Genesis 1:1-31

  • Kulengedwa kwa dziko lapansi ndi kumwamba (1, 2)

  • Masiku 6 okonza dziko lapansi  (3-31)

    • Tsiku Loyamba: kuwala; masana ndi usiku (3-5)

    • Tsiku Lachiwiri: mlengalenga (6-8)

    • Tsiku Lachitatu: mtunda ndi zomera (9-13)

    • Tsiku la 4: zounikira zakumwamba (14-19)

    • Tsiku la 5: nsomba ndi mbalame (20-23)

    • Tsiku la 6: nyama ndi anthu (24-31)

1  Pachiyambi, Mulungu analenga kumwamba ndi dziko lapansi.+  Dziko lapansi linali lopanda chilichonse. Padzikoli panali madzi ambiri+ ndipo pamwamba pake panali mdima wokhawokha. Mphamvu ya Mulungu+ inkayendayenda* pamwamba pa madziwo.+  Ndiyeno Mulungu anati: “Pakhale kuwala.” Ndipo kuwala+ kunakhalapo.  Zitatero, Mulungu anaona kuti kuwalako kunali kwabwino. Kenako Mulungu anayamba kulekanitsa kuwala ndi mdima.  Ndiyeno Mulungu anapatsa kuwalako dzina lakuti Masana, koma mdimawo anaupatsa dzina lakuti Usiku.+ Panali madzulo ndiponso panali mʼmawa, tsiku loyamba.  Kenako Mulungu ananena kuti: “Pakhale mlengalenga+ pakati pa madzi kuti madziwo+ alekane.”  Choncho Mulungu anapanga mlengalenga nʼkulekanitsa madzi kuti ena akhale pansi pa mlengalenga ndipo ena akhale pamwamba pa mlengalenga.+ Ndipo zinaterodi.  Mlengalengawo Mulungu anaupatsa dzina lakuti Kumwamba. Panali madzulo ndiponso panali mʼmawa, tsiku lachiwiri.  Kenako Mulungu anati: “Madzi apadziko lapansi akhale pamalo amodzi kuti mtunda uonekere.”+ Ndipo zinaterodi. 10  Mulungu anapatsa mtundawo dzina lakuti Dziko,+ koma madziwo anawapatsa dzina lakuti Nyanja.+ Ndipo Mulungu anaona kuti zili bwino.+ 11  Kenako Mulungu anati: “Padziko lapansi pamere udzu, zomera zobereka mbewu ndiponso mitengo yobereka zipatso zokhala ndi nthangala, monga mwa mitundu yake.” Ndipo zinaterodi. 12  Choncho dziko lapansi linayamba kumera udzu, zomera zobereka mbewu+ monga mwa mitundu yake komanso mitengo yobereka zipatso zokhala ndi nthangala monga mwa mitundu yake. Zitatero, Mulungu anaona kuti zili bwino. 13  Panali madzulo ndiponso panali mʼmawa, tsiku lachitatu. 14  Kenako Mulungu anati: “Kumwamba kukhale zounikira+ kuti zilekanitse masana ndi usiku+ ndipo zidzakhala zizindikiro zosonyeza nyengo, masiku ndi zaka.+ 15  Zidzakhala zounikira zokhala mumlengalenga ndipo zizidzaunikira dziko lapansi.” Ndipo zinaterodi. 16  Choncho Mulungu anapanga zounikira ziwiri. Chounikira chowala kwambiri anachipanga kuti chiziwala* masana,+ ndipo chowala pangʼono kuti chiziwala* usiku, komanso anapanga nyenyezi.+ 17  Mulungu atatero, anaziika mumlengalenga kuti ziunikire dziko lapansi. 18  Anaziika kuti ziziwala masana ndi usiku, komanso kuti zizilekanitsa kuwala ndi mdima.+ Zitatero, Mulungu anaona kuti zili bwino. 19  Panali madzulo ndiponso panali mʼmawa, tsiku la 4. 20  Kenako Mulungu anati: “Mʼmadzi mukhale zamoyo zambirimbiri, ndiponso zolengedwa zouluka ziziuluka mumlengalenga mwa dziko lapansi.”+ 21  Mulungu analenga nyama zikuluzikulu zamʼnyanja ndi zamoyo zonse zokhala mʼmadzi mogwirizana ndi mitundu yake. Analenganso chamoyo chilichonse chouluka mogwirizana ndi mtundu wake. Ndipo Mulungu anaona kuti zili bwino. 22  Mulungu atatero, anazidalitsa ponena kuti: “Muswane ndipo muchulukane nʼkudzaza nyanja zonse.+ Ndipo zamoyo zouluka zichuluke padziko lapansi.” 23  Panali madzulo ndiponso panali mʼmawa, tsiku la 5. 24  Kenako Mulungu anati: “Dziko lapansi likhale ndi zamoyo monga mwa mitundu yake, nyama zoweta, nyama zokwawa,* komanso nyama zakutchire monga mwa mitundu yake.”+ Ndipo zinaterodi. 25  Choncho Mulungu anapanga nyama zakutchire monga mwa mitundu yake komanso nyama zoweta monga mwa mitundu yake. Anapanganso nyama zonse zokwawa panthaka monga mwa mitundu yake. Ndipo Mulungu anaona kuti zili bwino. 26  Kenako Mulungu anati: “Tiyeni+ tipange munthu mʼchifaniziro+ chathu, kuti akhale wofanana nafe.+ Ayangʼanire nsomba zamʼnyanja, zamoyo zouluka mumlengalenga, nyama zoweta ndiponso nyama iliyonse yokwawa padziko lapansi. Komanso asamalire dziko lonse lapansi.”+ 27  Choncho Mulungu analenga munthu mʼchifaniziro chake, mʼchifaniziro cha Mulungu analenga munthu. Anawalenga mwamuna ndi mkazi.+ 28  Komanso, Mulungu anawadalitsa nʼkuwauza kuti: “Muberekane, muchuluke, mudzaze dziko lapansi+ ndipo muziliyangʼanira.+ Muyangʼanirenso+ nsomba zamʼnyanja ndi zamoyo zouluka mumlengalenga, komanso chamoyo chilichonse choyenda padziko lapansi.” 29  Kenako Mulungu anati: “Ndakupatsani zomera zonse zimene zili padziko lapansi zobereka mbewu komanso mitengo yonse yobereka zipatso zokhala ndi nthangala kuti zikhale chakudya chanu.+ 30  Ndapereka zomera zonse kuti zikhale chakudya+ cha nyama iliyonse yamʼtchire padziko lapansi, chamoyo chilichonse chouluka mumlengalenga komanso chokwawa chilichonse chapadziko lapansi chimene chili ndi moyo.” Ndipo zinaterodi. 31  Pambuyo pa zimenezi Mulungu anaona kuti zonse zimene anapanga zinali zabwino kwambiri.+ Panali madzulo ndiponso panali mʼmawa, tsiku la 6.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “Mzimu wa Mulungu unkayendayenda.”
Kapena kuti, “chizilamulira.”
Kapena kuti, “chizilamulira.”
Mawu a Chiheberi amene amasuliridwa kuti “nyama zokwawa” amatanthauza zamoyo zimene zimayenda chokwawa monga nyama zingʼonozingʼono, mbewa, abuluzi, njoka, ndi tizilombo tina tingʼonotingʼono.