Salimo 94:1-23

  • Pemphero lopempha kuti Mulungu abwezere adani

    • “Kodi anthu oipa adzapitiriza kusangalala mpaka liti?” (3)

    • Kulangizidwa ndi Ya nʼkosangalatsa (12)

    • Mulungu sadzataya anthu ake (14)

    • “Akuyambitsa mavuto pogwiritsa ntchito malamulo” (20)

94  Inu Yehova, Mulungu amene amabwezera anthu oipa,+Inu Mulungu amene amabwezera anthu oipa, onetsani kuwala kwanu!   Nyamukani, inu Woweruza dziko lapansi.+ Perekani chilango kwa anthu onyada chifukwa cha zimene achita.+   Inu Yehova, kodi anthu oipa adzapitiriza kusangalala mpaka liti?Adzapitiriza kukondwera mpaka liti?+   Zolankhula zawo zimasonyeza kuti ndi opusa komanso onyada.Anthu onse ochita zoipa amalankhula modzitama.   Iwo amaphwanya anthu anu, inu Yehova,+Ndipo amapondereza cholowa chanu.   Amapha mkazi wamasiye komanso mlendo,Ndipo amaphanso ana amasiye.   Iwo amanena kuti: “Ya sakuona,+Ndipo Mulungu wa Yakobo sakudziwa zimene zikuchitika.”+   Zindikirani izi, anthu opanda nzeru inu.Anthu opusa inu, kodi mudzasonyeza liti kuti ndinu ozindikira?+   Kodi amene anapanga* makutu, sangamve? Kodi amene anapanga maso, sangaone?+ 10  Kodi amene amalangiza mitundu ya anthu, sangathe kudzudzula?+ Iye ndi amene amaphunzitsa anthu kuti akhale ozindikira.+ 11  Yehova amadziwa maganizo a anthu,Amadziwa kuti ali ngati mpweya.+ 12  Wosangalala ndi munthu amene inu Ya, mumamulangiza,+Amene inu mumamuphunzitsa chilamulo chanu,+ 13  Kuti mumupatse mtendere pa nthawi ya masoka,Mpaka dzenje la oipa litakumbidwa.+ 14  Yehova sadzataya anthu ake,+Kapena kusiya cholowa chake.+ 15  Chifukwa oweruza adzayambiranso kupereka zigamulo zachilungamo,Ndipo onse owongoka mtima adzazitsatira. 16  Ndi ndani amene adzanditeteze kwa oipa? Ndi ndani amene adzakhale kumbali yanga polimbana ndi anthu ochita zoipa? 17  Yehova akanapanda kundithandiza,Bwenzi nditafa* kalekale.+ 18  Pamene ndinanena kuti: “Phazi langa likuterereka,” Chikondi chanu chokhulupirika, inu Yehova, chinapitiriza kundithandiza.+ 19  Nkhawa zitandichulukira,*Munanditonthoza komanso kundisangalatsa.*+ 20  Kodi inu mungagwirizane ndi olamulira achinyengoPamene akuyambitsa mavuto pogwiritsa ntchito malamulo?+ 21  Iwo amaukira mwankhanza munthu wolungama,*+Ndipo munthu wosalakwa amamuweruza kuti akuyenera kuphedwa.*+ 22  Koma Yehova adzakhala malo anga othawirako otetezeka,*Mulungu wanga ndi thanthwe langa lothawirako.+ 23  Iye adzachititsa kuti zoipa zimene akuchita zibwerere kwa iwo.+ Iye adzawawononga* pogwiritsa ntchito zoipa zawo zomwe. Yehova Mulungu wathu adzawawononga.*+

Mawu a M'munsi

Mʼchilankhulo choyambirira, “anadzala.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “nditatsikira kuli chete.”
Kapena kuti, “Maganizo osautsa atandichulukira;” “Nkhawa zitandichulukira mumtima mwanga.”
Kapena kuti, “Mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “Ndipo magazi a munthu wosalakwa amawaweruza kuti ndi olakwa (oipa).”
Kapena kuti, “moyo wa munthu wolungama.”
Kapena kuti, “malo okwezeka achitetezo.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzawakhalitsa chete.”
Mʼchilankhulo choyambirira, “adzawakhalitsa chete.”