Wolembedwa ndi Mateyu 7:1-29

  • ULALIKI WAPAPHIRI (1-27)

    • Siyani kuweruza (1-6)

    • Pitirizani kupempha, kufunafuna, kugogoda (7-11)

    • Muzichitira anthu zimene mukufuna kuti akuchitireni (12)

    • Geti lalingʼono (13, 14)

    • Amadziwika ndi zipatso zawo (15-23)

    • Nyumba yapathanthwe, nyumba yapamchenga (24-27)

  • Gulu la anthu linadabwa ndi kaphunzitsidwe ka Yesu (28, 29)

7  “Siyani kuweruza ena+ kuti inunso musaweruzidwe,  chifukwa mmene mumaweruzira ena inunso adzakuweruzani choncho.+ Ndipo muyezo umene mukuyezera ena iwonso adzakuyezerani womwewo.+  Nanga nʼchifukwa chiyani umayangʼana kachitsotso mʼdiso la mʼbale wako, koma osaona mtanda wa denga la nyumba umene uli mʼdiso lako?+  Kapena ungauze bwanji mʼbale wako kuti, ‘Taima ndikuchotse kachitsotso mʼdiso lako,’ pamene iwe mʼdiso lako muli mtanda wa denga la nyumba?  Wachinyengo iwe! Yamba wachotsa mtanda wa denga la nyumba umene uli mʼdiso lakowo. Ukatero udzatha kuona bwino moti udzakwanitsa kuchotsa kachitsotso mʼdiso la mʼbale wako.  Musamapatse agalu zinthu zopatulika, kapena kuponyera nkhumba ngale zanu,+ kuopera kuti zingapondeponde ngalezo kenako zingatembenuke nʼkukukhadzulani.  Pitirizani kupempha ndipo adzakupatsani.+ Pitirizani kufunafuna ndipo mudzapeza. Pitirizani kugogoda ndipo adzakutsegulirani.+  Chifukwa aliyense wopempha amalandira,+ aliyense wofunafuna amapeza, ndipo aliyense wogogoda adzamutsegulira.  Inde, ndi ndani wa inu amene mwana wake atamupempha mkate angamupatse mwala? 10  Kapena atamupempha nsomba, kodi angamupatse njoka? 11  Choncho ngati inuyo mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, ngakhale kuti ndinu oipa, kuli bwanji Atate wanu wakumwamba? Ndithudi, iye adzapereka mowolowa manja zinthu zabwino+ kwa amene akumupempha.+ 12  Choncho zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akuchitireni, inunso muwachitire zomwezo.+ Zimenezi ndi zomwe Chilamulo chimafuna komanso zimene aneneri analemba.+ 13  Lowani pageti lalingʼono.+ Chifukwa msewu umene ukupita kuchiwonongeko ndi wotakasuka komanso geti lake ndi lalikulu ndipo anthu ambiri akudzera pageti limenelo. 14  Koma geti lolowera ku moyo ndi lalingʼono komanso msewu wake ndi wopanikiza ndipo amene akuupeza ndi ochepa.+ 15  Chenjerani ndi aneneri abodza+ amene amabwera kwa inu atavala ngati nkhosa,+ koma mkati mwa mitima yawo ali ngati mimbulu yolusa.+ 16  Mudzawazindikira chifukwa cha zipatso zawo. Anthu sathyola mphesa paminga kapena nkhuyu pamtengo wa nthula, amatero kodi?+ 17  Mofanana ndi zimenezi, mtengo uliwonse wabwino umabereka zipatso zabwino, koma mtengo uliwonse wovunda umabereka zipatso zopanda pake.+ 18  Mtengo wabwino sungabereke zipatso zopanda pake ndipo mtengo wovunda sungabereke zipatso zabwino.+ 19  Mtengo uliwonse umene subereka zipatso zabwino amaudula nʼkuuponya pamoto.+ 20  Choncho anthu amenewo mudzawazindikira chifukwa cha zipatso zawo.+ 21  Sikuti aliyense amene amanditchula kuti, ‘Ambuye, Ambuye,’ adzalowa Ufumu wakumwamba, koma yekhayo amene akuchita zimene Atate wanga wakumwamba amafuna.+ 22  Pa tsiku limenelo ambiri adzandiuza kuti: ‘Ambuye, Ambuye,+ kodi ife sitinalosere mʼdzina lanu ndi kutulutsa ziwanda mʼdzina lanu ndiponso kuchita ntchito zambiri zamphamvu mʼdzina lanu?’+ 23  Koma ine ndidzawauza kuti: ‘Sindikukudziwani ngakhale pangʼono! Chokani pamaso panga, anthu osamvera malamulo inu.’+ 24  Choncho aliyense amene wamva mawu angawa nʼkuchita zimene wamvazo, adzafanana ndi munthu wanzeru, amene anamanga nyumba yake pathanthwe.+ 25  Ndiyeno kunagwa chimvula champhamvu ndipo madzi anasefukira. Kenako chimphepo chinawomba mwamphamvu, koma nyumbayo sinagwe chifukwa chakuti inakhazikika pathanthwepo. 26  Aliyense amene wamva mawu angawa koma osachita zimene wamvazo adzafanana ndi munthu wopusa amene anamanga nyumba yake pamchenga.+ 27  Ndiye kunagwa chimvula champhamvu ndipo madzi anasefukira. Kenako chimphepo chinawomba mwamphamvu moti nyumbayo inagwa+ ndipo kugwa kwake kunali kwakukulu.” 28  Yesu atamaliza kulankhula mawu amenewa, gulu la anthulo linakhudzidwa moti linadabwa ndi kaphunzitsidwe kake,+ 29  chifukwa ankawaphunzitsa monga munthu waulamuliro,+ osati ngati alembi awo.

Mawu a M'munsi