Wolembedwa ndi Luka 23:1-56

  • Yesu anaonekera pamaso pa Pilato ndi Herode (1-25)

  • Yesu anapachikidwa pamtengo limodzi ndi zigawenga ziwiri (26-43)

    • “Iwe udzakhala ndi ine mʼParadaiso” (43)

  • Imfa ya Yesu (44-49)

  • Kuikidwa mʼmanda kwa Yesu (50-56)

23  Choncho gulu lonse linanyamuka pamodzi nʼkupita ndi Yesu kwa Pilato.+  Ndiyeno anayamba kumuneneza kuti:+ “Ife tapeza munthu uyu akupandutsa mtundu wathu, akuletsa anthu kuti asamakhome msonkho kwa Kaisara+ komanso akunena kuti ndi Khristu mfumu.”+  Tsopano Pilato anamufunsa kuti: “Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda?” Iye anayankha kuti: “Zili choncho, monga mmene mwanenera.”+  Kenako Pilato anauza ansembe aakulu ndi gulu la anthulo kuti: “Sindikupeza mlandu uliwonse mwa munthu uyu.”+  Koma iwo anaumirira nʼkunena kuti: “Iyeyu akusokoneza anthu mwa kuphunzitsa mu Yudeya monse, kuyambira ku Galileya mpaka kudzafika kuno.”  Atamva zimenezo, Pilato anafunsa ngati munthuyu ndi Mgalileya.  Ndiyeno atadziwa kuti akuchokera mʼchigawo chimene amalamulira Herode,+ anamutumiza kwa Herode, amenenso mʼmasiku amenewo anali mu Yerusalemu.  Herode ataona Yesu anasangalala kwambiri. Kwa nthawi yaitali ndithu ankafunitsitsa kuti aone Yesu chifukwa anali atamva zambiri zokhudza iye.+ Komanso ankayembekezera kuti aone chizindikiro chimene iye angachite.  Choncho anayamba kumufunsa zinthu zambiri, koma iye sanamuyankhe.+ 10  Komabe ansembe aakulu ndi alembi ankangonyamukanyamuka nʼkumamuneneza mwaukali. 11  Ndiyeno Herode limodzi ndi asilikali ake anamuchitira zachipongwe.+ Anamunyoza+ pomuveka chovala chokongola kwambiri, kenako anamutumizanso kwa Pilato. 12  Tsiku lomwelo Herode anakhala mnzake wa Pilato, koma mʼmbuyo monsemo zimenezi zisanachitike ankadana kwambiri. 13  Ndiyeno Pilato anasonkhanitsa ansembe aakulu, olamulira ndi anthu ena 14  nʼkuwauza kuti: “Inu mwabweretsa munthu uyu kwa ine ndi mlandu wakuti akulimbikitsa anthu kuukira. Koma mwaona nokha! Ine ndamufunsa pamaso panu ndipo sindinamupeze ndi chifukwa chomuimbira milandu imene mukumunenezayi.+ 15  Ndipotu ngakhale Herode sanamupeze ndi mlandu, nʼchifukwa chake wamubweza kwa ife. Ndithudi ameneyu sanachite chilichonse choyenera chilango cha imfa. 16  Choncho ndingomukwapula+ nʼkumumasula.” 17  *—— 18  Koma gulu lonse linafuula kuti: “Ameneyu muthane naye basi, koma ife mutimasulire Baraba!”+ 19  (Munthu ameneyu anaponyedwa mʼndende chifukwa cha kuukira boma kumene kunachitika mumzindawo komanso chifukwa chopha munthu.) 20  Pilato analankhula nawonso kachiwiri chifukwa ankafunitsitsa kuti amasule Yesu.+ 21  Ndiyeno anthuwo anayamba kufuula kuti: “Apachikidwe ameneyo! Apachikidwe ameneyo!”+ 22  Anawafunsa kachitatu kuti: “Chifukwa chiyani? Kodi iyeyu walakwa chiyani? Ine sindinamupeze ndi chifukwa chilichonse chomuphera. Choncho ndimukwapula nʼkumumasula.” 23  Atamva zimenezi anamuumiriza mokweza mawu kuti Yesu aphedwe basi. Anthuwo ankafuula mwamphamvu moti Pilato anangololera.+ 24  Choncho Pilato anapereka chiweruzo chogwirizana ndi zimene anthuwo ankafuna. 25  Iye anamasula munthu amene anthuwo ankafuna, amene anaikidwa mʼndende pa mlandu woukira boma komanso kupha munthu. Koma Yesu anamupereka mʼmanja mwawo kuti achite zimene ankafuna. 26  Pamene ankapita naye, iwo anagwira Simoni wa ku Kurene, amene ankachokera kudera lakumidzi. Iwo anamusenzetsa mtengo wozunzikirapo* kuti aunyamule nʼkumatsatira pambuyo pa Yesu.+ 27  Gulu lalikulu la anthu linkamutsatira kuphatikizapo azimayi ambiri amene ankadziguguda pachifuwa chifukwa cha chisoni komanso kumulirira. 28  Yesu anacheukira azimayiwo nʼkunena kuti: “Inu ana aakazi a Yerusalemu, siyani kundilirira. Koma mudzilirire nokha ndi ana anu.+ 29  Chifukwa masiku akubwera pamene anthu adzanena kuti, ‘Osangalala ndi akazi amene alibe ana, akazi amene sanaberekepo komanso akazi amene sanayamwitsepo!’+ 30  Mʼmasiku amenewo iwo adzayamba kuuza mapiri kuti, ‘Tigwereni!’ ndipo adzauza mapiri angʼonoangʼono kuti, ‘Tikwirireni!’+ 31  Ngati akuchita zinthu zimenezi mtengo uli wauwisi, kuli bwanji mtengowo ukadzauma?” 32  Anthuwo anatenganso amuna ena awiri, amene anali zigawenga, kuti akawaphe limodzi ndi Yesu.+ 33  Ndiyeno atafika pamalo otchedwa Chibade,+ anamukhomerera pamtengo limodzi ndi zigawenga zija. Mmodzi anamupachika kudzanja lake lamanja ndipo wina anali kumanzere kwake.+ 34  Koma Yesu ananena kuti: “Atate, akhululukireni, chifukwa sakudziwa zimene akuchita.” Iwo anagawana zovala zake pochita maere.+ 35  Anthu anangoima nʼkumaonerera zimene zinkachitikazo. Koma olamulira ankamunyogodola nʼkumanena kuti: “Ena anatha kuwapulumutsa, musiyeni adzipulumutse yekha, ngati alidi Khristu wa Mulungu, Wosankhidwa.”+ 36  Ngakhale asilikali nawonso ankamuchitira zachipongwe, ankabwera kudzamupatsa vinyo wowawasa+ 37  nʼkumanena kuti: “Ngati ndiwe Mfumu ya Ayuda, dzipulumutse wekha.” 38  Pamwamba pake analembapo mawu akuti: “Uyu ndi Mfumu ya Ayuda.”+ 39  Ndiyeno mmodzi wa zigawenga zimene zinapachikidwa naye limodzi zija, anayamba kumulankhulira zachipongwe+ kuti: “Kodi si iwe Khristu? Dzipulumutse wekha, limodzi ndi ife.” 40  Poyankha mnzake uja anamudzudzula kuti: “Kodi iwe sukuopa Mulungu poona kuti nawenso ukulandira chilango chofanana ndi cha munthu ameneyu? 41  Ifetu mpake kulangidwa chonchi, chifukwa tikulandira zimene timayenera kulandira mogwirizana ndi zimene tinachita. Koma munthu uyu sanalakwe chilichonse.” 42  Kenako ananena kuti: “Yesu, mukandikumbukire mukakalowa mu Ufumu wanu.”+ 43  Yesu anamuuza kuti: “Ndithu ndikukuuza lero, iwe udzakhala ndi ine mʼParadaiso.”+ 44  Apa nʼkuti nthawi ili cha mʼma 12 koloko masana,* koma kunagwa mdima mʼdziko lonselo mpaka 3 koloko masana,*+ 45  chifukwa dzuwa linachita mdima. Pa nthawi imeneyi nsalu yotchinga yamʼnyumba yopatulika+ inangʼambika pakati kuchokera pamwamba mpaka pansi.+ 46  Kenako Yesu anafuula mokweza mawu kuti: “Atate, ndikupereka mzimu wanga mʼmanja mwanu!”+ Atanena zimenezi anatsirizika.+ 47  Ataona zimene zinachitikazo, mtsogoleri wa asilikali anayamba kutamanda Mulungu kuti: “Ndithudi munthu uyu anali wolungama.”+ 48  Anthu onse amene anasonkhana kumeneko kudzaonerera zimene zinkachitikazo, ataona zonse zimene zinachitika, anabwerera kwawo akudziguguda pachifuwa. 49  Anthu onse amene ankamudziwa anaimirira chapatali ndithu. Komanso azimayi amene anamutsatira kuchokera ku Galileya anali pomwepo ndipo anaona zinthu zimenezi.+ 50  Ndiyeno panali mwamuna wina dzina lake Yosefe, amene anali wa mʼKhoti Lalikulu la Ayuda. Munthu ameneyu anali wabwino komanso wolungama.+ 51  (Iye sanavomereze chiwembu chawo komanso zimene anachita.) Yosefe anali wochokera ku Arimateya, mzinda wa Ayudeya ndipo ankayembekezera Ufumu wa Mulungu. 52  Iye anapita kwa Pilato kukapempha mtembo wa Yesu. 53  Choncho anautsitsa+ nʼkuukulunga munsalu yabwino kwambiri ndipo anakauika mʼmanda*+ amene anawagoba muthanthwe, mmene anali asanaikemo munthu chiyambire. 54  Tsopano linali Tsiku Lokonzekera,+ ndipo Sabata+ linali litatsala pangʼono kuyamba. 55  Koma azimayi amene anabwera limodzi ndi Yesu kuchokera ku Galileya, anamutsatira ndipo anaona mandawo* komanso mmene mtembo wakewo anauikira.+ 56  Atatero anabwerera kukakonza zonunkhiritsa ndi mafuta onunkhira. Komabe pa tsiku la Sabata anapuma+ malinga ndi chilamulo.

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 6,” kuwerenga kuchokera mʼma 6 koloko mʼmawa.
Mʼchilankhulo choyambirira, “ola la 9,” kuwerenga kuchokera mʼma 6 koloko mʼmawa.
Kapena kuti, “manda achikumbutso.”
Kapena kuti, “manda achikumbutsowo.”