Yesaya 53:1-12
53 Kodi ndi ndani amene wakhulupirira zinthu zimene anamva kwa ife?*+
Ndipo kodi dzanja la Yehova+ laonetsedwa kwa ndani?+
2 Iye adzaphuka ngati nthambi+ pamaso pawinawake* ndiponso ngati muzu wotuluka mʼnthaka youma.
Saoneka ngati munthu wapadera kapena waulemerero,+Ndipo tikamuona, maonekedwe ake si ochititsa chidwi moti ife nʼkukopeka naye.*
3 Iye ananyozedwa ndipo anthu ankamupewa,+Anali munthu amene kupweteka ankakudziwa bwino* ndipo matenda ankawadziwa.
Zinali ngati kuti nkhope yake yabisika kwa ife.*
Ananyozedwa ndipo tinkamuona ngati wopanda pake.+
4 Zoonadi, iye ananyamula matenda athu,+Ndipo anasenza zowawa zathu.+
Koma ifeyo tinkamuona ngati munthu amene wagwidwa ndi matenda, amene walangidwa* ndi Mulungu ndiponso kuzunzidwa.
5 Koma iye anabayidwa+ chifukwa cha zolakwa zathu.+Anaphwanyidwa chifukwa cha zochimwa zathu.+
Analandira chilango kuti ife tikhale pamtendere,+Ndipo chifukwa cha mabala ake ifeyo tinachiritsidwa.+
6 Tonsefe tikungoyendayenda uku ndi uku ngati nkhosa zosochera.+Aliyense akulowera njira yakeNdipo Yehova wachititsa kuti zolakwa za tonsefe zigwere pa ameneyo.+
7 Iye anachitiridwa zankhanza+ ndipo analola kuti azunzidwe,+Koma sanatsegule pakamwa pake.
Anamutengera kumalo oti akamuphere ngati nkhosa,+Mofanana ndi nkhosa yaikazi imene yangokhala chete pamene akufuna kuimeta ubweya,Ndipo sanatsegule pakamwa pake.+
8 Iye anaponderezedwa ndipo anatengedwa popanda kuweruzidwa mwachilungamo.Ndi ndani amene anaganizira tsatanetsatane wa mʼbadwo wa makolo ake?*
Popeza iye anadulidwa mʼdziko la anthu amoyo.+Iye anakwapulidwa* chifukwa cha zolakwa za anthu anga.+
9 Anapatsidwa manda* limodzi ndi anthu oipa,+Ndipo pamene anafa anaikidwa mʼmanda limodzi ndi anthu olemera,*+Ngakhale kuti iye sanalakwe chilichonse*Ndipo mʼkamwa mwake munalibe chinyengo.+
10 Koma Yehova ndi amene anafuna* kuti mtumiki wake aphwanyidwe ndipo anamulola kuti adwale.
Ngati mungapereke moyo wake kuti ukhale nsembe yakupalamula,+Iye adzaona ana ake,* adzakhala ndi moyo kwa nthawi yaitali,+Ndipo kudzera mwa iye, zofuna za* Yehova zidzatheka.+
11 Chifukwa cha kuvutika kwake, iye adzaona zabwino ndipo adzakhutira.
Chifukwa cha zimene mtumiki wanga wolungama akudziwa,+Adzachititsa kuti anthu ambiri azionedwa olungama,+Ndipo adzanyamula zolakwa zawo.+
12 Pa chifukwa chimenechi, ndidzamupatsa gawo pamodzi ndi ambiri,Ndipo iye adzagawana ndi amphamvu katundu amene alanda kunkhondo,Chifukwa anapereka moyo wake*+Ndipo anaikidwa mʼgulu la anthu ochimwa.+Ananyamula tchimo la anthu ambiri+Ndipo analowererapo kuti athandize anthu ochimwa.+
Mawu a M'munsi
^ Mabaibulo ena amati, “zimene ife tinamva.”
^ “Winawake” angaimire munthu wina amene akungoonerera kapena Mulungu.
^ Kapena kuti, “saoneka mwapadera moti nʼkumusirira.”
^ Kapena kuti, “amene ankamvetsa kuti kupweteka nʼchiyani.”
^ Mabaibulo ena amati, “Anali ngati munthu amene anzake amaphimba nkhope zawo akamuona.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “amene wakwapulidwa.”
^ Kapena kuti, “wa zochitika pa moyo wake.”
^ Kapena kuti, “anamenyedwa mpaka kufa.”
^ Kapena kuti, “Ndipo wina adzapereka manda ake.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “munthu wolemera.”
^ Kapena kuti, “sanachite zachiwawa.”
^ Kapena kuti, “zimene zimasangalatsa.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “mbewu zake.”
^ Kapena kuti, “Koma zinamukomera Yehova.”
^ Mʼchilankhulo choyambirira, “anakhuthula moyo wake mu imfa.”

