Kalata Yachiwiri ya Petulo 2:1-22

  • Kudzakhala aphunzitsi abodza (1-3)

  • Umboni wotsimikizira kuti aphunzitsi abodza adzaweruzidwa (4-10a)

    • Angelo anawaponya mu Tatalasi (4)

    • Chigumula; Sodomu ndi Gomora (5-7)

  • Mmene tingadziwire aphunzitsi abodza (10b-22)

2  Komabe pakati pa Aisiraeli, anthu ena anakhala aneneri abodza.* Mofanana ndi zimenezi pakati panu padzakhalanso aphunzitsi abodza.*+ Anthu amenewa adzayambitsa mwachinsinsi timagulu towononga tampatuko ndipo adzakana ngakhale Ambuye wawo amene anawagula.+ Chifukwa chochita zimenezi, iwo adzawonongedwa mofulumira kwambiri.  Kuwonjezera pamenepo, ambiri adzatengera khalidwe lopanda manyazi*+ la aphunzitsi abodzawo ndipo anthu azidzalankhula monyoza njira ya choonadi chifukwa cha aphunzitsiwo.+  Komanso mwadyera azidzagwiritsa ntchito mawu achinyengo nʼcholinga choti akudyereni masuku pamutu. Koma chilango chimene Mulungu anakonza kalelo kuti adzawapatse,+ chikubwera mofulumira ndipo chiwonongeko chawo chidzafika ndithu.+  Ndipotu Mulungu sanalekerere angelo amene anachimwa aja+ osawapatsa chilango. Koma anawaponya mu Tatalasi,*+ anawamanga mumdima wandiweyani podikira kuti adzawaweruze.+  Mulungu sanalekerere dziko lakale lija osalipatsa chilango,+ koma anasunga Nowa, yemwe ankalalikira za chilungamo cha Mulungu.+ Anamupulumutsa limodzi ndi anthu enanso 7,+ pamene anabweretsa chigumula padziko la anthu osaopa Mulungu.+  Anawononganso mizinda ya Sodomu ndi Gomora poitentha ndi moto.+ Anachita zimenezi kuti likhale chenjezo kwa anthu osaopa Mulungu la zimene zidzawachitikire mʼtsogolo.+  Koma anapulumutsa Loti yemwe anali munthu wolungama.+ Loti ankavutika kwambiri mumtima chifukwa cha khalidwe lopanda manyazi* limene anthu ophwanya malamulo ankachita.  (Munthu wolungamayu ankavutika mumtima tsiku ndi tsiku chifukwa cha zimene ankaona ndiponso kumva pamene ankakhala pakati pa anthu oipa. Iye ankavutika mumtima chifukwa cha zochita zawo zosamvera malamulo.)  Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova* amadziwa kupulumutsa anthu odzipereka kwa iye akakhala pa mayesero.+ Koma anthu osalungama amawasunga kuti adzawawononge pa tsiku lopereka chiweruzo,+ 10  makamaka anthu amene amafunafuna anthu ena nʼcholinga choti awaipitse pogonana nawo+ ndiponso amene amanyoza olamulira.+ Anthu amenewa saopa chilichonse komanso amamva zawo zokha. Iwo sachita mantha kulankhula zinthu zonyoza anthu amene Mulungu wawapatsa ulemerero. 11  Koma angelo, ngakhale kuti ndi amphamvu kwambiri, saneneza aphunzitsi abodzawo ndi mawu onyoza, chifukwa angelewo amalemekeza Yehova.*+ 12  Ndipo anthu amenewa, mofanana ndi nyama zopanda nzeru zimene zimangochita zinthu mwachibadwa komanso zimabadwa kuti zidzagwidwe ndi kuwonongedwa, amalankhula monyoza za zinthu zimene sakuzidziwa.+ Anthu amenewa adzawonongedwa chifukwa cha zochita zawo zoipa, 13  ndipo akukumana ndi mavuto monga mphoto ya zochita zawo zoipa. Iwo amaona kuti kuchita zinthu zimene amalakalaka nʼkosangalatsa,+ ngakhale atamazichita masana. Anthu amenewa ali ngati mawanga ndi litsiro lothimbirira pakati panu, ndipo amasangalala mopitirira malire akamakuphunzitsani zinthu zabodza pamene akudya nanu limodzi.+ 14  Amalakalaka kwambiri kuchita chigololo*+ komanso amalephera kupewa tchimo, ndipo amakopa anthu achikhulupiriro chosalimba. Ali ndi mtima wophunzitsidwa dyera. Iwo ndi ana otembereredwa. 15  Asocheretsedwa chifukwa anasiya njira yowongoka. Atsatira njira ya Balamu+ mwana wa Beori, amene anachita zinthu zoipa chifukwa chofunitsitsa kulandira mphoto,+ 16  koma anadzudzulidwa chifukwa cholephera kuchita zinthu zabwino.+ Bulu amene salankhula, analankhula ngati munthu nʼkulepheretsa zochita zamisala za mneneriyo.+ 17  Amenewa ndi akasupe opanda madzi komanso nkhungu yotengeka ndi mphepo yamkuntho, ndipo anawasungira mdima wandiweyani.+ 18  Amalankhula mawu odzitukumula opanda pake. Ndipo amagwiritsa ntchito zilakolako za thupi+ komanso khalidwe lopanda manyazi* pokopa anthu amene angothawa kumene kwa anthu ochita zoipa.+ 19  Ngakhale kuti akuwalonjeza ufulu, eni akewo ndi akapolo a khalidwe loipa.+ Chifukwa aliyense amene wagonjetsedwa ndi winawake, amakhala kapolo wa womugonjetsayo.*+ 20  Ndithudi, ngati anapulumuka ku zodetsa za dzikoli+ chifukwa chodziwa molondola Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu, koma nʼkuyambiranso kuchita zinthu zomwe zija mpaka kugonjetsedwa nazo, makhalidwe awo amakhala oipa kwambiri kuposa poyamba.+ 21  Zikanakhala bwino akanapanda kudziwa molondola njira ya chilungamo, kusiyana nʼkuidziwa bwinobwino kenako nʼkupatuka pa malamulo oyera omwe analandira.+ 22  Mwambi woona uja wakwaniritsidwa pa iwo. Mwambiwo umati: “Galu wabwerera ku masanzi ake, ndipo nkhumba imene inasambitsidwa yapita kukagubudukanso mʼmatope.”+

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “aphunzitsi onyenga.”
Kapena kuti, “aneneri onyenga.”
Kapena kuti “adzatengera zochita zawo zosonyeza khalidwe lopanda manyazi.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Mʼchilankhulo choyambirira, “Maso awo ndi odzaza ndi chigololo.”
Kapena kuti, “komanso zochita zawo zosonyeza khalidwe lopanda manyazi.” Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “amene wagonjetsedwa ndi chinachake, amakhala kapolo wa chinthucho.”