Salimo 59:1-17
Kwa wotsogolera nyimbo. Nyimboyi iimbidwe motsatira kaimbidwe ka nyimbo yakuti “Musandiwononge.” Salimo la Davide. Mikitamu.* Pa nthawi imene Sauli anatumiza anthu kukadikirira nyumba yake kuti amuphe.+
59 Inu Mulungu wanga, ndipulumutseni kwa adani anga.+Nditetezeni kwa anthu amene akundiukira.+
2 Ndilanditseni kwa anthu ochita zoipa,Ndipo ndipulumutseni kwa anthu achiwawa.*
3 Inu Yehova, taonani! Iwo amandidikirira panjira.+Anthu amphamvu amandiukiraKoma osati chifukwa chakuti ndapanduka kapena kuchita tchimo lililonse.+
4 Ngakhale kuti sindinalakwe chilichonse, iwo akuthamanga ndipo akukonzekera kundiukira.
Nyamukani pamene ine ndikuitana kuti muone zimene zikundichitikira.
5 Chifukwa inu Yehova, Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba, ndinu Mulungu wa Isiraeli.+
Nyamukani ndipo muone zimene mitundu yonse ya anthu ikuchita.
Musasonyeze chifundo kwa aliyense woipa komanso wachiwembu.+ (Selah)
6 Amabwera madzulo aliwonse.+Amauwa ngati agalu+ ndipo amazungulira mzinda wonse.+
7 Tamverani zimene zikutuluka pakamwa pawo.Milomo yawo ili ngati malupanga,+Chifukwa iwo akuti: “Ndani akumvetsera?”+
8 Koma inu Yehova, mudzawaseka.+Mudzanyoza mitundu yonse ya anthu.+
9 Inu Mphamvu yanga, ndidzayangʼanabe kwa inu.+Chifukwa Mulungu ndi malo anga othawirako otetezeka.*+
10 Mulungu amene amandisonyeza chikondi chokhulupirika adzandithandiza.+Mulungu adzachititsa kuti ndione adani anga atagonja.+
11 Musawaphe, kuti anthu a mtundu wanga asaiwale.
Ndi mphamvu zanu achititseni kuti aziyendayenda,Achititseni kuti agwe, inu Yehova, chishango chathu.+
12 Chifukwa cha tchimo lapakamwa pawo ndi mawu a milomo yawo,Ndiponso chifukwa cha mawu otukwana komanso achinyengo amene amalankhula,+Akodwe ndi kunyada kwawoko.
13 Muwawononge onse mutakwiya.+Muwawononge kuti asakhaleponso.Muwadziwitse kuti Mulungu akulamulira mbadwa za Yakobo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.+ (Selah)
14 Asiyeni abwerenso madzulo.Asiyeni auwe ngati agalu ndipo azizungulira mzinda wonse.+
15 Asiyeni aziyendayenda kufunafuna chakudya.+Musalole kuti akhute kapena kupeza malo ogona.
16 Koma ine, ndidzaimba za mphamvu zanu.+Mʼmawa ndidzanena mosangalala za chikondi chanu chokhulupirika.
Chifukwa inu ndinu malo anga othawirako otetezeka,+Ndiponso malo anga othawirako pa nthawi ya mavuto.+
17 Inu Mphamvu yanga, ndidzakuimbirani nyimbo zokutamandani,+Chifukwa Mulungu ndi malo anga othawirako otetezeka, Mulungu amene amandisonyeza chikondi chokhulupirika.+
Mawu a M'munsi
^ Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
^ Kapena kuti, “ofunitsitsa kukhetsa magazi.”
^ Kapena kuti, “malo okwezeka achitetezo.”