Genesis 8:1-22

  • Kuphwa kwa madzi a chigumula (1-14)

    • Anatumiza njiwa (8-12)

  • Kutuluka mʼchingalawa (15-19)

  • Lonjezo la Mulungu lokhudza dziko lapansi (20-22)

8  Koma Mulungu anakumbukira Nowa ndi nyama zonse zakutchire ndiponso nyama zonse zoweta zimene anali nazo mʼchingalawa chija.+ Ndiyeno Mulungu anachititsa kuti chimphepo chiwombe padziko lapansi, ndipo madzi anayamba kuchepa.  Madzi onse akumwamba anasiya kutuluka komanso zitseko zotchingira madziwo zinatsekeka, choncho chimvula chinasiya kugwa kuchokera kumwamba.+  Kenako madzi anayamba kuchepa pangʼonopangʼono padziko lapansi. Pamene masiku 150 ankatha, madziwo anali atachepa ndithu.  Mʼmwezi wa 7, pa tsiku la 17 la mweziwo, chingalawacho chinaima pamapiri a Ararati.  Madzi anapitirizabe kuchepa mpaka mwezi wa 10. Mʼmwezi wa 10 umenewo, pa tsiku loyamba la mweziwo, nsonga za mapiri zinaonekera.+  Ndiyeno patatha masiku 40, Nowa anatsegula windo+ limene anaika pa chingalawacho  ndipo anatumiza khwangwala. Choncho khwangwalayo ankangouluka kunja nʼkumabwerera kuchingalawacho mpaka madzi ataphwa padziko lapansi.  Kenako, Nowa anatumiza njiwa kuti aone ngati madzi anaphwa padziko lapansi.  Koma njiwayo sinapeze malo alionse oti nʼkuterapo. Choncho, inabwerera kwa iye mʼchingalawamo chifukwa madzi anali asanaphwe padziko lonse lapansi.+ Itabwerera, iye anatulutsa dzanja lake, nʼkuitenga ndipo anailowetsa mʼchingalawamo. 10  Anadikirabe masiku ena 7, kenako anatumizanso njiwa ija kuchokera mʼchingalawamo. 11  Njiwayo itabwerera kwa iye chakumadzulo, anaona kuti ili ndi tsamba laliwisi kukamwa kwake. Tsambalo linali la mtengo wa maolivi longothyoledwa kumene. Nowa ataona zimenezi, anadziwa kuti madzi anali ataphwa padziko lapansi.+ 12  Anadikiranso masiku ena 7. Kenako anatumizanso njiwa ija koma sinabwererenso kwa iye. 13  Tsopano mʼchaka cha 601 cha Nowa,+ mʼmwezi woyamba, pa tsiku loyamba la mweziwo, madzi anali ataphwa padziko lapansi. Nowa anatsegula chibowo chimene chinali padenga la chingalawacho nʼkuyangʼana kunja ndipo anaona kuti nthaka yayamba kuuma. 14  Mʼmwezi wachiwiri, pa tsiku la 27 la mweziwo, nthaka inali itaumiratu. 15  Ndiyeno Mulungu anauza Nowa kuti: 16  “Tsopano tulukani mʼchingalawamo, iweyo, mkazi wako, ana ako ndi akazi a ana ako.+ 17  Utuluke limodzi ndi zamoyo zamtundu uliwonse+ zimene uli nazo. Utuluke limodzi ndi zamoyo zouluka, zinyama ndi zonse zokwawa padziko lapansi, kuti zichulukane padziko lapansi, ziberekane ndipo zikhale zambiri padziko lapansi.”+ 18  Choncho Nowa anatuluka limodzi ndi ana ake,+ mkazi wake ndi akazi a ana ake. 19  Komanso, zamoyo zilizonse, nyama zilizonse zokwawa, zamoyo zouluka zilizonse, chilichonse chimene chimayenda padziko lapansi, zinatuluka mʼchingalawamo monga mwa magulu awo.+ 20  Kenako Nowa anamangira Yehova guwa lansembe.+ Atatero, anatenga zina mwa nyama zonse zosadetsedwa, ndi zina mwa zouluka zonse zosadetsedwa,+ nʼkuzipereka nsembe yopsereza paguwapo.+ 21  Ndiyeno Yehova anayamba kumva fungo losangalatsa.* Choncho Yehova ananena mumtima mwake kuti: “Sindidzatembereranso nthaka+ chifukwa cha zochita za anthu, popeza maganizo a anthu amakhala oipa kuyambira ali ana.+ Ndipo sindidzaphanso chamoyo chilichonse ngati mmene ndachitiramu.+ 22  Kuyambira pano mpaka mʼtsogolo, kudzala mbewu ndi kukolola sikudzatha padziko lapansi. Ndiponso nyengo yozizira ndi yotentha, chilimwe ndi chisanu, masana ndi usiku, zidzakhalapobe.”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “fungo lokhazika mtima pansi.”