Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira 21:1-27

  • Kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano (1-8)

    • Sikudzakhalanso imfa (4)

    • Zinthu zonse zidzakhala zatsopano (5)

  • Anafotokoza zokhudza Yerusalemu watsopano (9-27)

21  Ndiyeno ndinaona kumwamba kwatsopano ndi dziko lapansi latsopano,+ chifukwa kumwamba kwakale ndi dziko lapansi lakale zinali zitachoka+ ndipo kulibenso nyanja.+  Ndinaonanso mzinda woyera, Yerusalemu Watsopano, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu+ ndipo unali utakonzedwa ngati mkwatibwi amene wavala zokongola kuti akalandire mwamuna wake.+  Kenako ndinamva mawu ofuula kuchokera kumpando wachifumu akuti: “Taonani! Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu ndipo iye azidzakhala nawo. Iwo adzakhala anthu ake ndipo Mulunguyo adzakhala nawo.+  Iye adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo+ ndipo imfa sidzakhalaponso.+ Sipadzakhalanso kulira, kubuula kapena kupweteka.+ Zakalezo zapita.”  Ndipo Mulungu amene wakhala pampando wachifumu+ anati: “Taonani! Zinthu zonse zimene ndikupanga ndi zatsopano.”+ Ananenanso kuti: “Lemba, chifukwa mawu amenewa ndi odalirika komanso oona.”  Iye anandiuza kuti: “Zakwaniritsidwa! Ine ndine Alefa ndi Omega,* chiyambi ndi mapeto.+ Aliyense amene akumva ludzu ndidzamupatsa madzi a kasupe wa moyo kwaulere.*+  Aliyense amene wapambana pankhondo adzalandira zinthu zimenezi kuti zikhale cholowa chake. Ineyo ndidzakhala Mulungu wake ndipo iye adzakhala mwana wanga.  Koma anthu amantha, opanda chikhulupiriro,+ odetsedwa amenenso amachita zinthu zonyansa, opha anthu,+ achiwerewere,*+ amene amachita zamizimu, olambira mafano ndi anthu onse abodza,+ adzaponyedwa mʼnyanja yoyaka moto ndi sulufule.+ Nyanja imeneyi ikuimira imfa yachiwiri.”+  Mmodzi wa angelo 7 aja, amene anali ndi mbale 7 zodzaza ndi miliri 7 yotsiriza+ anabwera nʼkundiuza kuti: “Bwera kuno ndikuonetse mkwatibwi, mkazi wa Mwanawankhosa.”+ 10  Choncho, pogwiritsa ntchito mphamvu ya mzimu, ananditenga nʼkundipititsa kuphiri lalikulu ndi lalitali ndipo anandionetsa mzinda woyera wa Yerusalemu, ukutsika kuchokera kumwamba kwa Mulungu,+ 11  ndipo unali ndi ulemerero wa Mulungu.+ Unkanyezimira ngati mwala wamtengo wapatali kwambiri, ngati mwala wa yasipi wowala mbee! ngati galasi.+ 12  Mzindawo unali ndi mpanda waukulu komanso wautali ndipo unali ndi mageti 12. Pamagetiwo panali angelo 12 ndipo panalembedwa mayina a mafuko 12 a ana a Isiraeli. 13  Kumʼmawa kwa mzindawo kunali mageti atatu, kumpoto mageti atatu, kumʼmwera mageti atatu ndipo kumadzulo kwake kunali mageti atatu.+ 14  Mpanda wa mzindawo unalinso ndi miyala yomangira maziko yokwana 12 ndipo pamiyalayo panalembedwa mayina 12 a atumwi 12+ a Mwanawankhosa. 15  Ndiyeno amene ankandilankhula uja ananyamula bango lagolide loyezera, kuti ayeze mzindawo, mageti ake ndi mpanda wake.+ 16  Mzindawo unali ndi mbali 4 zofanana kutalika kwake. Mulitali mwake nʼchimodzimodzi ndi mulifupi mwake. Mngeloyo anayeza mzindawo ndi bangolo ndipo anapeza kuti unali masitadiya 12,000* kuuzungulira. Mulitali mwake, mulifupi mwake ndiponso kuchoka pansi kupita mʼmwamba ndi zofanana. 17  Anayezanso mpanda wake ndipo unali wautali mikono 144,* mogwirizana ndi muyezo umene munthu anapeza, umenenso ndi wofanana ndi muyezo wa mngelo. 18  Mpandawo unamangidwa ndi mwala wa yasipi+ ndipo mzindawo unamangidwa ndi golide woyenga bwino woonekera ngati galasi. 19  Maziko a mpanda wa mzindawo anawakongoletsa ndi miyala yamtengo wapatali ya mitundu yosiyanasiyana: maziko oyamba anali amwala wa yasipi, achiwiri wa safiro, achitatu wa kalikedo, a 4 wa emarodi, 20  a 5 wa sadonu, a 6 wa sadiyo, a 7 wa kulusolito, a 8 wa belulo, a 9 wa topazi, a 10 wa kulusopurazo, a 11 wa huwakinto ndipo a 12 wa ametusito. 21  Komanso zitseko za mageti 12 aja zinali ngale 12. Chitseko chilichonse chinapangidwa ndi ngale imodzi. Ndipo msewu waukulu wamumzindawo unapangidwa ndi golide woyenga bwino woonekera ngati galasi. 22  Mumzindawo sindinaonemo kachisi aliyense chifukwa kachisi wake ndi Yehova* Mulungu Wamphamvuyonse+ komanso Mwanawankhosa. 23  Mzindawo sunafunikirenso kuwala kwa dzuwa kapena kwa mwezi, chifukwa kuwala kwa ulemerero wa Mulungu kunkaunikira mzindawo+ ndipo Mwanawankhosa ndi amene anali nyale yake.+ 24  Kuwala kwake kudzaunikira njira ya mitundu ya anthu kuti ithe kuyenda+ ndipo mafumu a dziko lapansi adzabweretsa ulemerero wawo mumzindawo. 25  Mageti ake sadzatsekedwa nʼkomwe, chifukwa kudzakhala masana okha ndipo usiku sudzakhalako.+ 26  Iwo adzabweretsa ulemerero ndi ulemu wa mitundu ya anthu mumzindawo.+ 27  Koma chilichonse chodetsedwa komanso aliyense wochita zonyansa ndiponso zachinyengo, sadzalowa mumzindawo.+ Amene adzalowemo ndi okhawo amene mayina awo analembedwa mumpukutu wa moyo wa Mwanawankhosa.+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “ndine A ndi Z.” Alefa ndi chilembo choyambirira cha afabeti ya Chigiriki ndipo Omega ndi chilembo chomalizira.
Kapena kuti, “popanda mtengo.”
Pafupifupi makilomita 2,220. Sitadiya imodzi ndi yofanana ndi mamita 185. Onani Zakumapeto B14.
Mamita pafupifupi 64. Onani Zakumapeto B14.