Wolembedwa ndi Mateyu 9:1-38

  • Yesu anachiritsa munthu wakufa ziwalo (1-8)

  • Yesu anaitana Mateyu (9-13)

  • Funso lokhudza kusala kudya (14-17)

  • Mwana wamkazi wa Yairo; mzimayi anagwira chovala chakunja cha Yesu (18-26)

  • Yesu anachiritsa munthu wosaona komanso wosalankhula (27-34)

  • Zokolola nʼzochuluka, koma antchito ndi ochepa (35-38)

9  Choncho Yesu anakwera ngalawa nʼkuwolokera tsidya lina, ndipo anapita kumzinda umene ankakhala.+  Kumeneko anthu anamubweretsera munthu wakufa ziwalo, atagona pamachira. Yesu ataona chikhulupiriro chawo, anauza wakufa ziwaloyo kuti: “Limba mtima mwanawe! Machimo ako akhululukidwa.”+  Atatero, alembi ena ankanena chamumtima kuti: “Munthu ameneyu akunyoza Mulungu.”  Koma Yesu anadziwa zimene iwo ankaganiza ndipo anawafunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukuganiza zinthu zoipa mʼmitima mwanu?+  Mwachitsanzo, chosavuta nʼchiti, kunena kuti, ‘Machimo ako akhululukidwa,’ kapena kunena kuti, ‘Nyamuka uyendeʼ?+  Dikirani ndikuonetseni kuti Mwana wa munthu ali ndi mphamvu padziko lapansi zokhululukira machimo.” Kenako iye anauza wakufa ziwalo uja kuti: “Nyamuka, tenga machira akowa ndipo uzipita kwanu.”+  Ndipo ananyamuka nʼkupita kwawo.  Gulu la anthulo litaona zimenezi, linagwidwa ndi mantha ndipo linatamanda Mulungu, amene anapereka mphamvu zimenezo kwa anthu.  Atachoka pamenepo, Yesu anaona munthu wina dzina lake Mateyu atakhala mu ofesi yokhomeramo msonkho, ndipo anamuuza kuti: “Ukhale wotsatira wanga.” Nthawi yomweyo ananyamuka nʼkumutsatira.+ 10  Nthawi inayake, pamene ankadya chakudya* mʼnyumba ina, kunabwera anthu ambiri okhometsa msonkho komanso ochimwa ndipo anayamba kudya* limodzi ndi Yesu ndi ophunzira ake.+ 11  Koma Afarisi ataona zimenezi anafunsa ophunzira ake kuti: “Nʼchifukwa chiyani mphunzitsi wanu amadya limodzi ndi anthu okhometsa msonkho komanso ochimwa?”+ 12  Iye atamva zimenezo, anayankha kuti: “Anthu abwinobwino safunikira dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna.+ 13  Choncho pitani mukaphunzire tanthauzo la mawu akuti: ‘Ndikufuna chifundo, osati nsembe.’+ Chifukwa ine sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa.” 14  Kenako ophunzira a Yohane anabwera kwa iye nʼkumufunsa kuti: “Nʼchifukwa chiyani ife ndi Afarisi timasala kudya koma ophunzira anu sasala kudya?”+ 15  Yesu anawayankha kuti: “Anzake a mkwati samva chisoni ngati mkwatiyo+ ali nawo limodzi, si choncho kodi? Koma masiku akubwera pamene mkwatiyo adzachotsedwa pakati pawo+ ndipo pa nthawiyo adzasala kudya. 16  Palibe amene amasokerera chigamba cha nsalu yatsopano pamalaya akunja akale. Chifukwa chigambacho chingakoke nʼkungʼamba malayawo ndipo kungʼambikako kungawonjezeke kwambiri.+ 17  Ndiponso anthu sathira vinyo watsopano mʼmatumba achikopa akale. Akachita zimenezo, matumba achikopawo amaphulika ndipo vinyoyo amatayika moti matumbawo amawonongeka. Koma anthu amathira vinyo watsopano mʼmatumba achikopa atsopano, ndipo zonse ziwiri zimasungika bwino.” 18  Pamene ankawauza zimenezi, wolamulira wina anamuyandikira. Kenako anamugwadira nʼkunena kuti: “Panopa mwana wanga wamkazi ayenera kuti wamwalira kale. Koma tiyeni mukamukhudze ndi dzanja lanu ndipo akhala ndi moyo.”+ 19  Kenako Yesu ananyamuka ndi ophunzira ake nʼkumutsatira. 20  Ndiyeno mayi wina amene ankadwala matenda otaya magazi kwa zaka 12+ anafika kumbuyo kwake nʼkugwira ulusi wopota wamʼmphepete mwa malaya ake akunja,+ 21  chifukwa mumtima mwake ankanena kuti: “Ndikangogwira malaya ake akunja okhawo, ndichira ndithu.” 22  Yesu anatembenuka ndipo anaona mayiyo nʼkunena kuti: “Mwanawe, limba mtima, chikhulupiriro chako chakuchiritsa.”+ Kuchokera pa ola limenelo mayiyo anachira.+ 23  Ndiyeno atalowa mʼnyumba ya wolamulira uja, anaona anthu akuliza zitoliro komanso gulu la anthu likulira mofuula.+ 24  Yesu anawauza kuti: “Tulukani muno, chifukwa mtsikanayu sanamwalire, koma akugona.”+ Atanena zimenezi, anthuwo anayamba kumuseka monyoza. 25  Anthu aja atawatulutsa panja, Yesu analowa nʼkugwira dzanja la mtsikanayo,+ ndipo iye anadzuka.+ 26  Nkhani imeneyi inamveka mʼdera lonselo. 27  Yesu akuchokera kumeneko, amuna awiri amene anali ndi vuto losaona+ anamutsatira akufuula kuti: “Mutichitire chifundo, Mwana wa Davide.” 28  Yesu atalowa mʼnyumba, amuna amene anali ndi vuto losaona aja anabwera kwa iye, ndipo anawafunsa kuti: “Kodi mukukhulupirira kuti ndingachite zimenezi?”+ Iwo anamuyankha kuti: “Inde, Ambuye.” 29  Kenako anawagwira mʼmaso+ nʼkunena kuti: “Mogwirizana ndi chikhulupiriro chanu zimene mukufunazo zichitike kwa inu.” 30  Maso awo anatseguka ndipo Yesu anawachenjeza mwamphamvu kuti: “Samalani, aliyense asadziwe zimenezi.”+ 31  Koma iwo atatuluka kunja, anafalitsa paliponse zokhudza iye mʼdera lonselo. 32  Pamene amuna awiriwo ankanyamuka, anthu anamubweretsera munthu wosalankhula amene anagwidwa ndi chiwanda.+ 33  Atatulutsa chiwandacho, munthu wosalankhulayo analankhula,+ moti gulu la anthulo linadabwa ndipo linanena kuti: “Zoterezi sizinaonekepo nʼkale lonse mu Isiraeli.”+ 34  Koma Afarisi ankanena kuti: “Ameneyu amatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya wolamulira ziwanda.”+ 35  Ndiyeno Yesu anayamba ulendo woyendera mizinda ndi midzi yonse. Iye ankaphunzitsa mʼmasunagoge awo komanso kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu ndipo ankachiritsa matenda amtundu uliwonse amene anthu ankadwala.+ 36  Ataona chigulu cha anthu, iye anawamvera chisoni,+ chifukwa anali onyukanyuka komanso opanda wowasamalira ngati nkhosa zimene zilibe mʼbusa.+ 37  Kenako anauza ophunzira ake kuti: “Inde, pali zinthu zambiri zofunika kukolola, koma antchito ndi ochepa.+ 38  Choncho pemphani Mwiniwake wa munda kuti atumize antchito kukakolola.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “atakhala patebulo.”
Kapena kuti, “anakhala patebulo.”