Wolembedwa ndi Luka 2:1-52

  • Kubadwa kwa Yesu (1-7)

  • Angelo anaonekera kwa abusa (8-20)

  • Mdulidwe komanso kuyeretsedwa (21-24)

  • Simiyoni anaona Khristu (25-35)

  • Anna analankhula zokhudza mwanayo (36-38)

  • Anabwerera ku Nazareti (39, 40)

  • Yesu anapita kukachisi ali ndi zaka 12 (41-52)

2  Tsopano mʼmasiku amenewo, Kaisara Augusito analamula kuti anthu onse mʼdzikolo akalembetse mʼkaundula.  (Kalembera ameneyu anali woyamba ndipo anachitika pamene Kureniyo anali bwanamkubwa wa Siriya.)  Anthu onse anapita kukalembetsa ndipo aliyense anapita kumzinda wakwawo.  Yosefe+ nayenso anachoka ku Galileya, mumzinda wa Nazareti nʼkupita ku Yudeya, kumzinda wa Davide wotchedwa Betelehemu,+ chifukwa anali wa mʼbanja komanso fuko la Davide.  Anapita kukalembetsa limodzi ndi Mariya amene anamanga naye banja malinga ndi pangano.+ Pa nthawiyi nʼkuti Mariya atatsala pangʼono kubereka.+  Ali kumeneko, nthawi yoti abereke inakwana.  Iye anabereka mwana wake woyamba wamwamuna+ ndipo anamukulunga ndi nsalu nʼkumugoneka modyeramo ziweto,+ chifukwa sanapeze malo mʼnyumba ya alendo.  Mʼdera limeneli munalinso abusa amene ankagonera kumalo odyetsera ziweto nʼkumayangʼanira nkhosa zawo usiku wonse.  Mwadzidzidzi mngelo wa Yehova* anaima chapafupi ndi iwo, ndipo ulemerero wa Yehova* unawala pamalo onsewo moti anachita mantha kwambiri. 10  Koma mngeloyo anawauza kuti: “Musaope! Ine ndabwera kudzalengeza kwa inu uthenga wabwino wa chimwemwe chachikulu chimene anthu onse adzakhale nacho. 11  Chifukwa lero, mumzinda wa Davide+ mwabadwa mpulumutsi wanu,+ amene ndi Khristu Ambuye.+ 12  Ndikukupatsani chizindikiro ichi: Kumeneko mukapeza mwana wakhanda atamukulunga ndi nsalu nʼkumugoneka modyeramo ziweto.” 13  Mwadzidzidzi, panaoneka gulu lalikulu lakumwamba lili limodzi ndi mngeloyo+ ndipo linkatamanda Mulungu kuti: 14  “Ulemerero kwa Mulungu kumwambamwamba, ndipo padziko lapansi pano mtendere pakati pa anthu amene iye amasangalala nawo.” 15  Choncho angelowo atachoka nʼkubwerera kumwamba, abusawo anayamba kuuzana kuti: “Tiyeni tipite ndithu ku Betelehemu kuti tikaone zimene zachitikazo, zimene Yehova* watidziwitsa.” 16  Iwo anapita mwamsanga ndipo anakapeza Mariya ndi Yosefe komanso mwana wakhandayo, atamugoneka modyeramo ziweto. 17  Ataona zimenezi, anafotokoza uthenga umene anauzidwa wokhudza mwana ameneyu. 18  Onse amene anamva anadabwa ndi zimene abusawo anawauza. 19  Koma Mariya anasunga mawu onsewa ndipo anayamba kuganizira tanthauzo la zimenezi mumtima mwake.+ 20  Kenako abusa aja anabwerera, akulemekeza komanso kutamanda Mulungu chifukwa cha zonse zimene anamva ndi kuziona, mogwirizana ndi zimene anauzidwa. 21  Patatha masiku 8, nthawi yoti achite mdulidwe wa mwanayo itakwana,+ anamupatsa dzina lakuti Yesu. Limeneli ndi dzina limene mngelo uja anatchula Mariya asanakhale woyembekezera.+ 22  Komanso nthawi yoti iwo ayeretsedwe mogwirizana ndi Chilamulo cha Mose itakwana,+ anapita ndi mwanayo ku Yerusalemu kukamupereka kwa Yehova.* 23  Izi zinali zogwirizana ndi zimene zinalembedwa mʼChilamulo cha Yehova* kuti: “Mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa* adzakhala woyera kwa Yehova.”*+ 24  Kumeneko iwo anapereka nsembe mogwirizana ndi zimene Chilamulo cha Yehova* chimanena kuti: “njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda.”+ 25  Ndiyeno mu Yerusalemu munali munthu wina dzina lake Simiyoni. Mwamuna ameneyu anali wolungama komanso wodzipereka kwa Mulungu. Iye ankayembekezera nthawi imene Mulungu adzatonthoze Isiraeli+ ndipo mzimu woyera unali pa iye. 26  Komanso Mulungu anamuululira kudzera mwa mzimu woyera kuti sadzafa asanaone Khristu wa Yehova.* 27  Ndiye motsogoleredwa ndi mzimu, anabwera kukachisi. Ndipo pamene makolo a mwanayo, Yesu, anamubweretsa kudzamuchitira zimene Chilamulo chinkafuna,+ 28  iye ananyamula mwanayo mʼmanja mwake nʼkutamanda Mulungu kuti: 29  “Tsopano, Ambuye Wamkulu Koposa, mukulola kapolo wanu kupita mu mtendere+ mogwirizana ndi zimene inu munanena, 30  chifukwa maso anga aona njira yanu yopulumutsira anthu+ 31  imene mwakonza pamaso pa anthu a mitundu yonse.+ 32  Maso anga aona kuwala+ kochotsa nsalu yophimba imene ikulepheretsa mitundu ya anthu kuti isamaone,+ komanso ndaona ulemerero wa anthu anu Aisiraeli.” 33  Bambo ake a mwanayo ndiponso mayi ake ankangodabwa ndi zimene Simiyoni ankanena zokhudza mwanayo. 34  Komanso Simiyoni anadalitsa makolowo ndipo anauza Mariya, mayi a mwanayo kuti: “Tamvera! Mwanayu waikidwa kuti ambiri agwe+ ndiponso kuti ambiri adzukenso mu Isiraeli.+ Komanso kuti akhale chizindikiro chimene anthu adzachitsutse+ 35  (inde, lupanga lalitali lidzakubaya)+ kuti zimene anthu ambiri akuganiza mumtima mwawo zionekere poyera.” 36  Kunalinso mneneri wamkazi, dzina lake Anna mwana wa Fanueli, wa fuko la Aseri. Mayi ameneyu anali wachikulire kwambiri ndipo anakhala ndi mwamuna wake zaka 7 zokha kuchokera pamene anakwatirana.* 37  Tsopano anali mkazi wamasiye ndipo anali ndi zaka 84 koma sankasowa pakachisi. Ankachita utumiki wopatulika masana ndi usiku ndipo ankasala kudya komanso kupemphera mopembedzera. 38  Mu ola limenelo iye anafika pafupi nʼkuyamba kuyamika Mulungu komanso kulankhula zokhudza mwanayo kwa onse amene ankayembekezera chipulumutso cha Yerusalemu.+ 39  Choncho atachita zonse mogwirizana ndi Chilamulo cha Yehova,*+ anabwerera ku Galileya, kumzinda wawo wa Nazareti.+ 40  Mwanayo anapitiriza kukula ndiponso kukhala wamphamvu. Nzeru zake zinkachuluka ndipo Mulungu anapitiriza kusangalala naye.+ 41  Chaka ndi chaka makolo ake ankakonda kupita ku Yerusalemu, kuchikondwerero cha Pasika.+ 42  Ndiye ali ndi zaka 12, iwo anapita naye kumeneko mogwirizana ndi mwambo wa chikondwererocho.+ 43  Chikondwererocho chitatha, iwo ananyamuka kubwerera kwawo. Koma mnyamatayo Yesu anatsalira ku Yerusalemu ndipo makolo ake sanadziwe zimenezo. 44  Iwo ankaganiza kuti iye anali nawo mʼgulu la anthu a pa ulendowo, moti anayenda ulendo wa tsiku lathunthu. Kenako anayamba kumufunafuna mwa achibale ndi anzawo. 45  Koma atalephera kumupeza, anabwerera ku Yerusalemu. Kumeneko anamufufuza pena paliponse. 46  Ndiyeno patatha masiku atatu, anamupeza ali mʼkachisi, atakhala pakati pa aphunzitsi ndipo ankawamvetsera nʼkumawafunsa mafunso. 47  Koma onse amene ankamumvetsera anadabwa kwambiri ndi mayankho ake komanso poona kuti anali womvetsa zinthu kwambiri.+ 48  Makolo akewo atamuona anadabwa kwambiri, ndipo mayi ake anamufunsa kuti: “Mwanawe, nʼchifukwa chiyani wativutitsa chonchi? Ine ndi bambo akowa tinali ndi nkhawa kwambiri ndipo timakufunafuna.” 49  Koma iye anawayankha kuti: “Mumandifunafuna chifukwa chiyani? Kodi simumadziwa kuti ndiyenera kupezeka mʼnyumba ya Atate wanga?”+ 50  Koma iwo sanamvetse zimene ankawauzazo. 51  Kenako ananyamuka nawo limodzi nʼkubwerera ku Nazareti ndipo anapitiriza kuwamvera.+ Apanso mayi akewo anasunga mosamala kwambiri mawu onsewa mumtima mwawo.+ 52  Koma Yesu anapitiriza kukula mu nzeru ndi mu msinkhu. Ndipo Mulungu ndi anthu anapitiriza kusangalala naye.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “Mwamuna aliyense wotsegula mimba ya mayi ake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “kuchokera pa unamwali wake.”