Wolembedwa ndi Luka 20:1-47

  • Anthu anakayikira ulamuliro wa Yesu (1-8)

  • Fanizo la alimi opha anthu (9-19)

  • Mulungu komanso Kaisara (20-26)

  • Funso lokhudza kuuka kwa akufa (27-40)

  • Kodi Khristu ndi mwana wa Davide? (41-44)

  • Anachenjeza anthu kuti asamale ndi alembi (45-47)

20  Tsiku lina akuphunzitsa anthu mʼkachisi komanso kulengeza uthenga wabwino, kunabwera ansembe aakulu, alembi limodzi ndi akulu 2  nʼkudzamufunsa kuti: “Tiuzeni, kodi muli ndi ulamuliro wochitira zinthu zimenezi? Kapena ndi ndani amene anakupatsani ulamuliro umenewu?”+ 3  Yesu anawayankha kuti: “Inenso ndikufunsani funso limodzi ndipo mundiyankhe: 4  Kodi ubatizo umene Yohane ankachita unachokera kumwamba kapena kwa anthu?” 5  Choncho iwo anayamba kukambirana kuti: “Tikanena kuti, ‘Unachokera kumwamba,’ iye atifunsa kuti, ‘Nanga nʼchifukwa chiyani simunamukhulupirire?’ 6  Koma tikanena kuti, ‘Unachokera kwa anthu,’ anthu onsewa atiponya miyala, chifukwa iwo amakhulupirira ndi mtima wonse kuti Yohane anali mneneri.”+ 7  Choncho anayankha kuti sakudziwa kumene unachokera. 8  Yesu anawauza kuti: “Inenso sindikuuzani amene anandipatsa ulamuliro umene ndimachitira zimenezi.” 9  Ndiyeno iye anayamba kuuza anthuwo fanizo ili: “Munthu wina analima munda wa mpesa+ ndipo anausiya mʼmanja mwa alimi nʼkupita kudziko lina kumene anakhalako nthawi yaitali ndithu.+ 10  Ndiye nyengo ya zipatso itakwana, anatumiza kapolo wake kwa alimiwo kuti akamupatseko zina mwa zipatso zamʼmunda wa mpesawo. Koma alimiwo anamumenya nʼkumubweza chimanjamanja.+ 11  Koma iye anawatumiziranso kapolo wina. Ameneyonso anamumenya nʼkumuchitira zachipongwe,* ndipo anamubweza chimanjamanja. 12  Anatumizanso wachitatu. Ameneyunso anamuvulaza nʼkumuponya kunja. 13  Zitatero mwiniwake wa munda wa mpesa uja anati, ‘Ndichite chiyani tsopano? Chabwino, nditumiza mwana wanga wokondedwa.+ Mosakayikira mwana wanga yekhayu akamulemekeza.’ 14  Alimiwo atamuona anayamba kukambirana kuti, ‘Eyaa, uyu ndi amene adzalandire cholowa. Tiyeni timuphe kuti cholowacho chikhale chathu.’ 15  Choncho anamutulutsa mʼmunda wa mpesawo nʼkumupha.+ Ndiye kodi mwiniwake wa munda wa mpesawo adzachita chiyani kwa alimiwo? 16  Iye adzabwera nʼkupha alimiwo ndipo munda wa mpesawo adzaupereka kwa ena.” Atamva zimenezi iwo anati: “Ayi zisatero ndithu!” 17  Koma iye anawayangʼanitsitsa nʼkunena kuti: “Paja malemba amanena kuti, ‘Mwala umene omanga nyumba anaukana, wakhala mwala wapakona wofunika kwambiri.’*+ Kodi mawu amenewa amatanthauza chiyani? 18  Aliyense amene adzagwere pamwala umenewo adzaphwanyika.+ Ndipo aliyense amene mwalawo udzamugwere, adzanyenyeka.” 19  Alembi ndi ansembe aakulu aja atazindikira kuti mufanizolo akunena za iwowo, anayesetsa kupeza mpata kuti amugwire ola lomwelo, koma ankaopa anthu.+ 20  Ndiyeno ataonetsetsa zochita zake, anatuma aganyu mwachinsinsi kuti akadzionetse ngati olungama, nʼcholinga choti akamupezere zifukwa pa zimene angalankhule,+ kuti akamupereke kuboma ndi kwa bwanamkubwa. 21  Choncho iwo anamufunsa kuti: “Mphunzitsi, tikudziwa kuti zimene mumanena ndi kuphunzitsa ndi zolondola ndipo mulibe tsankho, koma mumaphunzitsa njira ya Mulungu mogwirizana ndi choonadi. 22  Kodi nʼzololeka* kuti ife tizipereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?” 23  Koma Yesu anazindikira ndale zawo ndipo anawauza kuti: 24  “Ndionetseni khobidi la dinari.* Kodi nkhope ndi mawu ali pamenepo ndi za ndani?” Iwo anayankha kuti: “Ndi za Kaisara.” 25  Iye anawauza kuti: “Choncho perekani zinthu za Kaisara kwa Kaisara,+ koma za Mulungu kwa Mulungu.”+ 26  Iwo analephera kumutapa mʼkamwa pa zimene ananenazi pamaso pa anthu, koma anadabwa ndi yankho lake moti anangokhala chete kusowa chonena. 27  Koma Asaduki ena, amene amanena kuti akufa sadzaukitsidwa,+ anabwera nʼkumufunsa kuti:+ 28  “Mphunzitsi, Mose anatilembera kuti, ‘Ngati mwamuna wamwalira nʼkusiya mkazi koma sanabereke ana, mchimwene wake akuyenera kutenga mkazi wamasiyeyo nʼkuberekera mchimwene wake uja ana.’+ 29  Ndiyeno panali amuna 7 apachibale. Woyamba anakwatira mkazi, koma anamwalira asanabereke mwana. 30  Wachiwirinso chimodzimodzi. 31  Kenako wachitatu anamukwatira. Zinachitika chimodzimodzi kwa amuna onse 7 aja, onse anamwalira osasiya ana. 32  Pamapeto pake mkazi uja anamwaliranso. 33  Kodi pamenepa, akufa akadzaukitsidwa mkazi ameneyu adzakhala wa ndani? Popeza onse 7 anamukwatira.” 34  Yesu anawayankha kuti: “Ana a mʼnthawi* ino amakwatira ndi kukwatiwa. 35  Koma amene aonedwa kuti ndi oyenerera kudzapeza moyo pa nthawi imeneyo nʼkudzaukitsidwa kwa akufa sadzakwatira kapena kukwatiwa.+ 36  Komanso iwo sadzafanso, chifukwa adzakhala ngati angelo. Iwo adzakhalanso ana a Mulungu pokhala ana a kuuka kwa akufa. 37  Koma zakuti akufa amaukitsidwa ngakhalenso Mose anafotokoza munkhani ya chitsamba cha minga, pamene ananena kuti Yehova* ndi ‘Mulungu wa Abulahamu, Mulungu wa Isaki ndi Mulungu wa Yakobo.’+ 38  Iye ndi Mulungu wa anthu amoyo, osati akufa, chifukwa kwa iye* onsewa ndi amoyo.”+ 39  Poyankha, ena mwa alembiwo ananena kuti: “Mphunzitsi, mwanena bwino.” 40  Ananena zimenezi chifukwa sanathenso kulimba mtima kuti amufunse funso lina ngakhale limodzi. 41  Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani amanena kuti Khristu ndi mwana wa Davide?+ 42  Chifukwa Davideyo ananena mʼbuku la Masalimo kuti, ‘Yehova* anauza Ambuye wanga kuti: “Khala kudzanja langa lamanja 43  mpaka nditaika adani ako kuti akhale chopondapo mapazi ako.”’+ 44  Choncho Davide anamutchula kuti Ambuye. Ndiye zikutheka bwanji kuti akhale mwana wake?” 45  Kenako anthu onse akumvetsera, iye anauza ophunzira akewo kuti: 46  “Chenjerani ndi alembi amene amakonda kuyendayenda atavala mikanjo komanso amakonda kupatsidwa moni mʼmisika. Amakondanso kukhala mʼmipando yakutsogolo* mʼmasunagoge komanso mʼmalo olemekezeka kwambiri pachakudya chamadzulo.+ 47  Iwo amalanda chuma cha akazi* amasiye ndipo amapereka mapemphero ataliatali pofuna kudzionetsera.* Anthu amenewa adzalandira chilango chowawa kwambiri.”*

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “anamumenya nʼkumunyoza.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mutu wa kona.”
^ Kapena kuti, “nʼzoyenera.”
^ Kapena kuti, “chifukwa iye amaona kuti.”
^ Kapena kuti, “mʼmipando yabwino kwambiri.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Iwo amadya nyumba za akazi.”
^ Kapena kuti, “ataliatali mwachiphamaso.”
^ Kapena kuti, “chilango champhamvu.”