1 Mafumu 7:1-51

  • Nyumba yachifumu ya Solomo (1-12)

  • Hiramu waluso anathandiza Solomo (13-47)

    • Zipilala ziwiri zakopa (15-22)

    • Thanki yosungira madzi (23-26)

    • Zotengera 10 zakopa (27-39)

  • Anamaliza kupanga zinthu zagolide (48-51)

7  Panatenga zaka 13 kuti Solomo amange nyumba* yake+ nʼkuimaliza.+  Kenako anamanga nyumba yotchedwa Nkhalango ya Lebanoni.+ Nyumbayi inali mikono* 100 mulitali, mikono 50 mulifupi ndiponso mikono 30 kupita mʼmwamba. Anaimanga pamwamba pa nsanamira za mtengo wa mkungudza.+ Nsanamirazo zinali mʼmizere 4 ndipo pamwamba pake anaikapo mitengo ya mkungudza.  Nyumbayi anaikuta ndi matabwa a mkungudza kuyambira pazitsulo zimene zinali pamwamba pa nsanamira. Zinalipo 45 ndipo pamzere uliwonse panali 15.  Nyumbayi inali yosanja kawiri. Nsanjika iliyonse inali ndi mzere wa mawindo. Choncho nyumba yonseyo inali ndi mizere itatu ya mawindo okhala ndi mafelemu. Mawindo a mbali ina anayangʼanizana ndi mawindo a mbali inanso ya nyumbayo.  Makomo komanso mafelemu a nyumbayo anali ofanana mbali zonse 4 ndipo ndi mmene zinalilinso ndi mawindo onse amʼmizere itatu ya nyumbayo.  Kenako anamanga Khonde la Zipilala. Mulitali mwake linali mikono 50 ndipo mulifupi linali mikono 30. Kutsogolo kwa khondelo kunalinso kakhonde kena kokhala ndi zipilala ndi denga.  Anamanganso Bwalo la Mpando Wachifumu,+ kumene ankaweruzira milandu. Bwaloli linkatchedwa Bwalo Loweruzira Milandu.+ Makoma ake anawakuta ndi matabwa a mkungudza kuyambira pansi mpaka kudenga.  Kenako Solomo anamanga nyumba* yake yokhalamo chapatali ndi nyumba ya Bwalo la Mpando Wachifumu.+ Kamangidwe ka nyumbayi kanali kofanana ndi ka nyumba ya Bwalo la Mpando Wachifumu. Solomo anamanganso nyumba ina yofanana ndi Bwaloli ndipo anamangira mwana wamkazi wa Farao amene iye anamʼkwatira.+  Nyumba zonsezi, kuyambira pamaziko ake mpaka pamwamba pa khoma, ndiponso kuchokera panja pa nyumbazo mpaka kubwalo lalikulu,+ zinamangidwa ndi miyala yokwera mtengo+ yochita kuyeza ndiponso yocheka ndi macheka a miyala, mkati ndi kunja komwe. 10  Maziko ake anawamanga ndi miyala ikuluikulu yokwera mtengo ndipo miyala ina inali yaikulu mikono 10, ina mikono 8. 11  Pamwamba pa miyala ya mazikoyo panalinso miyala ina yokwera mtengo yochita kuyeza ndiponso yosema. Panalinso matabwa a mkungudza. 12  Bwalo lalikulu linazunguliridwa ndi khoma la miyala yosema lotalika mizere itatu kuchokera pansi ndi mzere umodzi wa matabwa a mkungudza pamwamba pake. Ndi mmenenso zinalili ndi bwalo lamkati+ la nyumba ya Yehova komanso khonde la nyumbayo.+ 13  Mfumu Solomo anatuma anthu kuti akatenge Hiramu+ ku Turo. 14  Mayi ake anali mkazi wamasiye wa fuko la Nafitali. Bambo ake anali a ku Turo odziwa kupanga zinthu zakopa.*+ Hiramu anali waluso, womvetsa zinthu+ ndiponso wodziwa bwino ntchito yopanga zinthu zakopa. Iye anabwera kwa Mfumu Solomo ndipo anamugwirira ntchito yake yonse. 15  Anaumba zipilala ziwiri zakopa.+ Chipilala chilichonse chinali chachitali mikono 18, ndipo kuzungulira chipilala chilichonse inali mikono 12.+ 16  Anapanga mitu iwiri yakopa nʼkuiika pamwamba pa zipilalazo. Mutu umodzi unali wautali mikono 5, ndipo mutu winawo unalinso wautali mikono 5. 17  Pamutu wa chipilala chilichonse anaikapo maukonde opangidwa ndi matcheni opotanapotana.+ Pamutu wina anaikapo ukonde wopangidwa ndi matcheni 7 ndipo pamutu winawo anaikaponso ukonde wopangidwa ndi matcheni 7. 18  Kenako anapanga mizere iwiri ya makangaza* kuzungulira maukonde awiri aja, nʼkuveka mitu imene inali pamwamba pa zipilalazo. Anachita zimenezi pamitu yonse iwiri. 19  Mbali yokwana mikono 4 ya mitu imene inali pamwamba pa zipilala, pafupi ndi khonde, anaipanga ngati maluwa. 20  Mitu iwiriyo inali pamwamba pa zipilala komanso pamwamba pa malo ozungulira amene analumikizira maukonde aja. Kuzungulira mutu uliwonse, panali makangaza 200 amene anali mʼmizere.+ 21  Ndiyeno Hiramu anaika zipilala zija pakhonde la kachisi.*+ Chipilala chimodzi anachiika mbali yakumanja* nʼkuchipatsa dzina lakuti Yakini.* Chipilala china anachiika mbali yakumanzere* nʼkuchipatsa dzina lakuti Boazi.*+ 22  Pamwamba pa chipilala chilichonse panali pooneka ngati maluwa. Choncho, anamaliza ntchito yopanga zipilalazo. 23  Kenako iye anapanga thanki yosungira madzi.*+ Thankiyo inali yozungulira ndipo inali mikono 10 kuchokera mbali ina kufika ina, kuyeza modutsa pakati. Thankiyo inali yaitali mikono 5 ndipo kuzungulira thanki yonseyo inali mikono 30.+ 24  Kuzungulira mʼkhosi mwake monse munali zokongoletsera zooneka ngati zipanda.+ Pamalo alionse otalika mkono umodzi ankaikapo zokongoletsera 10. Zokongoletsera zooneka ngati zipandazo zinalipo mizere iwiri, ndipo anaziumbira kumodzi ndi thankiyo. 25  Thankiyo anaikhazika pangʼombe zamphongo 12.+ Ngʼombe zitatu zinayangʼana kumpoto, zitatu zinayangʼana kumadzulo, zitatu zinayangʼana kumʼmwera ndipo zitatu zinayangʼana kumʼmawa. Thankiyo inali pamwamba pa ngʼombezo ndipo mbuyo zonse za ngʼombezo zinaloza pakati. 26  Kuchindikala kwa thankiyo kunali chikhatho* chimodzi. Milomo yake inali ngati kukamwa kwa mphika kapena ngati maluwa. Muthankiyo munkalowa madzi okwana mitsuko* 2,000. 27  Kenako anapanga zotengera 10+ zakopa zokhala ndi mawilo. Chotengera chilichonse chinali mikono 4 mulitali, mikono 4 mulifupi komanso mikono itatu kupita mʼmwamba. 28  Zotengerazo anazipanga chonchi: Mʼmbali mwake zinali zamalata ndipo malatawo anali pakati pa zitsulo zopingasana. 29  Pamalata amene anali pakati pa zitsulo zopingasana anajambulapo mikango,+ ngʼombe zamphongo ndiponso akerubi.+ Pazitsulo zopingasana anajambulaponso zinthu zimenezi. Pamwamba ndi pansi pa mikango ndi ngʼombe zamphongozo, anajambulapo nkhata zamaluwa. 30  Chotengera chilichonse chinali ndi mawilo 4 akopa ndiponso mapaipi akopa olumikiza mawilo. Mʼmakona 4 a chotengeracho munali zogwiriziza mawilo ndi mapaipiwo. Pansi pa beseni panalinso zogwiriziza ndipo anazipangira kumodzi ndi nkhata zamaluwa pafupi ndi chogwiriziza chilichonse. 31  Besenilo linali mkati mwa mbali yapamwamba ya chotengeracho ndipo kuchoka pansi kufika mumkombero linali mkono umodzi. Pakamwa pake panali pozungulira ndipo tikaphatikiza ndi mkomberowo, beseni lonse linali lalitali mkono umodzi ndi hafu. Mʼmbali mwa pakamwa pake anajambulamo zokongoletsera mochita kugoba. Malata amʼmbali mwake anali a mbali 4 zofanana, osati ozungulira. 32  Pansi pa malata a mʼmbaliwo panali mawilo 4. Zogwiriziza za mawilowo anazilumikiza ku chotengeracho ndipo wilo lililonse linali lalitali mkono umodzi ndi hafu. 33  Mawilowo anawapanga ngati mawilo a galeta. Zogwiriziza zake, malimu ake,* masipoko ake ndiponso mahabu ake, zonse zinali zakopa. 34  Chotengera chilichonse chinali ndi makona 4, ndipo pakona iliyonse panali chogwiriziza. Zogwirizizazo anaziumbira kumodzi ndi chotengeracho. 35  Pamwamba pa chotengeracho panali chokhazikapo beseni chozungulira. Chinali chachitali hafu ya mkono. Chokhazikapo besenicho chinali chozungulira, ndipo kutalika kwake kunali hafu ya mkono kuchokera pansi kufika pamwamba. Timafelemu take komanso malata ake amʼmbali anazipangira kumodzi ndi chotengeracho. 36  Patimafelemuto ndiponso pamalata amʼmbaliwo anajambulapo mochita kugoba akerubi, mikango komanso mitengo ya kanjedza mogwirizana ndi kukula kwa malo ake. Anajambulanso nkhata zamaluwa kuzungulira chokhazikapo besenicho.+ 37  Umu ndi mmene anapangira zotengera 10 zonsezo.+ Zinali zofanana kaumbidwe kake,+ kukula kwake ndiponso maonekedwe ake. 38  Kenako anapanga mabeseni 10 akopa.+ Mʼbeseni lililonse munkalowa madzi okwana mitsuko 40, ndipo linali mikono 4 kuchokera mbali ina kufika mbali ina. Pa zotengera 10 zija, chilichonse chinali ndi beseni lake. 39  Anaika zotengera 5 mbali yakumanja kwa nyumbayo komanso zotengera 5 mbali yakumanzere. Thanki ija anaiika kumanja kwa nyumbayo, kumʼmwera chakumʼmawa.+ 40  Hiramu+ anapanganso mabeseni, mafosholo+ ndi mbale zolowa.+ Choncho iye anamaliza ntchito yonse imene ankagwirira Mfumu Solomo yopanga zinthu zotsatirazi panyumba ya Yehova:+ 41  zipilala ziwiri,+ mitu ya zipilala yooneka ngati mbale zolowa imene anaiika pamwamba pa zipilala ziwirizo ndi maukonde awiri+ okutira mitu iwiri imene inali pamwamba pa zipilalazo. 42  Anapanganso makangaza 400+ oika pamaukonde awiri aja ndipo panali mizere iwiri ya makangaza pa ukonde uliwonse. Makangazawo anali okutira mitu iwiri yooneka ngati mbale zolowa imene inali pazipilala ziwiri zija. 43  Anapanganso zotengera 10,+ mabeseni 10+ oika pazotengerazo, 44  thanki+ imodzi, ngʼombe zamphongo 12 zokhala pansi pa thankiyo, 45  ndowa, mafosholo, mbale zolowa ndi ziwiya zina zonse. Hiramu anapanga zinthu zimenezi ndi kopa wonyezimira kuti Mfumu Solomo aziike mʼnyumba ya Yehova. 46  Mfumuyo inaumba zinthu zimenezi mʼzikombole zadongo mʼchigawo cha Yorodano, pakati pa Sukoti ndi Zeretani. 47  Solomo sanayeze kulemera kwa ziwiya zonse chifukwa zinali zambiri. Kopayo sanadziwike kulemera kwake.+ 48  Solomo anapanga zinthu zonse zapanyumba ya Yehova. Anapanga guwa lansembe+ lagolide komanso tebulo yagolide+ yoikapo mkate wachionetsero. 49  Anapanganso zoikapo nyale+ zagolide woyenga bwino ndipo anaziika pafupi ndi chipinda chamkati, anaika 5 kumanja, 5 kumanzere. Ndiponso anapanga maluwa agolide,+ nyale zagolide, zopanira zagolide zozimitsira nyale,+ 50  mabeseni, zozimitsira nyale,+ mbale zolowa, makapu+ ndiponso zopalira moto.+ Zonsezi zinali zagolide woyenga bwino. Anapanganso molowa miyendo ya zitseko za chipinda chamkati,+ kutanthauza Malo Oyera Koposa ndiponso molowa miyendo ya zitseko za nyumbayo.+ Zonsezi zinali zagolide. 51  Choncho Mfumu Solomo anamaliza ntchito yonse yokhudza nyumba ya Yehova imene anayenera kugwira. Kenako Solomo anabweretsa zinthu zimene bambo ake Davide anaziyeretsa.+ Anatenga siliva, golide ndiponso zinthu zina nʼkuziika mosungira chuma chapanyumba ya Yehova.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “nyumba yachifumu.”
Mkono umodzi ndi wofanana ndi masentimita 44 ndi hafu. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “nyumba yachifumu.”
Kapena kuti, “zamkuwa.”
“Makangaza” ndi mtundu wa chipatso. Ena amati chimanga chachizungu.
Apa akunena za Malo Oyera.
Nʼkutheka kuti dzinali likutanthauza “Mu Mphamvu.”
Kapena kuti, “yakumpoto.”
Kutanthauza “Iye [Yehova] Akhazikitse.”
Kapena kuti, “yakumʼmwera.”
Kapena kuti, “anapanga nyanja yachitsulo chosungunula.”
Pafupifupi masentimita 7.4. Onani Zakumapeto B14.
Mtsuko umodzi unkakwana malita 22. Onani Zakumapeto B14.
Kapena kuti, “zingelengele zake.”