Levitiko 2:1-16

  • Nsembe yambewu (1-16)

2  “‘Ngati munthu akupereka nsembe yambewu+ kwa Yehova, azipereka ufa wosalala. Azithira mafuta nʼkuika lubani* pa ufawo.+  Akatero azibweretsa nsembe yakeyo kwa ana a Aroni, ansembe. Ndipo wansembe azitapa ufa wothira mafutawo pamodzi ndi lubani yense kudzaza dzanja limodzi, nʼkuuwotcha paguwa lansembe kuimira nsembe yonseyo.+ Imeneyi ndi nsembe yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa* yoperekedwa kwa Yehova.  Ndipo zotsala pa nsembe yambewu zizikhala za Aroni ndi ana ake,+ chifukwa ndi zopatulika koposa,+ zochokera pansembe zowotcha pamoto zoperekedwa kwa Yehova.  Ngati mukupereka nsembe yambewu yophikidwa mu uvuni, izikhala ya ufa wabwino kwambiri. Muzipereka mkate wozungulira woboola pakati, wopanda zofufumitsa, wothira mafuta. Kapena muzipereka timitanda ta mkate topyapyala topanda zofufumitsa, topaka mafuta.+  Ngati mukupereka nsembe yambewu yophika mʼchiwaya,+ izikhala ya ufa wabwino kwambiri wothira mafuta, yopanda zofufumitsa.  Muziibenthula zidutswazidutswa nʼkuithira mafuta.+ Imeneyi ndi nsembe yambewu.  Ngati mukupereka nsembe yambewu yophika mʼchiwaya, izikhala yopangidwa ndi ufa wosalala ndiponso mafuta.  Nsembe yambewu imene yapangidwa ndi zinthu zimenezi muzibwera nayo kwa Yehova. Muziipereka kwa wansembe ndipo iye azipita nayo paguwa lansembe.  Kenako wansembe azitengako pangʼono nsembe yambewu kuimira nsembe yonseyo,+ ndipo aziwotcha zimene watengazo paguwa lansembe. Imeneyi ndi nsembe yowotcha pamoto yakafungo kosangalatsa* yoperekedwa kwa Yehova.+ 10  Ndipo zimene zatsala pansembe yambewu zizikhala za Aroni ndi ana ake, chifukwa ndi zopatulika koposa zochokera pansembe zowotcha pamoto+ zoperekedwa kwa Yehova. 11  Nsembe yambewu imene mukupereka kwa Yehova isakhale ndi zofufumitsa,+ chifukwa simukuyenera kuwotcha ufa wokanda wokhala ndi zofufumitsa kapena uchi,* ngati nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova. 12  Zimenezi mungathe kuzipereka kwa Yehova ngati nsembe ya zipatso zoyambirira,+ koma simukuyenera kuzibweretsa paguwa lansembe kuti zikhale nsembe yakafungo kosangalatsa.* 13  Nsembe yanu iliyonse yambewu muziithira mchere. Popereka nsembe yambewu musamaiwale kupereka mchere wokukumbutsani pangano la Mulungu. Mukamapereka nsembe iliyonse, muziperekanso mchere.+ 14  Mukamapereka kwa Yehova nsembe yambewu ya zipatso zoyambirira kucha, muzipereka tirigu watsopano* wokazinga pamoto, wosinja kuti akhale nsembe yambewu ya zipatso zanu zoyambirira kucha.+ 15  Muzithira mafuta ndi kuika lubani pansembeyo. Imeneyi ndi nsembe yambewu. 16  Wansembe aziwotcha zinthu zimenezi kuimira nsembe yonseyo,+ zomwe ndi wina mwa tirigu wosinja uja komanso mafuta, pamodzi ndi lubani wake yense, kuti zikhale nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova.’”

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Zikuoneka kuti uchi umenewu sunali wa njuchi koma anali madzi azipatso, chifukwa ukutchulidwa kuti zipatso zoyambirira. (Le 2:12; 2Mb 31:5)
Mʼchilankhulo choyambirira, “yakafungo kokhazika mtima pansi.”
Kapena kuti, “muzipereka tirigu wamuwisi.”