Wolembedwa ndi Luka 14:1-35

  • Munthu amene anali ndi manja komanso miyendo yotupa anachiritsidwa tsiku la Sabata (1-6)

  • Mukakhala mlendo muzidzichepetsa (7-11)

  • Muziitana anthu amene sangathe kukubwezerani (12-14)

  • Fanizo la anthu amene anakana kupita kuphwando (15-24)

  • Zimene zimafunika kuti munthu akhale wophunzira (25-33)

  • Mchere umene watha mphamvu (34, 35)

14  Nthawi ina anapita kukadya chakudya mʼnyumba ya mmodzi wa atsogoleri a Afarisi pa Sabata ndipo anthu amene anali mʼnyumbamo ankamuyangʼanitsitsa.  Patsogolo pake panali munthu amene ankadwala matenda amene anachititsa kuti manja ndi miyendo yake itupe.*  Atamuona, Yesu anafunsa anthu odziwa Chilamulo komanso Afarisiwo kuti: “Kodi nʼzololeka kuchiritsa pa Sabata kapena ayi?”+  Koma iwo anangokhala chete. Zitatero iye anagwira munthu uja nʼkumuchiritsa ndipo anamuuza kuti azipita kwawo.  Ndiyeno anawafunsa kuti: “Ndi ndani wa inu amene mwana wake kapena ngʼombe yake itagwera mʼchitsime+ tsiku la Sabata, sangaitulutse nthawi yomweyo?”+  Iwo sanathe kumuyankha funso limeneli.  Ataona kuti anthu amene anaitanidwawo akusankha malo olemekezeka kwambiri,+ anawauza fanizo kuti:  “Wina akakuitana kuphwando laukwati, usakhale pamalo olemekezeka kwambiri.+ Mwina nʼkutheka kuti waitananso wina wolemekezeka kuposa iwe.  Ndiye amene anakuitanani uja angabwere nʼkudzakuuza kuti, ‘Choka pamenepa pakhale bambo awa.’ Zikatero ungachokepo mwamanyazi nʼkukakhala kumapeto kwenikweni. 10  Koma ukaitanidwa, pita ndipo ukakhale kumapeto kwenikweni, kuti munthu amene anakuitana uja akafika adzakuuze kuti, ‘Bwanawe, khala pamalo aulemuwa.’ Zikadzatero udzalemekezeka pamaso pa alendo anzako onse.+ 11  Chifukwa aliyense amene amadzikweza adzatsitsidwa, koma aliyense amene amadzichepetsa adzakwezedwa.”+ 12  Kenako anauzanso munthu amene anamuitana uja kuti: “Ukakonza chakudya chamasana kapena chamadzulo, usaitane anzako, kapena azichimwene ako, kapena achibale ako, kapena anthu olemera omwe amakhala nawe pafupi. Mwina nthawi ina iwonso angadzakuitane ndipo adzakhala ngati akukubwezera. 13  Koma ukakonza phwando, uziitana anthu osauka, otsimphina, olumala ndi osaona.+ 14  Ukatero udzakhala wosangalala chifukwa alibe choti adzakubwezere. Mulungu adzakubwezera anthu olungama akamadzaukitsidwa.”+ 15  Atamva zimenezi, mmodzi wa alendo anzake anamuuza kuti: “Wosangalala ndi munthu amene adzadye chakudya* mu Ufumu wa Mulungu.” 16  Yesu anamuuza kuti: “Munthu wina anakonza phwando lalikulu la chakudya chamadzulo+ ndipo anaitana anthu ambiri. 17  Nthawi ya chakudya chamadzulocho itakwana, anatumiza kapolo wake kukauza anthu amene anawaitanawo kuti, ‘Tiyeni, chifukwa zonse zakonzedwa tsopano.’ 18  Koma onse anayamba kupereka zifukwa zokanira.+ Woyamba anamuuza kuti, ‘Ine ndagula munda ndipo ndikuyenera kupita kukauona. Pepani sinditha kubwera.’ 19  Wina ananena kuti, ‘Ine ndagula ngʼombe 10 zapagoli ndipo ndikupita kukaziyesa. Pepani sinditha kubwera.’+ 20  Komanso wina ananena kuti, ‘Ine ndangokwatira kumene, choncho sindingathe kubwera.’ 21  Ndiyeno kapolo uja anabwerera kukanena zimenezi kwa mbuye wake. Mwininyumbayo atamva zimenezi anakwiya ndipo anauza kapolo wakeyo kuti, ‘Pita mwamsanga mʼmisewu ndi mʼnjira zamumzindawu, ukatenge anthu osauka, otsimphina, osaona komanso olumala nʼkubwera nawo kuno.’ 22  Patapita kanthawi kapolo uja anati, ‘Mbuyanga, zimene munalamula zachitika, komabe malo adakalipo.’ 23  Ndiyeno mbuye uja anauza kapolo wakeyo kuti, ‘Pita mʼmisewu ina yakunja kwa mzinda ndipo ukalimbikitse anthu abwere kuno kuti nyumba yanga idzaze.+ 24  Chifukwa ndikukuuzani kuti, palibe ndi mmodzi yemwe mwa anthu amene anaitanidwa aja amene adzalaweko chakudya changa chamadzulo.’”+ 25  Ndiyeno gulu lalikulu la anthu linkayenda limodzi ndi Yesu ndipo iye anacheuka nʼkuwauza kuti: 26  “Ngati wina akunditsatira koma osadana ndi* bambo ake, mayi ake, mkazi wake, ana ake, azichimwene ake komanso azichemwali ake, inde ngakhale moyo wake umene,+ sangakhale wophunzira wanga.+ 27  Aliyense wosanyamula mtengo wake wozunzikirapo* nʼkunditsatira sangakhale wophunzira wanga.+ 28  Mwachitsanzo, ndi ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja sayamba wakhala pansi nʼkuwerengera ndalama zimene adzawononge, kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kumalizira nsanjayo? 29  Akapanda kutero, angayale maziko koma osatha kuimaliza ndipo onse oona angayambe kumuseka 30  nʼkumanena kuti: ‘Munthu uyu anayamba bwinobwino kumanga, koma zamukanika kumaliza.’ 31  Kapena ndi mfumu iti, imene popita kukakumana ndi mfumu inzake kunkhondo, siyamba yakhala pansi nʼkuganizira mofatsa ngati asilikali ake 10,000 angathe kulimbana ndi asilikali 20,000 a mfumu imene ikubwera kudzalimbana naye? 32  Koma akaona kuti sangakwanitse, mwamsanga amatumiza akazembe kwa mfumu inayo isanafike pafupi, kukapempha mtendere. 33  Mofanana ndi zimenezi, ndithu palibe aliyense wa inu amene akulephera kusiya chuma chake chonse, amene angathe kukhala wophunzira wanga.+ 34  Kunena zoona, mchere ndi wabwino. Koma ngati mcherewo watha mphamvu, kodi mphamvu yakeyo ingabwezeretsedwe bwanji?+ 35  Ndi wosayenera kuuthira munthaka kapena mʼmanyowa. Anthu amangoutaya kunja. Amene ali ndi makutu akumva, amve.”+

Mawu a M'munsi

Munthu amene ali ndi matenda amenewa amatupa chifukwa cha kuchuluka kwa madzi mʼthupi.
Mʼchilankhulo choyambirira, “mkate.”
Kapena kuti, “koma osachepetsa chikondi chake kwa.”