Ekisodo 11:1-10
11 Choncho Yehova anauza Mose kuti: “Patsala mliri umodzi wokha woti ndigwetsere Farao ndi Iguputo. Kenako adzakulolani kuchoka mʼdziko lino.+ Pokuuzani kuti muchoke, adzachita kukuthamangitsani.+
2 Tsopano uza anthu kuti mwamuna aliyense ndi mkazi aliyense apemphe kwa munthu wokhala naye pafupi zinthu zasiliva ndi zagolide.”+
3 Ndiyeno Yehova anachititsa kuti Aiguputo akomere mtima Aisiraeli. Komanso Mose ankalemekezedwa kwambiri mʼdziko la Iguputo, pamaso pa atumiki a Farao ndi pamaso pa Aiguputo onse.
4 Choncho Mose anati: “Yehova wanena kuti, ‘Pakati pa usiku ndilowa mu Iguputo,+
5 ndipo mwana aliyense woyamba kubadwa mʼdziko la Iguputo adzafa.+ Kuyambira mwana woyamba wa Farao amene wakhala pampando wachifumu, mpaka mwana woyamba wa kapolo wamkazi amene akugwira ntchito pamphero* ndiponso mwana woyamba kubadwa wa nyama iliyonse.+
6 Mʼdziko lonse la Iguputo mudzakhala kulira kwakukulu kumene sikunachitikepo ndiponso kumene sikudzachitikanso.+
7 Ngakhale galu sadzauwa aliyense wa Aisiraeli, sadzauwa anthu kapena ziweto zawo, kuti mudziwe kuti Yehova akhoza kuchitira Aisiraeli zinthu zosiyana ndi zimene angachitire Aiguputo.’+
8 Ndipo atumiki anu onsewa adzabwera kwa ine nʼkundigwadira komanso kundiweramira. Iwo adzanena kuti, ‘Pita, iweyo ndi anthu onse amene amakutsatira.’+ Akadzatero ndidzapitadi.” Atanena mawu amenewa anachoka kwa Farao atakwiya.
9 Kenako Yehova anauza Mose kuti: “Farao sadzakumverani inu.+ Izi zili choncho kuti ndichite zodabwitsa zochuluka mʼdziko la Iguputo.”+
10 Mose ndi Aroni anachita zodabwitsa zonsezi pamaso pa Farao.+ Koma Yehova analola Farao kuumitsa mtima wake, moti sanalole kuti Aisiraeli achoke mʼdziko lake.+
Mawu a M'munsi
^ “Mphero” ndi mwala umene ankaugwiritsa ntchito popera mbewu kuti apange ufa.