Genesis 16:1-16
-
Hagara ndi Isimaeli (1-16)
16 Sarai mkazi wa Abulamu, analibe ana.+ Koma iye anali ndi kapolo wake wa ku Iguputo, dzina lake Hagara.+
2 Ndiye Sarai anauza Abulamu kuti: “Yehova wapangitsa kuti ndisabereke ana. Chonde gonani ndi kapolo wangayu. Mwina ndingapeze ana kuchokera kwa iye.”+ Choncho Abulamu anamvera mawu a Sarai.
3 Abulamu atakhala zaka 10 mʼdziko la Kanani, Sarai mkazi wake anapereka Hagara, kapolo wake wa ku Iguputo uja kwa mwamuna wake Abulamu kuti akhale mkazi wake.
4 Zitatero Abulamu anagona ndi Hagara ndipo iye anakhala woyembekezera. Hagara atazindikira kuti ndi woyembekezera, anayamba kuchitira mwano mbuye wake, Sarai.
5 Sarai ataona zimenezi anauza Abulamu kuti: “Mlandu wa zimene zikundichitikirazi ukhale pa inu. Ine ndinapereka kapolo wanga kwa inu kuti akhale mkazi wanu, koma iye ataona kuti ndi woyembekezera wayamba kundichitira mwano. Yehova aweruze pakati pa ine ndi inu.”
6 Abulamu anauza Sarai kuti: “Kapolo wakoyutu ali mʼmanja mwako. Chita chimene ukuchiona kuti nʼchabwino.” Ndiyeno Sarai anayamba kuzunza Hagara, mpaka Hagarayo anathawa.
7 Pambuyo pake, mngelo wa Yehova anakumana ndi Hagara mʼchipululu ali pakasupe wamadzi. Kasupeyo anali panjira yopita ku Shura.+
8 Ndiyeno mngeloyo anati: “Hagara kapolo wa Sarai, kodi ukuchokera kuti ndipo ukupita kuti?” Iye anayankha kuti: “Ndikuthawa mbuye wanga, Sarai.”
9 Mngelo wa Yehovayo anauza Hagara kuti: “Bwerera kwa mbuye wako ndipo uzikamvera modzichepetsa zimene azikakuuza.”
10 Kenako mngelo wa Yehovayo anamuuzanso kuti: “Ndidzachulukitsa kwambiri mbadwa* zako, moti zidzakhala zosawerengeka.”+
11 Mngelo wa Yehovayo ananenanso kuti: “Taona, panopa ndiwe woyembekezera, ndipo udzabereka mwana wamwamuna. Mwanayo udzamʼpatse dzina lakuti Isimaeli,* chifukwa Yehova wamva kulira kwako.
12 Mwanayo adzakhala ngati bulu wamʼtchire.* Dzanja lake lidzalimbana ndi aliyense, ndipo dzanja la aliyense lidzalimbana naye. Iye adzakhala pafupi ndi abale ake onse.”*
13 Ndiyeno Hagara anapemphera kwa Yehova* kuti: “Inu ndinu Mulungu amene amaona chilichonse.”+ Ananenanso kuti: “Kodi nanenso pano ndaona amene amatha kundionayo?”
14 Nʼchifukwa chake chitsimecho anachipatsa dzina lakuti Beere-lahai-roi.* (Chili pakati pa Kadesi ndi Beredi.)
15 Choncho Hagara anaberekera Abulamu mwana wamwamuna ndipo Abulamu anamʼpatsa mwanayo dzina lakuti Isimaeli.+
16 Pamene Hagara anaberekera Abulamu Isimaeli, Abulamuyo nʼkuti ali ndi zaka 86.
Mawu a M'munsi
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu.”
^ Kutanthauza kuti, “Mulungu Amamva.”
^ Anthu ena amaganiza kuti bulu wamʼtchireyu anali mbidzi mwina chifukwa chakuti imakonda kuchita zinthu payokha osati limodzi ndi nyama zina.
^ Mabaibulo ena amati, “azidzachitira nkhanza abale ake onse.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “anaitanira pa dzina la Yehova.”
^ Kutanthauza kuti, “Chitsime cha Wamoyo Amene Amatha Kundiona.”