Ekisodo 34:1-35

  • Anapanganso miyala ina yosema (1-4)

  • Mose anaona ulemerero wa Yehova (5-9)

  • Mfundo zokhudza pangano zinabwerezedwa (10-28)

  • Nkhope ya Mose inkawala (29-35)

34  Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Sema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija,+ ndipo ine ndidzalemba pamiyala yosemayo mawu amene anali pamiyala yoyamba ija,+ imene iwe unaswa.+ 2  Ndipo ukonzeke kuti mawa mʼmawa ukakwere phiri la Sinai nʼkukakhala pamaso panga kumeneko pamwamba pa phirilo.+ 3  Koma usakwere mʼphirimo ndi wina aliyense, ndipo musapezeke wina aliyense mmenemo. Ngakhale nkhosa kapena ngʼombe zisadye mʼmunsi mwa phirilo.”+ 4  Choncho Mose anasema miyala iwiri yofanana ndi yoyamba ija, ndipo anadzuka mʼmamawa kwambiri nʼkukwera phiri la Sinai atanyamula miyala iwiriyo mʼmanja mwake, mogwirizana ndi zimene Yehova anamulamula. 5  Kenako Yehova anatsika+ mumtambo nʼkuima pafupi ndi Mose ndipo analengeza dzina lake lakuti Yehova.+ 6  Ndiyeno Yehova anadutsa pamaso pa Mose akulengeza kuti: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo+ ndi wokoma mtima,*+ wosakwiya msanga+ ndiponso wachikondi chokhulupirika chochuluka+ komanso choonadi.*+ 7  Amasonyeza chikondi chokhulupirika kwa mibadwo masauzande,+ amakhululuka zolakwa ndi machimo,+ koma sadzalekerera wolakwa osamʼpatsa chilango.+ Amalanga ana, zidzukulu ndi ana a zidzukuluzo chifukwa cha zolakwa za abambo awo.”+ 8  Nthawi yomweyo Mose anagwada nʼkuweramira pansi. 9  Kenako iye anati: “Tsopano ngati mwandikomera mtima, inu Yehova, chonde Yehova, muyende nafe ndipo mukhale pakati pathu,+ ngakhale kuti ndife anthu ouma khosi.+ Mutikhululukirenso zolakwa zathu ndi machimo athu,+ ndipo mutitenge kukhala chuma chanu.” 10  Poyankha Mulungu anati: “Ine ndikuchita nanu pangano ili: Ndidzachita zinthu zodabwitsa pamaso pa anthu ako onse, zimene sizinachitikepo padziko lonse lapansi kapena pakati pa mitundu yonse.+ Ndipo anthu onse okuzungulirani adzaonadi ntchito za Yehova, chifukwa ndidzakuchitirani chinthu chochititsa mantha.+ 11  Koma inu mumvere mosamala zimene ndikukulamulani lero.+ Inetu ndikuthamangitsa pamaso panu Aamori, Akanani, Ahiti, Aperezi, Ahivi ndi Ayebusi.+ 12  Samalani kuti musachite pangano ndi anthu amʼdziko limene mukupitako,+ kuopera kuti ungakhale msampha kwa inu.+ 13  Koma maguwa awo ansembe mukawagwetse, zipilala zawo zopatulika mukaziphwanye ndipo mizati* yawo yopatulika mukaidule.+ 14  Musagwadire mulungu wina,+ chifukwa Yehova amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.* Iye ndi Mulungu amene amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.*+ 15  Samalani kuti musachite pangano ndi anthu okhala mʼdzikomo, chifukwa akamachita uhule ndi milungu yawo komanso kupereka nsembe kwa milungu yawo,+ wina adzakuitanani kunyumba kwake ndipo nanunso mudzadya nsembe yakeyo.+ 16  Kenako mudzatengadi ena mwa ana awo aakazi kuti akhale akazi a ana anu aamuna.+ Ndipo ana awo aakazi adzachita uhule ndi milungu yawo nʼkuchititsa ana anu aamuna kuchita uhule ndi milungu yawo.+ 17  Musapange milungu ya chitsulo chosungunula.+ 18  Muzichita Chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa.+ Mogwirizana ndi zimene ndinakulamulani, muzidya mikate yopanda zofufumitsa masiku 7 mʼmwezi wa Abibu* pa nthawi imene inaikidwa,+ chifukwa munatuluka mu Iguputo mʼmwezi wa Abibu. 19  Mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa* ndi wanga,+ kuphatikizapo mwana woyamba kubadwa wa ziweto zanu zonse, kaya ndi mwana woyamba kubadwa wa ngʼombe kapena nkhosa.+ 20  Mwana woyamba kubadwa wa bulu muzimuwombola ndi nkhosa. Koma ngati simungamuwombole, muzimuthyola khosi. Ndipo muziwombola mwana wanu wamwamuna aliyense woyamba kubadwa.+ Palibe amene ayenera kuonekera kwa ine chimanjamanja. 21  Muzigwira ntchito zanu kwa masiku 6, koma pa tsiku la 7 muzipuma.*+ Ngakhale pa nthawi yolima ndi yokolola muzipuma. 22  Muzichita Chikondwerero cha Masabata,* ndipo pochita chikondwerero chimenechi muzipereka tirigu woyamba kucha pa tirigu amene mwakolola. Kumapeto kwa chaka muzichita Chikondwerero cha Zokolola.*+ 23  Katatu pa chaka, mwamuna aliyense pakati panu azikaonekera pamaso pa Ambuye woona, Yehova, Mulungu wa Isiraeli.+ 24  Mitundu ya anthu ndidzaithamangitsira kutali ndi inu,+ ndipo ndidzakulitsa dera lanu. Palibe aliyense amene adzasirire dziko lanu mukapita kukaona nkhope ya Yehova Mulungu wanu katatu pa chaka. 25  Mukamapereka magazi a nsembe yanga musawapereke limodzi ndi chilichonse chokhala ndi zofufumitsa.+ Musamasunge nsembe ya chikondwerero cha Pasika mpaka mʼmawa.+ 26  Zipatso zoyamba kucha zabwino kwambiri zamʼmunda mwanu muzibwera nazo kunyumba ya Yehova Mulungu wanu.+ Musamawiritse mwana wa mbuzi mumkaka wa mayi ake.”+ 27  Yehova anapitiriza kuuza Mose kuti: “Ulembe mawuwa+ chifukwa ine ndikuchita pangano ndi iwe komanso Isiraeli mogwirizana ndi mawu amenewa.”+ 28  Choncho Mose anakhalabe mʼphirimo ndi Yehova masiku 40, masana ndi usiku. Iye sanadye mkate kapena kumwa madzi.+ Ndipo Mulungu analemba mawu a pangano, Malamulo Khumi,* pamiyala yosemayo.+ 29  Ndiyeno Mose anatsika mʼphiri la Sinai atanyamula miyala iwiri ya Umboni ija mʼmanja mwake.+ Pamene ankatsika mʼphirimo, Mose sankadziwa kuti nkhope yake ikuwala chifukwa choti amalankhula ndi Mulungu. 30  Aroni ndi Aisiraeli onse ataona Mose, anaona kuti nkhope yake ikuwala ndipo anaopa kumuyandikira.+ 31  Koma Mose anawaitana. Choncho Aroni ndi atsogoleri onse a gulu la Isiraeli anapita kwa iye, ndipo Mose analankhula nawo. 32  Kenako Aisiraeli onse anamuyandikira, ndipo iye anawapatsa malamulo onse amene Yehova anamupatsa mʼphiri la Sinai.+ 33  Mose akamaliza kulankhula nawo ankaika chophimba pankhope yake.+ 34  Koma Mose akamalowa mʼchihema chokumanako kukaonekera kwa Yehova kuti akalankhule naye, ankachotsa chophimbacho mpaka atatulukamo.+ Kenako ankapita kwa Aisiraeli nʼkuwauza zimene walamulidwa.+ 35  Ndipo Aisiraeli anaona kuti nkhope ya Mose ikuwala. Choncho Mose anaphimbanso nkhope yake mpaka atabwerera kukalankhula ndi Mulungu.+

Mawu a M'munsi

^ Kapena kuti, “wokhulupirika.”
^ Kapena kuti, “wachisomo.”
^ Kapena kuti, “Yehova, dzina lake ndi amafuna kuti anthu azidzipereka kwa iye yekha.”
^ Kapena kuti, “amene salekerera opikisana naye.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “aliyense wotsegula mimba ya mayi ake.”
^ Kapena kuti, “muzisunga sabata.”
^ Kapena kuti, “Mawiki.”
^ Chimadziwikanso kuti Chikondwerero cha Misasa (Mahema).
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “Mawu Khumi.”