Levitiko 16:1-34

  • Tsiku la Mwambo Wophimba Machimo (1-34)

16  Yehova analankhula ndi Mose pambuyo pa imfa ya ana awiri a Aroni, amene anafa chifukwa choonekera pamaso pa Yehova mosavomerezeka.+ 2  Yehova anauza Mose kuti: “Uza Aroni mʼbale wako kuti asamalowe mʼmalo oyera+ kuseri kwa katani,+ patsogolo pa chivundikiro cha Likasa, pa nthawi iliyonse imene wafuna, kuopera kuti angafe+ chifukwa ine ndidzaonekera mumtambo+ pamwamba pa chivundikirocho.+ 3  Polowa mʼmalo oyera, Aroni azitenga zotsatirazi: ngʼombe yaingʼono yamphongo kuti ikhale nsembe yamachimo+ ndi nkhosa yamphongo kuti ikhale nsembe yopsereza.+ 4  Azivala mkanjo wopatulika wansalu,+ kabudula wansalu+ wobisa* thupi lake, azimanga lamba wansalu wapamimba,+ ndipo azikulunga kumutu kwake ndi nduwira yansalu.+ Zimenezi ndi zovala zopatulika.+ Iye azivala zimenezi atasamba thupi lonse.+ 5  Gulu la Aisiraeli lizimupatsa+ ana a mbuzi amphongo awiri kuti akhale nsembe yamachimo ndiponso nkhosa yamphongo imodzi kuti ikhale nsembe yopsereza. 6  Akatero Aroni azibweretsa ngʼombe yamphongo ya nsembe yake yamachimo, ndipo aziphimba machimo ake+ ndi a banja lake.* 7  Kenako azitenga mbuzi ziwiri zija nʼkuziimika pamaso pa Yehova, pakhomo la chihema chokumanako. 8  Ndiyeno Aroni azichita maere pa mbuzi ziwirizo. Maere amodzi akhale a Yehova, ndipo ena akhale a mbuzi yotenga machimo a anthu.* 9  Aroni azibweretsa mbuzi imene maere asonyeza+ kuti ndi ya Yehova, ndipo izikhala nsembe yamachimo. 10  Koma mbuzi imene maere asonyeza kuti ndi yotenga machimo a anthu, aziibweretsa yamoyo nʼkuiimika pamaso pa Yehova kuti machimo a anthu aphimbidwe. Akatero aziitumiza mʼchipululu monga mbuzi yotenga machimo a anthu.+ 11  Aroni azibweretsa ngʼombe yamphongo ya nsembe yake yamachimo, ndipo aziphimba machimo ake ndi a banja lake. Pambuyo pake azipha ngʼombe ya nsembe yake yamachimoyo.+ 12  Kenako iye azitenga chofukizira+ chodzaza ndi makala amoto ochokera paguwa lansembe+ limene lili pamaso pa Yehova. Azitenganso zofukiza zonunkhira zabwino kwambiri+ zokwana manja awiri odzaza nʼkulowa nazo kuchipinda, kuseri kwa katani.+ 13  Akatero aziika zofukizazo pamoto umene uli pamaso pa Yehova,+ ndipo utsi wa zofukizazo uziphimba chivundikiro cha Likasa+ chimene chili pamwamba pa Umboni+ kuti asafe. 14  Ndiyeno azitenga ena mwa magazi a ngʼombe yamphongoyo+ nʼkuwadontheza ndi chala chake patsogolo pa chivundikiro, mbali ya kumʼmawa. Azidontheza magaziwo ndi chala chake maulendo 7 patsogolo pa chivundikirocho.+ 15  Kenako azipha mbuzi ya nsembe yamachimo yoperekera anthuwo,+ nʼkulowa ndi magazi ake kuchipinda, kuseri kwa katani.+ Kumeneko magaziwo+ azichita nawo zimene anachita ndi magazi a ngʼombe yamphongo ija. Azidontheza magaziwo patsogolo pa chivundikiro. 16  Aziphimba machimo a malo oyera chifukwa cha zinthu zodetsa zimene Aisiraeli achita komanso chifukwa cha zolakwa ndi machimo awo.+ Azichita zimenezi ndi chihema chokumanako chimene chili pakati pa Aisiraeli, amene amachita zinthu zodetsa. 17  Mʼchihema chokumanako musamapezeke munthu wina aliyense kuyambira nthawi imene Aroni walowa mʼmalo oyera kukaphimba machimo mpaka kutulukamo. Ndipo aziphimba machimo ake, a banja lake+ ndi a mpingo wonse wa Isiraeli.+ 18  Akatero azituluka nʼkupita kuguwa lansembe+ limene lili pamaso pa Yehova kuti akaliphimbire machimo. Ndiyeno azitenga ena mwa magazi a ngʼombe yamphongo ndi a mbuzi nʼkuwapaka panyanga zonse za guwa lansembe. 19  Ena mwa magaziwo aziwadonthezera paguwalo ndi chala chake maulendo 7, kuti likhale lopatulika komanso kuti aliyeretse ku zinthu zodetsa za Aisiraeli. 20  Akamaliza kuphimbira machimo+ malo oyera, chihema chokumanako ndi guwa lansembe,+ azibweretsanso mbuzi yamoyo ija.+ 21  Ndipo Aroni aziika manja ake onse pamutu pa mbuziyo ndi kuvomereza zolakwa zonse za Aisiraeli ndiponso machimo awo onse. Zonsezi aziziika pamutu pa mbuzi+ ija nʼkuipereka kwa munthu amene amusankhiratu kuti akaisiye kuchipululu. 22  Mbuziyo izinyamula zolakwa zawo zonse+ pamutu pake ndipo aziitumiza kuchipululu.+ 23  Kenako Aroni azilowa mʼchihema chokumanako nʼkuvula zovala zake zimene anavala polowa mʼmalo oyera, ndipo azizisiya momwemo. 24  Akatero azisamba thupi lonse+ mʼmalo oyera nʼkuvala zovala zake.+ Kenako azituluka nʼkukapereka nsembe yake yopsereza+ ndi nsembe yopsereza ya anthuwo+ ndipo aziphimba machimo ake ndi a anthuwo.+ 25  Ndiyeno aziwotcha mafuta a nsembe yamachimo paguwa lansembe. 26  Munthu amene anapititsa mbuzi yotenga machimo a anthu+ uja azichapa zovala zake nʼkusamba thupi lonse. Akatero angathe kulowa mumsasa. 27  Ngʼombe yamphongo ya nsembe yamachimo ndi mbuzi ya nsembe yamachimo, zimene magazi ake analowa nawo mʼmalo oyera pokaphimba machimo, azipita nazo kunja kwa msasa ndipo aziwotcha pamoto zikopa zake, nyama ndi ndowe zake.+ 28  Munthu amene wawotcha zimenezi azichapa zovala zake nʼkusamba thupi lonse, akatero angathe kulowa mumsasa. 29  Mʼmwezi wa 7, pa tsiku la 10 la mweziwo, muzisonyeza kuti mukudzimvera chisoni* chifukwa cha machimo anu ndipo aliyense wa inu asamagwire ntchito ina iliyonse,+ kaya ndi nzika kapena mlendo wokhala pakati panu. Limeneli likhale lamulo kwa inu mpaka kalekale. 30  Pa tsiku limeneli machimo anu adzaphimbidwa+ kuti muyesedwe oyera. Mudzakhala oyeretsedwa ku machimo anu onse pamaso pa Yehova.+ 31  Limeneli ndi sabata lanu lopuma pa ntchito zonse ndipo muzisonyeza kuti mukudzimvera chisoni chifukwa cha machimo anu.+ Limeneli ndi lamulo mpaka kalekale. 32  Wansembe amene adzadzozedwe+ nʼkuikidwa* kuti atumikire monga wansembe,+ kulowa mʼmalo mwa bambo ake,+ aziphimba machimo ndipo azivala zovala za nsalu,+ zomwe ndi zovala zopatulika.+ 33  Iye aziphimba machimo a malo opatulika koposa,+ chihema chokumanako+ ndi guwa lansembe.+ Aziphimbanso machimo a ansembe ndi a mpingo wonse wa anthu.+ 34  Limeneli likhale lamulo kwa inu mpaka kalekale,+ kuti machimo onse a Aisiraeli aziphimbidwa kamodzi pa chaka.”+ Choncho iye anachita mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “zovala zamʼkati zobisa.”
Kapena kuti, “a fuko lake.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbuzi ya Azazeli.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Ankasonyeza chisoni chimenechi posala kudya ndiponso kudzimana zinthu zina.
Mʼchilankhulo choyambirira, “amene dzanja lake lidzadzazidwe.”