Genesis 23:1-20

  • Imfa ya Sara komanso manda ake (1-20)

23  Sara anakhala ndi moyo zaka 127. Zaka zimene Sara anakhala ndi moyo ndi zimenezi.+  Sara anamwalirira ku Kiriyati-ariba,+ kapena kuti ku Heburoni,+ mʼdziko la Kanani.+ Ndiye Abulahamu anayamba kumulira Sara.  Kenako Abulahamu anachoka pamene panali mtembo wa mkazi wake nʼkupita kukalankhula ndi ana a Heti+ kuti:  “Ine ndinadzakhala kwanu kuno ngati mlendo.+ Choncho mundipatseko malo kuti ndikhale ndi manda angaanga, ndiikemo mkazi wanga.”  Ana a Heti anayankha Abulahamu kuti:  “Timvereni mbuyathu. Inu ndinu mtsogoleri wathu woikidwa ndi Mulungu.*+ Sankhani manda abwino kwambiri pa manda amene tili nawo kuti muikemo malemuwo. Palibe aliyense wa ife amene angakanize manda ake kuti muikemo malemuwo.”  Choncho Abulahamu anaimirira nʼkugwada pamaso pa eni dzikowo, ana a Heti.+  Iye analankhula nawo kuti: “Ngati mukuvomera kuti ndiike mʼmanda malemu mkazi wanga kunoko, chonde mundipemphereko kwa Efuroni mwana wa Zohari  kuti andigulitse phanga lake la Makipela limene lili mʼmalire a malo ake. Andigulitse pa mtengo wake wonse+ inu mukuona, kuti ndikhale ndi manda.”+ 10  Pa nthawiyi nʼkuti Efuroni atakhala pansi limodzi ndi ana a Heti. Choncho Efuroni Muhiti anayankha Abulahamu, ana a Hetiwo akumva limodzi ndi onse amene analowa pageti la mzinda+ wake kuti: 11  “Ayi mbuyanga! Ndimvereni. Malowo, pamodzi ndi phanga limene lili pamalopo, ndikukupatsani pamaso pa anthu a mtundu wangawa. Kaikeni malemuwo.” 12  Zitatero Abulahamu anagwada pamaso pa eni dzikowo. 13  Kenako iye anauza Efuroni pamaso pa eni dzikowo kuti: “Ndimvere chonde. Ine ndikupatsa ndalama zonse zimene ungandiuze zogulira malowo. Landira silivayu kuti ndikaike mkazi wanga kumeneko.” 14  Ndiyeno Efuroni anayankha Abulahamu kuti: 15  “Ndimvereni mbuyanga. Malowo mtengo wake ndi siliva wolemera masekeli 400.* Koma ndalamazo si nkhani yaikulu pakati pa ine ndi inu. Kaikeni malemuwo.” 16  Abulahamu anamvera Efuroni, ndipo anamuyezera siliva wokwanira mtengo umene Efuroniyo ananena pamaso pa ana a Heti. Anamuyezera siliva wolemera masekeli 400,* mogwirizana ndi muyezo umene amalonda ankauvomereza.+ 17  Choncho Efuroni anagulitsa malo ake amene anali ku Makipela pafupi ndi Mamure. Anagulitsa malowo, phanga komanso mitengo yonse imene inali pamalopo, ndipo anatsimikizira 18  pamaso pa ana a Heti ndi onse amene analowa pageti la mzinda, kuti Abulahamu wagula malowo ndipo ndi ake. 19  Kenako Abulahamu anaika Sara mkazi wake mʼmanda kuphanga la Makipela, pafupi ndi Mamure, kapena kuti Heburoni, mʼdziko la Kanani. 20  Choncho ana a Heti anapereka kwa Abulahamu malowo ndi phanga limene linali pamenepo kuti akhale manda.+

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “mtsogoleri wamkulu.”
Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.
Sekeli imodzi inali yofanana ndi magalamu 11.4. Onani Zakumapeto B14.