Wolembedwa ndi Mateyu 19:1-30

  • Ukwati komanso kutha kwa banja (1-9)

  • Mphatso ya kusakwatira (10-12)

  • Yesu anadalitsa ana (13-15)

  • Funso limene wachinyamata wolemera anafunsa (16-24)

  • Zinthu zimene tiyenera kudzimana chifukwa cha Ufumu (25-30)

19  Yesu atamaliza kulankhula zinthu zimenezi, anachoka ku Galileya nʼkupita kumalire a Yudeya kutsidya lina la Yorodano.+  Gulu lalikulu la anthu linamutsatira kumeneko ndipo iye anawachiritsa.  Ndiyeno Afarisi anabwera kwa iye nʼcholinga chodzamuyesa ndipo anamufunsa kuti: “Kodi nʼzololeka kuti mwamuna asiye mkazi wake pa chifukwa chilichonse?”+  Yesu anayankha kuti: “Kodi simunawerenge kuti amene analenga anthu pachiyambi anawalenga mwamuna ndi mkazi+  nʼkunena kuti: ‘Chifukwa cha zimenezi mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake nʼkudziphatika kwa mkazi wake ndipo awiriwo adzakhala thupi limodziʼ?+  Moti sakhalanso kuti ndi awiri, koma thupi limodzi. Choncho chimene Mulungu wachimanga pamodzi,* munthu asachilekanitse.”+  Iwo anamufunsa kuti: “Nanga nʼchifukwa chiyani Mose analamula kuti mwamuna azipereka kalata yothetsera ukwati kwa mkazi nʼkumusiya?”+  Iye anawayankha kuti: “Chifukwa cha kuuma mtima kwanu, Mose anakulolezani kuti muzithetsa ukwati,+ koma kuyambira pachiyambi sizinali choncho.+  Ine ndikukuuzani kuti aliyense amene wasiya mkazi wake nʼkukwatira wina wachita chigololo, kupatulapo ngati wamusiya chifukwa cha chiwerewere.”*+ 10  Kenako ophunzira ake ananena kuti: “Ngati zili choncho kwa munthu ndi mkazi wake, ndiyetu ndi bwino osakwatira.” 11  Iye anawauza kuti: “Si onse amene angathe kuchita zimenezi, koma okhawo amene ali ndi mphatso.+ 12  Chifukwa ena sakwatira chifukwa chakuti anabadwa choncho ndipo ena chifukwa chakuti anafulidwa ndi anthu. Koma pali ena amene safuna kukwatira chifukwa cha Ufumu wakumwamba. Amene angathe kuchita zimenezi achite.”+ 13  Kenako anthu anamubweretsera ana aangʼono kuti awaike manja nʼkuwapempherera, koma ophunzirawo anawakalipira.+ 14  Koma Yesu anawauza kuti: “Asiyeni anawo ndipo musawaletse kuti abwere kwa ine, chifukwa Ufumu wakumwamba ndi wa anthu ngati amenewa.”+ 15  Ndiyeno anaika manja ake pa anawo kenako anachoka kumeneko. 16  Tsopano munthu wina anabwera kwa iye nʼkumufunsa kuti: “Mphunzitsi, kodi ndi zinthu zabwino ziti zimene ndikuyenera kuchita kuti ndikapeze moyo wosatha?”+ 17  Iye anamuyankha kuti: “Nʼchifukwa chiyani ukundifunsa zokhudza zinthu zabwino? Pali mmodzi yekha amene ndi wabwino.+ Choncho ngati ukufuna kukapeza moyo, uzisunga malamulo nthawi zonse.”+ 18  Iye anafunsa kuti: “Malamulo ake ati?” Yesu anayankha kuti: “Musaphe munthu,*+ musachite chigololo,+ musabe,+ musapereke umboni wabodza.+ 19  Muzilemekeza bambo anu ndi mayi anu,+ komanso lakuti, Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”+ 20  Mnyamatayo anayankha Yesu kuti: “Ndakhala ndikutsatira zonsezi, nʼchiyaninso china chimene ndikuyenera kuchita?” 21  Yesu anamuuza kuti: “Ngati ukufuna kukhala wangwiro,* pita ukagulitse katundu wako yense ndipo ndalama zake ukapatse osauka. Ukatero udzakhala ndi chuma kumwamba,+ ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.”+ 22  Mnyamatayo atamva zimenezi anachoka ali ndi chisoni, chifukwa anali ndi katundu wambiri.+ 23  Ndiyeno Yesu anauza ophunzira ake kuti: “Ndithu ndikukuuzani, zidzakhala zovuta kuti munthu wolemera adzalowe mu Ufumu wakumwamba.+ 24  Ndiponso ndikukuuzani kuti, nʼzosavuta kuti ngamila ilowe pakabowo ka singano kusiyana nʼkuti munthu wolemera alowe mu Ufumu wa Mulungu.”+ 25  Ophunzirawo atamva zimenezi, anadabwa kwambiri ndipo anafunsa kuti: “Ndiye angapulumuke ndi ndani?”+ 26  Yesu anawayangʼanitsitsa nʼkuwauza kuti: “Kwa anthu zimenezi nʼzosatheka, koma zinthu zonse nʼzotheka kwa Mulungu.”+ 27  Kenako Petulo ananena kuti: “Taonani! Ife tasiya zinthu zonse nʼkukutsatirani, ndiye kodi tidzapeza chiyani?”+ 28  Yesu anawauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani, pa nthawi ya kulenganso zinthu, Mwana wa munthu adzakhala pampando wake wachifumu waulemerero, inu amene mwakhala mukunditsatira mudzakhalanso mʼmipando yachifumu 12, nʼkumaweruza mafuko 12 a Isiraeli.+ 29  Aliyense amene wasiya nyumba, azichimwene, azichemwali, abambo, amayi, ana kapena minda chifukwa cha dzina langa adzalandira zochuluka kuwirikiza maulendo 100 kuposa zimenezi ndiponso adzapeza moyo wosatha.+ 30  Koma ambiri amene ali oyamba adzakhala omaliza ndipo omaliza adzakhala oyamba.”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “wachimanga mugoli limodzi.”
MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kupha uku ndi kupha munthu mwachiwembu osati mwalamulo.
Kapena kuti, “kukhala wokwanira pamaso pa Mulungu.”