Genesis 2:1-25

  • Mulungu anapuma pa tsiku la 7 (1-3)

  • Yehova Mulungu anapanga kumwamba ndi dziko lapansi (4)

  • Mwamuna ndi mkazi mʼmunda wa Edeni  (5-25)

    • Munthu anapangidwa kuchokera kudothi (7)

    • Mtengo woletsedwa wodziwitsa chabwino ndi choipa (15-17)

    • Kulengedwa kwa mkazi (18-25)

2  Choncho Mulungu anamaliza kulenga kumwamba ndi dziko lapansi komanso zonse zimene zili mmenemo.+  Pofika tsiku la 7, Mulungu anali atamaliza ntchito imene ankagwira. Pa tsiku la 7 limeneli, iye anayamba kupuma pa ntchito yonse imene ankagwira.+  Kenako Mulungu anadalitsa tsiku la 7 komanso ananena kuti likhale lopatulika, chifukwa kuyambira pa tsikuli wakhala akupuma pa ntchito yake yonse. Pamenepa Mulungu anali atamaliza kulenga zinthu zonse zimene ankafuna.  Iyi ndi nkhani yofotokoza mmene kumwamba ndi dziko lapansi zinalili pa nthawi imene zinkalengedwa, pa tsiku limene Yehova* Mulungu anapanga dziko lapansi ndi kumwamba.+  Padziko lapansi panalibe tchire ndi zomera zina, chifukwa Yehova Mulungu anali asanagwetse mvula padziko lapansi komanso panalibe munthu woti nʼkulima nthaka.  Koma nkhungu* inkakwera mʼmwamba kuchokera padziko lapansi, ndipo inkanyowetsa nthaka yonse.  Kenako Yehova Mulungu anaumba munthu kuchokera kudothi,*+ ndipo anauzira mpweya wa moyo+ mumphuno mwake, munthuyo nʼkukhala wamoyo.+  Zitatero Yehova Mulungu anadzala munda ku Edeni,+ chakumʼmawa, ndipo mʼmundamo anaikamo munthu amene anamuumba uja.+  Choncho Yehova Mulungu anameretsa munthaka mtengo wamtundu uliwonse wooneka bwino komanso wazipatso zabwino kudya. Anameretsanso mtengo wa moyo+ pakati pa mundawo komanso mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa.+ 10  Mu Edeni munali mtsinje umene unkathirira mundawo. Potuluka mʼmundawo, mtsinjewo unagawikana nʼkukhala mitsinje 4. 11  Dzina la mtsinje woyamba ndi Pisoni. Mtsinjewu umazungulira dera lonse la Havila kumene kuli golide. 12  Golide wamʼdera limeneli ndi wabwino. Kulinso utomoni wonunkhira wa bedola ndi miyala yamtengo wapatali ya onekisi. 13  Dzina la mtsinje wachiwiri ndi Gihoni. Mtsinje umenewu umazungulira dera lonse la Kusi. 14  Dzina la mtsinje wachitatu ndi Hidekeli.*+ Mtsinjewu umalowera kumʼmawa kwa Asuri.+ Ndipo mtsinje wa 4 ndi Firate.+ 15  Tsopano Yehova Mulungu anatenga munthu uja nʼkumuika mʼmunda wa Edeni kuti aziulima komanso kuusamalira.+ 16  Ndiyeno Yehova Mulungu anapatsa munthuyo lamulo lakuti: “Zipatso za mtengo uliwonse wa mʼmundamu uzidya mmene ungafunire.+ 17  Koma usadye zipatso za mtengo wodziwitsa chabwino ndi choipa. Chifukwa tsiku limene udzadye, udzafa ndithu.”+ 18  Kenako Yehova Mulungu anati: “Si bwino kuti munthu azikhala yekha. Ndimupangira womuthandiza, monga mnzake womuyenerera.”+ 19  Ndiyeno Yehova Mulungu anaumba ndi dothi nyama iliyonse yakutchire komanso chamoyo chilichonse chouluka mumlengalenga ndipo anazipititsa kwa munthuyo kuti azipatse mayina. Dzina lililonse limene munthuyo anapatsa chamoyo chilichonse linakhaladi dzina lake.+ 20  Munthuyo anapereka mayina kwa nyama zonse zoweta, ndiponso zamoyo zonse zouluka mumlengalenga, komanso nyama iliyonse yakutchire. Koma munthuyo analibe womuthandiza, monga mnzake womuyenerera. 21  Choncho Yehova Mulungu anagonetsa munthuyo tulo tofa nato. Munthuyo ali mʼtulo, Mulungu anamuchotsa nthiti imodzi kenako nʼkutseka pamalopo. 22  Ndiyeno Yehova Mulungu anapanga mkazi kuchokera kunthiti imene anaichotsa kwa mwamunayo. Atatero, anamupititsa kwa iye.+ 23  Ndiyeno mwamunayo anati: “Tsopano uyu ndi fupa la mafupa angaKomanso mnofu wa mnofu wanga. Ameneyu azitchedwa Mkazi,Chifukwa anachokera kwa mwamuna.”+ 24  Chifukwa cha zimenezi, mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake nʼkudziphatika kwa mkazi wake* ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.+ 25  Choncho onsewo, mwamuna ndi mkazi wakeyo, ankakhala maliseche+ koma sankachita manyazi.

Mawu a M'munsi

Malo oyamba kupezeka dzina lenileni la Mulungu, יהוה (YHWH). Onani Zakumapeto A4.
Zikuoneka kuti madzi ankasanduka nthunzi nʼkukwera mʼmwamba ndipo zikatero nthunziyo inkasandukanso madzi omwe ankanyowetsa nthaka.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kuchokera kufumbi.”
Kapena kuti, “Tigirisi.”
Kapena kuti, “nʼkukhalabe ndi mkazi wake.”