Wolembedwa ndi Mateyu 26:1-75

  • Ansembe anakonza chiwembu kuti aphe Yesu (1-5)

  • Yesu anathiridwa mafuta onunkhira (6-13)

  • Pasika womaliza komanso kuperekedwa (14-25)

  • Anayambitsa mwambo wa Chakudya Chamadzulo cha Ambuye (26-30)

  • Ananeneratu kuti Petulo adzamukana (31-35)

  • Yesu anapemphera ku Getsemane (36-46)

  • Yesu anagwidwa (47-56)

  • Anazengedwa mlandu ndi Khoti Lalikulu la Ayuda (57-68)

  • Petulo anakana Yesu (69-75)

26  Yesu atamaliza kunena zinthu zonsezi, anauza ophunzira ake kuti:  “Inu mukudziwa kuti Pasika achitika pakangopita masiku awiri+ ndipo Mwana wa munthu aperekedwa kuti akapachikidwe.”+  Pa nthawiyi, ansembe aakulu ndiponso akulu anasonkhana mʼbwalo lapanyumba ya mkulu wa ansembe dzina lake Kayafa.+  Iwo anapangana+ zoti agwire* Yesu mochenjera nʼkumupha.  Koma ankanena kuti: “Tisadzamugwire pachikondwerero kuopera kuti anthu angadzachite chipolowe.”  Pa nthawi imene Yesu anali ku Betaniya mʼnyumba mwa Simoni wakhate,+  kunafika mayi wina atatenga botolo lopangidwa ndi mwala wa alabasitala muli mafuta onunkhira okwera mtengo ndipo anayamba kuthira mafutawo mʼmutu mwa Yesu pamene iye ankadya patebulo.  Ophunzira ake ataona zimenezi anakwiya nʼkunena kuti: “Akuwonongeranji mafutawa?  Mafuta amenewa akanagulitsidwa ndalama zambiri ndipo ndalamazo zikanaperekedwa kwa anthu osauka.” 10  Yesu anadziwa zimenezi ndipo anawauza kuti: “Nʼchifukwa chiyani mukumuvutitsa mayiyu? Iyetu wandichitira zinthu zabwino. 11  Osaukawo muli nawo nthawi zonse,+ koma ine simudzakhala nane nthawi zonse.+ 12  Zimene mayiyu wachita pothira mafuta onunkhirawa pathupi langa, wazichita pokonzekera kuikidwa mʼmanda kwanga.+ 13  Ndithu ndikukuuzani, kulikonse kumene uthenga wabwino udzalalikidwe padziko lonse, anthu azidzanena zimene mayiyu wachita kuti azidzamukumbukira.”+ 14  Kenako mmodzi wa ophunzira 12 aja, amene ankadziwika kuti Yudasi Isikariyoti,+ anapita kwa ansembe aakulu+ 15  nʼkuwafunsa kuti: “Kodi mudzandipatsa chiyani ndikamupereka kwa inu?”+ Iwo anamulonjeza ndalama 30 zasiliva.+ 16  Choncho kuyambira nthawi imeneyo anayesetsa kufunafuna mpata wabwino kuti amupereke. 17  Pa tsiku loyamba la chikondwerero cha Mikate Yopanda Zofufumitsa,+ ophunzira anabwera kwa Yesu nʼkumufunsa kuti: “Kodi mukufuna tikakukonzereni kuti malo odyerako Pasika?”+ 18  Iye anati: “Pitani mumzinda kwa Munthu wakutiwakuti ndipo mukamuuze kuti, ‘Mphunzitsi wanena kuti: “Nthawi yanga yoikidwiratu yayandikira. Ndidzachita phwando la Pasika pamodzi ndi ophunzira anga kunyumba kwako.”’” 19  Choncho ophunzirawo anachitadi mogwirizana ndi zimene Yesu anawauza ndipo anakonza zinthu zonse zofunika pa Pasika. 20  Nthawi yamadzulo,+ iye ndi ophunzira ake 12 aja anakhala patebulo nʼkumadya chakudya.+ 21  Akudya chakudyacho iye ananena kuti: “Ndithu ndikukuuzani, mmodzi wa inu andipereka.”+ 22  Chifukwa chomva chisoni kwambiri ndi zimenezi, aliyense anayamba kumufunsa kuti: “Ambuye, kodi ndine kapena?” 23  Iye anayankha kuti: “Amene akusunsa nane limodzi mʼmbalemu ndi amene andipereke.+ 24  Zoonadi, Mwana wa munthu achoka, mogwirizana ndi zimene Malemba amanena za iye. Koma tsoka+ kwa munthu amene akupereka Mwana wa munthu!+ Zikanakhala bwino kwa munthu ameneyu ngati akanapanda kubadwa.”+ 25  Yudasi amene anali atatsala pangʼono kumupereka anayankha kuti: “Nanga nʼkukhala ine Rabi?” Yesu anamuyankha kuti: “Wanena wekha.” 26  Akupitiriza kudya, Yesu anatenga mkate ndipo atayamika Mulungu, anaunyemanyema+ nʼkuupereka kwa ophunzira ake. Iye ananena kuti: “Eni, idyani. Mkate uwu ukuimira thupi langa.”+ 27  Kenako anatenga kapu ya vinyo ndipo atayamika, anaipereka kwa iwo nʼkunena kuti: “Imwani nonsenu.+ 28  Vinyoyu akuimira ‘magazi anga+ a pangano,’+ amene adzakhetsedwe chifukwa cha anthu ambiri+ kuti machimo awo akhululukidwe.+ 29  Koma ndikukuuzani kuti: Sindidzamwanso chakumwa chilichonse chochokera ku mphesa ngati ichi mpaka tsiku limene ndidzamwe chatsopano limodzi ndi inu mu Ufumu wa Atate wanga.”+ 30  Pamapeto pake, atamaliza kuimba nyimbo zotamanda Mulungu,* anatuluka nʼkupita kuphiri la Maolivi.+ 31  Kenako Yesu anawauza kuti: “Nonsenu muthawa nʼkundisiya ndekha usiku uno, chifukwa Malemba amanena kuti: ‘Ndidzapha mʼbusa ndipo nkhosa zamʼgululo zidzabalalika.’+ 32  Koma ndikadzauka kwa akufa, ndidzatsogola kukafika ku Galileya inu musanafikeko.”+ 33  Koma Petulo anamuyankha kuti: “Ngakhale ena onse atathawa nʼkukusiyani, ine ndekha sindingathawe!”+ 34  Yesu anamuuza kuti: “Ndithudi ndikukuuza iwe, usiku womwe uno tambala asanalire, undikana katatu.”+ 35  Petulo anayankha kuti: “Ngati kuli kufa, ine ndifa nanu limodzi, sindingakukaneni.”+ Ophunzira ena onse ananenanso chimodzimodzi. 36  Kenako Yesu anafika nawo pamalo otchedwa Getsemane,+ ndipo anauza ophunzirawo kuti: “Khalani pansi panopa, ine ndikupita uko kukapemphera.”+ 37  Popita kumeneko anatenga Petulo ndi ana awiri a Zebedayo. Ndipo anayamba kumva chisoni komanso kuvutika kwambiri mumtima mwake.+ 38  Kenako anawauza kuti: “Ine ndikumva chisoni* chofa nacho. Khalani pompano ndipo mukhalebe maso pamodzi ndi ine.”+ 39  Choncho atapita patsogolo pangʼono, anagwada mpaka nkhope yake pansi ndipo anapemphera kuti:+ “Atate wanga, ngati nʼkotheka lolani kuti kapu iyi+ indipitirire. Koma osati mwa kufuna kwanga, koma mwa kufuna kwanu.”+ 40  Atatero anabwerera pamene panali ophunzira ake aja ndipo anawapeza akugona. Choncho anafunsa Petulo kuti: “Zoona simungathe kukhalabe maso limodzi ndi ine kwa ola limodzi?+ 41  Khalani maso+ ndipo mupitirize kupemphera+ kuti musalowe mʼmayesero.+ Zoona, mzimu ndi wofunitsitsa, koma thupi ndi lofooka.”+ 42  Anachokanso kachiwiri nʼkupita kukapemphera kuti: “Atate wanga, ngati sizingatheke kuti kapuyi indipitirire mpaka nditamwa ndithu, zimene inu mukufuna zichitike.”+ 43  Anabweranso nʼkuwapeza akugona, chifukwa zikope zawo zinali zitalemera. 44  Choncho anawasiya nʼkupitanso kukapemphera kachitatu ndipo anabwereza mawu omwe aja. 45  Kenako anabwerera kwa ophunzira aja nʼkuwauza kuti: “Zoona nthawi ngati ino mukugona ndi kupumula? Taonani! Nthawi yoti Mwana wa munthu aperekedwe mʼmanja mwa anthu ochimwa yayandikira. 46  Nyamukani, tiyeni tizipita. Onani! Wondipereka uja ali pafupi.” 47  Mawu adakali mʼkamwa, Yudasi, mmodzi wa ophunzira 12 aja, anafika limodzi ndi gulu lalikulu la anthu kuchokera kwa ansembe aakulu ndi kwa akulu, atanyamula malupanga ndi zibonga.+ 48  Apa nʼkuti womuperekayu atawapatsa chizindikiro chakuti: “Amene ndikamukise ndi yemweyo, mukamugwire.” 49  Atafika, Yudasi analunjika kwa Yesu nʼkunena kuti: “Moni Rabi!” Ndipo anamukisa. 50  Koma Yesu anamufunsa kuti: “Bwanawe, wabwera kudzatani kuno?”+ Nthawi yomweyo iwo anayandikira ndipo anagwira Yesu nʼkumumanga. 51  Koma mmodzi mwa anthu amene anali ndi Yesu anasolola lupanga lake nʼkutema nalo kapolo wa mkulu wa ansembe mpaka kuduliratu khutu lake.+ 52  Ndiyeno Yesu anamuuza kuti: “Bwezera lupanga lako mʼchimake,+ chifukwa onse ogwira lupanga adzafa ndi lupanga.+ 53  Kapena ukuganiza kuti sindingapemphe Atate wanga kuti anditumizire magulu ankhondo oposa 12 a angelo nthawi yomwe ino?+ 54  Koma ndikachita zimenezo, nanga Malemba amene amanena kuti zimenezi ziyenera kuchitika adzakwaniritsidwa bwanji?” 55  Mu ola lomwelo Yesu anafunsa gulu la anthulo kuti: “Bwanji mwabwera kudzandigwira mutatenga malupanga ndi zibonga ngati mukudzalimbana ndi wachifwamba? Tsiku ndi tsiku ndinkakhala pansi mʼkachisi nʼkumaphunzitsa,+ koma simunandigwire.+ 56  Koma zonsezi zachitika kuti zimene aneneri analemba zikwaniritsidwe.”*+ Kenako ophunzira ake onse anamuthawa nʼkumusiya yekha.+ 57  Anthu amene anagwira Yesu aja anapita naye kwa Kayafa+ mkulu wa ansembe, kumene alembi ndi akulu anali atasonkhana.+ 58  Koma Petulo anapitiriza kumutsatira ali chapatali ndithu, mpaka anafika mʼbwalo lapanyumba ya mkulu wa ansembeyo. Atalowa mkati, anakhala pansi limodzi ndi antchito amʼnyumbamo kuti aone zotsatira zake.+ 59  Ndiyeno ansembe aakulu ndi Khoti lonse Lalikulu la Ayuda* ankafunafuna umboni wabodza kuti anamizire Yesu mlandu nʼcholinga choti amuphe.+ 60  Koma sanaupeze ngakhale kuti kunabwera mboni zambiri zabodza.+ Patapita nthawi, kunabwera mboni zina ziwiri 61  nʼkunena kuti: “Munthu ameneyu ananena kuti, ‘Ndikhoza kugwetsa kachisi wa Mulungu nʼkumumanganso mʼmasiku atatu.’”+ 62  Atamva zimenezo mkulu wa ansembe anaimirira nʼkumufunsa kuti: “Kodi suyankha? Kodi sukumva zimene anthuwa akukunenezazi?”+ 63  Koma Yesu anangokhala chete.+ Choncho mkulu wa ansembe anamuuza kuti: “Ndikukulumbiritsa pali Mulungu wamoyo, utiuze ngati ndiwedi Khristu, Mwana wa Mulungu!”+ 64  Yesu anamuyankha kuti: “Mwanena nokha. Koma ndikukuuzani kuti: Kuyambira panopa mpaka mʼtsogolo mudzaona Mwana wa munthu+ atakhala kudzanja lamanja lamphamvu.+ Mudzamuonanso akubwera pamitambo yakumwamba.”+ 65  Kenako mkulu wa ansembe anangʼamba malaya ake akunja nʼkunena kuti: “Wanyoza Mulungu! Nanga tingafunenso mboni zina pamenepa? Pano mwadzimvera nokha mmene akunyozera Mulungu. 66  Ndiye inu mukuona bwanji pamenepa?” Iwo anayankha kuti: “Akuyenera kufa basi.”+ 67  Ndiyeno anayamba kumulavulira kunkhope+ komanso kumumenya nkhonya.+ Ena anamuwomba mbama+ 68  nʼkunena kuti: “Losera tione Khristu iwe. Wakumenya ndi ndani?” 69  Tsopano Petulo anali atakhala pansi mʼbwalolo ndipo mtsikana wina wantchito anabwera kwa iye nʼkunena kuti: “Inunso munali ndi Yesu wa ku Galileyayu!”+ 70  Koma iye anakana pamaso pa onse kuti: “Sindikudziwa zimene ukunena.” 71  Atatuluka nʼkupita pakanyumba kapageti, mtsikana winanso anamuzindikira nʼkuuza ena amene anali pafupi kuti: “Bambo awa anali limodzi ndi Yesu Mnazaretiyu.”+ 72  Apanso Petulo anakana mochita kulumbira ndipo ananena kuti: “Ndithudi munthu ameneyu ine sindikumudziwa ayi!” 73  Patapita kanthawi pangʼono, amene anali ataimirira chapafupi anabwera nʼkuuza Petulo kuti: “Ndithu iwenso uli mʼgulu la ophunzira ake ndipo kalankhulidwe kako kakugwiritsa.” 74  Pamenepo iye anayamba kutemberera ndi kulumbira kuti: “Munthu ameneyu ine sindikumudziwa ayi!” Nthawi yomweyo tambala analira. 75  Ndiyeno Petulo anakumbukira mawu a Yesu aja akuti: “Tambala asanalire, udzandikana katatu.”+ Ndipo anatuluka panja nʼkuyamba kulira mopwetekedwa mtima kwambiri.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “amange.”
Kapena kuti, “masalimo.”
Kapena kuti, “Moyo wanga ukumva chisoni.”
Kapena kuti, “malemba akwaniritsidwe.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Sanihedirini.”