Ekisodo 32:1-35

  • Kulambira mwana wangʼombe wagolide (1-35)

    • Mose anamva kuimba kwa mtundu wina (17, 18)

    • Mose anaphwanya miyala imene analembapo malamulo (19)

    • Alevi anakhala okhulupirika kwa Yehova (26-29)

32  Mose ali mʼphirimo, anthu anaona kuti akuchedwa kutsika.+ Choncho anthuwo anasonkhana kwa Aroni nʼkumuuza kuti: “Tipangire mulungu woti atitsogolere,+ chifukwa sitikudziwa zimene zachitikira Mose, amene ankatitsogolera pochoka ku Iguputo.”  Ndiyeno Aroni anawauza kuti: “Tengani ndolo zagolide+ zimene avala akazi anu, ana anu aamuna ndi ana anu aakazi, ndipo mubwere nazo kwa ine.”  Choncho anthu onse anayamba kuvula ndolo zagolide zimene anavala nʼkuzipereka kwa Aroni.  Kenako iye analandira golideyo kuchokera kwa anthuwo ndipo pogwiritsa ntchito chosemera, anapanga fano* la mwana wa ngʼombe.+ Zitatero iwo anayamba kunena kuti: “Uyu ndi Mulungu wanu, Aisiraeli inu, amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo.”+  Aroni ataona zimenezi, anamanga guwa lansembe patsogolo pa fanolo. Kenako iye anafuula kuti: “Mawa kuli chikondwerero cha Yehova.”  Choncho pa tsiku lotsatira, anthuwo anadzuka mʼmamawa kwambiri nʼkuyamba kupereka nsembe zopsereza ndi zamgwirizano. Atatero, iwo anakhala pansi ndipo anadya ndi kumwa. Kenako anaimirira nʼkuyamba kusangalala.+  Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: “Pita, tsika, chifukwa anthu ako amene unawatsogolera potuluka mʼdziko la Iguputo aja achita zinthu zoipa.+  Apatuka mofulumira panjira imene ndinawalamula kuti aziyendamo.+ Iwo adzipangira fano* la mwana wa ngʼombe. Akuligwadira komanso kupereka nsembe kwa fanolo ndipo akunena kuti, ‘Aisiraeli inu, uyu ndi Mulungu wanu amene anakutsogolerani potuluka mʼdziko la Iguputo.’”  Yehova anapitiriza kuuza Mose kuti: “Ndaona kuti anthu amenewa ndi okanika.+ 10  Ndisiye kuti mkwiyo wanga uwayakire ndipo ndiwafafanize, koma iwe ndikupange kukhala mtundu waukulu.”+ 11  Kenako Mose anachonderera Yehova Mulungu wake+ kuti: “Nʼchifukwa chiyani inu Yehova mukufuna kuti mkwiyo wanu uyakire anthu anu, pambuyo powatulutsa mʼdziko la Iguputo pogwiritsa ntchito mphamvu zazikulu ndiponso dzanja lamphamvu?+ 12  Mukawawonongatu Aiguputo anena kuti, ‘Anali ndi zolinga zoipa powatulutsa mʼdziko lino. Iye amafuna kuti akawaphe kumapiri nʼkuwafafaniza padziko lapansi.’+ Bwezani mkwiyo wanu woyaka motowo, ndipo sinthani maganizo anu ofuna kubweretsera anthu anu tsoka limeneli. 13  Kumbukirani Abulahamu, Isaki ndi Isiraeli atumiki anu, amene munawalumbirira powauza kuti: ‘Ndidzachulukitsa mbadwa* zanu ngati nyenyezi zakumwamba+ ndipo dziko lonseli limene ndinalisankha, ndidzalipereka kwa mbadwa* zanu, kuti likhale lawo mpaka kalekale.’”+ 14  Choncho Yehova anasintha maganizo ake ndipo sanawononge anthu ake ngati mmene ananenera.+ 15  Kenako Mose anatembenuka nʼkutsika mʼphirimo atanyamula miyala yosema ya Umboni+ mʼmanja mwake.+ Pamiyalayo analembapo mawu mbali zonse ziwiri. Anawalemba kutsogolo ndi kumbuyo kwake. 16  Miyalayo inapangidwa ndi Mulungu, ndipo mawuwo analembedwapo ndi Mulungu mochita kugoba.+ 17  Yoswa atayamba kumva phokoso la kufuula kwa anthu, anauza Mose kuti: “Kukumveka phokoso la nkhondo kumsasa.” 18  Koma Mose anati: “Limeneli si phokoso la nyimbo ya kupambana,Komanso si phokoso la anthu amene akulira chifukwa chogonjetsedwa;Ndikumva ngati ndi kuimba kwa mtundu wina.” 19  Mose atayandikira msasawo nʼkuona mwana wa ngʼombe+ ndi anthu akuvina, mkwiyo wake unayaka ndipo anaponya pansi miyala ija nʼkuiswa ali mʼmunsi mwa phiri.+ 20  Ndiyeno anatenga mwana wa ngʼombe amene iwo anapanga nʼkumuwotcha pamoto kenako anamupera kuti akhale fumbi.+ Atatero anamwaza fumbilo pamadzi ndipo analamula Aisiraeli kuti amwe.+ 21  Kenako Mose anafunsa Aroni kuti: “Kodi anthuwa akuchitira chiyani kuti uwabweretsere tchimo lalikulu chonchi?” 22  Ndiyeno Aroni anayankha kuti: “Musakwiye mbuyanga. Inuyo mukudziwa bwino kuti anthuwa amakonda kuchita zoipa.+ 23  Choncho anandiuza kuti, ‘Tipangire mulungu woti atitsogolere, chifukwa sitikudziwa zimene zachitikira Mose, amene ankatitsogolera pochoka ku Iguputo.’+ 24  Ndiye ndinawauza kuti, ‘Aliyense amene wavala chinthu chagolide avule nʼkundipatsa.’ Kenako golideyo ndinamuponya pamoto nʼkukhala mwana wa ngʼombeyu.” 25  Mose anaona kuti anthuwo akuchita zinthu motayirira, chifukwa Aroni sanawaletse ndipo anachita zinthu zochititsa manyazi pamaso pa adani awo. 26  Ndiyeno Mose anakaima pageti la msasawo ndipo anati: “Ndani ali kumbali ya Yehova? Abwere kwa ine!”+ Ndipo Alevi onse anapita kwa Mose. 27  Kenako iye anawauza kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Aliyense wa inu amange lupanga lake mʼchiuno. Ndiyeno mudutse mkati mwa msasa kuchoka pageti lina kufika pageti lina, ndipo aliyense wa inu aphe mʼbale wake, munthu wokhala naye pafupi ndi mnzake wapamtima.’”+ 28  Alevi anachita zimene Mose anawauza. Choncho pa tsiku limenelo amuna pafupifupi 3,000 anaphedwa. 29  Zitatero Mose anati: “Dziyeretseni* kuti mutumikire Yehova lero, chifukwa aliyense wa inu waukira mwana wake ndi mʼbale wake+ ndipo lero Mulungu akudalitsani.”+ 30  Pa tsiku lotsatira, Mose anauza anthuwo kuti: “Mwachita tchimo lalikulu kwambiri. Choncho ndipita kuphiri kwa Yehova kuti mwina ndingakamuchonderere kuti akukhululukireni tchimo lanu.”+ 31  Ndiyeno Mose anabwerera kwa Yehova nʼkunena kuti: “Anthuwa achita tchimo lalikulu. Adzipangira mulungu wagolide!+ 32  Ngati mukufuna akhululukireni tchimo lawo.+ Koma ngati simukufuna, chonde ndifufuteni mʼbuku lanu limene mwalemba.”+ 33  Komabe Yehova anauza Mose kuti: “Amene wandichimwira ndi amene ndimufufute mʼbuku langa. 34  Choncho pita uwatsogolere anthuwa kumalo amene ndakuuza. Taona! Mngelo wanga akhala patsogolo panu,+ ndipo pa tsiku limene ndidzapereke chilango, ndidzawalanga chifukwa cha tchimo lawo.” 35  Ndiyeno Yehova anagwetsera anthuwo mliri chifukwa cha mwana wa ngʼombe amene iwo anamʼpanga kudzera mwa Aroni.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “fano lagolide wosungunula.”
Kapena kuti, “fano lagolide wosungunula.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Dzazani manja anu.”