Genesis 7:1-24

  • Kulowa mʼchingalawa (1-10)

  • Chigumula cha dziko lonse (11-24)

7  Kenako Yehova anauza Nowa kuti: “Lowa mʼchingalawacho, iwe ndi banja lako, chifukwa iwe ndi amene ndakuona kuti ndiwe wolungama pakati pa mʼbadwo uwu.+  Pa nyama zosadetsedwa zamtundu uliwonse utengepo zokwanira 7,*+ yaimuna ndi yaikazi yake. Koma pa nyama zodetsedwa zilizonse utengepo ziwiri zokha, yaimuna ndi yaikazi yake.  Komanso pa zamoyo zilizonse zouluka mumlengalenga, utengepo zokwanira 7,* chachimuna ndi chachikazi, kuti zisungike padziko lonse lapansi.+  Kwangotsala masiku 7 okha kuti ndigwetse chimvula+ padziko lapansi kwa masiku 40, masana ndi usiku.+ Ndipo ndidzaseseratu padziko lapansi chamoyo chilichonse chimene ndinachipanga.”+  Choncho Nowa anachita zonse zimene Yehova anamulamula.  Nowa anali ndi zaka 600 pamene chigumula chinachitika padziko lapansi.+  Choncho chigumulacho chisanayambe, Nowa analowa mʼchingalawacho, limodzi ndi ana ake aamuna, mkazi wake ndi akazi a ana ake.+  Nyama zilizonse zosadetsedwa, nyama zilizonse zodetsedwa, zamoyo zilizonse zouluka komanso zilizonse zoyenda panthaka,+  zinalowa ziwiriziwiri mʼchingalawa mmene munali Nowa, yaimuna ndi yaikazi, monga mmene Mulungu analamulira Nowa. 10  Ndiyeno patapita masiku 7, kunayamba kugwa chimvula ndipo madzi anayamba kudzaza padziko lapansi. 11  Mʼchaka cha 600 cha moyo wa Nowa, mʼmwezi wachiwiri,* pa tsiku la 17 la mweziwo, pa tsiku limeneli madzi onse akumwamba anaphulika ndipo zitseko zotchingira madzi akumwamba zinatseguka.+ 12  Ndiyeno chimvula chinakhuthuka padziko lapansi kwa masiku 40 masana ndi usiku. 13  Pa tsiku limenelo Nowa analowa mʼchingalawacho. Analowa limodzi ndi ana ake Semu, Hamu ndi Yafeti,+ ndiponso mkazi wake ndi akazi atatu a ana akewo.+ 14  Iwo analowa limodzi ndi nyama zakutchire zamtundu uliwonse, nyama zoweta zamtundu uliwonse, nyama zokwawa* zapadziko lapansi zamtundu uliwonse, zamoyo zouluka zamtundu uliwonse, mbalame zilizonse ndiponso zamoyo zilizonse zamapiko. 15  Zamoyo zamtundu uliwonse zokhala ndi mpweya wa moyo* mʼthupi mwake, zinkapita ziwiriziwiri mʼchingalawa mmene munali Nowa. 16  Choncho zamoyo zamtundu uliwonse, zazimuna ndi zazikazi, zinalowa mʼchingalawamo mogwirizana ndi mmene Mulungu analamulira Nowa. Kenako Yehova anatseka chitseko. 17  Chimvulacho chinapitiriza kugwa padziko lapansi kwa masiku 40. Madziwo anachulukirachulukira ndipo anayamba kunyamula chingalawacho, moti chinkayandama pamwamba pa dziko lapansi. 18  Madziwo anapitiriza kuwonjezeka kwambiri padziko lapansi, ndipo chingalawacho chinkayandama pamwamba pa madzi. 19  Madziwo anawonjezeka kwambiri padziko lapansi moti mapiri onse ataliatali amene anali pansi pa thambo anamira.+ 20  Madziwo anakwera kwambiri kupitirira mapiriwo ndi mamita pafupifupi 6 ndi hafu.* 21  Choncho zamoyo zonse zoyenda padziko lapansi, monga zamoyo zouluka, nyama zoweta, nyama zakutchire, ndiponso tizilombo tonse tingʼonotingʼono toyenda mʼmagulu, zinafa+ pamodzi ndi anthu onse.+ 22  Chilichonse chapadziko lapansi chokhala ndi mpweya wa moyo mʼmphuno mwake, chinafa.+ 23  Choncho Mulungu anaseseratu chamoyo chilichonse chimene chinali padziko lapansi, kuyambira munthu, nyama, nyama zokwawa komanso zamoyo zouluka mumlengalenga. Zonsezi anazisesa padziko lapansi.+ Nowa yekha komanso amene anali naye limodzi mʼchingalawacho, anapulumuka.+ 24  Ndipo dziko lapansi linamirabe mʼmadzi kwa masiku 150.+

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “utengepo 7 zazimuna komanso 7 zazikazi.”
Mabaibulo ena amati, “utengepo 7 zazimuna komanso 7 zazikazi.”
“Mwezi wachiwiri” umene ukutchulidwa mʼvesili unadzakhala mwezi wa 8 pakalendala yopatulika imene Yehova anapatsa Aisiraeli atatuluka mʼdziko la Iguputo. Mwezi umenewu, wotchedwa Buli, unkayambira chapakati pa October nʼkutha chapakati pa November. Onani Zakumapeto B15.
Onani mawu amʼmunsi pa Ge 1:24.
Kapena kuti, “mzimu wa moyo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mikono 15.” Onani zakumapeto B14.