Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Mateyu

Machaputala

Mitu

 • 1

  • Mzere wa makolo a Yesu Khristu (1-17)

  • Kubadwa kwa Yesu (18-25)

 • 2

  • Okhulupirira nyenyezi anapita kukamuona (1-12)

  • Anathawira ku Iguputo (13-15)

  • Herode anapha ana aamuna (16-18)

  • Anabwerera ku Nazareti (19-23)

 • 3

  • Yohane Mʼbatizi ankalalikira (1-12)

  • Ubatizo wa Yesu (13-17)

 • 4

  • Mdyerekezi anayesa Yesu (1-11)

  • Yesu anayamba kulalikira ku Galileya (12-17)

  • Anasankha ophunzira oyambirira (18-22)

  • Yesu ankalalikira, kuphunzitsa komanso kuchiritsa (23-25)

 • 5

  • ULALIKI WAPAPHIRI (1-48)

   • Yesu anayamba kuphunzitsa paphiri (1, 2)

   • Zinthu 9 zimene zimapangitsa anthu kuti azikhala osangalala (3-12)

   • Mchere komanso kuwala (13-16)

   • Yesu anakwaniritsa Chilamulo (17-20)

   • Malangizo okhudza mkwiyo (21-26), chigololo (27-30), kutha kwa ukwati (31, 32), malumbiro (33-37), kubwezera (38-42), kukonda adani athu (43-48)

 • 6

  • ULALIKI WAPAPHIRI (1-34)

   • Muzipewa kudzionetsera kuti ndinu olungama (1-4)

   • Mmene tingapempherere (5-15)

    • Pemphero la chitsanzo (9-13)

   • Kusala kudya (16-18)

   • Chuma padziko lapansi komanso kumwamba (19-24)

   • Siyani kuda nkhawa (25-34)

    • Nthawi zonse muziika Ufumu pamalo oyamba (33)

 • 7

  • ULALIKI WAPAPHIRI (1-27)

   • Siyani kuweruza (1-6)

   • Pitirizani kupempha, kufunafuna, kugogoda (7-11)

   • Muzichitira anthu zimene mukufuna kuti akuchitireni (12)

   • Geti lalingʼono (13, 14)

   • Amadziwika ndi zipatso zawo (15-23)

   • Nyumba yapathanthwe, nyumba yapamchenga (24-27)

  • Gulu la anthu linadabwa ndi kaphunzitsidwe ka Yesu (28, 29)

 • 8

  • Anachiritsa munthu wakhate (1-4)

  • Chikhulupiriro cha mtsogoleri wa asilikali (5-13)

  • Yesu anachiritsa anthu ambiri ku Kaperenao (14-17)

  • Zimene tingachite kuti tizitsatira Yesu (18-22)

  • Yesu analetsa mphepo yamphamvu (23-27)

  • Yesu anatumiza ziwanda munkhumba (28-34)

 • 9

  • Yesu anachiritsa munthu wakufa ziwalo (1-8)

  • Yesu anaitana Mateyu (9-13)

  • Funso lokhudza kusala kudya (14-17)

  • Mwana wamkazi wa Yairo; mzimayi anagwira chovala chakunja cha Yesu (18-26)

  • Yesu anachiritsa munthu wosaona komanso wosalankhula (27-34)

  • Zokolola nʼzochuluka, koma antchito ndi ochepa (35-38)

 • 10

  • Atumwi 12 (1-4)

  • Malangizo okhudza kulalikira (5-15)

  • Ophunzira adzazunzidwa (16-25)

  • Muziopa Mulungu, osati anthu (26-31)

  • Osati mtendere, koma lupanga (32-39)

  • Kulandira ophunzira a Yesu (40-42)

 • 11

  • Yohane Mʼbatizi analemekezedwa (1-15)

  • Anadzudzula mʼbadwo wosamvera (16-24)

  • Yesu anatamanda Atate wake chifukwa chokomera mtima anthu wamba (25-27)

  • Goli la Yesu limatsitsimula (28-30)

 • 12

  • Yesu ndi “Mbuye wa Sabata” (1-8)

  • Anachiritsa munthu wolumala dzanja (9-14)

  • Mtumiki amene Mulungu amamukonda (15-21)

  • Anatulutsa ziwanda pogwiritsa ntchito mzimu woyera (22-30)

  • Tchimo losakhululukidwa (31, 32)

  • Mtengo umadziwika ndi zipatso zake (33-37)

  • Chizindikiro cha Yona (38-42)

  • Mzimu wonyansa ukabwerera (43-45)

  • Amayi ake a Yesu komanso azichimwene ake (46-50)

 • 13

  • MAFANIZO OKHUDZA UFUMU (1-52)

   • Wofesa mbewu (1-9)

   • Chifukwa chake Yesu ankagwiritsa ntchito mafanizo (10-17)

   • Tanthauzo la fanizo la wofesa mbewu (18-23)

   • Tirigu ndi namsongole (24-30)

   • Kanjere kampiru komanso zofufumitsa (31-33)

   • Kugwiritsa ntchito mafanizo kunakwaniritsa ulosi (34, 35)

   • Tanthauzo la fanizo la tirigu ndi namsongole (36-43)

   • Chuma chobisika ndi ngale yamtengo wapatali (44-46)

   • Khoka (47-50)

   • Chuma chatsopano ndi chakale (51, 52)

  • Yesu anakanidwa mʼdera lakwawo (53-58)

 • 14

  • Yohane Mʼbatizi anadulidwa mutu (1-12)

  • Yesu anadyetsa anthu 5,000 (13-21)

  • Yesu anayenda pamadzi (22-33)

  • Anachiritsa anthu ku Genesareti (34-36)

 • 15

  • Anadzudzula miyambo ya makolo (1-9)

  • Zodetsa zimachokera mumtima (10-20)

  • Chikhulupiriro cholimba cha mayi wa ku Foinike (21-28)

  • Yesu anachiritsa matenda ambiri (29-31)

  • Yesu anadyetsa anthu 4,000 (32-39)

 • 16

  • Kupempha chizindikiro (1-4)

  • Zofufumitsa za Afarisi ndi Asaduki (5-12)

  • Makiyi a Ufumu (13-20)

   • Mpingo umene udzamangidwe pathanthwe (18)

  • Ananeneratu zokhudza imfa ya Yesu (21-23)

  • Chizindikiro cha ophunzira enieni (24-28)

 • 17

  • Yesu anasintha maonekedwe (1-13)

  • Chikhulupiriro chofanana ndi kanjere ka mpiru (14-21)

  • Yesu ananeneratunso zokhudza imfa yake (22, 23)

  • Anapereka msonkho pogwiritsa ntchito ndalama yamkamwa mwa nsomba (24-27)

 • 18

  • Wamkulu kwambiri mu Ufumu (1-6)

  • Zopunthwitsa (7-11)

  • Fanizo la nkhosa yosochera (12-14)

  • Zimene tingachite kuti tibweze mʼbale wathu (15-20)

  • Fanizo la kapolo wosakhululuka (21-35)

 • 19

  • Ukwati komanso kutha kwa banja (1-9)

  • Mphatso ya kusakwatira (10-12)

  • Yesu anadalitsa ana (13-15)

  • Funso limene wachinyamata wolemera anafunsa (16-24)

  • Zinthu zimene tiyenera kudzimana chifukwa cha Ufumu (25-30)

 • 20

  • Anthu amene ankagwira ntchito mʼmunda wampesa analandira malipiro ofanana (1-16)

  • Yesu ananeneratunso zokhudza imfa yake (17-19)

  • Anapempha kuti adzapatsidwe malo apadera mu Ufumu (20-28)

   • Yesu anapereka dipo kuwombola anthu ambiri (28)

  • Amuna awiri osaona anachiritsidwa (29-34)

 • 21

  • Yesu analowa mumzinda mwaulemerero (1-11)

  • Yesu anayeretsa kachisi (12-17)

  • Anatemberera mtengo wa mkuyu (18-22)

  • Anakayikira ulamuliro wa Yesu (23-27)

  • Fanizo la ana awiri aamuna (28-32)

  • Fanizo la alimi amene anapha anthu (33-46)

   • Mwala wofunika kwambiri wapakona unakanidwa (42)

 • 22

  • Fanizo la phwando laukwati (1-14)

  • Mulungu komanso Kaisara (15-22)

  • Funso lokhudza kuukitsidwa kwa akufa (23-33)

  • Malamulo awiri akuluakulu (34-40)

  • Kodi Khristu ndi mwana wa Davide? (41-46)

 • 23

  • Musamatsanzire alembi ndi Afarisi (1-12)

  • Tsoka kwa alembi ndi Afarisi (13-36)

  • Yesu analirira Yerusalemu (37-39)

 • 24

  • CHIZINDIKIRO CHA KUKHALAPO KWA KHRISTU (1-51)

   • Nkhondo, njala, zivomerezi (7)

   • Uthenga wabwino udzalalikidwa (14)

   • Chisautso chachikulu (21, 22)

   • Chizindikiro cha Mwana wa munthu (30)

   • Mtengo wa mkuyu (32-34)

   • Mofanana ndi masiku a Nowa (37-39)

   • Khalanibe maso (42-44)

   • Kapolo wokhulupirika komanso kapolo woipa (45-51)

 • 25

  • CHIZINDIKIRO CHA KUKHALAPO KWA KHRISTU (1-46)

   • Fanizo la anamwali 10 (1-13)

   • Fanizo la matalente (14-30)

   • Nkhosa komanso mbuzi (31-46)

 • 26

  • Ansembe anakonza chiwembu kuti aphe Yesu (1-5)

  • Yesu anathiridwa mafuta onunkhira (6-13)

  • Pasika womaliza komanso kuperekedwa (14-25)

  • Anayambitsa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye (26-30)

  • Ananeneratu kuti Petulo adzamukana (31-35)

  • Yesu anapemphera ku Getsemane (36-46)

  • Yesu anagwidwa (47-56)

  • Anazengedwa mlandu ndi Khoti Lalikulu la Ayuda (57-68)

  • Petulo anakana Yesu (69-75)

 • 27

  • Yesu anaperekedwa kwa Pilato (1, 2)

  • Yudasi anadzimangirira (3-10)

  • Yesu anaonekera kwa Pilato (11-26)

  • Anamuchitira zachipongwe pamaso pa anthu (27-31)

  • Anamukhomerera pamtengo ku Gologota (32-44)

  • Imfa ya Yesu (45-56)

  • Kuikidwa mʼmanda kwa Yesu (57-61)

  • Anakhwimitsa chitetezo pamanda ake (62-66)

 • 28

  • Yesu anaukitsidwa (1-10)

  • Asilikali anapatsidwa ndalama kuti aname (11-15)

  • Analamulidwa kuti azithandiza anthu kuti akhale ophunzira (16-20)