Wolembedwa ndi Mateyu 28:1-20

  • Yesu anaukitsidwa (1-10)

  • Asilikali anapatsidwa ndalama kuti aname (11-15)

  • Analamulidwa kuti azithandiza anthu kuti akhale ophunzira (16-20)

28  Tsiku la Sabata litatha, mʼbandakucha wa tsiku loyamba la mlunguwo, Mariya wa ku Magadala ndi Mariya wina uja anabwera kudzaona manda.+  Atafika pafupi, anazindikira kuti pachitika chivomerezi champhamvu, chifukwa mngelo wa Yehova* anatsika kumwamba ndipo anafika nʼkugubuduza chimwala chija, nʼkukhala pachimwalapo.+  Mngeloyo ankaoneka ngati mphezi ndipo zovala zake zinali zoyera kwambiri.+  Alonda aja anachita mantha ndi mngeloyo ndipo ananjenjemera nʼkuuma gwa ngati afa.  Koma mngeloyo anauza azimayiwo kuti: “Inu musachite mantha, chifukwa ndikudziwa kuti mukufuna Yesu amene anaphedwa popachikidwa pamtengo.+  Muno mulibe chifukwa waukitsidwa mogwirizana ndi zimene ananena.+ Bwerani muone pamene anagona.  Ndipo pitani mwamsanga mukauze ophunzira ake kuti waukitsidwa kwa akufa, moti panopa watsogola kupita ku Galileya.+ Kumeneko mukamuona. Umenewutu ndi uthenga wanga kwa inu.”+  Choncho iwo anachoka mwamsanga pamandapo ali ndi mantha ndiponso chimwemwe chochuluka ndipo anathamanga kukauza ophunzira ake.+  Mwadzidzidzi Yesu anakumana nawo nʼkunena kuti: “Moni azimayi!” Kenako iwo anafika pafupi nʼkugwira mapazi ake ndipo anamuweramira mpaka nkhope zawo pansi. 10  Kenako Yesu anawauza kuti: “Musaope! Pitani mukauze abale anga kuti apite ku Galileya ndipo akandiona kumeneko.” 11  Iwo akupita, ena mwa alonda+ anapita mumzinda ndipo anakauza ansembe aakulu zonse zimene zinachitika. 12  Ansembe aakuluwo atakumana ndi akulu nʼkukambirana, anagwirizana zochita ndipo anapereka ndalama zasiliva zambiri kwa asilikaliwo 13  nʼkuwauza kuti: “Muzinena kuti, ‘Ophunzira ake anabwera usiku kudzamuba ife titagona.’+ 14  Ngati bwanamkubwa atamva zimenezi, timufotokozera nkhani yonse* ndipo inu simukuyenera kuda nkhawa.” 15  Choncho anatenga ndalama zasilivazo nʼkuchita mogwirizana ndi zimene anawauza ndipo nkhani imeneyi ndi yofala kwambiri pakati pa Ayuda mpaka lero. 16  Koma ophunzira 11 aja anapita ku Galileya,+ kuphiri kumene Yesu anawauza kuti akakumane nawo.+ 17  Atamuona anamugwadira, koma ena anakayikira ngati analidi iyeyo. 18  Tsopano Yesu anayandikira nʼkuwauza kuti: “Ulamuliro wonse waperekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.+ 19  Choncho pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzira anga.+ Muziwabatiza+ mʼdzina la Atate, la Mwana ndi la mzimu woyera, 20  ndipo muziwaphunzitsa kuti azisunga zinthu zonse zimene ndinakulamulani.+ Ndipo dziwani kuti ine ndili limodzi ndi inu masiku onse mpaka mʼnyengo ya mapeto a nthawi* ino.”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “timunyengerera.”