Salimo 134:1-3

  • Kutamanda Mulungu usiku

    • “Muzikhala oyera mukamapemphera mutakweza manja anu” (2)

Nyimbo Yokwerera Kumzinda. 134  Tamandani Yehova,Inu nonse atumiki a Yehova,+Inu amene mumaimirira mʼnyumba ya Yehova usiku.+  2  Muzikhala oyera mukamapemphera mutakweza manja anu*+Ndipo muzitamanda Yehova.  3  Yehova, amene anapanga kumwamba ndi dziko lapansi,Akudalitseni ali ku Ziyoni.

Mawu a M'munsi

Mabaibulo ena amati, “Kwezani manja anu mʼmalo opatulika.”