Kalata Yachiwiri ya Petulo 1:1-21

  • Moni (1)

  • Mupitirizebe kukhala pakati pa anthu oitanidwa (2-15)

    • Makhalidwe ofunika kuwonjezera pa chikhulupiriro (5-9)

  • Mawu aulosi adzakwaniritsidwa (16-21)

1  Ndine Simoni Petulo, kapolo komanso mtumwi wa Yesu Khristu. Ndikulembera anthu amene apeza chikhulupiriro chamtengo wapatali chofanana ndi chathu kudzera mʼchilungamo cha Mulungu wathu ndiponso cha Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.  Kukoma mtima kwakukulu kwa Mulungu ndi mtendere wake ziwonjezereke kwa inu. Kuti zimenezi zitheke, muyenera kudziwa molondola+ Mulungu komanso Yesu Ambuye wathu.  Pogwiritsa ntchito mphamvu yake, Mulungu watipatsa kwaulere zonse zofunikira kuti tikhale ndi moyo komanso kuti tikhale odzipereka kwa iye. Zimenezi zatheka chifukwa chodziwa molondola za Mulungu amene anatiitana+ kudzera mu ulemerero ndi ubwino wake.  Kudzera mʼzinthu zimenezi, iye watilonjeza zinthu zamtengo wapatali ndi zazikulu kwambiri,+ kuti mogwirizana ndi malonjezo amenewa mukhale ndi ulemerero umene Mulungu ali nawo.+ Wachita zimenezi chifukwa tinasiya kuchita makhalidwe oipa amʼdzikoli amene amayamba chifukwa cholakalaka zinthu zoipa.  Chifukwa cha zimenezi, yesetsani mwakhama+ kuwonjezera makhalidwe abwino+ pa chikhulupiriro chanu, pa makhalidwe anu abwino muwonjezerepo kudziwa zinthu,+  pa kudziwa zinthu kudziletsa,+ pa kudziletsa kupirira, pa kupirira kudzipereka kwa Mulungu,+  pa kudzipereka kwa Mulungu kukonda abale, pa kukonda abale, chikondi.+  Mukamachita zinthu zonsezi komanso mukamasonyeza kwambiri makhalidwewa, mudzagwiritsa ntchito zinthu zimene mukuzidziwa molondola zokhudza Ambuye wathu Yesu Khristu ndipo zidzakuthandizani kuti musamangokhala kapena kulephera kubereka zipatso.+  Munthu amene alibe makhalidwe amenewa ndi wakhungu, watseka maso ake kuti asaone kuwala+ ndipo waiwala kuti anayeretsedwa ku machimo+ omwe ankachita kalekale. 10  Choncho abale, chitani chilichonse chotheka kuti mukhalebe okhulupirika, nʼcholinga choti mupitirizebe kukhala pakati pa anthu amene Mulungu wawaitana+ ndi kuwasankha. Mukapitiriza kuchita zimenezi, simudzalephera ngakhale pangʼono.+ 11  Ndipotu mudzadalitsidwa kwambiri moti mudzalowa mwaulemerero mu Ufumu wosatha+ wa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Khristu.+ 12  Pa chifukwa chimenechi, ndikufuna kuti ndizikukumbutsani zinthu zimenezi nthawi zonse, ngakhale kuti mukuzidziwa kale ndipo ndinu olimba mʼchoonadi chimene munaphunzira. 13  Choncho ndikuona kuti ndi bwino kuti ndizikugwedezani pokukumbutsani zimenezi+ pamene ndidakali mʼthupi langali, lomwe lili ngati msasa.*+ 14  Ndikuona choncho chifukwa ndikudziwa kuti ndatsala pangʼono kutuluka mumsasa wangawu, mogwirizana ndi mmene Ambuye wathu Yesu Khristu anandiuzira.+ 15  Nthawi zonse ndiziyesetsa kukukumbutsani kuti ndikadzachoka muzidzatha kukumbukira nokha zinthu zimenezi. 16  Pamene tinkakudziwitsani za mphamvu za Ambuye wathu Yesu Khristu komanso zokhudza kukhalapo* kwake, sitinatengere nkhani zabodza zimene anthu amapeka mochenjera. Koma tinakuuzani zinthu zokhudza ulemerero wake zimene tinachita kuona ndi maso athu.+ 17  Chifukwa Khristu analandira ulemu ndi ulemerero kuchokera kwa Mulungu, Atate wathu, pamene mawu anamveka kwa iye kuchokera mu ulemerero waukulu kuti: “Uyu ndi Mwana wanga wokondedwa, amene amandisangalatsa kwambiri.”+ 18  Tinamva mawu amenewa kuchokera kumwamba pamene tinali naye limodzi mʼphiri loyera. 19  Nʼchifukwa chake sitikayikira ngakhale pangʼono kuti mawu aulosiwa adzakwaniritsidwa ndipo mukuchita bwino kuwaganizira mozama. Mawu amenewa aziwala mʼmitima yanu ngati nyale+ imene ikuwala mumdima. Pitirizani kuchita zimenezi mpaka mʼbandakucha, nthanda*+ itatuluka. 20  Inu mukudziwa mfundo yofunika yakuti, palibe ulosi wa mʼMalemba umene umachokera mʼmaganizo a munthu. 21  Chifukwa ulosi sunachokere kwa anthu,+ koma anthuwo analankhula mawu ochokera kwa Mulungu motsogoleredwa* ndi mzimu woyera.+

Mawu a M'munsi

Mawuwa amatanthauza malo amene munthu akukhala mongoyembekezera ndipo Petulo anawagwiritsa ntchito mophiphiritsa ponena za thupi lake.
“Nthanda” ndi nyenyezi yomalizira kutuluka imene imaonekera dzuwa likangotsala pangʼono kutuluka.
Mʼchilankhulo choyambirira, “motengedwa; mokankhidwa.”