Ekisodo 15:1-27

  • Mose ndi Aisiraeli anaimba nyimbo yosonyeza kupambana (1-19)

  • Miriamu anathirira mangʼombe (20, 21)

  • Madzi owawa anakhala okoma (22-27)

15  Pa nthawiyo Mose ndi Aisiraeli anaimbira Yehova nyimbo iyi:+ “Ndiimbira Yehova, chifukwa walemekezeka kwambiri.+ Mahatchi ndi okwera pamahatchiwo wawaponyera mʼnyanja.+   Mphamvu ndi nyonga zanga ndi Ya,* chifukwa wandipulumutsa.+ Ameneyu ndi Mulungu wanga ndipo ndidzamʼtamanda.+ Ndi Mulungu wa bambo anga,+ ndipo ndidzamulemekeza.+   Yehova ndi msilikali wamphamvu.+ Dzina lake ndi Yehova.+   Magaleta a Farao ndi gulu lake lankhondo wawaponyera mʼnyanja.+Asilikali odalirika a Farao amira mʼNyanja Yofiira.+   Mafunde amphamvu awakwirira. Amira pansi pa nyanja ngati mwala.+   Dzanja lanu lamanja, inu Yehova, ndi lamphamvu zochuluka.+Dzanja lanu lamanja, inu Yehova, limaphwanya mdani.   Ndi mphamvu zanu zazikulu mumagwetsa otsutsana nanu.+Mumatulutsa mkwiyo wanu woyaka moto, ndipo umanyeketsa otsutsana nanu ngati mapesi.   Ndi mpweya wotuluka mʼmphuno mwanu, madzi anaunjikana pamodzi.Madzi oyenda anaima ngati khoma.Mafunde amphamvu anaundana pakatikati pa nyanja.   Mdaniyo anati: ‘Ndiwathamangira nʼkuwapeza! Ndigawa chuma chawo mpaka nditakhutira! Ndisolola lupanga langa! Dzanja langa liwawononga!’+ 10  Mwapemerera mpweya wanu, ndipo nyanja yawamiza.+Amira mʼmadzi akuya ngati chitsulo cholemera. 11  Ndi mulungu uti amene angafanane nanu, inu Yehova?+ Mumasonyeza kuti ndinu woyera koposa,+ ndani angafanane ndi inu? Ndinu woyenera kuopedwa ndi kukuimbirani nyimbo zotamanda. Inu mumachita zodabwitsa.+ 12  Mwatambasula dzanja lanu lamanja ndipo dziko lapansi lawameza.+ 13  Munasonyeza chikondi chanu chokhulupirika potsogolera anthu amene munawawombola.+Ndi mphamvu zanu, mudzawatsogolera kudziko lanu lopatulika kumene mudzakhala. 14  Anthu adzamva+ ndipo adzanjenjemera.Anthu okhala ku Filisitiya adzamva ululu.* 15  Pa nthawi imeneyo mafumu a ku Edomu adzachita mantha.Ndipo olamulira amphamvu a ku Mowabu adzanjenjemera.+ Anthu onse okhala mu Kanani adzataya mtima.+ 16  Adzaopa ndipo adzagwidwa ndi mantha aakulu.+ Chifukwa cha dzanja lanu lamphamvu, adzakhala ngati mwala, osachita kanthu.Mpaka anthu anu atadutsa, inu Yehova,Mpaka anthu anu amene munawapanga+ atadutsa.+ 17  Mudzawabweretsa nʼkuwakhazikitsa mʼphiri limene ndi cholowa chanu.+Malo okhazikika amene mwakonzeratu kuti mukhalemo, inu Yehova.Malo opatulika amene manja anu, inu Yehova, anakhazikitsa. 18  Yehova adzalamulira monga mfumu mpaka kalekale.+ 19  Mahatchi a Farao, magaleta ake ankhondo ndi asilikali ake apamahatchi atalowa mʼnyanja,+Yehova wabweza madzi amʼnyanjamo nʼkuwamiza.+Koma Aisiraeli ayenda panthaka youma pakati pa nyanja.”+ 20  Kenako Miriamu, mneneri wamkazi, yemwe anali mchemwali wake wa Aroni, anatenga maseche mʼmanja mwake ndipo akazi ena onse ankamutsatira akuimba maseche nʼkumavina. 21  Pamene amuna ankaimba, Miriamu ankathirira mangʼombe kuti: “Imbirani Yehova chifukwa walemekezeka kwambiri.+ Mahatchi ndi okwera pamahatchiwo wawaponyera mʼnyanja.”+ 22  Kenako Mose anatsogolera Isiraeli kuchoka ku Nyanja Yofiira ndipo analowa mʼchipululu cha Shura. Iwo anayenda mʼchipululumo kwa masiku atatu, koma sanapeze madzi. 23  Iwo anafika ku Mara,+ koma sanathe kumwa madzi a ku Mara chifukwa anali owawa. Nʼchifukwa chake malowo anawapatsa dzina lakuti Mara.* 24  Choncho anthu anayamba kungʼungʼudza motsutsana ndi Mose+ kuti: “Timwa chiyani?” 25  Zitatero Mose anafuulira Yehova+ ndipo Yehova anamusonyeza kamtengo. Mose anaponya kamtengoko mʼmadzi moti madziwo anakhala okoma. Pamalo amenewo Mulungu anawapatsa lamulo ndi maziko operekera chiweruzo, ndipo kumeneko anawayesa.+ 26  Iye anawauza kuti: “Mukadzamvera ndi mtima wonse mawu a Yehova Mulungu wanu, nʼkuchita zinthu zoyenera pamaso pake ndiponso kumvera malamulo ake ndi kusunga malangizo ake onse,+ sindidzakugwetserani matenda aliwonse amene ndinagwetsera Aiguputo,+ chifukwa ine Yehova ndi amene ndikukuchiritsani.”+ 27  Kenako anafika ku Elimu kumene kunali akasupe 12 a madzi ndi mitengo 70 ya kanjedza. Choncho iwo anamanga msasa pamenepo pafupi ndi madzi.

Mawu a M'munsi

Mawu akuti “Ya” ndi chidule cha dzina lakuti Yehova.
Mʼchilankhulo choyambirira, “zowawa za pobereka.”
Kutanthauza, “Kuwawa.”