Levitiko 17:1-16

  • Chihema, malo operekera nsembe (1-9)

  • Analetsa kudya magazi (10-14)

  • Malamulo okhudza nyama zopezeka zitafa (15, 16)

17  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti:  “Uza Aroni ndi ana ake komanso Aisiraeli onse kuti, ‘Izi ndi zimene Yehova walamula:  “Munthu aliyense wamʼnyumba ya Isiraeli akapha ngʼombe, nkhosa kapena mbuzi mumsasa, kapena kunja kwa msasa,  mʼmalo mobwera nayo pakhomo la chihema chokumanako, kuti aipereke monga nsembe kwa Yehova patsogolo pa chihema cha Yehova, ameneyo adzakhala ndi mlandu wa magazi. Munthu ameneyo wakhetsa magazi, ndipo ayenera kuphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake.  Lamulo limeneli laperekedwa kuti nsembe zimene Aisiraeli akuzipereka kunja, azibwera nazo kwa wansembe pakhomo la chihema chokumanako kuti azipereke kwa Yehova. Zimenezi ziziperekedwa monga nsembe zamgwirizano kwa Yehova.+  Wansembe aziwaza magazi a nyamazo paguwa lansembe la Yehova limene lili pakhomo la chihema chokumanako, ndipo aziwotcha mafuta ake kuti likhale kafungo kosangalatsa* kwa Yehova.+  Choncho asamaperekenso nsembe zawo kwa ziwanda zooneka ngati mbuzi+ zimene akuzilambira.*+ Limeneli likhale lamulo kwa inu mpaka kalekale, mʼmibadwo yanu yonse.”’  Uwauze kuti, ‘Munthu aliyense wamʼnyumba ya Isiraeli kapena mlendo wokhala pakati panu, amene wapereka nsembe yopsereza kapena nsembe iliyonse,  koma osabwera nayo pakhomo la chihema chokumanako kuti aipereke kwa Yehova, ayenera kuphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake.+ 10  Munthu aliyense wamʼnyumba ya Isiraeli kapena mlendo wokhala pakati panu, akadya magazi alionse,+ ndidzadana naye ndipo ndidzamupha kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake. 11  Chifukwa moyo wa nyama uli mʼmagazi+ ndipo ine ndawapereka paguwa lansembe+ kuti azikuphimbirani machimo. Zili choncho chifukwa magazi ndi amene amaphimba machimo+ chifukwa cha moyo umene uli mʼmagaziwo. 12  Nʼchifukwa chake ndauza Aisiraeli kuti: “Aliyense wa inu asamadye magazi ndipo mlendo wokhala pakati panu+ asamadye magazi.”+ 13  Ngati munthu wa Chiisiraeli kapena mlendo amene akukhala pakati panu wapita kokasaka, ndipo wapha nyama kapena mbalame imene munaloledwa kuti muzidya, azithira magazi ake pansi+ nʼkuwakwirira ndi dothi. 14  Moyo wa nyama iliyonse ndi magazi ake chifukwa mʼmagazimo ndi mmene muli moyo. Nʼchifukwa chake ndauza Aisiraeli kuti: “Musamadye magazi a nyama iliyonse, chifukwa moyo wa nyama ina iliyonse ndi magazi ake. Aliyense wodya magaziwo ayenera kuphedwa.”+ 15  Ngati munthu aliyense wadya nyama imene waipeza yakufa kapena imene yaphedwa ndi chilombo,+ kaya akhale nzika kapena mlendo wokhala pakati panu, munthu ameneyo azichapa zovala zake nʼkusamba thupi lonse, ndipo azikhala wodetsedwa mpaka madzulo.+ Kenako azikhala woyera. 16  Koma ngati sanachape zovala zakezo komanso sanasambe thupi lonse, ameneyo ayenera kuyankha mlandu chifukwa cha kulakwa kwakeko.’”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “kafungo kokhazika mtima pansi.”
Kapena kuti, “zimene akuchita nazo uhule.”