Wolembedwa ndi Mateyu 5:1-48

 • ULALIKI WAPAPHIRI (1-48)

  • Yesu anayamba kuphunzitsa paphiri (1, 2)

  • Zinthu 9 zimene zimapangitsa anthu kuti azikhala osangalala (3-12)

  • Mchere komanso kuwala (13-16)

  • Yesu anakwaniritsa Chilamulo (17-20)

  • Malangizo okhudza mkwiyo (21-26), chigololo (27-30), kutha kwa ukwati (31, 32), malumbiro (33-37), kubwezera (38-42), kukonda adani athu (43-48)

5  Yesu ataona gulu la anthu, anakwera mʼphiri ndipo atakhala pansi, ophunzira ake anabwera kwa iye.  Kenako anayamba kuwaphunzitsa kuti:  “Osangalala ndi anthu amene amazindikira zosowa zawo zauzimu+ chifukwa Ufumu wakumwamba ndi wawo.  Osangalala ndi anthu amene akumva chisoni chifukwa adzalimbikitsidwa.+  Osangalala ndi anthu ofatsa+ chifukwa adzalandira dziko lapansi.+  Osangalala ndi anthu amene akumva njala ndi ludzu+ la chilungamo chifukwa adzakhuta.+  Osangalala ndi anthu achifundo+ chifukwa adzachitiridwa chifundo.  Osangalala ndi anthu oyera mtima+ chifukwa adzaona Mulungu.  Osangalala ndi anthu amene amabweretsa mtendere+ chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu. 10  Osangalala ndi anthu amene azunzidwa chifukwa cha chilungamo+ chifukwa Ufumu wakumwamba ndi wawo. 11  Ndinu osangalala pamene anthu akukunyozani,+ kukuzunzani komanso kukunamizirani+ zoipa zilizonse chifukwa cha ine.+ 12  Sangalalani ndi kukondwera+ kwambiri chifukwa mphoto+ imene Mulungu adzakupatseni ndi yaikulu,* ndipo umu ndi mmenenso anazunzira aneneri amene analipo inu musanakhaleko.+ 13  Inu ndinu mchere+ wa dziko lapansi. Koma ngati mchere watha mphamvu, kodi mphamvu yakeyo angaibwezeretse bwanji? Sungagwirenso ntchito iliyonse koma ungafunike kungoutaya kunja+ kuti anthu azikaupondaponda. 14  Inu ndinu kuwala kwa dziko.+ Mzinda ukakhala paphiri subisika. 15  Anthu akayatsa nyale saivindikira ndi dengu, koma amaiika pachoikapo nyale ndipo imaunikira onse mʼnyumbamo.+ 16  Mofanana ndi zimenezi, nanunso muzionetsa kuwala kwanu pamaso pa anthu,+ kuti aone ntchito zanu zabwino+ nʼkulemekeza Atate wanu wakumwamba.+ 17  Musaganize kuti ndinabwera kudzawononga Chilamulo kapena zimene aneneri analemba. Sindinabwere kudzaziwononga koma kudzazikwaniritsa.+ 18  Ndithu ndikukuuzani kuti kumwamba ndi dziko lapansi zingachoke mosavuta, kusiyana nʼkuti chilembo chimodzi chachingʼono kwambiri kapena kachigawo kakangʼono ka chilembo cha mʼChilamulo kachoke zinthu zonse zisanachitike.+ 19  Choncho aliyense amene waphwanya lililonse la malamulo aangʼono awa nʼkumaphunzitsanso ena kuchita zomwezo, adzakhala wosayenera kulowa mu Ufumu wakumwamba. Koma aliyense wotsatira ndi kuphunzitsa malamulowa adzakhala woyenera kulowa mu Ufumu wakumwamba. 20  Ndikukuuzani kuti ngati chilungamo chanu sichimaposa cha alembi ndi Afarisi,+ ndithu simudzalowa mu Ufumu wakumwamba.+ 21  Inu munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti: ‘Musaphe munthu.+ Aliyense amene wapha munthu wapalamula mlandu wa kukhoti.’+ 22  Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense wopitiriza kupsera mtima+ mʼbale wake wapalamula mlandu wa kukhoti. Ndipo aliyense wonenera mʼbale wake mawu achipongwe wapalamula mlandu wa ku Khoti Lalikulu. Komanso aliyense wonena mnzake kuti, ‘Ndiwe chitsiru!’ adzapita ku Gehena* wamoto.+ 23  Ndiye ngati wabweretsa mphatso yako paguwa lansembe,+ ndipo uli pomwepo wakumbukira kuti mʼbale wako ali nawe chifukwa, 24  siya mphatso yako patsogolo pa guwa lansembe pomwepo nʼkuchokapo. Choyamba pita ukakhazikitse mtendere ndi mʼbale wakoyo. Kenako ukabwerenso nʼkudzapereka mphatso yakoyo.+ 25  Uzithetsa nkhani mofulumira ndi munthu wokuimba mlandu pamene ukupita naye kukhoti, kuti mwina wokuimba mlanduyo asakakupereke kwa woweruza. Komanso kuti woweruzayo asakakupereke kwa msilikali wakukhoti kuti akuponye mʼndende.+ 26  Kunena zoona, sudzatulukamo mpaka utalipira kakhobidi kotsirizira kochepa mphamvu kwambiri.* 27  Inu munamva kuti anati: ‘Musachite chigololo.’+ 28  Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense woyangʼanitsitsa mkazi+ mpaka kumulakalaka, wachita naye kale chigololo mumtima mwake.+ 29  Ndiye ngati diso lako lakumanja limakuchimwitsa,* ulikolowole nʼkulitaya.+ Chifukwa ndi bwino kuti ukhale wopanda chiwalo chimodzi kusiyana ndi kuti thupi lako lonse lidzaponyedwe mʼGehena.*+ 30  Komanso ngati dzanja lako lamanja limakuchimwitsa, ulidule nʼkulitaya.+ Chifukwa ndi bwino kuti ukhale wopanda chiwalo chimodzi kusiyana ndi kuti thupi lako lonse lidzaponyedwe mʼGehena.*+ 31  Pajanso anati: ‘Aliyense amene akuthetsa ukwati ndi mkazi wake, azipatsa mkaziyo kalata yothetsera ukwati.’+ 32  Koma ine ndikukuuzani kuti aliyense amene wathetsa ukwati ndi mkazi wake, osati chifukwa cha chiwerewere,* amachititsa kuti mkaziyo achite chigololo akakwatiwanso. Ndipo aliyense amene wakwatira mkazi wosiyidwayo nayenso wachita chigololo.+ 33  Komanso munamva kuti anthu akale anauzidwa kuti: ‘Musamalumbire koma osachita,+ mʼmalomwake muzikwaniritsa zimene mwalonjeza kwa Yehova.’*+ 34  Koma ine ndikukuuzani kuti: Musamalumbire nʼkomwe,+ kutchula kumwamba, chifukwa nʼkumene kuli mpando wachifumu wa Mulungu, 35  kapena kutchula dziko lapansi chifukwa ndi chopondapo mapazi ake,+ kapenanso kutchula Yerusalemu chifukwa ndi mzinda wa Mfumu yamphamvu.+ 36  Musamalumbire potchula mutu wanu, chifukwa simungathe kusandutsa tsitsi lanu, ngakhale limodzi, kuti likhale loyera kapena lakuda. 37  Tangotsimikizani kuti mukati ‘Indeʼ akhaledi inde, ndipo mukati ‘Ayiʼ akhaledi ayi,+ chifukwa mawu owonjezera pamenepa ndi ochokera kwa woipayo.+ 38  Inu munamva kuti anati: ‘Diso kulipira diso, ndi dzino kulipira dzino.’+ 39  Koma ine ndikukuuzani kuti: Musamalimbane ndi munthu woipa, koma wina akakumenyani mbama patsaya lakumanja, muzimupatsanso tsaya linalo.+ 40  Ngati munthu akufuna kukutengera kukhoti kuti akulande malaya ako amkati, uzimupatsanso akunja.+ 41  Ngati munthu waudindo wakulamula kuti umunyamulire katundu mtunda wa kilomita imodzi,* uzimunyamulira mtunda wa makilomita awiri. 42  Munthu akakupempha kanthu uzimupatsa ndipo munthu amene akufuna kukongola* kanthu kwa iwe usamukanize.+ 43  Inu munamva kuti anati: ‘Uzikonda mnzako+ ndipo uzidana ndi mdani wako.’ 44  Koma ine ndikukuuzani kuti: Pitirizani kukonda adani anu+ ndi kupempherera amene akukuzunzani,+ 45  kuti musonyeze kuti ndinudi ana a Atate wanu wakumwamba.+ Chifukwa iye amawalitsira dzuwa lake anthu abwino ndi oipa omwe, ndipo amagwetsera mvula anthu olungama ndi osalungama omwe.+ 46  Ndiye mukamakonda anthu okhawo amene amakukondani, mudzalandira mphoto yotani?+ Kodi okhometsa msonkho sachitanso zomwezo? 47  Ngati mukupereka moni kwa abale anu okha, kodi nʼchiyani chachilendo chimene mukuchita? Kodi anthu a mitundu ina nawonso sachita zomwezo? 48  Choncho khalani angwiro,* mofanana ndi Atate wanu wakumwamba amene ndi wangwiro.”+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “chifukwa mphoto yanu ndi yaikulu kumwamba.”
Gehena ndi malo amene ankawotcherako zinyalala kunja kwa mzinda wa Yerusalemu. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “kwadiranti yomalizira.” Onani Zakumapeto B14.
Mʼchilankhulo choyambirira, “limakupunthwitsa.”
MʼChigiriki por·nei′a. Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kumeneku ndi kukongola popanda kupereka chiwongola dzanja.
Kapena kuti, “khalani okwanira.’ʼ