Levitiko 12:1-8
-
Kudziyeretsa pambuyo pobereka mwana (1-8)
12 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti:
2 “Uza Aisiraeli kuti, ‘Mkazi akakhala woyembekezera nʼkubereka mwana wamwamuna, azikhala wodetsedwa kwa masiku 7. Azikhala wodetsedwa ngati mmene amakhalira pa nthawi imene akusamba.+
3 Pa tsiku la 8, mwanayo azidulidwa.+
4 Mkaziyo azipitiriza kudziyeretsa ku magazi ake kwa masiku enanso 33. Asamakhudze chilichonse chopatulika komanso asamalowe mʼmalo oyera mpaka atakwanitsa masiku a kuyeretsedwa kwake.
5 Akabereka mwana wamkazi, azikhala wodetsedwa kwa masiku 14 ngati mmene amakhalira pa nthawi imene akusamba. Mkaziyo azipitiriza kudziyeretsa ku magazi ake kwa masiku enanso 66.
6 Masiku a kuyeretsedwa kwake chifukwa chobereka mwana wamwamuna kapena wamkazi akakwana, azibweretsa kwa wansembe, pakhomo la chihema chokumanako, nkhosa yaingʼono yamphongo yosapitirira chaka chimodzi kuti ikhale nsembe yopsereza.+ Azibweretsanso mwana wa nkhunda kapena njiwa kuti ikhale nsembe yamachimo.
7 Wansembeyo aziipereka kwa Yehova ndi kumʼphimbira machimo ndipo mkaziyo adzakhala woyera pa kukha magazi kwake. Limeneli ndi lamulo lokhudza mkazi amene wabereka mwana wamwamuna kapena wamkazi.
8 Koma ngati sangakwanitse kupeza nkhosa, azipereka njiwa ziwiri kapena ana awiri a nkhunda.+ Mbalame imodzi izikhala ya nsembe yopsereza, inayo izikhala ya nsembe yamachimo. Akatero wansembe adzamuphimbira machimo ndipo mkaziyo adzakhala woyera.’”