Wolembedwa ndi Maliko 8:1-38

  • Yesu anadyetsa anthu 4,000 (1-9)

  • Anapempha chizindikiro (10-13)

  • Zofufumitsa za Afarisi ndi Herode (14-21)

  • Munthu wavuto losaona anachiritsidwa ku Betsaida (22-26)

  • Petulo anazindikira kuti Yesu ndi Khristu (27-30)

  • Yesu ananeneratu za imfa yake (31-33)

  • Chizindikiro cha wophunzira weniweni (34-38)

8  Mʼmasiku amenewo, gulu la anthu linasonkhananso koma linalibe chakudya. Ndiyeno Yesu anaitana ophunzira ake nʼkuwauza kuti:  “Gulu la anthuli likundimvetsa chisoni,+ chifukwa anthuwa akhala ndi ine kwa masiku atatu ndipo alibe chakudya.+  Ndikawauza kuti azipita kwawo ali ndi njala,* alenguka panjira. Ndipo ena a iwo achokera kutali kwambiri.”  Koma ophunzira ake anamuyankha kuti: “Munthu angaipeze kuti mitanda ya mkate yokwanira kudyetsa anthu onsewa, kumalo kopanda anthu ngati kuno?”  Ndiyeno Yesu anawafunsa kuti: “Muli ndi mitanda ingati ya mkate?” Iwo anayankha kuti: “Tili nayo 7.”+  Ndiyeno anauza anthuwo kuti akhale pansi. Kenako, anatenga mitanda 7 ya mkate ija nʼkuyamika. Atatero anainyemanyema nʼkuyamba kupereka kwa ophunzira ake kuti agawe, ndipo iwo anagawira gulu la anthulo.+  Ophunzirawo analinso ndi tinsomba towerengeka ndipo atadalitsa tinsombato, anawauza kuti agawirenso anthuwo.  Choncho anthu onsewo anadya nʼkukhuta, moti zotsala zimene anatolera zinadzaza madengu akuluakulu 7.+  Komatu panali amuna pafupifupi 4,000. Kenako anawauza kuti azipita. 10  Nthawi yomweyo iye anakwera ngalawa limodzi ndi ophunzira ake nʼkufika mʼchigawo cha Dalamanuta.+ 11  Kumeneku kunafika Afarisi ndipo anayamba kutsutsana naye. Ankafuna kuti iye awaonetse chizindikiro chochokera kumwamba, pofuna kumuyesa.+ 12  Choncho anausa moyo mwamphamvu nʼkunena kuti: “Nʼchifukwa chiyani mʼbadwo umenewu ukufunitsitsa chizindikiro?+ Ndithu ndikukuuzani, mʼbadwo umenewu sudzapatsidwa chizindikiro chilichonse.”+ 13  Atanena zimenezi anawasiya nʼkukakweranso ngalawa kupita kutsidya lina. 14  Komano iwo anaiwala kutenga mikate, choncho analibe chilichonse mʼngalawamo kupatulapo mtanda wa mkate umodzi wokha basi.+ 15  Ndipo anawachenjeza mwamphamvu kuti: “Khalani maso! Chenjerani ndi chofufumitsa cha Afarisi ndi cha Herode.”+ 16  Choncho ophunzirawo anayamba kukangana pa nkhani yosowa mkate. 17  Yesu ataona zimenezo, anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukukangana pa nkhani yosowa mkate? Kodi simukuzindikira ndi kumvetsa tanthauzo lake mpaka pano? Kodi mitima yanu ikadali yosazindikira? 18  ‘Ngakhale kuti muli ndi maso, simukuona. Ndipo ngakhale kuti muli ndi makutu, simukumva.’ Kodi simukukumbukira 19  zimene zinachitika nditanyemanyema mitanda 5 ya mkate+ nʼkudyetsa amuna 5,000? Kodi munatolera madengu angati a zotsala?” Iwo anayankha kuti: “Anali madengu 12.”+ 20  “Nditanyemanyema mitanda 7 ya mkate nʼkudyetsa amuna 4,000, kodi munatolera madengu akuluakulu angati a zotsala?” Iwo anamuyankha kuti: “Analipo 7.”+ 21  Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Kodi simukumvetsabe tanthauzo lake?” 22  Tsopano anafika ku Betsaida. Kumeneku anthu anamubweretsera munthu amene anali ndi vuto losaona. Anthuwo anamuchonderera kuti akhudze munthuyo.+ 23  Iye anagwira dzanja la munthu wosaonayo nʼkupita naye kunja kwa mudzi. Kumeneko iye anaika malovu mʼmaso mwa munthuyo+ nʼkuika manja ake pa munthuyo ndipo anamufunsa kuti: “Kodi ukuona chilichonse?” 24  Munthuyo anayangʼana mʼmwamba nʼkunena kuti: “Ndikuona anthu, koma akuoneka ngati mitengo imene ikuyendayenda.” 25  Iye anagwiranso mʼmaso mwa munthuyo ndipo anayamba kuona bwinobwino. Munthuyo anachiriratu moti anayamba kuona chilichonse bwinobwino. 26  Kenako anamuuza kuti azipita kwawo nʼkunena kuti: “Koma usalowe mʼmudzimu.” 27  Ndiyeno Yesu ndi ophunzira ake anachoka nʼkupita kumidzi ya Kaisareya wa Filipi. Ali mʼnjira, anayamba kufunsa ophunzira ake kuti: “Kodi anthu akumanena kuti ine ndine ndani?”+ 28  Iwo anamuyankha kuti: “Akumanena kuti Yohane Mʼbatizi,+ ena akumati Eliya,+ koma ena akumanena kuti mmodzi wa aneneri.” 29  Ndiyeno anafunsa ophunzirawo kuti: “Nanga inuyo mumati ndine ndani?” Petulo anayankha kuti: “Ndinu Khristu.”+ 30  Atanena zimenezo, anawalamula mwamphamvu kuti asauze aliyense za iye.+ 31  Komanso anayamba kuwaphunzitsa kuti Mwana wa munthu akuyenera kukumana ndi mavuto ambiri ndiponso kukanidwa ndi akulu, ansembe aakulu ndi alembi. Ndipo adzaphedwa+ nʼkuukitsidwa patapita masiku atatu.+ 32  Ndithudi, iye analankhula mawu amenewa mosapita mʼmbali. Koma Petulo anatengera Yesu pambali nʼkuyamba kumudzudzula.+ 33  Atamva zimenezi, Yesu anatembenuka nʼkuyangʼana ophunzira ake, kenako anadzuzula Petulo kuti: “Pita kumbuyo kwanga, Satana! Chifukwa zimene umaganiza si maganizo a Mulungu, koma maganizo a anthu.”+ 34  Kenako iye anaitana gulu la anthu limodzi ndi ophunzira ake nʼkuwauza kuti: “Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha ndipo anyamule mtengo wake wozunzikirapo* nʼkupitiriza kunditsatira.+ 35  Chifukwa aliyense amene akufuna kupulumutsa moyo wake adzautaya. Koma aliyense wotaya moyo wake chifukwa cha ine ndi uthenga wabwino, adzaupulumutsa.+ 36  Kodi munthu angapindule chiyani ngati atapeza zinthu zonse zamʼdzikoli koma nʼkutaya moyo wake?+ 37  Kapena kodi munthu angapereke chiyani choti asinthanitse ndi moyo wake?+ 38  Chifukwa aliyense wochita manyazi ndi ine komanso mawu anga mu mʼbadwo wachigololo* ndi wochimwa uno, Mwana wa munthu adzachitanso naye manyazi+ akadzabwera mu ulemerero wa Atate wake limodzi ndi angelo oyera.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “asanadye.”
Kapena kuti, “wosakhulupirika.”