Levitiko 14:1-57

  • Kudziyeretsa ku khate (1-32)

  • Kuyeretsa nyumba zimene munali nthenda (33-57)

14  Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 2  “Ili likhale lamulo lokhudza wakhate pa tsiku limene adzamubweretse kwa wansembe+ pa nthawi yoti ayeretsedwe. 3  Wansembe azipita kunja kwa msasa kukamuona. Ngati munthuyo wachira khate lake, 4  wansembe azimulamula kuti abweretse mbalame zamoyo ziwiri zosadetsedwa, nthambi ya mtengo wa mkungudza, ulusi wofiira kwambiri ndi kamtengo ka hisope* kuti adzazigwiritse ntchito pomuyeretsa.+ 5  Ndipo wansembe azilamula kuti mbalame imodzi aiphere pamwamba pa madzi otunga kumtsinje, amene ali mʼchiwiya chadothi. 6  Koma azitenga mbalame yamoyo ija pamodzi ndi nthambi ya mtengo wa mkungudza, ulusi wofiira kwambiri ndi kamtengo ka hisope, nʼkuviika zinthu zonsezi mʼmagazi a mbalame imene aiphera pamwamba pa madzi otunga kumtsinje ija. 7  Kenako wansembe azidontheza magaziwo maulendo 7 pamunthu amene akudziyeretsa ku khateyo, ndipo azigamula kuti munthuyo ndi woyera. Akatero aziulutsa mbalame yamoyo ija pabwalo.+ 8  Munthu amene akudziyeretsayo azichapa zovala zake ndi kumeta tsitsi lake lonse, kenako azisamba ndipo azikhala woyera. Akatero angathe kulowa mumsasa, koma azikhala kunja kwa tenti yake kwa masiku 7. 9  Pa tsiku la 7 azimeta tsitsi lake lonse lakumutu, ndevu zake zonse ndi nsidze zonse. Akamaliza kumeta tsitsi lake lonse azichapa zovala zake nʼkusamba mʼmadzi ndipo adzakhala woyera. 10  Pa tsiku la 8, iye adzatenge nkhosa zazingʼono zamphongo ziwiri zopanda chilema komanso nkhosa yaingʼono yaikazi+ imodzi yopanda chilema, yosapitirira chaka chimodzi. Adzatengenso ufa wosalala wokwana magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa,* monga nsembe yake ya mbewu+ yothira mafuta ndi muyezo umodzi* wa mafuta.+ 11  Ndipo wansembe amene wagamula kuti munthuyo ndi woyera, azionetsa amene akudziyeretsayo, limodzi ndi zinthu zakezo kwa Yehova, pakhomo la chihema chokumanako. 12  Wansembeyo azidzatenga nkhosa yaingʼono yamphongo imodzi nʼkuipereka monga nsembe yakupalamula+ pamodzi ndi muyezo umodzi wa mafuta uja. Zimenezi aziziyendetsa uku ndi uku monga nsembe yoperekedwa kwa Yehova.+ 13  Kenako azipha nkhosa yaingʼono yamphongoyo pamalo amene nthawi zonse amapherapo nyama ya nsembe yamachimo ndi nsembe yopsereza,+ pamalo oyera. Azichita zimenezi chifukwa nsembe yakupalamula ndi ya wansembe+ mofanana ndi nsembe yamachimo. Nsembe yakupalamula ndi yopatulika koposa.+ 14  Ndiyeno wansembe azidzatenga ena mwa magazi a nsembe yakupalamula, nʼkuwapaka mʼmunsi pakhutu lakumanja la munthu amene akudziyeretsayo, pachala chake chamanthu kudzanja lamanja, ndi pachala chake chachikulu cha mwendo wakumanja. 15  Akatero, wansembeyo azitenga ena mwa mafuta pamuyezo umodzi+ uja nʼkuwathira pachikhatho cha dzanja lake lamanzere. 16  Kenako wansembe aziviika chala chake chakudzanja lamanja mʼmafuta amene ali pachikhatho cha dzanja lake lamanzere, ndipo azidontheza pansi ena mwa mafutawo ndi chala chakecho maulendo 7, pamaso pa Yehova. 17  Koma mafuta amene atsala pachikhatho cha wansembe aziwapaka mʼmunsi pakhutu lakumanja la munthu amene akudziyeretsayo, pachala chake chamanthu kudzanja lamanja, ndi pachala chake chachikulu cha mwendo wakumanja pamene anamupaka magazi a nsembe yakupalamula. 18  Mafuta otsala pachikhatho cha wansembe aziwapaka pamutu pa munthu amene akudziyeretsayo, ndipo wansembe adzamuphimbira machimo ake pamaso pa Yehova.+ 19  Wansembe adzapereke nsembe yamachimo+ nʼkuphimba machimo a munthu amene akudziyeretsayo. Kenako wansembe adzaphe nyama ya nsembe yopsereza. 20  Ndiyeno wansembe adzapereke nsembe yopsereza ndi nsembe yambewu+ paguwa lansembe. Akatero, wansembe adzamuphimbira machimo,+ ndipo munthuyo adzakhala woyera.+ 21  Koma ngati munthuyo ali wosauka ndipo sangakwanitse kupeza zinthu zimenezi, azibweretsa nkhosa yaingʼono yamphongo imodzi monga nsembe yakupalamula. Nsembeyo aziiyendetsa uku ndi uku kuti amuphimbire machimo. Azibweretsanso muyezo umodzi wa mafuta ndi ufa wosalala wothira mafuta wokwana gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa,* monga nsembe yake yambewu. 22  Komanso azibweretsa njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda, mogwirizana ndi zimene iye angakwanitse. Mbalame imodzi ikhale nsembe yamachimo ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza.+ 23  Pa tsiku la 8+ azibweretsa zinthuzi kwa wansembe pakhomo la chihema chokumanako pamaso pa Yehova,+ kuti wansembeyo agamule kuti munthuyo ndi woyera. 24  Kenako wansembe azitenga nkhosa yaingʼono yamphongo ya nsembe yakupalamula+ ndi muyezo umodzi wa mafuta uja, ndipo wansembeyo aziyendetsa zinthu zimenezi uku ndi uku, monga nsembe yoperekedwa kwa Yehova.+ 25  Ndiyeno wansembe azipha nkhosa yaingʼono yamphongo ya nsembe yakupalamula. Akatero azitenga ena mwa magazi a nsembe yakupalamulayo nʼkuwapaka mʼmunsi pakhutu lakumanja la munthu amene akudziyeretsayo, pachala chake chamanthu kudzanja lamanja, ndi pachala chake chachikulu cha mwendo wakumanja.+ 26  Wansembeyo adzathire ena mwa mafutawo pachikhatho cha dzanja lake lamanzere.+ 27  Akatero adzadontheze ndi chala chake cha dzanja lamanja ena mwa mafuta amene ali pachikhatho cha dzanja lake lamanzerewo maulendo 7 pamaso pa Yehova. 28  Kenako wansembe adzapake ena mwa mafuta amene ali pachikhatho chake, mʼmunsi pakhutu lakumanja la munthu amene akudziyeretsayo, pachala chake chamanthu kudzanja lamanja, ndi pachala chake chachikulu cha mwendo wakumanja pamene anamupaka magazi a nsembe yakupalamula ija. 29  Ndiyeno mafuta amene atsala pachikhatho cha wansembe aziwapaka pamutu pa munthu amene akudziyeretsayo, kuti amuphimbire machimo ake pamaso pa Yehova. 30  Kenako wansembe azipereka mmodzi mwa ana a njiwa kapena mmodzi mwa ana a nkhunda, mogwirizana ndi zimene munthuyo angakwanitse.+ 31  Mbalame imodzi ikhale nsembe yamachimo ndipo inayo ikhale nsembe yopsereza,+ azipereka imene angakwanitse pamodzi ndi nsembe yambewu. Ndipo wansembe aziphimba machimo a munthu amene akudziyeretsayo pamaso pa Yehova.+ 32  Limeneli ndi lamulo lokhudza munthu amene ali ndi nthenda ya khate, amene sangakwanitse kupeza zinthu zimene zimafunika pa tsiku la kuyeretsedwa kwake.” 33  Ndiyeno Yehova anauza Mose ndi Aroni kuti: 34  “Mukakafika mʼdziko la Kanani,+ limene ine ndikukupatsani kuti likhale lanu,+ ndipo ndikadzalola nthenda ya khate kuti ikhale mʼnyumba ina mʼdziko lanulo,+ 35  mwiniwake wa nyumbayo azibwera kwa wansembe nʼkumuuza kuti, ‘Ndaona chinachake chooneka ngati nthenda ya khate mʼnyumba mwanga.’ 36  Wansembe adzalamula kuti atulutse katundu mʼnyumbamo iye asanafike kudzaona nthendayo. Adzachite zimenezi kuti wansembe asadzagamule kuti chilichonse mʼnyumbamo nʼchodetsedwa. Kenako wansembe adzabwere kudzaona nyumbayo. 37  Akaona nthendayo nʼkupeza kuti ili mʼmakoma a nyumba, ndipo ikuoneka ngati mawanga obiriwira mopitira ku chikasu kapena ofiirira, komanso mawangawo akuoneka kuti alowa mkati mwa khoma, 38  wansembe azituluka mʼnyumbamo nʼkukaima pakhomo, ndipo azitseka nyumbayo masiku 7.+ 39  Kenako pa tsiku la 7, wansembe azibweranso kudzaona nyumbayo. Ngati nthendayo yafalikira mʼmakoma ake, 40  wansembe azilamula kuti achotse miyala imene ili ndi nthendayo, nʼkukaiponya kunja kwa mzinda, kumalo odetsedwa. 41  Ndiyeno wansembe alamule kuti apale mkati mwa nyumba yonseyo, nʼkukataya zimene apalazo kunja kwa mzinda, kumalo odetsedwa. 42  Akatero azitenga miyala ina nʼkumanga pamene panali miyala yakaleyo. Kenako aziwalamula kuti apange pulasitala nyumbayo ndi dothi lina. 43  Koma ngati nthendayo yabwerera nʼkufalikiranso mʼnyumbamo, atachotsa miyala ija, kupala nyumbayo nʼkuipanganso pulasitala, 44  wansembe azibweranso kudzaiona. Ngati nthendayo yafalikira mʼnyumbamo, limenelo ndi khate loopsa.+ Nyumbayo ndi yodetsedwa. 45  Kenako azilamula kuti nyumbayo aigwetse pamodzi ndi miyala yake, matabwa ake ndi dothi lake lonse lomangira, ndipo zonsezi azitengere kunja kwa mzinda, kumalo odetsedwa.+ 46  Koma aliyense wolowa mʼnyumbayo pa masiku amene wansembe walamula kuti munthu asalowemo,+ azikhala wodetsedwa mpaka madzulo.+ 47  Aliyense amene wagona mʼnyumbamo ndiponso aliyense amene wadyeramo chakudya azichapa zovala zake. 48  Koma ngati wansembe wabwera kudzaona nyumbayo ataipanganso pulasitala nʼkupeza kuti nthendayo sinafalikire mʼnyumbayo, wansembe azigamula kuti nyumbayo ndi yoyera chifukwa nthendayo yatha. 49  Ndiyeno kuti ayeretse nyumbayo, azitenga mbalame ziwiri, nthambi ya mtengo wa mkungudza, ulusi wofiira kwambiri ndi kamtengo ka hisope.+ 50  Wansembe azipha mbalame imodzi pamwamba pa madzi akumtsinje, amene ali mʼchiwiya chadothi. 51  Kenako azitenga nthambi ya mtengo wa mkungudza, kamtengo ka hisope, ulusi wofiira kwambiri ndi mbalame yamoyo ija. Zimenezi aziziviika mʼmagazi a mbalame imene yaphedwa pamwamba pa madzi otunga kumtsinje ija, ndipo azidontheza magaziwo maulendo 7+ cha kumene kuli nyumbayo. 52  Ndiyeno aziyeretsa nyumbayo pogwiritsa ntchito magazi a mbalame ija, madzi otunga kumtsinje, mbalame yamoyo ija, nthambi ya mtengo wa mkungudza, kamtengo ka hisope ndi ulusi wofiira kwambiri. 53  Kenako aziulutsa mbalame yamoyo ija pabwalo, kunja kwa mzinda. Akatero aziyeretsa nyumbayo, ndipo idzakhala yoyera. 54  Limeneli ndi lamulo lokhudza nthenda iliyonse ya khate, nthenda yapamutu kapena pandevu,+ 55  khate lapachovala+ kapena lamʼnyumba,+ 56  zotupa, nkhanambo* ndi zikanga.+ 57  Lamulo limeneli laperekedwa kuti akhale malangizo othandiza kudziwa ngati chinthu chili chodetsedwa kapena choyera.+ Limeneli ndi lamulo lokhudza nthenda ya khate.”+

Mawu a M'munsi

“Magawo atatu mwa magawo 10 a muyezo wa efa” ndi ofanana ndi malita 6.6. Onani Zakumapeto B14.
“Muyezo umodzi” umenewu ndi wofanana ndi malita 0.31. Onani Zakumapeto B14.
Gawo limodzi mwa magawo 10 a muyezo wa efa ndi lofanana ndi malita 2.2. Onani Zakumapeto B14.
Amenewa ndi matenda amene amachititsa kuti khungu liume nʼkumakanganuka ngati mmene zimakhalira bala likamapola.