Ekisodo 3:1-22

  • Mose komanso chitsamba chaminga choyaka moto (1-12)

  • Yehova anafotokoza za dzina lake (13-15)

  • Yehova anapatsa Mose malangizo (16-22)

3  Mose anakhala mʼbusa wa ziweto za Yetero*+ apongozi ake, wansembe wa ku Midiyani. Pamene ankaweta ziwetozo chakumadzulo kwa chipululu, anafika kuphiri la Mulungu woona, ku Horebe.+  Kenako mngelo wa Yehova anaonekera kwa iye pakati pa chitsamba chaminga+ chimene chinkayaka moto. Atachiyangʼanitsitsa, anaona kuti chitsamba chamingacho chikuyaka, koma sichikunyeka.  Choncho Mose anati: “Ndipite kuti ndikaonetsetse zodabwitsa zimenezi. Ndikaone chifukwa chake chitsamba chamingachi chikuyaka koma osanyeka.”  Yehova ataona kuti Mose wapita kuti akaonetsetse, Mulungu anamuitana kuchokera pachitsamba chamingacho kuti: “Mose! Mose!” ndipo iye anayankha kuti: “Ine mbuyanga.”  Ndiyeno Mulungu anati: “Usayandikire kuno. Vula nsapato zako chifukwa malo waimawo ndi malo oyera.”  Iye ananenanso kuti: “Ndine Mulungu wa makolo* ako, Mulungu wa Abulahamu,+ Mulungu wa Isaki+ ndi Mulungu wa Yakobo.”+ Atatero Mose anaphimba nkhope yake chifukwa ankaopa kuyangʼana Mulungu woona.  Yehova anawonjezera kuti: “Ndaona mmene anthu anga amene ali ku Iguputo akuvutikira, ndipo ndamva kulira kwawo chifukwa cha amene akuwagwiritsa ntchito mwankhanza. Ndikudziwa bwino ululu umene akumva.+  Choncho ndipita kuti ndikawapulumutse mʼmanja mwa Aiguputo+ ndi kuwatulutsa mʼdzikolo nʼkuwalowetsa mʼdziko labwino komanso lalikulu, dziko loyenda mkaka ndi uchi.+ Ndiwalowetsa mʼdziko la Akanani, Ahiti, Aamori, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi.+  Taona, ndamva kulira kwa Aisiraeli komanso ndaona nkhanza zimene Aiguputo akuwachitira powapondereza.+ 10  Tsopano tamvera, ndikutuma kwa Farao kuti ukatulutse anthu anga Aisiraeli ku Iguputo.”+ 11  Koma Mose anayankha Mulungu woona kuti: “Ndine ndani ine kuti ndipite kwa Farao nʼkukatulutsa Aisiraeli ku Iguputo?” 12  Pamenepo Mulungu anati: “Ndidzakhala nawe,+ ndipo chizindikiro chosonyeza kuti ine ndi amene ndakutuma ndi ichi: Pambuyo potulutsa anthuwo mu Iguputo, anthu inu mudzatumikira* Mulungu woona paphiri lino.”+ 13  Koma Mose anafunsa Mulungu woona kuti: “Nditati ndapita kwa Aisiraeli nʼkuwauza kuti, ‘Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu,’ iwo nʼkundifunsa kuti, ‘Dzina lake ndi ndani?’+ Ndikawayankhe kuti chiyani?” 14  Mulungu anayankha Mose kuti: “Ndidzakhala Amene Ndidzafune Kukhala.”*+ Ndiyeno anawonjezera kuti: “Aisiraeli ukawauze kuti, ‘Ndidzakhala Amene Ndidzafune Kukhala ndi amene wandituma kwa inu.’”+ 15  Kenako Mulungu anauzanso Mose kuti: “Aisiraeli ukawauze kuti, ‘Yehova Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abulahamu,+ Mulungu wa Isaki+ ndi Mulungu wa Yakobo,+ wandituma kwa inu.’ Dzina langa ndi limeneli mpaka kalekale,+ ndipo mibadwo yonse izidzakumbukira dzina limeneli. 16  Ndiye pita ukasonkhanitse akulu a Isiraeli nʼkuwauza kuti, ‘Yehova Mulungu wa makolo anu, Mulungu wa Abulahamu, Isaki ndi Yakobo, anaonekera kwa ine nʼkundiuza kuti: “Ndithu, ndaona zimene zikukuchitikirani+ komanso ndaona zimene akukuchitirani ku Iguputo. 17  Choncho ndikulonjeza kuti, Ndidzakupulumutsani mʼmanja mwa Aiguputo amene akukuzunzani+ nʼkukulowetsani mʼdziko la Akanani, Ahiti, Aamori,+ Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi,+ dziko loyenda mkaka ndi uchi.”’+ 18  Iwo adzamvera ndithu mawu ako+ ndipo iweyo ndi akulu a Isiraeli mudzapite kwa mfumu ya Iguputo nʼkukaiuza kuti: ‘Yehova Mulungu wa Aheberi+ walankhula nafe. Ndiye chonde mutilole kuti tiyende ulendo wamasiku atatu kupita mʼchipululu, kuti tikapereke nsembe kwa Yehova Mulungu wathu.’+ 19  Koma ine ndikudziwa bwino kuti mfumu ya Iguputo sidzakulolani kupita, pokhapokha dzanja lamphamvu litaikakamiza kuchita zimenezi.+ 20  Choncho ndidzatambasula dzanja langa nʼkulanga Iguputo ndi ntchito zanga zonse zodabwitsa zimene ndidzachite mʼdzikolo. Ndipo ndikadzachita zimenezi, adzakulolani kuti muchoke.+ 21  Kenako ndidzachititsa kuti Aiguputo akomere mtima anthu anga, moti pochoka simudzachoka chimanjamanja.+ 22  Mkazi aliyense adzapemphe zinthu zasiliva, zagolide ndi zovala kwa munthu wokhala naye pafupi ndi kwa mkazi amene akukhala mʼnyumba mwake. Zinthu zimenezi mudzaveke ana anu aamuna ndi ana anu aakazi, ndipo mudzatenge zinthu zambiri za Aiguputo.”+

Mawu a M'munsi

Yetero amatchedwanso kuti Reueli.
Mʼchilankhulo choyambirira, “bambo.”
Kapena kuti, “mudzalambira.”
Kapena kuti, “Ndidzakhala Amene Ndidzasankhe Kukhala.” Onani Zakumapeto A4.