Wolembedwa ndi Maliko 9:1-50

  • Yesu anasintha maonekedwe ake (1-13)

  • Mnyamata wogwidwa ndi chiwanda anachiritsidwa (14-29)

    • Zinthu zonse ndi zotheka kwa munthu amene ali ndi chikhulupiriro (23)

  • Yesu ananeneratu kachiwiri za imfa yake (30-32)

  • Ophunzira anakangana kuti wamkulu ndi ndani (33-37)

  • Aliyense amene sakulimbana nafe ali kumbali yathu (38-41)

  • Zopunthwitsa (42-48)

  • “Khalani ndi mchere mwa inu nokha” (49, 50)

9  Ndiye anawauzanso kuti: “Ndithu ndikukuuzani kuti pali ena mwa amene aimirira pano amene sadzalawa imfa mʼpangʼono pomwe mpaka choyamba ataona Ufumu wa Mulungu utabwera ndi mphamvu zake.”+  Patapita masiku 6, Yesu anatenga Petulo, Yakobo ndi Yohane nʼkukwera nawo mʼphiri lalitali kwaokhaokha. Ndiyeno iye anasintha maonekedwe ake iwo akuona.+  Malaya ake akunja anayamba kunyezimira nʼkuyera kwambiri kuposa mmene wochapa zovala aliyense padziko lapansi angayeretsere zovala.  Komanso Eliya ndi Mose anaonekera kwa iwo ndipo ankakambirana ndi Yesu.  Ndiye Petulo anauza Yesu kuti: “Rabi, zingakhale bwino ife titamakhala pano. Choncho timange matenti atatu pano, imodzi yanu, imodzi ya Mose ndi ina ya Eliya.”  Petulo sanadziwe choti anene, chifukwa ophunzirawo anachita mantha kwambiri.  Ndiyeno kunachita mtambo umene unawaphimba. Kenako panamveka mawu+ kuchokera mumtambomo akuti: “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa.+ Muzimumvera.”+  Kenako iwo anayangʼana uku ndi uku ndipo anangoona kuti palibe wina aliyense koma Yesu yekha basi.  Pamene ankatsika mʼphirimo, Yesu anawalamula mwamphamvu kuti asauze aliyense zimene anaonazo,+ mpaka Mwana wa munthu atauka kwa akufa.+ 10  Iwo anasungadi zimenezo mumtima,* koma anayamba kukambirana zimene kuuka kwa akufa kumeneku kukutanthauza. 11  Ndiyeno anayamba kumufunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani alembi amanena kuti Eliya+ ayenera kubwera choyamba?”+ 12  Iye anawayankha kuti: “Eliya adzabweradi choyamba nʼkubwezeretsa zinthu zonse.+ Koma nʼchifukwa chiyani malemba amanena kuti Mwana wa munthu ayenera kukumana ndi mavuto ambiri+ komanso kumuchitira zinthu zachipongwe?+ 13  Koma ine ndikukuuzani kuti Eliya+ anabwera kale ndipo anamuchitira zilizonse zimene iwo anafuna, mogwirizana ndi zimene Malemba amanena zokhudza iye.”+ 14  Atayandikira kumene kunali ophunzira ena aja, iwo anaona gulu lalikulu la anthu litawazungulira ndipo panali alembi amene ankakangana nawo.+ 15  Koma gulu lonselo litangomuona linadabwa ndipo linamuthamangira kuti likamupatse moni. 16  Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Mukukangana nawo chiyani?” 17  Munthu wina amene anali mʼgululo anamuyankha kuti: “Mphunzitsi, ine ndabweretsa mwana wanga wamwamuna kwa inu chifukwa ali ndi mzimu umene umamulepheretsa kulankhula.+ 18  Mzimuwo umati ukamugwira, umamugwetsera pansi. Akatero amachita thovu mʼkamwa komanso kukukuta mano ndipo amafooka. Ndinapempha ophunzira anu kuti autulutse koma alephera.” 19  Iye anayankha kuti: “Inu mʼbadwo wopanda chikhulupiriro,+ kodi ndikhala nanube mpaka liti? Ndipitirize kukupirirani mpaka liti? Bwera nayeni kuno.”+ 20  Choncho iwo anapita naye kwa Yesu. Koma mzimuwo utamuona, nthawi yomweyo unachititsa kuti mwanayo aphuphe. Anagwa pansi nʼkumagubudukagubuduka ndipo ankachita thovu kukamwa. 21  Ndiyeno Yesu anafunsa bambo ake kuti: “Izi zakhala zikumuchitikira kwa nthawi yaitali bwanji?” Bambo a mwanayo ananena kuti: “Kuyambira ali wamngʼono 22  ndipo nthawi zambiri umamugwetsera pamoto komanso mʼmadzi kuti umuwononge. Koma ngati mungathe kuchitapo kanthu, tichitireni chifundo nʼkutithandiza.” 23  Yesu anafunsa bambowo kuti: “Mukuti ‘Ngati mungatheʼ? Chilichonsetu nʼchotheka kwa munthu amene ali ndi chikhulupiriro.”+ 24  Nthawi yomweyo bambo a mwanayo anafuula nʼkunena kuti: “Chikhulupiriro ndili nacho! Limbitsani chikhulupiriro changa!”+ 25  Tsopano Yesu ataona kuti gulu la anthu likuthamangira kwa iwo, anakalipira mzimu wonyansawo kuti: “Iwe mzimu wolepheretsa munthu kulankhula komanso kumva, ndikukulamula, tuluka ndipo usadzalowenso mwa iye.”+ 26  Mwanayo atafuula ndi kuphupha kwambiri, mzimuwo unatuluka ndipo ankaoneka ngati wafa, moti anthu ambiri ankanena kuti: “Wamwalira!” 27  Koma Yesu anamugwira dzanja nʼkumudzutsa ndipo mwanayo anaimirira. 28  Ndiyeno atalowa mʼnyumba, ophunzira ake anamufunsa ali kwaokha kuti: “Nʼchifukwa chiyani ife tinalephera kutulutsa chiwanda chija?”+ 29  Iye anawayankha kuti: “Mzimu wa mtundu umenewu sungathe kutuluka ndi chilichonse, koma pemphero basi.” 30  Atachoka kumeneko anapitiriza ulendo wawo kudutsa mu Galileya, koma iye sanafune kuti aliyense adziwe zoti ali kumeneko. 31  Chifukwa iye ankaphunzitsa ophunzira ake nʼkuwauza kuti: “Mwana wa munthu adzaperekedwa mʼmanja mwa anthu ndipo adzamupha.+ Koma ngakhale adzamuphe, adzauka patatha masiku atatu.”+ 32  Komabe ophunzirawo sanamvetse mawu akewo ndipo ankaopa kuti amufunse. 33  Kenako anafika ku Kaperenao. Ndiyeno pamene anali mʼnyumba anawafunsa kuti: “Mʼnjira muja mumakangana chiyani?”+ 34  Iwo anangokhala chete, chifukwa mʼnjira amakangana kuti wamkulu ndi ndani pakati pawo. 35  Choncho anakhala pansi nʼkuitana ophunzira 12 aja nʼkuwauza kuti: “Ngati aliyense akufuna kukhala woyamba, ayenera kukhala wotsiriza pa onse ndiponso mtumiki wa onse.”+ 36  Kenako anatenga mwana wamngʼono nʼkumuimika pakati pawo ndipo anamukumbatira nʼkuwauza kuti: 37  “Aliyense amene walandira mwana wamngʼono+ ngati ameneyu mʼdzina langa, walandiranso ine. Ndipo aliyense amene walandira ine, sanalandire ine ndekha, koma walandiranso Mulungu amene anandituma.”+ 38  Kenako Yohane anauza Yesu kuti: “Mphunzitsi, ife tinaona munthu wina akutulutsa ziwanda mʼdzina lanu ndiye tinamuletsa, chifukwa sakuyenda ndi ife.”+ 39  Koma Yesu ananena kuti: “Musamuletse, chifukwa palibe amene angachite ntchito zamphamvu mʼdzina langa, nthawi yomweyo nʼkundinenera zachipongwe. 40  Chifukwa amene sakutsutsana ndi ife ali kumbali yathu.+ 41  Komanso aliyense amene wakupatsani kapu ya madzi akumwa chifukwa chakuti ndinu ophunzira a Khristu,+ ndithu ndikukuuzani, ameneyo mphoto yake sidzatayika.+ 42  Koma aliyense wokhumudwitsa mmodzi wa tiana iti timene tili ndi chikhulupiriro, zingamukhalire bwino kwambiri ngati atamumangirira chimwala champhero mʼkhosi mwake chimene bulu amayendetsa nʼkumuponya munyanja.+ 43  Ngati dzanja lako limakuphunthwitsa, ulidule. Ndi bwino kuti ukapeze moyo ulibe chiwalo chimodzi, kusiyana nʼkupita ku Gehena,* kumoto umene sungazimitsidwe, uli ndi manja onse awiri.+ 44 *⁠—— 45  Ndipo ngati phazi lako limakupunthwitsa, ulidule. Ndi bwino kuti ukapeze moyo uli wolumala, kusiyana nʼkuti uponyedwe mʼGehena* uli ndi mapazi onse awiri.+ 46 *⁠—— 47  Ngati diso lako limakuchimwitsa,* ulitaye.+ Ndi bwino kuti ukalowe mu Ufumu wa Mulungu uli ndi diso limodzi, kusiyana nʼkuti uponyedwe mu Gehena* uli ndi maso onse awiri,+ 48  kumene mphutsi za mitembo sizifa ndipo moto wake suzima.+ 49  Chifukwa aliyense akuyenera kuwazidwa mchere umene ukuimira moto.+ 50  Mchere ndi wabwino, koma ngati mcherewo watha mphamvu, kodi mphamvuyo mungaibwezeretse bwanji?+ Khalani ndi mchere mwa inu nokha+ ndipo sungani mtendere pakati panu.”+

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “Iwo sanauzedi aliyense zimenezo.”
Kapena kuti, “limakupunthwitsa.”