Wolembedwa ndi Maliko 14:1-72

  • Ansembe anakonza zoti aphe Yesu (1, 2)

  • Anathira Yesu mafuta onunkhira kwambiri (3-9)

  • Yudasi anapereka Yesu (10, 11)

  • Pasika womaliza (12-21)

  • Anayambitsa Mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye (22-26)

  • Ananeneratu zoti Petulo adzamukana (27-31)

  • Yesu anapemphera ku Getsemane (32-42)

  • Yesu anagwidwa (43-52)

  • Anaimbidwa mlandu Mʼkhoti Lalikulu la Ayuda (53-65)

  • Petulo anakana Yesu (66-72)

14  Tsopano kunangotsala masiku awiri kuti Pasika+ ndi Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa+ zichitike. Ndipo ansembe aakulu ndi alembi ankafunafuna njira yoti agwiritse ntchito pogwira* Yesu mochenjera nʼkumupha.+  Iwo ankanena kuti: “Tisadzamugwire pachikondwerero, kuopera kuti anthu angadzachite chipolowe.”  Pa nthawi imene Yesu anali ku Betaniya mʼnyumba mwa Simoni wakhate, kunafika mayi wina ali ndi botolo lopangidwa ndi mwala wa alabasitala la mafuta onunkhira. Mafutawa anali nado weniweni ndipo anali okwera mtengo kwambiri. Iye anatsegula botolo la alabasitala lija mochita kuswa, nʼkuyamba kuthira mafutawo mʼmutu mwa Yesu.+  Anthu ena ataona zimenezi, anayamba kuuzana mokwiya kuti: “Nʼchifukwa chiyani akuwononga chonchi mafuta onunkhirawa?  Mafuta onunkhirawatu akanatha kugulitsidwa ndalama zoposa madinari* 300 ndipo ndalamazo zikanaperekedwa kwa anthu osauka!” Choncho iwo anakhumudwa kwambiri ndi mayiyo.*  Koma Yesu anawauza kuti: “Musiyeni, nʼchifukwa chiyani mukumuvutitsa? Iyetu wandichitira zinthu zabwino.+  Chifukwa osaukawo muli nawo nthawi zonse,+ ndipo mungathe kuwachitira zabwino nthawi iliyonse imene mwafuna. Koma ine simudzakhala nane nthawi zonse.+  Mayiyu wachita zimene akanatha. Iye wathiriratu mafuta onunkhira pathupi langa pokonzekera kuikidwa mʼmanda kwanga.+  Ndithu ndikukuuzani, kulikonse kumene uthenga wabwino udzalalikidwe padziko lonse,+ anthu azidzanena zimene mayiyu wachita kuti azidzamukumbukira.”+ 10  Kenako Yudasi Isikariyoti, mmodzi wa ophunzira 12 aja, anachoka nʼkupita kwa ansembe aakulu kuti akapereke Yesu kwa iwo.+ 11  Atamva zimenezo, iwo anasangalala ndipo anamulonjeza kuti amupatsa ndalama zasiliva.+ Choncho iye anayamba kufunafuna mpata wabwino kuti amupereke. 12  Pa tsiku loyamba la chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa,+ pamene mwamwambo ankapereka nsembe nyama ya Pasika,+ ophunzira ake anamufunsa kuti: “Kodi mukufuna tikakukonzereni kuti malo odyerako Pasika?”+ 13  Ndiyeno Yesu anatuma awiri mwa ophunzira akewo nʼkuwauza kuti: “Pitani mumzinda ndipo mwamuna wina akakumana nanu atasenza mtsuko wa madzi. Mukamutsatire,+ 14  ndipo mʼnyumba imene akalowe, mukauze mwininyumbayo kuti, ‘Mphunzitsi wanena kuti: “Chipinda cha alendo chili kuti mmene ine ndingadyeremo Pasika limodzi ndi ophunzira anga?”’ 15  Iye akakuonetsani chipinda chachikulu chamʼmwamba chokonzedwa bwino. Mukatikonzere Pasika mmenemo.” 16  Choncho ophunzirawo anapita nʼkulowa mumzinda ndipo zinachitikadi ndendende mmene iye anawauzira. Ndipo kumeneko anakonza zinthu zonse zofunika pa Pasika. 17  Chakumadzulo ndithu, Yesu anafika limodzi ndi ophunzira ake 12 aja.+ 18  Ndipo atakhala patebulo nʼkumadya chakudya, Yesu anati: “Ndithu ndikukuuzani, mmodzi wa inu, amene akudya nane limodzi, andipereka.”+ 19  Iwo anamva chisoni ndipo anayamba kumufunsa mmodzimmodzi kuti: “Kodi ndine kapena?” 20  Iye anati: “Ndi mmodzi wa inu 12, amene akusunsa nane limodzi mʼmbalemu.+ 21  Mwana wa munthu achoka, mogwirizana ndi zimene Malemba amanena za iye. Koma tsoka kwa munthu amene akupereka Mwana wa munthu!+ Zikanakhala bwino kwa munthu ameneyu ngati akanapanda kubadwa.”+ 22  Akupitiriza kudya, iye anatenga mkate nʼkuyamika Mulungu. Kenako anaunyemanyema nʼkuwapatsa ndipo anati: “Tengani, mkate uwu ukuimira thupi langa.”+ 23  Kenako anatenga kapu ya vinyo ndipo atayamika anaipereka kwa iwo moti onse anamwa.+ 24  Ndiyeno anawauza kuti: “Vinyoyu akuimira ‘magazi anga+ a pangano,’+ amene adzakhetsedwe chifukwa cha anthu ambiri.+ 25  Ndithu ndikukuuzani, sindidzamwanso chakumwa chochokera ku mphesa mpaka tsiku limene ndidzamwe chatsopano mu Ufumu wa Mulungu.” 26  Pamapeto pake, atamaliza kuimba nyimbo zotamanda Mulungu,* anatuluka nʼkupita kuphiri la Maolivi.+ 27  Yesu anawauza kuti: “Nonsenu muthawa nʼkundisiya ndekha, chifukwa Malemba amanena kuti: ‘Ndidzapha mʼbusa+ ndipo nkhosa zidzabalalika.’+ 28  Koma ndikadzauka kwa akufa, ndidzatsogola kukafika ku Galileya inu musanafikeko.”+ 29  Koma Petulo anayankha kuti: “Ngakhale ena onse atathawa nʼkukusiyani, ine ndekha sindidzathawa.”+ 30  Atatero Yesu anamuyankha kuti: “Ndithu ndikukuuza iwe kuti lero, usiku womwe uno, tambala asanalire kawiri, undikana katatu.”+ 31  Koma iye anapitiriza kunena kuti: “Ngati kuli kufa, ine ndifa nanu limodzi, sindingakukaneni.” Ndipo ena onse anayamba kunenanso chimodzimodzi.+ 32  Kenako anafika pamalo otchedwa Getsemane ndipo anauza ophunzira akewo kuti: “Khalani pansi panopa, ine ndikukapemphera.”+ 33  Popita kumeneko anatenga Petulo, Yakobo ndi Yohane+ ndipo anayamba kumva chisoni komanso kuvutika kwambiri mumtima mwake. 34  Kenako anawauza kuti: “Ine ndikumva* chisoni+ chofa nacho. Khalani pompano ndipo mukhalebe maso.”+ 35  Choncho atapita patsogolo pangʼono, anagwada mpaka nkhope yake pansi ndipo anayamba kupemphera kuti ngati zikanatheka, ola limeneli limupitirire. 36  Kenako anati: “Abba,* Atate,+ zinthu zonse nʼzotheka kwa inu. Ndichotsereni kapu iyi. Komatu osati mwa kufuna kwanga, koma mwa kufuna kwanu.”+ 37  Atatero anabwerera ndipo anawapeza akugona. Choncho anafunsa Petulo kuti: “Simoni, zoona ukugona? Kodi unalibe mphamvu kuti ukanakhalabe maso kwa ola limodzi?+ 38  Khalani maso ndipo mupitirize kupemphera kuti musalowe mʼmayesero.+ Zoona, mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.”+ 39  Atatero anachokanso kupita kukapemphera ndipo ananenanso mawu omwe aja.+ 40  Anabweranso nʼkuwapeza akugona, chifukwa zikope zawo zinali zitalemera, choncho iwo anasowa chomuyankha. 41  Anabweranso kachitatu nʼkuwauza kuti: “Zoona nthawi ngati ino mukugona ndi kupumula? Basi! Nthawi yakwana!+ Taonani! Mwana wa munthu akuperekedwa mʼmanja mwa anthu ochimwa. 42  Nyamukani, tiyeni tizipita. Onani! Wondipereka uja ali pafupi.”+ 43  Nthawi yomweyo, mawu adakali mʼkamwa, Yudasi, mmodzi wa ophunzira 12 aja, anafika limodzi ndi gulu la anthu kuchokera kwa ansembe aakulu, alembi ndi akulu, atanyamula malupanga ndi zibonga.+ 44  Apa nʼkuti womuperekayu atawapatsa chizindikiro chakuti: “Amene ndikamukise* ndi yemweyo, mukamugwire nʼkupita naye ndipo muonetsetse kuti asathawe.” 45  Ndiyeno Yudasi anayenda molunjika nʼkufika kwa iye. Kenako anati: “Rabi!” Ndipo anamukisa. 46  Choncho iwo anamugwira nʼkumumanga. 47  Koma mmodzi mwa anthu amene anaimirira chapafupi anasolola lupanga lake nʼkutema nalo kapolo wa mkulu wa ansembe mpaka kuduliratu khutu lake.+ 48  Koma Yesu anawafunsa kuti: “Bwanji mwabwera kudzandigwira mutatenga malupanga ndi zibonga ngati mukudzalimbana ndi wachifwamba?+ 49  Tsiku ndi tsiku ndinali nanu mʼkachisi nʼkumaphunzitsa,+ koma simunandigwire. Komabe, izi zikuchitika kuti Malemba akwaniritsidwe.”+ 50  Zitatero ophunzira ake onse anamuthawa nʼkumusiya yekha.+ 51  Koma mnyamata wina amene anangofunda nsalu yabwino popanda chovala china mkati, anayamba kumutsatira chapafupi ndipo anthuwo anayesa kuti amugwire. 52  Koma mnyamatayo anawasiyira mʼmanja nsalu yake ija nʼkuthawa ali maliseche.* 53  Tsopano iwo anatenga Yesu nʼkupita naye kwa mkulu wa ansembe+ ndipo ansembe aakulu komanso akulu ndi alembi onse anasonkhana kumeneko.+ 54  Koma Petulo ankamutsatira ali chapatali ndithu, mpaka anafika mʼbwalo lapanyumba ya mkulu wa ansembeyo. Petuloyo anakhala pansi limodzi ndi antchito amʼnyumbamo nʼkumawotha moto walawilawi.+ 55  Ndiyeno ansembe aakulu ndi Khoti lonse Lalikulu la Ayuda ankafunafuna umboni kuti anamizire Yesu mlandu nʼcholinga choti amuphe, koma sanaupeze.+ 56  Anthu ambiri ankapereka umboni wabodza kuti amunamizire mlandu,+ koma maumboni awowo ankatsutsana. 57  Komanso, anthu ena ankaimirira nʼkumapereka umboni womunamizira kuti: 58  “Ife tinamva iyeyu akunena kuti, ‘Ine ndidzagwetsa kachisi uyu amene anamangidwa ndi manja ndipo mʼmasiku atatu okha ndidzamanga wina osati womangidwa ndi manja.’”+ 59  Komabe ngakhale pa mfundo zimenezi, umboni wawo sunali wogwirizana. 60  Kenako, mkulu wa ansembe anaimirira pakati pawo nʼkufunsa Yesu kuti: “Kodi suyankha? Kodi sukumva zimene anthuwa akukunenezazi?”+ 61  Koma iye anangokhala chete osayankha chilichonse.+ Apanso mkulu wa ansembe anayamba kumufunsa kuti: “Kodi ndiwe Khristu Mwana wa Wodalitsidwayo?” 62  Ndiyeno Yesu ananena kuti: “Inde ndinedi, ndipo mudzaona Mwana wa munthu+ atakhala kudzanja lamanja+ lamphamvu. Mudzamuonanso akubwera ndi mitambo yakumwamba.”+ 63  Mkulu wa ansembe atamva zimenezi anangʼamba zovala zake nʼkunena kuti: “Nanga tingafunenso mboni zina pamenepa?+ 64  Mwadzimvera nokha mmene akunyozera Mulungu. Mukuona bwanji pamenepa?”* Onse ananena kuti akuyenera kufa basi.+ 65  Ndipo ena anayamba kumulavulira,+ kumuphimba nkhope nʼkumamukhoma nkhonya. Iwo ankamuuza kuti: “Losera!” Atamuwomba mbama, asilikali apakhoti anamutenga.+ 66  Tsopano pamene Petulo anali mʼmunsi, mʼbwalo, kunabwera mmodzi wa atsikana antchito a mkulu wa ansembe.+ 67  Ataona Petulo akuwotha moto, anamuyangʼanitsitsa nʼkunena kuti: “Inunso munali ndi Yesu, Mnazareti uja.” 68  Koma iye anakana kuti: “Sindikumudziwa ngakhale pangʼono ameneyo ndipo sindikumvetsa zimene ukunena.” Atatero anatuluka panja nʼkupita pageti.* 69  Kumenekonso mtsikana wantchito anamuona ndipo anayambanso kuuza anthu amene anali ataimirira chapafupi kuti: “Bambo awanso ali mʼgulu la ophunzira ake.” 70  Apanso Petulo anakana. Patapita kanthawi pangʼono, amene anali ataimirira chapafupi anayambanso kuuza Petulo kuti: “Ndithu iwenso uli mʼgulu la ophunzira ake. Ndipo ndiwenso Mgalileya.” 71  Koma iye anayamba kutemberera ndi kulumbira kuti: “Munthu amene mukunenayu ine sindikumudziwa ayi.” 72  Nthawi yomweyo tambala analira kachiwiri+ ndipo Petulo anakumbukira mawu a Yesu aja akuti: “Tambala asanalire kawiri, udzandikana katatu.”+ Ndipo anamva chisoni nʼkuyamba kulira.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “amangire.”
Kapena kuti, “anamulankhula mokwiya mayiyo; anakalipira mayiyo.”
Kapena kuti, “kuimba masalimo.”
Kapena kuti, “Moyo wanga ukumva.”
Mawu a Chiheberi kapena Chiaramu otanthauza “Ababa,” kapena, “Bambo anga!”
Kapena kuti, “ndikamupsompsone.”
Kapena kuti, “asanavale mokwanira; atavala zovala zamkati zokha.”
Kapena kuti, “Mukuganiza bwanji pamenepa?”
Kapena kuti, “nʼkupita pakanyumba kapageti.”