Wolembedwa ndi Luka 12:1-59

 • Zofufumitsa za Afarisi (1-3)

 • Muziopa Mulungu, osati anthu (4-7)

 • Kuvomereza kuti ndife ophunzira a Khristu (8-12)

 • Fanizo la munthu wolemera koma wopusa (13-21)

 • Siyani kuda nkhawa (22-34)

  • Kagulu ka nkhosa (32)

 • Kukhala maso (35-40)

 • Mtumiki woyangʼanira nyumba wokhulupirika komanso wosakhulupirika (41-48)

 • Sanabweretse mtendere, koma kudzagawanitsa (49-53)

 • Kufunika kozindikira tanthauzo la zimene zikuchitika (54-56)

 • Kuthetsa mikangano (57-59)

12  Pa nthawiyi, chigulu cha anthu masauzande ambirimbiri chinasonkhana, moti ankapondanapondana. Ndiyeno Yesu anayamba kulankhula ndi ophunzira ake choyamba kuti: “Samalani ndi zofufumitsa za Afarisi, zimene ndi chinyengo.+  Komatu palibe chimene chabisidwa mwachinsinsi kwambiri chimene sichidzaululika komanso palibe chinsinsi chimene sichidzadziwika.+  Choncho chilichonse chimene mumanena mumdima chidzamveka poyera ndipo zimene mumanongʼona kwanokha mʼzipinda zanu zidzalalikidwa padenga.  Komanso ndikukuuzani mabwenzi anga,+ musamaope amene amapha thupi lokha, omwe sangathe kuchita zoposa pamenepa.+  Koma ndikuuzani woti muzimuopa: Muziopa Iye amene amati akapha, amakhalanso ndi mphamvu zoponya munthu mʼGehena.*+ Ndithu ndikukuuzani, muziopa Ameneyu.+  Mpheta 5 amazigulitsa makobidi awiri ochepa mphamvu,* si choncho? Komatu palibe ngakhale imodzi mwa mbalame zimenezi imene Mulungu amaiiwala.*+  Ndipotu ngakhale tsitsi lonse lamʼmutu mwanu amaliwerenga.+ Musachite mantha, ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zambiri.+  Ndikukuuzani kuti, aliyense amene akuvomereza pamaso pa anthu kuti ndi wophunzira wanga,+ Mwana wa munthunso adzamuvomereza pamaso pa angelo a Mulungu kuti ndi wophunzira wake.+  Koma aliyense amene adzandikane pamaso pa anthu, adzakanidwa pamaso pa angelo a Mulungu.+ 10  Ndipo aliyense amene wanena mawu onyoza Mwana wa munthu, adzakhululukidwa. Koma aliyense amene wanyoza mzimu woyera, sadzakhululukidwa.+ 11  Akapita nanu kumabwalo amilandu,* kwa akuluakulu aboma komanso kwa olamulira, musade nkhawa kuti mukadziteteza bwanji kapena mukanena chiyani,+ 12  chifukwa mzimu woyera udzakuphunzitsani mu ola lomwelo zimene mukuyenera kunena.”+ 13  Kenako munthu wina mʼgululo anauza Yesu kuti: “Mphunzitsi, mumuuze mchimwene wanga kuti andigawireko cholowa.” 14  Iye anamuuza kuti: “Munthu iwe, ndi ndani amene anandisankha kuti ndikhale woweruza wanu kapena wogawa chuma chanu?” 15  Kenako anauza anthuwo kuti: “Khalani maso ndipo chenjerani ndi dyera* lamtundu uliwonse,+ chifukwa ngakhale munthu atakhala ndi zochuluka chotani, moyo wake suchokera mʼzinthu zimene ali nazo.”+ 16  Atatero anawauza fanizo lakuti: “Munda wa munthu wina wachuma unabereka bwino. 17  Choncho anayamba kudzifunsa kuti, ‘Ndichite chiyani tsopano, popeza ndilibe mosungira zokolola zangazi?’ 18  Ndiyeno anati, ‘Ndichita izi:+ Ndigwetsa nyumba zanga zosungiramo zinthu nʼkumanga zikuluzikulu, ndipo tirigu wanga yense ndi zinthu zanga zonse ndidzazitutira mmenemo, 19  ndiye ndidzadziuza kuti: “Uli ndi zinthu zambiri zabwino ndipo zisungika kwa zaka zambiri. Mtima mʼmalo, udye, umwe ndi kusangalala.”’ 20  Koma Mulungu anamuuza kuti, ‘Wopanda nzeru iwe, usiku womwe uno moyo wako aufuna. Nanga zinthu zimene wasungazi zidzakhala za ndani?’+ 21  Umu ndi mmene zimakhalira ndi munthu amene wadziunjikira chuma, koma si wolemera kwa Mulungu.”+ 22  Kenako anauza ophunzira ake kuti: “Nʼchifukwa chake ndikukuuzani kuti, siyani kudera nkhawa za moyo wanu kuti mudzadya chiyani kapena kudera nkhawa za matupi anu kuti mudzavala chiyani.+ 23  Chifukwa moyo ndi wofunika kwambiri kuposa chakudya ndipo thupi ndi lofunika kwambiri kuposa chovala. 24  Ganizirani za akhwangwala: Iwo safesa mbewu kapena kukolola. Alibe nkhokwe kapena nyumba yosungiramo zinthu, koma Mulungu amawadyetsa.+ Kodi inu si amtengo wapatali kuposa mbalame?+ 25  Ndi ndani wa inu amene angatalikitse moyo wake pangʼono pokha* chifukwa cha kuda nkhawa? 26  Choncho ngati inu simungathe kuchita zimenezi, nʼchifukwa chiyani mukuda nkhawa ndi zinthu zinazo?+ 27  Ganizirani za mmene maluwa amakulira: Iwo sagwira ntchito kapena kuwomba nsalu. Koma ndikukuuzani kuti ngakhale Solomo mu ulemerero wake wonse sanavalepo zokongola ngati lililonse la maluwa amenewa.+ 28  Ndiye ngati Mulungu amaveka chonchi zomera zakutchire, zimene zimangokhalapo lero lokha mawa nʼkuzisonkhezera pamoto, kuli bwanji inu, achikhulupiriro chochepa inu! Ndithudi, iye adzakuvekani kuposa pamenepo. 29  Choncho siyani kudera nkhawa kuti mudzadya chiyani komanso kuti mudzamwa chiyani ndipo siyani kuvutika mumtima.+ 30  Chifukwa zonsezi ndi zinthu zimene anthu a mitundu ina mʼdzikoli amazifunafuna mwakhama, koma Atate wanu amadziwa kuti inuyo mumafunikira zinthu zonsezi.+ 31  Mʼmalomwake nthawi zonse muziika Ufumu pamalo oyamba pa moyo wanu, ndipo iye adzakupatsani zinthu zina zonsezi.+ 32  Musaope, kagulu ka nkhosa inu,+ chifukwa Atate wanu wavomereza kukupatsani Ufumu.+ 33  Gulitsani zinthu zanu nʼkupereka mphatso zachifundo.*+ Pangani zikwama za ndalama zomwe sizingathe, kutanthauza chuma chosatha kumwamba,+ kumene akuba sangafikeko komanso njenjete* sizingawononge. 34  Chifukwa kumene kuli chuma chanu, mitima yanunso idzakhala komweko. 35  Valani epuloni ndipo mukhale okonzeka.*+ Nyale zanu zikhale zikuyaka+ 36  ndipo mukhale ngati anthu amene akuyembekezera kuti mbuye wawo abwere+ kuchokera ku ukwati,+ kuti akafika nʼkugogoda amutsegulire mwamsanga. 37  Osangalala ndi akapolo amene mbuye wawo pobwera adzawapeza akudikira! Ndithu ndikukuuzani, iye adzavala epuloni kuti agwire ntchito ndipo adzawakhazika patebulo kuti adye chakudya nʼkumawatumikira. 38  Iwo adzakhala osangalala ngati atawapeza akudikirabe ngakhale atafika pa ulonda wachiwiri* kapenanso wachitatu.* 39  Koma dziwani izi, ngati mwininyumba atadziwa nthawi imene wakuba angabwere, sangalole kuti wakuba athyole nʼkulowa mʼnyumba mwake.+ 40  Inunso khalani okonzeka, chifukwa Mwana wa munthu adzafika pa ola limene simukuliganizira.”+ 41  Kenako Petulo anafunsa kuti: “Ambuye, kodi fanizoli mukutiuza ife tokha kapena mukuuzanso aliyense?” 42  Ndiye Ambuye ananena kuti: “Ndi ndani kwenikweni amene ndi mtumiki woyangʼanira nyumba wokhulupirika komanso wanzeru, amene mbuye wake adzamuike kuti aziyangʼanira gulu la atumiki ake,* kuti aziwapatsa chakudya chokwanira pa nthawi yoyenera?+ 43  Kapolo ameneyo adzakhala wosangalala, ngati mbuye wake pobwera adzamupeze akuchita zimenezo! 44  Ndithu ndikukuuzani, adzamuika kuti aziyangʼanira zinthu zake zonse. 45  Koma ngati kapolo ameneyu anganene mumtima mwake kuti, ‘Mbuye wanga akuchedwa kubwera.’ Ndiyeno nʼkuyamba kumenya antchito anzake aamuna ndi aakazi komanso kudya, kumwa ndi kuledzera,+ 46  mbuye wa kapoloyo adzabwera pa tsiku limene iye sakuyembekezera ndi pa ola limene sakulidziwa, ndipo adzamupatsa chilango choopsa nʼkumupatsa gawo, limodzi ndi anthu osakhulupirika. 47  Ndiyeno kapolo ameneyo, amene anadziwa zimene mbuye wake ankafuna koma osakonzekera kubwera kwake kapena kuchita zimene anamuuza,* adzakwapulidwa zikoti zambiri.+ 48  Koma amene sanadziwe ndipo wachita zinthu zofunika kumʼkwapula, adzamukwapula zikoti zochepa. Inde, aliyense amene anapatsidwa zambiri, zambirinso zidzafunika kwa iye. Ndipo aliyense amene anaikidwa kuti aziyangʼanira zinthu zochuluka, anthu adzafunanso zochuluka kwa iye.+ 49  Ndinabwera kudzakoleza moto padziko lapansi, ndiye ngati motowo wayaka kale, ndingafunenso chiyani? 50  Ndithudi pali ubatizo umene ndikuyenera kubatizidwa, ndipotu ndikuvutika kwambiri mumtima mpaka utatha!+ 51  Kodi mukuganiza kuti ndinabwera padziko lapansi kudzakhazikitsa mtendere? Ayi ndithu, koma ndinabwera kudzagawanitsa anthu.+ 52  Chifukwa kuyambira panopa kupita mʼtsogolo, mʼnyumba imodzi mudzakhala anthu 5 osemphana maganizo, atatu kutsutsana ndi awiri, awiri kutsutsana ndi atatu. 53  Iwo adzagawanika, bambo kutsutsana ndi mwana wake wamwamuna ndipo mwana wamwamuna kutsutsana ndi bambo ake. Mayi kutsutsana ndi mwana wake wamkazi ndipo mwana wamkazi kutsutsana ndi mayi ake. Mpongozi kutsutsana ndi mkazi wa mwana wake ndipo mkazi wokwatiwa kutsutsana ndi apongozi ake aakazi.”+ 54  Kenako anauzanso gulu la anthulo kuti: “Mukaona mtambo ukukwera chakumadzulo, nthawi yomweyo mumanena kuti, ‘Kukubwera chimvula,’ ndipo chimabweradi. 55  Ndipo mukaona mphepo yakumʼmwera ikuwomba, mumanena kuti, ‘Lero kutentha kwambiri,’ ndipo zimachitikadi. 56  Anthu achinyengo inu! Mumatha kuzindikira maonekedwe a dziko lapansi ndi kuthambo. Nanga zimakukanikani bwanji kuzindikira tanthauzo la zimene zikuchitika pa nthawi ino?+ 57  Nʼchifukwa chiyani panokha simutha kuzindikiranso zinthu zimene ndi zolungama? 58  Mwachitsanzo, ukamapita ndi munthu amene akukuimba mlandu kwa wolamulira, muli mʼnjira udziyesetsa kuchitapo kanthu kuti uthetse mlanduwo. Uzichita zimenezi kuti asakutengere kwa woweruza, woweruzayo nʼkukupereka kwa msilikali wapakhoti, msilikaliyo nʼkukuponya mʼndende.+ 59  Ndithu ndikukuuza, sudzatulukamo mpaka utalipira kakhobidi kotsiriza kochepa mphamvu kwambiri.”*

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “maasaliyoni awiri.” Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “amainyalanyaza.”
Mabaibulo ena amati, “Akapita nanu kumasunagoge.”
Kapena kuti, “kusirira kwa nsanje.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene angatalikitse moyo wake ndi mkono umodzi.” Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “nʼkupereka mphatso kwa osauka.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mawu a Chigiriki amene amasuliridwa kuti “njenjete” amatanthauza mtundu winawake wa kadziwotche amene amadya zovala.
Kapena kuti, “Mangani lamba mʼchiuno mwanu.”
Nthawi imeneyi inkayamba pakati pa usiku mpaka cha mʼma 3 koloko mʼbandakucha.
Nthawi imeneyi inkayamba cha mʼma 9 koloko usiku mpaka pakati pa usiku.
Kapena kuti, “gulu la antchito ake apakhomo.”
Kapena kuti, “kuchita mogwirizana ndi zimene amafuna.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “lepitoni yomalizira.” Onani Zakumapeto B14.