Wolembedwa ndi Luka 1:1-80

  • Kalata yopita kwa a Teofilo (1-4)

  • Gabrieli ananeneratu za kubadwa kwa Yohane Mʼbatizi (5-25)

  • Gabrieli ananeneratu za kubadwa kwa Yesu (26-38)

  • Mariya anapita kwa Elizabeti (39-45)

  • Mariya analemekeza Yehova (46-56)

  • Kubadwa kwa Yohane komanso mmene anamupatsira dzina (57-66)

  • Ulosi wa Zekariya (67-80)

1  Anthu ambiri ayesetsa kulemba nkhani yofotokoza zochitika zenizeni zimene ife tonse timazikhulupirira.*+  Iwo analemba ndendende mmene anatiuzira anthu amene kuchokera pachiyambi, anali mboni zoona ndi maso+ komanso atumiki a uthengawo.+  Inenso, popeza kuti ndafufuza zinthu zonse mosamala kwambiri kuchokera pachiyambi, ndatsimikiza kuti ndikulembereni mwatsatanetsatane, inu wolemekezeka kwambiri, a Teofilo.+  Ndachita zimenezi kuti mudziwe bwinobwino kuti zinthu zimene anakuphunzitsani ndi mawu apakamwa nʼzodalirika.+  Mʼmasiku a Herode,*+ mfumu ya Yudeya, kunali wansembe wina dzina lake Zekariya wa mʼgulu la ansembe la Abiya.+ Mkazi wake anali wochokera mwa ana aakazi a Aroni ndipo dzina lake anali Elizabeti.  Awiri onsewo anali olungama pamaso pa Mulungu chifukwa ankayenda mokhulupirika, mogwirizana ndi malamulo onse komanso zimene chilamulo cha Yehova* chimafuna.  Koma iwo analibe mwana chifukwa Elizabeti anali wosabereka ndipo onse awiri anali okalamba.  Tsopano pamene Zekariya ankagwira ntchito monga wansembe pamaso pa Mulungu, kuimira gulu lake la ansembe,+  mogwirizana ndi zimene ansembe ankachita nthawi zonse,* inali nthawi yake yakuti akalowa mʼnyumba yopatulika ya Yehova,*+ akapereke nsembe zofukiza.+ 10  Gulu lonse la anthu linkapemphera panja, pa ola lopereka nsembe zofukizalo. 11  Mngelo wa Yehova* anaonekera kwa iye, ataimirira mbali yakumanja ya guwa lansembe zofukiza. 12  Koma Zekariya ataona zimenezo anavutika mumtima ndipo anachita mantha kwambiri. 13  Ndiye mngeloyo anamuuza kuti: “Usachite mantha Zekariya chifukwa pemphero lako lopembedzera lamveka ndithu. Mkazi wako Elizabeti adzakuberekera mwana wamwamuna ndipo udzamupatse dzina lakuti Yohane.+ 14  Udzasangalala komanso kukondwera kwambiri ndipo anthu ambiri adzasangalala ndi kubadwa kwake+ 15  chifukwa adzakhala wamkulu pamaso pa Yehova.*+ Koma asadzamwe vinyo ngakhale pangʼono kapena chakumwa chilichonse choledzeretsa+ ndipo adzadzazidwa ndi mzimu woyera asanabadwe nʼkomwe.*+ 16  Iye adzathandiza Aisiraeli ambiri kuti alape nʼkuyambiranso kumvera Yehova* Mulungu wawo.+ 17  Komanso adzatsogola monga kalambulabwalo wa Mulungu ali ndi mzimu ndi mphamvu ngati za Eliya.+ Iye adzatembenuza mitima ya abambo kuti ikhale ngati ya ana+ ndipo anthu osamvera adzawatembenuzira ku nzeru yeniyeni ya anthu olungama. Adzachita zimenezi kuti asonkhanitse anthu amene akonzekera kutumikira Yehova.”*+ 18  Ndiyeno Zekariya anafunsa mngeloyo kuti: “Nditsimikiza bwanji zimenezi? Inetu ndine wokalamba ndipo mkazi wanganso ali ndi zaka zambiri.” 19  Mngeloyo anamuyankha kuti: “Ine ndine Gabirieli+ amene ndimaima pamaso pa Mulungu+ ndipo wandituma kudzalankhula nawe komanso kudzalengeza uthenga wabwinowu kwa iwe. 20  Ndiye tamvera! Udzakhala chete osatha kulankhula, mpaka tsiku limene zinthu zimenezi zidzachitike chifukwa sunakhulupirire mawu anga amene adzakwaniritsidwe pa nthawi yake imene inaikidwiratu.” 21  Pa nthawiyi nʼkuti anthu akuyembekezerabe Zekariya ndipo anadabwa chifukwa chakuti anachedwa kwambiri mʼnyumba yopatulikayo. 22  Atatuluka sanathenso kulankhula nawo ndipo iwo anazindikira kuti waona zinthu zodabwitsa* mʼnyumba yopatulikayo. Iye ankalankhula nawo ndi manja, sankathanso kutulutsa mawu. 23  Masiku ake ochita utumiki wopatulika* atatha, anapita kwawo. 24  Patapita masiku angapo, mkazi wake Elizabeti anakhala woyembekezera ndipo anakhala kwayekha miyezi 5. Iye ananena kuti: 25  “Izitu nʼzimene Yehova* wandichitira masiku ano. Iye wandikumbukira kuti achotse kunyozeka kwanga pamaso pa anthu.”+ 26  Elizabeti ali woyembekezera kwa miyezi 6, Mulungu anatumiza mngelo Gabirieli+ kumzinda wina wa ku Galileya, wotchedwa Nazareti. 27  Anamutumiza kwa namwali+ amene mwamuna wina dzina lake Yosefe, wa mʼnyumba ya Davide, anamulonjeza* kuti adzamukwatira. Namwali ameneyu dzina lake anali Mariya.+ 28  Mngelo uja atafika kwa namwaliyu ananena kuti: “Moni, iwe wodalitsidwa koposawe, Yehova* ali nawe.” 29  Koma mawu amenewa anamudabwitsa kwambiri moti anayamba kuganizira za moni wamtundu umenewu. 30  Choncho mngeloyo anamuuza kuti: “Usaope Mariya, chifukwa Mulungu wakukomera mtima. 31  Tsopano mvetsera! Udzakhala woyembekezera nʼkubereka mwana wamwamuna+ ndipo udzamupatse dzina lakuti Yesu.+ 32  Ameneyu adzakhala wamkulu+ ndipo adzatchedwa Mwana wa Wamʼmwambamwamba.+ Yehova* Mulungu adzamupatsa mpando wachifumu wa Davide atate wake.+ 33  Iye adzalamulira monga Mfumu panyumba ya Yakobo kwamuyaya ndipo Ufumu wake sudzatha.”+ 34  Koma Mariya anafunsa mngeloyo kuti: “Zimenezi zidzatheka bwanji, chifukwa sindinagonepo ndi mwamuna?”+ 35  Poyankha mngeloyo anauza Mariya kuti: “Mzimu woyera udzafika pa iwe+ ndipo mphamvu ya Wamʼmwambamwamba idzakuphimba. Pa chifukwa chimenechi amene adzabadweyo adzatchedwa woyera,+ Mwana wa Mulungu.+ 36  Ndipotu mʼbale wako Elizabeti, amene anthu amamunena kuti mkazi wosabereka, nayenso ndi woyembekezera ndipo adzabereka mwana wamwamuna mu ukalamba wake, moti uno ndi mwezi wake wa 6. 37  Izi zachitika chifukwa zimene Mulungu wanena sizilephereka.”*+ 38  Ndiyeno Mariya ananena kuti: “Ndine kapolo wa Yehova!* Zimene mwanenazo zichitike ndithu kwa ine.” Atatero mngeloyo anamusiya. 39  Choncho mʼmasiku amenewo Mariya ananyamuka mofulumira nʼkupita kudera lamapiri, kumzinda wina mʼdziko la fuko la Yuda. 40  Kumeneko analowa mʼnyumba ya Zekariya nʼkupereka moni kwa Elizabeti. 41  Ndiyeno Elizabeti atamva moni wa Mariya, khanda limene linali mʼmimba mwakemo linadumpha ndipo Elizabetiyo anadzazidwa ndi mzimu woyera. 42  Choncho anafuula mwamphamvu kuti: “Ndiwe wodalitsidwa mwa akazi onse ndipo chipatso cha mimba yako nʼchodalitsidwanso! 43  Koma zatheka bwanji kuti ndipeze mwayi umenewu, kuti mayi wa Mbuye wanga abwere kwa ine? 44  Mawu a moni wako atalowa mʼmakutu mwangamu, khanda ladumpha mosangalala mʼmimba mwangamu. 45  Ndipotu ndiwe wosangalala chifukwa unakhulupirira, moti zonse zimene unauzidwa zochokera kwa Yehova* zidzakwaniritsidwa.” 46  Ndiyeno Mariya ananena kuti: “Moyo wanga ukulemekeza Yehova,*+ 47  ndipo mzimu wanga sungalephere kusefukira ndi chimwemwe mwa Mulungu, Mpulumutsi wanga,+ 48  chifukwa waona malo otsika a kapolo wake wamkazi.+ Ndipo taonani! kuyambira tsopano mibadwo yonse idzanditcha wosangalala.+ 49  Chifukwa Wamphamvuyo wandichitira zazikulu ndipo dzina lake ndi loyera.+ 50  Kumibadwomibadwo iye amachitira chifundo anthu amene amamuopa.+ 51  Wachita zamphamvu ndi dzanja lake, wabalalitsira kutali amene zolinga zamʼmitima yawo zikusonyeza kuti ndi odzikuza.+ 52  Watsitsa anthu amphamvu pamipando yachifumu+ ndipo wakweza anthu onyozeka.+ 53  Wakhutitsa anthu anjala ndi zinthu zabwino+ koma amene anali ndi chuma wawathamangitsa chimanjamanja. 54  Iye wathandiza mtumiki wake Isiraeli pokumbukira lonjezo lake lakuti adzasonyeza chifundo+ 55  kwamuyaya, mogwirizana ndi zimene anauza makolo athu akale, Abulahamu ndi mbadwa* zake.”+ 56  Mariya anakhala ndi Elizabeti pafupifupi miyezi itatu kenako anabwerera kwawo. 57  Tsopano nthawi yoti Elizabeti abereke inakwana ndipo anabereka mwana wamwamuna. 58  Anthu oyandikana naye komanso achibale ake anamva kuti Yehova* anamuchitira chifundo chachikulu ndipo anasangalala naye limodzi.+ 59  Pa tsiku la 8, iwo anabwera kudzachita mdulidwe wa mwanayo+ komanso ankafuna kumupatsa dzina la bambo ake, lakuti Zekariya. 60  Koma mayi ake anayankha kuti: “Limenelo ayi! Dzina lake akhala Yohane.” 61  Atanena zimenezi, iwo anamuuza kuti: “Palibe wachibale wako aliyense amene amadziwika ndi dzina limenelo.” 62  Kenako anafunsa bambo ake, polankhula ndi manja, dzina limene akufuna kuti amupatse mwanayo. 63  Choncho iye anapempha poti alembepo ndipo analemba kuti: “Dzina lake ndi Yohane.”+ Ataona zimenezi onse anadabwa. 64  Nthawi yomweyo pakamwa pake panatseguka ndipo lilime lake linamasuka moti anayamba kulankhula+ ndi kutamanda Mulungu. 65  Anthu onse amene ankakhala mʼdera limenelo anagwidwa ndi mantha ndipo nkhani imeneyi inali mʼkamwamʼkamwa mʼdera lonse lamapiri ku Yudeya. 66  Onse amene anamva zimenezi anazisunga mʼmitima yawo ndipo ankanena kuti: “Kodi mwana ameneyu adzakhala wotani?” Chifukwa dzanja la Yehova* linalidi pa iye. 67  Ndiyeno Zekariya, bambo a mwanayo, anadzazidwa ndi mzimu woyera ndipo ananenera kuti: 68  “Atamandike Yehova* Mulungu wa Isiraeli,+ chifukwa wakumbukira anthu ake nʼkuwabweretsera chipulumutso.+ 69  Iye watikwezera nyanga yachipulumutso*+ mʼnyumba ya mtumiki wake Davide,+ 70  mogwirizana ndi zimene ananena kudzera pakamwa pa aneneri ake oyera akale,+ 71  zoti adzatipulumutsa kwa adani athu ndiponso mʼmanja mwa onse amene amadana nafe.+ 72  Adzakwaniritsa zimene analonjeza makolo athu akale ndipo adzawasonyeza chifundo. Iye adzakumbukira pangano lake loyera,+ 73  lumbiro limene analumbira kwa kholo lathu Abulahamu,+ 74  kuti pambuyo poti tapulumutsidwa mʼmanja mwa adani, atipatse mwayi wochita utumiki wopatulika kwa iye mopanda mantha, 75  mokhulupirika komanso mwachilungamo pamaso pake masiku athu onse. 76  Koma kunena za mwana wamngʼonowe, udzatchedwa mneneri wa Wamʼmwambamwamba, chifukwa udzatsogola pamaso pa Yehova* kuti ukakonze njira zake.+ 77  Kuti ukathandize anthu ake kudziwa za chipulumutso chimene chidzatheke machimo awo akadzakhululukidwa,+ 78  chifukwa cha chifundo chachikulu cha Mulungu wathu. Ndi chifundo chimenechi, kuwala kwamʼmawa kudzatifikira kuchokera kumwamba, 79  ndipo kudzaunikira amene akukhala mumdima komanso mumthunzi wa imfa+ ndi kutsogolera mapazi athu panjira yamtendere.” 80  Choncho mwana uja anakula ndipo analimba mwauzimu. Iye anapitiriza kukhala mʼchipululu mpaka tsiku limene anadzionetsera poyera kwa Isiraeli.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “timaona kuti nʼzodalirika.”
Kapena kuti, “mogwirizana ndi mwambo wa ansembe.”
Kapena kuti, “kuyambira ali mʼmimba mwa mayi ake.”
Kapena kuti, “waona masomphenya.”
Kapena kuti, “utumiki wotumikira anthu.”
Kapena kuti, “anali pachibwenzi.”
Kapena kuti, “chifukwa palibe chosatheka ndi Mulungu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Kapena kuti, “watikwezera mpulumutsi wamphamvu.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena, “Nyanga.”