Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira 7:1-17

  • Angelo 4 anagwira mphepo kuti zisawononge (1-3)

  • Anthu okwana 144,000 anaikidwa chidindo (4-8)

  • Khamu lalikulu limene lavala mikanjo yoyera (9-17)

7  Zimenezi zitatha, ndinaona angelo 4 ataimirira mʼmakona 4 a dziko lapansi. Iwo anali atagwira mwamphamvu mphepo 4 za dziko lapansi, kuti mphepo iliyonse isawombe padziko lapansi, panyanja kapena pamtengo uliwonse. 2  Ndinaonanso mngelo wina akukwera kuchokera kotulukira dzuwa,* ali ndi chidindo cha Mulungu wamoyo. Iye anafuula mokweza mawu kwa angelo 4, amene anapatsidwa mphamvu zowononga dziko lapansi ndi nyanja aja, 3  kuti: “Musawononge dziko lapansi, kapena nyanja, kapena mitengo, mpaka titadinda chidindo+ pazipumi za akapolo a Mulungu wathu.”+ 4  Ndiyeno ndinamva chiwerengero cha amene anadindidwa chidindo. Anthu okwana 144,000,+ ochokera mʼfuko lililonse la ana a Isiraeli, anadindidwa chidindo:+ 5  Mu fuko la Yuda, anadindamo anthu 12,000.Mu fuko la Rubeni, 12,000.Mu fuko la Gadi, 12,000. 6  Mu fuko la Aseri, 12,000.Mu fuko la Nafitali, 12,000.Mu fuko la Manase,+ 12,000. 7  Mu fuko la Simiyoni, 12,000.Mu fuko la Levi, 12,000.Mu fuko la Isakara, 12,000. 8  Mu fuko la Zebuloni, 12,000.Mu fuko la Yosefe, 12,000.Ndipo mu fuko la Benjamini, anadindamo anthu 12,000. 9  Zimenezi zitatha, nditayangʼana ndinaona khamu lalikulu la anthu, amene palibe munthu aliyense amene anatha kuwawerenga, ochokera mʼdziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse ndi chilankhulo chilichonse.+ Iwo anali ataimirira pamaso pa mpando wachifumu ndi pamaso pa Mwanawankhosa, atavala mikanjo yoyera+ ndiponso atanyamula nthambi za kanjedza mʼmanja mwawo.+ 10  Iwo anapitiriza kufuula ndi mawu okweza akuti: “Chipulumutso chathu chachokera kwa Mulungu wathu, amene wakhala pampando wachifumu,+ ndi kwa Mwanawankhosa.”+ 11  Angelo onse anali ataima kuzungulira mpando wachifumu, akulu+ komanso angelo 4 aja. Ndipo onse anagwada nʼkuwerama mpaka nkhope zawo pansi, pamaso pa mpando wachifumuwo ndi kulambira Mulungu. 12  Iwo ankanena kuti: “Ame! Mulungu wathu ndi amene ali ndi nzeru, mphamvu komanso nyonga ndipo ndi amene akuyenera kutamandidwa, kupatsidwa ulemerero ndi ulemu komanso kuyamikiridwa mpaka kalekale.+ Ame.” 13  Ndiyeno mmodzi wa akulu aja anandifunsa kuti: “Kodi amene avala mikanjo yoyerawa+ ndi ndani ndipo achokera kuti?” 14  Nthawi yomweyo, ndinamuyankha kuti: “Mbuyanga, mukudziwa ndinu.” Ndipo iye anandiuza kuti: “Amenewa ndi amene atuluka mʼchisautso chachikulu+ ndipo achapa mikanjo yawo nʼkuiyeretsa mʼmagazi a Mwanawankhosa.+ 15  Nʼchifukwa chake ali pamaso pa mpando wachifumu wa Mulungu. Iwo akumuchitira utumiki wopatulika usana ndi usiku mʼkachisi wake, ndipo Amene wakhala pampando wachifumuyo+ adzawaphimba ndi tenti yake kuti awateteze.+ 16  Iwo sadzamvanso njala kapena ludzu. Dzuwa kapena kutentha kulikonse sikudzawawotcha,+ 17  chifukwa Mwanawankhosa,+ amene ali pambali* pa mpando wachifumu, adzawaweta+ nʼkuwatsogolera ku akasupe a madzi a moyo.+ Ndipo Mulungu adzapukuta misozi yonse mʼmaso mwawo.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “kuchokera kumʼmawa.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “ali pakati.”