Salimo 3:1-8

  • Kudalira Mulungu ngakhale kuti tikukumana ndi mavuto

    • ‘Nʼchifukwa chiyani adani achuluka chonchi?’ (1)

    • “Chipulumutso chimachokera kwa Yehova” (8)

Nyimbo ya Davide pamene ankathawa mwana wake Abisalomu.+ 3  Inu Yehova, nʼchifukwa chiyani adani anga achuluka chonchi?+ Nʼchifukwa chiyani anthu ambiri akundiukira?+   Anthu ambiri akunena za ine* kuti: “Mulungu samupulumutsa ameneyu.”+ (Selah)*   Koma inu Yehova, mumanditeteza mbali zonse+ ngati chishango,Ndinu ulemerero wanga+ komanso ndinu amene mumatukula mutu wanga.+   Ndidzaitana Yehova mokweza,Ndipo iye adzandiyankha mʼphiri lake loyera.+ (Selah)   Ine ndidzagona pansi nʼkupeza tulo,Ndipo ndidzadzuka ndili wotetezeka,Chifukwa Yehova akupitiriza kundithandiza.+   Sindikuopa anthu masauzandemasauzandeAmene andizungulira kumbali zonse kuti andiukire.+   Nyamukani, inu Yehova! Ndipulumutseni+ inu Mulungu wanga! Mudzamenya adani anga onse pachibwano.Mudzaphwanya mano a anthu oipa.+   Chipulumutso chimachokera kwa Yehova.+ Madalitso anu ali pa anthu anu. (Selah)

Mawu a M'munsi

Kapena kuti, “za moyo wanga.”