Wolembedwa ndi Luka 19:1-48

  • Yesu anakacheza kwa Zakeyu (1-10)

  • Fanizo la ndalama zokwana ma mina 10 (11-27)

  • Yesu analowa mumzinda mwaulemerero (28-40)

  • Yesu analirira Yerusalemu (41-44)

  • Yesu anayeretsa kachisi (45-48)

19  Ndiyeno Yesu analowa mu Yeriko, koma anangodutsamo.  Kumeneko kunali munthu wina dzina lake Zakeyu. Iyeyu anali mkulu wa okhometsa msonkho ndipo anali wolemera.  Zakeyu ankafunitsitsa ataona Yesu, koma sanathe kumuona chifukwa cha gulu la anthu popeza anali wamfupi.  Choncho anathamangira kutsogolo nʼkukwera mumtengo wamkuyu kuti athe kumuona, chifukwa ankadutsa njira imeneyo.  Yesu atafika pamalopo, anayangʼana mʼmwambamo nʼkumuuza kuti: “Zakeyu, fulumira tsika, chifukwa lero ndikuyenera kukakhala mʼnyumba mwako.”  Atamva zimenezo anatsika mofulumira ndipo anamulandira mʼnyumba mwake monga mlendo mosangalala.  Anthu ataona Yesu akulowa mʼnyumbamo, onse anayamba kungʼungʼudza kuti: “Wapita kukakhala mlendo mʼnyumba ya munthu wochimwa.”+  Koma Zakeyu anaimirira nʼkuuza Ambuye kuti: “Ambuye, ine ndipereka ndithu hafu ya chuma changa kwa osauka. Ndipo chilichonse chimene ndinalanda munthu aliyense* ndibweza kuwirikiza ka 4.”+  Atamva zimenezi, Yesu anamuuza kuti: “Lero chipulumutso chafika panyumba ino, chifukwa nayenso ndi mwana wa Abulahamu. 10  Mwana wa munthu anabwera kudzafunafuna ndiponso kudzapulumutsa anthu osochera.”+ 11  Pamene iwo ankamvetsera zimenezi, iye anawauza fanizo lina, chifukwa anali pafupi ndi Yerusalemu ndipo anthuwo ankaganiza kuti Ufumu wa Mulungu uonekera nthawi yomweyo.+ 12  Choncho iye ananena kuti: “Munthu wina wa mʼbanja lachifumu ankakonzekera kuti apite kudziko lakutali+ kuti akalandire ufumu nʼkubwerako. 13  Ndiyeno anaitana akapolo ake 10 nʼkuwapatsa ndalama zokwana ma mina* 10 ndipo anawauza kuti, ‘Muchite malonda ndi ndalamazi mpaka nditabwera.’+ 14  Koma anthu amʼdziko lakwawo anadana naye ndipo iye atapita anatumiza akazembe kuti akanene kuti, ‘Ife sitikufuna kuti munthu ameneyu akhale mfumu yathu.’ 15  Atabwerera kwawo pambuyo polandira ufumuwo, anaitana akapolo amene anawapatsa ndalama* aja kuti abwere kwa iye, kuti awerengerane nʼkuona mmene apindulira pa malonda awo.+ 16  Woyamba anabwera ndipo ananena kuti, ‘Mbuyanga, ndalama yanu ya mina ija yapindula ndalama zina zokwana ma mina 10.’+ 17  Iye anamuuza kuti, ‘Wachita bwino, ndiwe kapolo wabwino! Chifukwa wasonyeza kuti ndiwe wokhulupirika pa chinthu chachingʼono, ndikupatsa ulamuliro woyangʼanira mizinda 10.’+ 18  Kenako kunabwera wachiwiri ndipo anati, ‘Mbuyanga, ndalama yanu ya mina ija yapindula ndalama zina zokwana ma mina 5.’+ 19  Iye anauzanso ameneyu kuti, ‘Nawenso ukhala woyangʼanira mizinda 5.’ 20  Koma kunabwera wina ndipo ananena kuti, ‘Mbuyanga, ndalama yanu ya mina ija ndi iyi. Ndinaimanga pansalu nʼkuibisa. 21  Ndinachita zimenezi chifukwa ndimakuopani. Inutu ndinu munthu wouma mtima. Mumatenga zimene simunasungitse ndipo mumakolola zimene simunafese.’+ 22  Iye anamuuza kuti, ‘Ndikuweruza potengera zimene wanena, kapolo woipa iwe. Ukuti umadziwa kuti ine ndine munthu wouma mtima, wotenga zimene sindinasungitse ndi kukolola zimene sindinafese.+ 23  Ndiye nʼchifukwa chiyani sunasungitse ndalama yangayo* kubanki? Ukanatero, ine pobwera ndikanaitenga limodzi ndi chiwongoladzanja chake.’ 24  Atatero anauza anthu amene anaima chapafupi kuti, ‘Mulandeni ndalama ya minayo nʼkuipereka kwa amene ali ndi ndalama za mina 10.’+ 25  Koma iwo anamuuza kuti, ‘Mbuyathu, iyetu ali ndi ndalama za mina 10!’— 26  ‘Ndithu ndikukuuzani, aliyense amene ali nazo, adzapatsidwa zinanso zambiri, koma amene alibe adzalandidwa ngakhalenso zimene ali nazo.+ 27  Komanso adani angawa, amene sanafune kuti ine ndikhale mfumu yawo, bwerani nawo kuno muwaphe ine ndikuona.’” 28  Atamaliza kunena zimenezi, anapitiriza ulendo wake wopita ku Yerusalemu. 29  Ndiyeno atayandikira ku Betefage ndi Betaniya paphiri lotchedwa phiri la Maolivi,+ anatumiza ophunzira ake awiri.+ 30  Iye anawauza kuti: “Pitani mʼmudzi umene mukuuonawo, ndipo mukalowa mmenemo mukapeza bulu wamngʼono wamphongo atamumangirira, amene munthu sanakwerepo chiyambire. Mukamumasule nʼkubwera naye kuno. 31  Koma aliyense akakakufunsani kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani mukumasula buluyu?’ Mukanene kuti, ‘Ambuye akumufuna.’” 32  Choncho anthu amene anatumidwawo ananyamuka ndipo anakamupezadi mmene iye anawauzira.+ 33  Koma pamene ankamasula buluyo, eniake anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukumasula buluyu?” 34  Iwo anayankha kuti: “Ambuye akumufuna.” 35  Pamenepo iwo anamutenga nʼkupita naye kwa Yesu. Kenako iwo anaponya malaya awo akunja pabuluyo ndipo Yesu anakwerapo.+ 36  Pamene ankayenda, anthu ankayala malaya awo akunja mumsewu.+ 37  Atangofika pafupi ndi msewu wochokera mʼphiri la Maolivi, gulu lonse la ophunzirawo linayamba kusangalala ndi kutamanda Mulungu mokweza mawu chifukwa cha ntchito zonse zamphamvu zimene anaona. 38  Iwo ankanena kuti: “Wodalitsidwa ndi amene akubwera monga Mfumu mʼdzina la Yehova!* Mtendere kumwamba ndi ulemerero kumwambamwambako!”+ 39  Koma Afarisi ena mʼgululo anauza Yesu kuti: “Mphunzitsi, adzudzuleni ophunzira anuwa.”+ 40  Poyankha iye anati: “Ndithu ndikukuuzani, ngati awa atakhala chete, miyala ingathe kufuula.” 41  Tsopano Yesu atayandikira mzinda wa Yerusalemu, anaona mzindawo nʼkuyamba kuulirira.+ 42  Iye anati: “Ngati iwe lero ukanazindikira zinthu zamtendere—* koma tsopano zabisika kuti usathe kuziona.+ 43  Chifukwa masiku adzakufikira pamene adani ako adzamanga mpanda wazisonga kukuzungulira. Adaniwo adzakutsekereza nʼkukuukira* kuchokera kumbali zonse.+ 44  Iwo adzakugwetsa pansi nʼkukuwononga limodzi ndi ana ako amene ali mwa iwe.+ Ndipo sadzasiya mwala pamwamba pa mwala unzake mwa iwe,+ chifukwa sunazindikire kuti nthawi yokuyendera inali itakwana.” 45  Ndiyeno analowa mʼkachisi nʼkuyamba kuthamangitsa anthu amene ankagulitsamo zinthu+ 46  nʼkuwauza kuti: “Malemba amati, ‘Nyumba yanga idzakhala nyumba yopemphereramo,’+ koma inu mwaisandutsa phanga la achifwamba.”+ 47  Ndipo tsiku ndi tsiku iye anapitiriza kuphunzitsa mʼkachisimo. Koma ansembe aakulu, alembi ndi akuluakulu a anthu ankafunitsitsa kumupha.+ 48  Koma sanathe kuchita zimenezi chifukwa anthu ambiri ankangomuunjirira kuti amumvetsere ndipo sankasiyana naye.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “ndinalanda munthu aliyense pomunamizira mlandu.”
Mina yotchulidwa mʼMalemba a Chigiriki inkalemera magalamu 340 ndipo inali yofanana ndi madalakima 100. Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “siliva.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “siliva wanga.”
Kamzere kameneka kakusonyeza kuti mawuwa anathera mʼmalere.
Kapena kuti, “kukusautsa.”