Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira 14:1-20

  • Mwanawankhosa ndi enanso 144,000 (1-5)

  • Mauthenga ochokera kwa angelo atatu (6-12)

    • Mngelo amene ali ndi uthenga wabwino, akuuluka mumlengalenga (6, 7)

  • Osangalala ndi anthu amene akufa ali ogwirizana ndi Khritsu (13)

  • Anakolola mpesa kawiri padziko lapansi (14-20)

14  Kenako ndinayangʼana ndipo ndinaona Mwanawankhosa+ ataimirira paphiri la Ziyoni.+ Iye anali limodzi ndi enanso 144,000+ amene analembedwa dzina lake ndi dzina la Atate+ wake pazipumi zawo.  Ndiyeno ndinamva phokoso kuchokera kumwamba ngati mkokomo wa madzi ambiri ndiponso ngati phokoso la bingu lamphamvu. Phokoso ndinamvalo linali ngati la oimba amene akuimba pogwiritsa ntchito azeze awo.  Iwo ankaimba nyimbo imene inkamveka ngati nyimbo yatsopano+ pamaso pa mpando wachifumu, pamaso pa angelo 4+ ndi pamaso pa akulu.+ Palibe amene anatha kuphunzira nyimboyo kupatulapo 144,000+ amene anagulidwa padziko lapansi.  Amenewa ndi amene sanadzidetse ndi akazi ndipo ali ngati anamwali.+ Iwo ndi amene amatsatira Mwanawankhosa kulikonse kumene akupita.+ Iwowa anagulidwa+ pakati pa anthu ngati zipatso zoyambirira+ zoperekedwa kwa Mulungu ndi kwa Mwanawankhosa.  Mʼkamwa mwawo simunapezeke chinyengo ndipo alibe chilema.+  Ndinaona mngelo wina akuuluka chapafupi mumlengalenga. Iye anali ndi uthenga wabwino wosatha woti aulengeze kwa anthu amene akukhala padziko lapansi, kudziko lililonse, fuko lililonse, chilankhulo chilichonse ndi mtundu uliwonse.+  Iye ankanena mofuula kuti: “Opani Mulungu ndi kumupatsa ulemerero chifukwa ola lakuti apereke chiweruzo lafika.+ Choncho lambirani Iye amene anapanga kumwamba, dziko lapansi, nyanja+ ndi akasupe amadzi.”  Kenako mngelo wachiwiri anamutsatira ndipo anati: “Wagwa! Babulo Wamkulu+ wagwa,+ amene anachititsa kuti mitundu yonse ya anthu imwe vinyo wa chilakolako cha* chiwerewere* chake!”+  Mngelo wina wachitatu anawatsatira ndipo ankanena mofuula kuti: “Ngati wina walambira chilombo+ ndi chifaniziro chake ndipo walandira chizindikiro pachipumi kapena padzanja lake,+ 10  adzamwanso vinyo wosasungunula wa mkwiyo wa Mulungu amene akuthiridwa mʼkapu ya mkwiyo wake.+ Ndipo adzazunzidwa ndi moto ndi sulufule+ pamaso pa angelo oyera komanso pamaso pa Mwanawankhosa. 11  Ndipo utsi wa kuzunzidwa kwawo udzafuka mpaka kalekale.+ Amene akulambira chilombo ndi chifaniziro chake ndiponso aliyense amene walandira chizindikiro cha dzina lake, adzazunzidwa masana ndi usiku osapuma.+ 12  Apa mʼpamene oyerawo, amene akusunga malamulo a Mulungu ndi kutsatira chikhulupiriro+ cha Yesu, akufunika kupirira.”+ 13  Kenako ndinamva mawu kuchokera kumwamba akuti, “Lemba kuti: Osangalala ndi anthu amene akufa ali ogwirizana ndi Ambuye+ kuyambira pa nthawi ino kupita mʼtsogolo. Mzimu ukuti asiyeni apume ku ntchito yawo imene anaigwira mwakhama, chifukwa zimene anachita zikupita nawo limodzi.” 14  Kenako ndinayangʼana ndipo ndinaona mtambo woyera. Pamtambopo panali patakhala winawake wooneka ngati mwana wa munthu,+ atavala chisoti chachifumu chagolide kumutu kwake ndipo mʼdzanja lake munali chikwakwa chakuthwa. 15  Mngelo wina anatuluka mʼnyumba yopatulika yapakachisi akulankhula mofuula kwa amene anakhala pamtambo uja kuti: “Tsitsa chikwakwa chako nʼkuyamba kumweta, chifukwa ola lomweta lafika ndipo zokolola zapadziko lapansi zakhwima.”+ 16  Choncho amene anakhala pamtambo uja anatsitsira chikwakwa chake chija padziko lapansi mwamphamvu ndipo anamweta zokolola zapadziko lapansi. 17  Mngelo winanso anatuluka mʼnyumba yopatulika yapakachisi amene ali kumwamba, nayenso anali ndi chikwakwa chakuthwa. 18  Mngelo winanso anatuluka kuguwa lansembe ndipo anali ndi ulamuliro pa moto. Iye analankhula mofuula ndi mngelo amene anali ndi chikwakwa chakuthwa uja kuti: “Tsitsa chikwakwa chako chakuthwacho nʼkumweta mpesa wapadziko lapansi ndipo usonkhanitse pamodzi maphava ake chifukwa mphesazo zapsa.”+ 19  Mngeloyo anatsitsira chikwakwa chake padziko lapansi mwamphamvu nʼkumweta mpesa wapadziko lapansi. Kenako anauponya mʼchoponderamo mphesa chachikulu cha mkwiyo wa Mulungu.+ 20  Anapondaponda mopondera mphesamo kunja kwa mzinda ndipo magazi anatuluka mʼchoponderamo mphesacho mpaka kufika mʼzibwano za mahatchi, nʼkuyenderera mtunda wa masitadiya 1,600.*

Mawu a M'munsi

MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “imwe mkwiyo wa.”
Pafupifupi makilomita 296. Sitadiya imodzi ndi yofanana ndi mamita 185. Onani Zakumapeto B14.