapita nthawi, mawuwa ankanena za zombo zikuluzikulu zimene zinkatha kuyenda mtunda wautali. Solomo ndi Yehosafati ankagwiritsa ntchito zombo za mtundu umenewu.—1Mf 9:26; 10:22; 22:48.

 • Zopanira.

  Zinthu zagolide zomwe ankazigwiritsa ntchito kuchihema ndi kukachisi pozimitsa nyale.—Eks 37:23.

 • Zozimitsira nyale.

  Zipangizo zimene ankagwiritsa ntchito mʼchihema komanso mʼkachisi ndipo zinkakhala zagolide kapena zakopa. Mwina zinkaoneka ngati sizasi ndipo pozimitsapo ankangodula pangʼono chingwe cha nyale.—2Mf 25:14.