Salimo 2:1-12

  • Yehova ndi wodzozedwa wake

    • Yehova adzaseka mitundu ya anthu (4)

    • Yehova anasankha mfumu yake (6)

    • Lemekezani mwanayo (12)

2  Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akuchita zipolowe,Ndiponso nʼchifukwa chiyani mitundu ya anthu ikungʼungʼudza za chinthu chopanda pake?*+   Mafumu a dziko lapansi aima pamalo awo,Ndipo anthu olemekezeka asonkhana pamodzi* mogwirizana+Kuti alimbane ndi Yehova komanso wodzozedwa wake.*+   Iwo akunena kuti: “Tiyeni tidule zomangira zawo,Ndipo titaye zingwe zawo!”   Amene wakhala pampando wachifumu kumwamba adzaseka.Yehova adzawanyogodola.   Pa nthawiyo, adzalankhula nawo atakwiya,Ndipo adzawachititsa mantha ndi mkwiyo wake.   Iye adzawauza kuti: “Inetu ndasankha mfumu yanga+Ndipo ikulamulira ku Ziyoni,+ phiri langa lopatulika.”   Ndifotokoza zimene Yehova wanena.Iye wandiuza kuti: “Iwe ndiwe mwana wanga,+Lero, ine ndakhala bambo ako.+   Tandipempha, ndipo ndikupatsa mitundu ya anthu kuti ikhale cholowa chako,Ndiponso dziko lonse lapansi kuti likhale lako.+   Mitunduyo udzaiphwanya ndi ndodo yachifumu yachitsulo,+Ndipo udzaiswa ngati chiwiya chadothi.”+ 10  Tsopano inu mafumu, sonyezani kuzindikira,Mverani malangizo,* inu oweruza a dziko lapansi. 11  Tumikirani Yehova mwamantha,Ndipo muzisangalala komanso kunjenjemera pamaso pake. 12  Mulemekezeni* mwanayo+ kuopera kuti Mulungu angakwiye,Ndipo mungawonongedwe nʼkuchotsedwa panjira yachilungamo,+Chifukwa mkwiyo wake umayaka mofulumira. Osangalala ndi anthu onse amene amathawira kwa iye.

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “ikuganizira kuchita chinthu chopanda pake.”
Kapena kuti, “akukambirana.”
Kapena kuti, “Khristu wake.”
Kapena kuti, “mverani chenjezo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Mukiseni.”