Wolembedwa ndi Mateyu 16:1-28

  • Kupempha chizindikiro (1-4)

  • Zofufumitsa za Afarisi ndi Asaduki (5-12)

  • Makiyi a Ufumu (13-20)

    • Mpingo umene udzamangidwe pathanthwe (18)

  • Ananeneratu zokhudza imfa ya Yesu (21-23)

  • Chizindikiro cha ophunzira enieni (24-28)

16  Kenako Afarisi ndi Asaduki anafika kwa Yesu ndipo pofuna kumuyesa, anamupempha kuti awaonetse chizindikiro chochokera kumwamba.+  Koma Yesu anawayankha kuti: “Kunja kukamada mumanena kuti, ‘Nyengo ikhala yabwino, chifukwa kumwamba kwafiira ngati moto.’  Koma mʼmawa mumanena kuti, ‘Lero kukuoneka kuti kugwa mvula, chifukwa kumwamba kwafiira ndipo kuli mitambo.’ Mumadziwa kumasulira kaonekedwe ka kumwamba, koma mukulephera kumasulira zizindikiro za nthawi ino.  Mʼbadwo woipa komanso wachigololo* ukufunitsitsabe chizindikiro, koma sudzapatsidwa chizindikiro chilichonse+ kupatulapo chizindikiro cha Yona chokha.”+ Atanena zimenezi, anachoka nʼkuwasiya.  Kenako ophunzira ake anawolokera kutsidya lina koma anaiwala kutenga mikate.+  Ndiyeno Yesu anawauza kuti: “Khalani maso ndipo musamale ndi chofufumitsa cha Afarisi ndi Asaduki.”+  Koma iwo anayamba kukambirana kuti: “Sitinatenge mikate pobwera kuno.”  Yesu anadziwa zimenezi ndipo ananena kuti: “Achikhulupiriro chochepa inu, nʼchifukwa chiyani mukukambirana kuti mulibe mikate?  Kodi mfundo yake simukuimvetsabe? Kapena kodi simukukumbukira anthu 5,000 amene anadya mitanda 5 ya mikate, komanso kuchuluka kwa madengu amene munatolera a chakudya chimene chinatsala?+ 10  Kapena kodi simukukumbukira anthu 4,000 amene anadya mitanda 7 ya mikate, komanso kuchuluka kwa madengu akuluakulu a chakudya chimene chinatsala amene munatolera?+ 11  Nanga bwanji simukuzindikira kuti sindikunena za mkate, koma zakuti musamale ndi zofufumitsa za Afarisi ndi Asaduki?”+ 12  Atatero anazindikira kuti sakunena zakuti asamale ndi zofufumitsa za mkate, koma kuti asamale ndi zimene Afarisi ndi Asaduki amaphunzitsa. 13  Atafika mʼchigawo cha Kaisareya wa Filipi, Yesu anafunsa ophunzira ake kuti: “Kodi anthu akumanena kuti Mwana wa munthu ndi ndani?”+ 14  Iwo anayankha kuti: “Ena akumanena kuti ndinu Yohane Mʼbatizi,+ ena akumati Eliya,+ koma ena akumanena kuti Yeremiya kapena mmodzi wa aneneri.” 15  Ndiyeno iye anawafunsa kuti: “Nanga inuyo mumati ndine ndani?” 16  Simoni Petulo anayankha kuti: “Ndinu Khristu,+ Mwana wa Mulungu wamoyo.”+ 17  Yesu anamuuza kuti: “Ndiwe wosangalala Simoni mwana wa Yona, chifukwa si munthu* amene wakuululira zimenezi, koma Atate wanga amene ali kumwamba ndi amene wachita zimenezi.+ 18  Choncho inenso ndikukuuza kuti: Iwe ndiwe Petulo+ ndipo pathanthwe+ ili ndidzamangapo mpingo wanga. Mageti a Manda* sadzaugonjetsa. 19  Ine ndidzakupatsa makiyi a Ufumu wakumwamba. Chilichonse chimene udzamanga padziko lapansi chidzakhala chitamangidwa kale kumwamba, ndipo chilichonse chimene udzamasula padziko lapansi chidzakhala chitamasulidwa kale kumwamba.” 20  Ndiyeno analamula ophunzirawo mwamphamvu kuti asauze aliyense kuti iye ndi Khristu.+ 21  Kuyambira nthawi imeneyo, Yesu anayamba kuuza ophunzira ake kuti iyeyo akuyenera kupita ku Yerusalemu. Kumeneko akazunzidwa kwambiri ndi akulu, ansembe aakulu ndi alembi ndipo akaphedwa, koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.+ 22  Ndiyeno Petulo anatengera Yesu pambali nʼkuyamba kumudzudzula kuti: “Dzikomereni mtima Ambuye. Musalole kuti zimenezi zikuchitikireni ngakhale pangʼono.”+ 23  Koma iye anatembenuka nʼkuuza Petulo kuti: “Pita kumbuyo kwanga, Satana! Ndiwe chopunthwitsa kwa ine chifukwa zimene umaganiza si maganizo a Mulungu, koma maganizo a anthu.”+ 24  Kenako Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha ndipo anyamule mtengo wake wozunzikirapo* nʼkupitiriza kunditsatira.+ 25  Chifukwa aliyense amene akufuna kupulumutsa moyo wake adzautaya, koma aliyense amene wataya moyo wake chifukwa cha ine adzaupeza.*+ 26  Kodi munthu angapindule chiyani ngati atapeza zinthu zonse zamʼdzikoli koma nʼkutaya moyo wake?+ Kapena kodi munthu angapereke chiyani choti asinthanitse ndi moyo wake?+ 27  Chifukwa Mwana wa munthu adzabwera mu ulemerero wa Atate wake limodzi ndi angelo ake. Pa nthawi imeneyo adzapereka mphoto kwa aliyense mogwirizana ndi makhalidwe ake.+ 28  Ndithu ndikukuuzani kuti pali ena mwa amene aimirira pano amene sadzalawa imfa mʼpangʼono pomwe mpaka choyamba ataona Mwana wa munthu akubwera monga Mfumu.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “wosakhulupirika.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “mnofu ndi magazi.”
Amenewa ndi manda a anthu onse. Onani Matanthauzo a Mawu ena.
Kapena kuti, “adzakhalanso ndi moyo.”